Yeremiya 49 – CCL & JCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 49:1-39

Uthenga Wonena za Aamoni

1Yehova ananena izi:

Amoni,

“Kodi Israeli alibe ana aamuna?

Kapena alibe mlowamʼmalo?

Tsono nʼchifukwa chiyani anthu opembedza Moleki alanda dziko la Gadi?

Nʼchifukwa chiyani anthu ake akukhala mʼmizinda ya Gadi?

2Koma nthawi ikubwera,”

akutero Yehova,

“pamene ndidzamveketse mfuwu wankhondo

ku Raba, likulu la Amoni;

ndipo malo awo opembedzera milungu yawo

adzatenthedwa ndi moto.

Choncho Aisraeli adzalandanso dziko lawo

kuchokera kwa amene anawalanda poyamba dzikolo,”

akutero Yehova.

3“Lirani, inu anthu a ku Hesiboni chifukwa wowononga uja wafika!

Fuwulani, inu anthu okhala ku Raba!

Valani ziguduli ndi kulira mwamphamvu;

thamangani uku ndi uku mʼkati mwa malinga,

chifukwa mulungu wanu Moleki adzapita ku ukapolo,

pamodzi ndi ansembe ake ndiponso akuluakulu ake.

4Chifukwa chiyani mukunyadira

chigwa chanu,

inu anthu osakhulupirika

amene munadalira chuma chanu nʼkumati:

‘Ndani angandithire nkhondo?’

5Ndidzabweretsa zoopsa pa iwe

zochokera kwa onse amene akuzungulira,”

akutero Ambuye, Mulungu Wamphamvuzonse.

“Mudzathawa, ndipo aliyense adzathawitsa moyo wake.

Sipadzapezeka munthu wosonkhanitsanso othawawo.

6“Komabe pambuyo pake, ndidzabwezera kwawo Aamoni,”

akutero Yehova.

Uthenga Wonena za Edomu

7Yehova Wamphamvuzonse ananena izi za Edomu:

“Kodi nzeru sizikupezekanso ku Temani?

Kodi anzeru analeka kupereka uphungu?

Kodi nzeru zawo zinatheratu?

8Inu anthu a ku Dedani, thawani,

bwererani ndi kukabisala ku makwalala

chifukwa ndidzagwetsa mavuto pa zidzukulu za Esau

popeza nthawi yawo ya chiweruzo yafika.

9Kodi anthu othyola mphesa akanafika kwa inu

akanakusiyiraniko mphesa pangʼono pokha?

Anthu akuba akanafika usiku

akanangotengako zimene akuzifuna zokha?

10Koma ine ndazivula zidzukulu za Esau.

Ndaonetsa poyera malo awo obisalamo,

kotero kuti sadzathanso kubisala.

Ana ake, abale ake pamodzi ndi anansi ake awonongeka.

Palibe wonena kuti,

11‘Siyani ana anu amasiye; Ine ndidzawateteza.

Amayi anu amasiye akhoza kudalira Ine.’ ”

12Yehova akuti, “Ngati iwo amene sanali oyenera kulangidwa adzamwa chikho cha chiweruzo, ndiye muyesa kuti inuyo simudzalangidwa? Ayi ndithu simudzakhala osalangidwa. Mudzamwa ndithu chikhocho. 13Ine ndikulumbira, akutero Yehova, kuti mzinda wa Bozira udzasanduka bwinja, chinthu chochititsa mantha, chomachiseka ndiponso chotembereredwa. Mizinda yake yonse idzakhala mabwinja mpaka muyaya.”

14Ndamva uthenga wochokera kwa Yehova:

Nthumwi yatumidwa kupita kwa anthu a mitundu ina kukanena kuti,

“Sonkhanani pamodzi kuti muthire nkhondo Edomu!

Konzekerani nkhondo!”

15“Ndidzakuchepetsani pakati pa anthu a mitundu ina.

Mudzakhala anthu onyozeka pakati pa anthu.

16Kuopseza kwako kwakunyenga;

kudzikuza kwa mtima wako kwakusocheretsa,

iwe amene umakhala mʼmapanga

a mʼmatanthwe ndi mʼmapiri.

Ngakhale utamanga chisa chako pamwamba kwambiri ngati chiwombankhanga,

ndidzakutsitsa pansi kuchokera kumeneko,”

akutero Yehova.

