Yesaya 26 – CCL & ASCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 26:1-21

Nyimbo ya Matamando

1Tsiku limenelo anthu a mʼdziko la Yuda adzayimba nyimbo iyi.

Tili ndi mzinda wolimba.

Mulungu amawuteteza ndi zipupa

ndi malinga.

2Tsekulani zipata za mzinda

kuti mtundu wolungama

ndi wokhulupirika ulowemo.

3Inu mudzamupatsa munthu

wa mtima wokhazikika

mtendere weniweni.

4Mudalireni Yehova mpaka muyaya,

chifukwa Yehova Mulungu ndiye Thanthwe losatha.

5Iye amatsitsa anthu amene amadziyika pamwamba,

iye amagwetsa pansi mzinda wodzitukumula,

amagumula makoma ake

ndi kuwagwetsa pansi pa fumbi penipeni.

6Mapazi a anthu akuwupondereza,

mapazi a anthu oponderezedwa,

mapazi anthu osauka.

7Njira ya munthu wolungama ndi yosalaza,

Inu Wolungamayo, mumasalaza njira ya wolungama.

8Inde Yehova, timayenda mʼnjira zanu zolungama,

ife timayembekezera Inu;

mitima yathu imakhumba kukumbukira

ndi kulemekeza dzina lanu.

9Moyo wanga umalakalaka Inu usiku wonse;

nthawi yammawa ndimafunafuna Inu.

Pamene muweruza dziko lapansi

anthu amaphunzira kuchita chilungamo.

10Ngakhale mukomere mtima anthu oyipa,

saphunzira chilungamo.

Amachita zoyipa mʼdziko la chilungamo,

ndipo sazindikira ululu wa Yehova.

11Inu Yehova, mwatukula dzanja lanu kuti muwalange,

koma iwo sakuliona dzanjalo.

Aloleni anthu aone ndi kuchita manyazi poona mmene mukondera anthu anu;

ndipo moto umene mwasonkhera adani anu uwapsereze.

12Yehova, mumatipatsa mtendere;

ndipo zonse zimene ife tinazichita munatichitira ndinu.

13Inu Yehova Mulungu wathu, ngakhale takhala tikulamulidwa ndi ena mʼmalo mwanu,

koma ife timalemekeza dzina lanu lokha.

14Iwo tsopano sadzadzukanso;

mizimu yawo sidzabwera kudzativutitsa

pakuti mwawalanga ndipo mwawawononga;

palibenso amene amawakumbukira.

15Inu Yehova, mwaukulitsa mtundu wathu;

mwauchulukitsa ndithu

ndipo mwalandirapo ulemu;

mwaukuza mbali zonse za dziko.

16Yehova, anthu anu anabwera kwa Inu pamene anali mʼmasautso;

pamene munawalanga,

iwo anapemphera kwa Inu.

17Monga mayi woyembekezera pamene nthawi yake yobereka yayandikira

amamva kupweteka ndipo amalira ndi ululu,

ifenso tinali chimodzimodzi pamaso panu, Inu Yehova.

18Ife chimodzimodzi tinamva ululu, ngati mayi pa nthawi yobala mwana,

koma sitinapindulepo kanthu,

kapena kupulumutsa dziko lapansi;

sitinabadwitse anthu atsopano pa dziko pano.

19Koma anthu anu amene anafa adzakhalanso ndi moyo;

matupi awo adzadzuka.

Iwo amene ali ku fumbi tsopano

adzadzuka ndi kuyimba mosangalala.

Monga mame amafewetsa pansi kutsitsimutsa zomera,

momwenso Yehova adzaukitsa anthu amene anafa kale.

20Abale anga, pitani mukalowe mʼnyumba zanu

ndipo mukadzitsekere;

mukabisale kwa kanthawi kochepa

mpaka ukali wake utatha.

21Taonani, Yehova akubwera kuchokera kumene amakhala;

akubwera kudzalanga anthu a dziko lapansi chifukwa cha machimo awo.

Dziko lapansi lidzawulula magazi amene anakhetsedwa pa dzikolo;

dziko lapansi silidzabisanso mitembo ya anthu ophedwa.

Asante Twi Contemporary Bible

Yesaia 26:1-21

Ayɛyie Dwom

1Saa ɛda no, wɔbɛto saa dwom yi wɔ Yuda asase so:

Yɛwɔ kuropɔn denden;

Onyankopɔn de nkwagyeɛ

ayɛ nʼafasuo ne nʼafaban a ɛkorɔn.

