Yesaya 44 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 44:1-28

Israeli Wosankhidwa wa Yehova

1Yehova akuti, “Mvera tsopano, iwe Yakobo, mtumiki wanga,

Israeli, amene ndinakusankha.

2Yehova

amene anakupanga iwe, anakuwumba iwe mʼmimba ya amayi ako,

ndi amene adzakuthandiza iwe. Iye akuti,

Usachite mantha, iwe Yakobo, mtumiki wanga,

Yesuruni, amene ndinakusankha.

3Pakuti ndidzathira madzi pa nthaka yowuma,

ndi kuyendetsa mitsinje mʼdziko lowuma;

ndidzatumiza Mzimu wanga pa ana anu,

ndi kutsitsa madalitso anga pa zidzukulu zanu.

4Iwo adzakula ngati udzu wothirira bwino

ndi ngati bango lomera mʼmbali mwa mitsinje ya madzi oyenda.

5Wina adzanena kuti, ‘Ine ndine wa Yehova;’

wina adzadzitcha yekha wa banja la Yakobo;

winanso adzalemba pa dzanja lake, ‘Wa Yehova’

ndipo adzadzitcha wa banja la Israeli.

Yehova, Osati Mafano

6“Yehova Mfumu

ndi Mpulumutsi wa Israeli, Yehova Wamphamvuzonse akuti:

Ine ndine woyamba ndi wotsiriza;

palibenso Mulungu wina koma Ine ndekha.

7Ndani nanga angafanane ndi Ine? Muloleni kuti ayankhule.

Muloleni andifotokozere ndi kundiyalira bwino lomwe

zimene zinachitika kuyambira pamene ndinkakhazikitsa anthu anga akalekale,

ndi ziti zimene zidzachitike;

inde, muloleni alosere zimene zikubwera.

8Musanjenjemere, musachite mantha.

Kodi sindinakuwuzeni zimenezi ndi kuzilosera kalekale lomwe?

Inu ndinu mboni zanga. Kodi aliponso Mulungu wina kupatula Ine?

Ayi, palibe Thanthwe linanso limene sindikulidziwa.”

9Onse amene amapanga mafano ngachabe,

ndipo milungu imene amayilemekeza ndi yopanda phindu.

Iwo amene amapembedza mafano ndi wosaona;

ndipo sazindikira kanthu. Choncho adzawachititsa manyazi.

10Ndani amasema mulungu ndi kuwumba fano,

limene silingamupindulire?

11Iye pamodzi ndi anzake onse adzawachititsa manyazi;

amisiri a mafano ndi anthu chabe.

Aloleni onse asonkhane ndi kuyima pabwalo la milandu;

onse adzaopsedwa ndipo adzachita manyazi.

12Mmisiri wa zitsulo amatenga chitsulo

ndipo amachiyika pa makala amoto;

ndi dzanja lake lamphamvu

amachisula pochimenya ndi nyundo.

Pambuyo pake mʼmisiri uja amamva njala natha mphamvu;

iye samwa madzi, ndipo amalefuka.

13Mmisiri wa matabwa nayenso amayeza mtengo ndi chingwe

ndipo amajambula chithunzi ndi cholembera;

amasema bwinobwino ndi chipangizo chake

ndipo amachiwongola bwino ndi chida chake.

Amachipanga ngati munthu,

munthu wake wokongola

kuti aliyike mʼnyumba yake yachipembedzo.

14Amagwetsa mitengo ya mkungudza,

mwinanso amatenga mtengo wa payini kapena wa thundu

nʼkudzisankhira mtengo wabwino pakati pa mitengo ya mʼnkhalango,

ndipo amadzala mtengo wa payini ndi kuwuleka kuti ukule ndi mvula.

15Mitengoyo munthu amachitako nkhuni;

nthambi zina amasonkhera moto wowotha,

amakolezera moto wophikira buledi

ndi mbali ina ya mtengowo amapangira mulungu ndipo amapembedza;

iye amapanga fano ndi kumaligwadira.

16Chigawo china cha mtengowo amasonkhera moto

wowotcherapo nyama imene

amadya, nakhuta.

Iye amawotha motowo ndipo amanena kuti,

“Aa! Ndikumva kutentha; pano pali moto.”

17Chigawo chotsala amapanga kamulungu, fano lake limenelo;

amaligwadira ndi kulipembedza.

Amapemphera kwa fanolo ndipo amanena kuti,

“Iwe ndiwe mulungu wanga, ndipulumutse.”

18Anthu otere sadziwa kanthu, samvetsa kanthu kalikonse;

maso awo ndi omatirira ndipo sangathe kuona,

ndipo mitu yawo ndi yogontha kotero sangathe kumvetsa.

19Palibe amene amayima nʼkulingalira.

Palibe wanzeru kapena womvetsa zinthu bwino woti nʼkunena kuti,

chigawo china cha mtengowo ndinasonkhera moto;

pa makala ake ndinaphikira buledi,

ndinawotchapo nyama ndipo ndinadya.

Chigawo chotsalachi ndipangire chinthu chonyansachi.

Kodi ndidzagwadira mtengo?

20Munthu wotere ali ngati wodya phulusa, maganizo ake opusa amusocheretsa;

motero kuti sangathe kudzipulumutsa yekha kapena kudzifunsa kuti,

“Kodi chinthu chili mʼmanja mwangachi si chabodza?”

21Yehova akuti, “Iwe Yakobo, kumbukira zinthu izi

popeza kuti ndiwe mtumiki wanga, iwe Israeli.

Ine ndinakupanga iwe, ndiwe mtumiki wanga;

iwe Israeli, sindidzakuyiwala.

22Ndachotsa zolakwa zako ngati mitambo,

ndi machimo ako ngati nkhungu ya mmawa.

Bwerera kwa Ine,

popeza ndakupulumutsa.”

23Imbani mwachimwemwe, inu zolengedwa zamlengalenga, pakuti Yehova wachita zimenezi;

fuwula, iwe dziko lapansi.

Imbani nyimbo, inu mapiri,

inu nkhalango ndi mitengo yonse,

chifukwa Yehova wawombola Yakobo,

waonetsa ulemerero wake mwa Israeli.

Anthu Adzakhalanso mu Yerusalemu

24Yehova Mpulumutsi wanu, amene

anakuwumbani mʼmimba ya amayi anu akuti:

“Ine ndine Yehova,

amene anapanga zinthu zonse,

ndinatambasula ndekha zinthu zakuthambo,

ndinayala ndekha dziko lapansi.

25Ndine amene ndinalepheretsa mipingo ya anthu onyenga,

ndipo ndimapusitsa owombeza mawula.

Ndimasokoneza anthu a nzeru,

ndi kuonetsa kuti nzeru zawo nʼzopusa.

26Ndine amene ndimatsimikiza mawu a atumiki ake

ndi kukwaniritsa zimene analosera amithenga ake.

“Ndine amene ndinanena za Yerusalemu kuti mudzakhalanso anthu.

Ndinanenanso za mizinda ya Yuda kuti idzamangidwanso.

Za mabwinja awo ndinanena kuti ndidzawawutsanso.

27Ndine amene ndinawuza nyanga yayikulu kuti, ‘Uma’

ndipo ndidzawumitsa mitsinje yako.

28Ndine amene ndinanena kwa Koresi kuti, ‘Iye ndiye mʼbusa wanga,’

ndipo adzachita zonse zimene ndikufuna;

iye adzalamula kuti, ‘Yerusalemu amangidwenso’

ndi kuti, ‘Maziko a Nyumba ya Mulungu ayikidwenso.’ ”