17“Dziko la Edomu lidzasanduka chinthu chochititsa mantha.

Onse odutsamo adzadabwa ndi kupukusa mitu yawo

chifukwa cha kuwonongeka kwake.

18Monga momwe anawonongekera Sodomu ndi Gomora,

pamodzi ndi mizinda yake yozungulira,”

akutero Yehova,

“motero palibe munthu

amene adzakhala mu Edomu.

19“Monga mkango wotuluka ku nkhalango za ku Yorodani

kupita ku malo a msipu wobiriwira,

Ine ndidzapirikitsa anthu a ku Edomu mwadzidzidzi kuchoka mʼdziko lawo.

Pambuyo pake ndidzawayikira owalamulira amene ndamufuna Ine.

Kodi ndani wofanana nane, ndipo angatsutsane nane ndani?

Ndipo ndi mʼbusa uti amene angalimbane nane?”

20Nʼchifukwa chake imvani. Izi ndi zimene Ine Yehova

ndakonza zolangira anthu a ku Edomu ndi a ku Temani.

Ngakhale ana omwe adzatengedwa ukapolo

ndipo aliyense adzachita mantha chifukwa cha iwo.

21Akadzagwa Edomu padzakhala mfuwu waukulu ndipo dziko lapansi lidzanjenjemera;

kulira kwawo kudzamveka mpaka ku Nyanja Yofiira.

22Taonani, mtundu wina udzachita kuwuluka

nʼkudzatera pa Bozira ngati chiwombankhanga chimene chatambalitsa mapiko ake.

Pa tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku Edomu

idzagunda ngati mtima wa mayi pa nthawi yake yochira.

Uthenga Wonena za Damasiko

23Mawu a Yehova onena za Damasiko ndi awa:

“Anthu a ku Hamati ndi a ku Aripadi akuchita mantha

chifukwa amva nkhani yoyipa.

Mitima yawo yagwidwa ndi mantha

ndipo ali ngati muja ichitira nyanja yosakhazikika.

24Anthu a ku Damasiko alefuka.

Abwerera mʼmbuyo kufuna kuthawa

chifukwa agwidwa ndi mantha aakulu.

Ali ndi nkhawa komanso mantha

ngati za mayi pa nthawi yake yochira.

25Mzinda wotchuka

ndi wachikondwerero uja wasiyidwa!

26Nʼchifukwa chake anyamata ake adzagwa mʼmisewu ndi kufa;

ankhondo ake onse adzawonongedwa tsiku limenelo,”

akutero Yehova Wamphamvuzonse.

27“Ndidzatentha malinga a Damasiko;

moto udzanyeketsa nyumba zaufumu za Beni-Hadadi.”

Uthenga Wonena za Kedara ndi Hazori

28Mawu a Yehova onena za Kedara ndi maufumu a ku Hazori, amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawagonjetsa ndi awa:

“Nyamukani mukathire nkhondo ku Kedara.

Kawonongeni anthu a kummawako.

29Landani matenti awo ndi nkhosa zawo,

ndiye kuti, mutenge nsalu zawo ndi katundu wawo.

Mutengenso ngamira zawo.

Anthu adzafuwula kwa iwo kuti,

‘Kuli zoopsa mbali zonse!’

30“Thawani mofulumira!

Kabisaleni mʼmakhwawa, inu anthu ku Hazori,”

akutero Yehova.

“Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni wakukonzerani chiwembu;

wakonzekera zoti alimbane nanu.

31“Nyamukani kathireni nkhondo mtundu wa anthu umene uli pamtendere,

umene ukukhala mosatekeseka,”

akutero Yehova,

“mzindawo ulibe zipata ngakhalenso mipiringidzo;

anthu ake amakhala pa okha.

32Ngamira zawo zidzafunkhidwa,

ndipo makola a ngʼombe zawo adzalandidwa.

Ndidzabalalitsira ku mphepo zinayi onse amene amameta tsitsi lawo chamʼmbali.

Ndidzawagwetsera mavuto kuchokera ku mbali zonse,”

akutero Yehova.

33“Hazori adzasanduka bwinja,

malo okhalamo nkhandwe

mpaka muyaya.

Palibe munthu amene adzayendemo.”