2Mommuebue apono no

na ateneneefoɔ ɔman no nhyɛne mu,

ɔman nokwafoɔ no.

3Obiara a ɔde ne ho to wo so no

wobɛkora ne so asomdwoeɛ mu,

ɛfiri sɛ ɔde ne ho ato wo so.

4Fa wo ho to Awurade so afebɔɔ,

ɛfiri sɛ, Awurade yɛ daa Botan.

5Ɔbrɛ wɔn a wɔtete soro ase,

na ɔbrɛ kuropɔn a ɛkorɔn no ase;

ɔbubu gu fam pasaa

ma ɛda mfuturo mu.

6Ahiafoɔ ne wɔn a wɔhyɛ wɔn so

de wɔn nan bɛtiatia so.

7Ɔteneneeni kwan so yɛ tamaa;

Ao ɔnokwafoɔ, woma ɔteneneeni kwan so yɛ tromtrom.

8Aane, Awurade, yɛnam wo mmara kwan so yi no,

yɛretwɛn wo;

na wo din ne ne kɛseyɛ

yɛ deɛ yɛn akoma pɛ.

9Me kra pere hwehwɛ wo anadwo;

anɔpa nso me honhom ani gyina wo.

Sɛ wʼatemmuo ba asase yi so a,

nnipa a wɔwɔ ewiase sua tenenee yɛ.

10Ɛwom sɛ woyi adom adi kyerɛ amumuyɛfoɔ deɛ,

nanso wɔnnsua tenenee yɛ;

na mpo teneneefoɔ asase so no, wɔkɔ so yɛ bɔne

na wɔmmu Awurade kɛseyɛ.

11Ao Awurade, wɔapagya wo nsa akɔ ɔsoro,

nanso wɔnhunu.

Ma wɔnhunu wo mmɔdemmɔ wɔ wo nkurɔfoɔ ho na ɛnhyɛ wɔn aniwuo;

ma ogya a woasɔ ama wʼatamfoɔ no nhye wɔn.

12Awurade, woama yɛn asomdwoeɛ;

deɛ yɛatumi ayɛ nyinaa wo na woayɛ ama yɛn.

13Ao, Awurade yɛn Onyankopɔn, awuranom afoforɔ bi adi yɛn so,

nanso wo din nko ara na yɛkamfo.

14Afei wɔawuwu, na wɔnte ase bio;

ahonhom a wɔafiri mu no, wɔrensɔre.

Wotwee wɔn aso na wo sɛee wɔn

na yɛn werɛ afiri wɔn.

15Woama ɔman no ayɛ kɛseɛ, Ao Awurade;

woama ɔman no ayɛ kɛseɛ;

woahyɛ wo ho animuonyam;

woatrɛtrɛ asase no ahyeɛ nyinaa mu.

16Awurade, yɛfiri ahohia mu baa wo nkyɛn;

ɛberɛ a wotwee wɔn aso no,

na yɛntumi mmue yɛn ano mpo mmɔ mpaeɛ.

17Sɛdeɛ ɔpemfoɔ a awoɔ aka no

firi ɔyea mu nukanuka ne mu na ɔsu no,

saa ara na yɛyɛeɛ wɔ wʼanim, Ao Awurade.

18Yɛnyinsɛnee, yɛkyemee wɔ ɔyea mu

nanso yɛwoo mframa.

Yɛamfa nkwagyeɛ amma asase so;

yɛanwo nnipa amma asase so.

19Nanso wʼawufoɔ bɛnya nkwa;

wɔn onipadua bɛsɔre.

Mo a motete mfuturo mu,

monsɔre mfa anigyeɛ nteam.

Mo bosuo te sɛ anɔpa bosuo;

asase bɛyi nʼafunu apue.

20Monkɔ, me nkurɔfoɔ, monhyɛne mo adan mu

na montoto apono no mu;

momfa mo ho nsie berɛ tiawa bi

kɔsi sɛ nʼabufuhyeɛ ano bɛdwo.

21Hwɛ, Awurade refiri nʼatenaeɛ

abɛtwe nnipa a wɔte asase so aso wɔ wɔn bɔne ho.

Asase bɛda mogya a wɔahwie agu no so adi;

ɛrentumi mfa nʼatɔfoɔ nsie bio.