Yesaya 46 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 46:1-13

Za Kupasuka kwa Babuloni ndi Mafano Ake

1Beli wagwada pansi, Nebo wawerama;

nyama zonyamula katundu za nyamula milungu yawo.

Mafano awo asanduka katundu wolemera pa msana pa ngʼombe.

Asandukadi ngati katundu pa msana pa nyama zotopa.

2Nyamazo zikuwerama ndi kufuna kugwa ndi milunguyo;

sizikutha kupulumutsa katunduyo,

izo zomwe zikupita ku ukapolo.

3Mverani Ine, Inu nyumba ya Yakobo,

inu nonse otsala a mʼnyumba ya Israeli,

Ine ndakhala ndi kukusamalirani kuyambira mʼmimba ya amayi anu,

ndakhala ndikukunyamulani chibadwire chanu.

4Mpaka pamene mudzakalambe ndi kumera imvi

ndidzakusamalirani ndithu.

Ndinakulengani ndipo ndidzakunyamulani,

ndidzakusamalirani ndi kukulanditsani.

5“Kodi inu mudzandifanizira ndi yani, kapena mufananitsa ndi yani?

Kodi mudzandiyerekeza kapena kundifanizitsa ndi yani?

6Anthu ena amakhuthula golide mʼzikwama zawo

ndipo amayeza siliva pa masikelo;

amalemba ntchito mʼmisiri wosula kuti awapangire mulungu,

kenaka iwo amagwada pansi ndikupembedza kamulunguko.

7Amanyamula nʼkumayenda nayo milunguyo pa mapewa awo;

amayikhazika pa malo pake ndipo imakhala pomwepo.

Singathe kusuntha pamalo pakepo.

Ngakhale wina apemphere kwa milunguyo singathe kuyankha;

kapena kumupulumutsa ku mavuto ake.

8“Kumbukirani zimenezi ndipo muchite manyazi,

Muzilingalire mu mtima, inu anthu owukira.

9Kumbukirani zinthu zakale zinthu zamakedzana;

chifukwa Ine ndine Mulungu

ndipo palibe wina ofanana nane.

10Ndinaneneratu zakumathero kuchokera pachiyambi pomwe.

Kuyambira nthawi yamakedzana ndinaloseratu zoti zidzachitike.

Ndikanena zimene ndifuna kuchita ndipo zimachitikadi.

Chilichonse chimene ndafuna ndimachichita.

11Ndikuyitana chiwombankhanga kuchokera kummawa.

Ndikuyitana kuchokera ku dziko lakutali munthu amene adzakwaniritsa cholinga changa.

Zimene ndanena ndidzazikwaniritsadi;

zimene ndafuna ndidzazichitadi.

12Ndimvereni, inu anthu owuma mtima,

inu amene muli kutali ndi chipulumutso.

13Ndikubweretsa pafupi tsiku la chipulumutso changa;

sichili kutali.

Tsikulo layandikira

ndipo sindidzachedwa kukupulumutsani

ndi kupereka ulemerero wanga kwa Israeli.