Yeremiya 6 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 6:1-30

Kuzingidwa kwa Yerusalemu

1“Thawani, inu anthu a ku Benjamini!

Tulukani mu Yerusalemu!

Lizani lipenga ku Tekowa!

Kwezani mbendera ku Beti-Hakeremu!

Pakuti tsoka lalikulu likubwera kuchokera kumpoto,

ndipo chiwonongekocho nʼchachikulu.

2Kodi mzinda wa Ziyoni suli ngati msipu wokongola kwambiri,

kumene abusa amafikako ndi ziweto zawo?

3Abusa ndi nkhosa zawo adzabwera kudzalimbana nawo;

adzamanga matenti awo mowuzinga,

ndipo aliyense adzakhazika anthu ake pamalo pake.”

4Adzanena kuti, “Konzekani kuwuthira nkhondo mzindawo!

Nyamukani, kuti tiwuthire nkhondo mzindawu masana ano.

Koma tili ndi tsoka, dzuwa lapendeka,

ndipo zithunzithunzi za kumadzulo zikunka zitalika.

5Tsono nyamukani kuti tiwuthire nkhondo mzindawu usiku uno

ndi kuwononga malinga ake!”

6Yehova Wamphamvuzonse akuti,

“Dulani mitengo

ndipo mumange mitumbira yankhondo kulimbana ndi Yerusalemu.

Mzinda umenewu uyenera kulangidwa;

wadzaza ndi kuponderezana.

7Monga momwe chitsime chimatulutsira madzi

ndi mmenenso Yerusalemu amatulutsira zoyipa zake.

Chiwawa ndi chiwonongeko ndi zomwe zimamveka mu mzindamo;

nthenda yake ndi mabala ake ndimaziona nthawi zonse.

8Iwe Yerusalemu, tengapo phunziro,

kuopa kuti chikondi changa pa iwe chingakuchokere

ndi kusandutsa dziko lako kukhala bwinja

mopanda munthu wokhalamo.”

9Yehova Wamphamvuzonse anandiwuza kuti,

“Adani adzawakunkha ndithu anthu otsala a Israeli,

monga momwe amachitira populula mphesa.

Tsono iwe yesetsa kupulumutsa amene ungathe

monga mmene amachitira munthu wokolola mphesa.”

10Kodi ndiyankhule ndi yani ndi kumuchenjeza?

Ndinene mawu ochenjeza kwa yani kuti amve?

Makutu awo ndi otsekeka

kotero kuti sangathe kumva.

Mawu a Yehova ndi onyansa kwa iwo;

sasangalatsidwa nawo.

11Koma ine ndadzazidwa ndi mkwiyo wa Yehova,

ndipo ndatopa ndi kusunga mkwiyo wa Yehova.

Yehova anandiwuza kuti, “Tsono ndidzawutulutsira mkwiyo umenewu pa ana oyenda mʼmisewu

ndi pa achinyamata amene asonkhana pamodzi;

pakutinso mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa,

pamodzi ndi okalamba amene ali ndi zaka zochuluka.

12Nyumba zawo adzazipereka kwa ena,

pamodzi ndi minda yawo ndi akazi awo.

Ndidzatambasula dzanja langa kukantha

anthu okhala mʼdzikomo,”

akutero Yehova.

13“Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,

onse ali ndi dyera lofuna kupeza phindu mwa kuba;

aneneri pamodzi ndi ansembe omwe,

onse amachita zachinyengo.

14Amapoletsa zilonda za anthu anga

pamwamba pokha.

Iwo amanena kuti, ‘Mtendere, mtendere,’

pamene palibe mtendere.

15Kodi amachita manyazi akamachita zonyansazo?

Ayi, sachita manyazi ndi pangʼono pomwe;

sadziwa ndi kugwetsa nkhope komwe.

Choncho iwo adzagwera pakati pa anzawo amene agwa kale;

adzagwa pansi tsiku limene ndidzawalange,”

akutero Yehova.

16Yehova akuti,

“Imani pa mphambano ndipo mupenye;

kumeneko ndiye kuli njira zakale,

funsani kumene kuli njira yabwino. Yendani mʼmenemo,

ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.

Koma inu munati, ‘Ife sitidzayenda njira imeneyo.’

17Ine ndinakupatsani alonda oti akuyangʼanireni

ndipo ndinati, ‘Imvani kulira kwa lipenga!’

koma inu munati, ‘Sitidzamvera.’

18Nʼchifukwa chake imvani, inu anthu a mitundu ina;

yangʼanitsitsani, inu amene mwasonkhana pano,

chimene chidzawachitikire anthuwo.

19Imvani, inu anthu okhala pa dziko lapansi,

ndikubweretsa masautso pa anthu awa.

Zimenezi ndi mphotho ya ntchito zawo.

Iwowa sanamvere mawu anga

ndipo anakana lamulo langa.

20Kodi pali phindu lanji ngakhale mubwere ndi lubani kuchokera ku Seba,

kapena zonunkhira zina kuchokera ku dziko lakutali?

Nsembe zanu zopsereza Ine sindidzalandira;

nsembe zanu sizindikondweretsa.”

21Choncho Yehova akuti,

“Ndidzayika zokhumudwitsa pamaso pa anthu awa.

Abambo ndi ana awo aamuna onse adzapunthwa ndi kugwa;

anansi awo ndi abwenzi awo adzawonongeka.”

22Yehova akunena kuti,

“Taonani, gulu lankhondo likubwera

kuchokera kumpoto;

mtundu wa anthu amphamvu wanyamuka

kuchokera kumathero a dziko lapansi.

23Atenga mauta ndi mikondo;

ndi anthu ankhanza ndi opanda chifundo.

Phokoso lawo lili ngati mkokomo wa nyanja.

Akwera pa akavalo awo

ndipo akonzekera ngati anthu ankhondo,

kudzakuthirani nkhondo anthu a ku Ziyoni.”

24A ku Ziyoni akuti “Ife tamva mbiri yawo,

ndipo manja anthu alefukiratu.

Nkhawa yatigwira,

ndipo tikumva ululu ngati mayi pa nthawi yake yochira.

25Musapite ku minda

kapena kuyenda mʼmisewu,

pakuti mdani ali ndi lupanga,

ndipo ponseponse anthu akuchita mantha.

26Inu anthu anga, valani ziguduli

ndipo gubudukani pa phulusa;

lirani mwamphamvu

ngati munthu wolirira mwana wake mmodzi yekha,

pakuti mwadzidzidzi wowonongayo

adzabwera kudzatipha.

27“Iwe Yeremiya, ndakuyika kuti ukhale choyesera zitsulo.

Uwayese anthu anga

monga ungayesere chitsulo

kuti uwone makhalidwe awo.

28Onsewo ali ndi khalidwe lokanika ndi lowukira

ndipo akunka nanena zamiseche.

Iwo ndi olimba ngati mkuwa ndi chitsulo.

Onse amangochita zoyipa zokhazokha.

29Moto mu mvukuto ukuyaka kwambiri;

mtovu watha kusungunuka ndi moto.

Koma ntchito yosungunulayo sikupindula

chifukwa zoyipa sizikuchokapo.

30Iwo ali ngati siliva wotayidwa,

chifukwa Yehova wawakana.”