1Yakobo, mtumiki wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu,
kulembera mafuko khumi ndi awiri obalalikana ku mayiko osiyanasiyana.
Landirani moni.
Masautso ndi Mayesero
2Abale, muchiyese ngati chimwemwe chenicheni nthawi zonse pamene mukukumana ndi mayesero amitundumitundu. 3Inu mukudziwa kuti kuyesedwa kwa chikhulupiriro chanu kumabweretsa chipiriro. 4Chipiriro chiyenera kugwira ntchito yake kuti mukhale okhwima ndi angwiro, osasowa kanthu kalikonse. 5Ngati wina pakati panu akusowa nzeru, apemphe kwa Mulungu amene amapereka kwa onse mwaulere ndi mosatonzera, ndipo adzapatsidwa. 6Koma pamene mupempha, muyenera kukhulupirira osakayika, chifukwa amene amakayika ali ngati mafunde pa nyanja amene amawinduka nakankhika ndi mphepo. 7Munthu wotere asayembekezere kulandira kalikonse kuchokera kwa Ambuye. 8Iyeyu ndi munthu wa mitima iwiri, wosakhazikika pa zimene akuchita.
9Abale omwe ndi anthu wamba anyadire pamene akwezedwa. 10Koma olemera anyadire pamene atsitsidwa, chifukwa adzatha ngati duwa lakuthengo. 11Pakuti dzuwa limatuluka nʼkutentha kwake, ndipo limafotetsa zomera. Duwa lake limathothoka ndipo kukongola kwake kumatheratu. Momwemonso munthu wachuma adzazimirira ngakhale atamachitabe malonda ake.
12Wodala ndi munthu amene amapirira mʼmayesero, chifukwa akapambana adzalandira chipewa cha ulemerero chimene Mulungu analonjeza anthu amene amamukonda.
13Munthu akayesedwa asanene kuti, “Mulungu akundiyesa.” Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi choyipa kapena Iyeyo kuyesa munthu aliyense. 14Koma munthu aliyense amayesedwa akakokedwa ndi zilakolako zake zoyipa ndi kukopedwa nazo. 15Pamenepo, chilakolako chikakula chimabala tchimo; ndipo tchimo likakhwima limabereka imfa.
16Musanyengedwe abale anga okondedwa. 17Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba, kwa Atate mwini kuwala, amene sasintha ngati mthunzi woyendayenda. 18Iye anasankha kutibereka ife kudzera mʼmawu a choonadi, kuti pakati pa zolengedwa zake zonse, tikakhale ngati zipatso zoyamba.
Kumva ndi Kuchita
19Abale anga okondedwa, gwiritsitsani mawu awa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma asamafulumire kuyankhula, ndipo asamafulumirenso kupsa mtima. 20Pakuti mkwiyo wa munthu subweretsa chilungamo chimene amafuna Mulungu. 21Choncho chotsani chizolowezi choyipa ndi khalidwe loyipa pakati panu, ndipo modzichepetsa landirani mawu amene anadzalidwa mwa inu, amene akhoza kukupulumutsani.
22Musamangomvetsera chabe mawu, ndi kumadzinyenga nokha. Chitani zimene mawuwo amanena. 23Munthu aliyense amene amangomva mawu koma osachita zimene mawuwo amanena, ali ngati munthu amene amayangʼana nkhope yake pa galasi. 24Akadziyangʼana amachoka, nthawi yomweyo nʼkuyiwala mmene akuonekera. 25Koma munthu amene amayangʼana mwachidwi lamulo langwiro limene limapatsa ufulu ndi kupitiriza kutero, osayiwala chimene wamva koma kuchita adzadalitsika pa zimene amachita.
26Ngati wina amadziyesa ngati ndi wachipembedzo, koma chonsecho saletsa lilime lake, amadzinyenga yekha ndipo chipembedzo chakecho ndi cha chabechabe. 27Chipembedzo chimene Mulungu Atate athu amachivomereza kuti ndi changwiro ndi chopanda zolakwika ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto awo, ndi kudzisunga bwino kuopa kudetsedwa ndi dziko lapansi.