Uthenga Wonena za Elamu

34Uthenga umene Yehova anapatsa mneneri Yeremiya wonena za Elamu, Zedekiya mfumu ya Yuda atangoyamba kulamulira ndi uwu:

35Yehova Wamphamvuzonse akuti,

“Taonani, ndidzathyola uta wa Elamu,

umene uli chida chawo champhamvu.

36Ndidzabweretsa mphepo zinayi pa Elamu

kuchokera ku zigawo zinayi zamlengalenga;

ndidzawabalalitsira ku mphepo zinayi,

ndipo sipadzakhala dziko

limene anthu a ku Elamu sadzafikako.

37A ku Elamuwo ndidzachititsa mantha pamaso pa adani awo

komanso pamaso pa iwo amene akufuna kuwononga moyo wawo.

Ndidzawagwetsera mkwiyo wanga

ndipo adzakhala pa mavuto,”

akutero Yehova.

“Ndidzawapirikitsa ndi lupanga

mpaka nditawatheratu.

38Ndidzakhazika mpando wanga waufumu ku Elamu

ndipo ndidzawononga mfumu yake pamodzi ndi akuluakulu ake,”

akutero Yehova.

39“Komabe mʼtsogolomo ndidzabwezera

anthu a ku Elamu dziko lawo,”

akutero Yehova.

Japanese Contemporary Bible

エレミヤ書 49:1-39

49

アモンについてのメッセージ

アモン人について――

1「おまえたちは、ここで何をしているのか。

なぜユダヤ人の町に住んでいるのか。

そこはユダヤ人だけの住みかであり、

彼らがわたしから受け継いだ所ではないか。

それなのに、ミルコムの神を拝むおまえたちが、

なぜガドとその町々を占領したのか。

2このため、わたしはおまえたちを罰し、

おまえたちの町ラバを破壊する。

そこは人の住まないごみの山となり、

近くの町々も焼き払われる。

そのあとイスラエルが来て、

おまえたちの手から国を取り戻し、

失った物を奪い返す。」

主はこう言います。

3「ヘシュボンよ、アイが滅びたのだから、

泣きわめくがいい。

ラバの娘よ、喪服を着て垣根に身を隠し、

ぞんぶんに泣け。

おまえの神ミルコムが、重立った人や祭司と共に、

遠い国へ連れて行かれるからだ。

4おまえは、よく肥えた谷間の地を自慢にしているが、

それはまもなく荒れ地になる。

根性の曲がった娘よ。

おまえは自分の財産を心の拠り所とし、

手出しする者はだれもいないと考えていた。

5だが、見ているがいい。

わたしはおまえに恐怖を送る。」

天の軍勢の主である神が、こう言います。

「隣人たちはおまえをおまえの国から追い出し、

おまえが捕虜になって連れ去られるのを

横目で見ながら逃げて行く。

6だが、後に、わたしはアモン人の国を

元どおりに繁栄させる。

エドムについてのメッセージ

エドム人について――

7天の軍勢の主はこう言います。

「昔いた賢い者たちはどこへ行ったのか。

テマンには、もう知恵のある者は一人もいないのか。

8デダン(隊商で栄えた、アラビヤ北部の町)の人よ、

荒野の一番奥まで逃げて行け。

わたしはエドムを罰する時に、

おまえたちをも罰するからだ。

9-10ぶどうを収穫する者は、

貧しい者のことを考えて少しは残しておく。

どろぼうでさえ、

すべてを盗んで行くようなことはしない。

だが、わたしがエドムを丸裸にするので、

隠れる所はどこにもない。

子どもも、兄弟も、隣人も、一人残らず殺され、

おまえ自身も滅びる。

11だがわたしは、生き残ったみなしごたちを守り、

未亡人たちがわたしを頼りとするようにする。」

12主はエドムに言います。「罪のない者さえ苦しむとしたら、おまえは、どれほど苦しまなければならないことか。罰を受けずにすむはずはない。どうしても、このさばきの杯を飲まなければならない。 13ボツラは荒れ果て、のろいとあざけりを受けるようになると、わたしは自分の名にかけて誓ったのだ。その町々は永遠に廃墟となる。」

14私は主から、次の知らせを聞きました。

神はエドムを滅ぼす同盟軍を起こすため、

国々に呼びかける使者を送り出しました。

15神は言います。

「わたしはこの国を弱くし、

周囲の国々にさげすまれるようにする。

16おまえはペトラの山々や岩の裂け目に住み、

自分の名声と思い上がりによって自分を欺いてきた。

だが、わしのように高い峰に住んでいても、

わたしはおまえを引きずり降ろす。

17エドムは非常に恐ろしい目に会う。そこに近づく者はみな、あまりにも悲惨な光景に背筋が凍り、息の止まる思いがする。 18おまえの町々は、ソドムとゴモラやその近くの町々のように静まり返る。二度とそこに住む者はいない。 19わたしが彼らのもとに、ヨルダンの密林から出て囲いの中の羊に忍び寄るライオンのような侵略者を送るので、エドムは一瞬のうちに滅びる。そのあとで、わたしの選んだ者をエドム人の上に立てよう。わたしのような者がいるだろうか。だれがわたしを呼びつけて、報告を求めることができるだろう。どの羊飼いが、わたしに反抗できるだろうか。」 20次のことを心に留めておきなさい。

主は間違いなくエドムとテマンの住民に、

小さな子どもさえ奴隷になって引きずられて行く光景を

見せます。それは、見るに耐えない悲惨なことです。

21エドムが倒れる音で地は揺れ動きます。

人々の叫び声は紅海にまで聞こえます。

22襲いかかる者は、わしのように速く飛んで来て、ボツラに向かって翼を広げます。それを見て、大勇士の勇気もくじけ、産みの苦しみをする女のようになります。

ダマスコについてのメッセージ

23ダマスコについて――

「ハマテとアルパデの町々は、恐れに取りつかれた。

彼らの運命がどうなるかを聞いたからだ。

彼らの心は、嵐の荒れ狂う海のように、

ざわめき立っている。

24ダマスコはすっかりおじけづき、住民はみな逃げた。

恐れと苦しみと悲しみが、産婦に取りつくように、

ダマスコに取りついた。

25ああ、名の知れた町、喜びの町よ。

どうしておまえは、今になって見捨てられたのか。

26若者たちは、路上に死体となって横たわっている。

おまえの軍隊は、ただの一日で蹴散らされてしまう。」

そう天の軍勢の主は言います。

27「わたしはダマスコの城壁に火をつける。

その火で、ベン・ハダデの宮殿は焼け落ちる。」

ケダルとハツォルについてのメッセージ

28次の預言は、ケダルとハツォル(どちらも、パレスチナ東方の荒野に住むアラブ遊牧民)の王国についてです。これらの王国は、主の命令を受けたバビロンのネブカデネザル王によって、まもなく滅ぼされようとしています。 29神は言います。

「彼らの羊の群れもテントも、

家庭用品ともども奪い取られる。

らくだも連れ去られ、

『われわれは包囲された。いよいよ最期だ』という

恐怖にひきつった叫び声が、あちこちから聞こえる。

30いのちが助かるために逃げなさい。

ハツォルの人たちは荒野の奥に隠れるのだ。

バビロンのネブカデネザル王が陰謀を巡らし、

おまえたちを根絶やしにしようと

手はずを整えているからだ。」

31主はネブカデネザル王に、こう言いました。

「さあ、のん気に荒野で孤立して住んでいる

金持ちのベドウィン族に襲いかかるのだ。

彼らは、だれの力も借りずにやっていけるとうぬぼれ、

城壁も門もいらないと大口をたたいている。

32彼らのらくだと家畜は、みなおまえのものになる。

わたしはこのアラブ人を風で吹き散らし、

四方八方から災難を呼び寄せる。」

33ハツォルは荒野の野獣の住みかになります。

人の住まない、永遠の荒れ地となるのです。

エラムについてのメッセージ

34ユダのゼデキヤ王の治世の初めに、エラムについてのことばが、エレミヤにありました。

35「天の軍勢の主はこう言います。

『わたしはエラムの軍隊を破る。

36また、四方からの風でエラムの住民を吹き散らす。

そのため、彼らは世界中の国々に流れ着く。

37わたしは激しく怒ってエラムに大きな災いを下し、

敵がこの地の住民を一掃するように仕向ける。

38わたしはわたしの王座をエラムに置き、

王と重立った者たちを滅ぼす。

39だが後に、わたしはエラム人を呼び戻す。