Oweruza 20 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Oweruza 20:1-48

Aisraeli Achita Nkhondo ndi Fuko la Benjamini

1Ndipo Aisraeli onse kuyambira ku dziko la Dani mpaka ku Beeriseba ndiponso ku dziko la Giliyadi ananyamuka ngati munthu mmodzi nakasonkhana pamaso pa Yehova ku Mizipa. 2Atsogoleri a anthu onse ndi a mafuko onse Aisraeli anali nawo pa msonkhano wa anthu a Mulungu. Onse pamodzi analipo asilikali oyenda pansi 400,000 atanyamula malupanga. 3Anthu a fuko la Benjamini anali atamva kuti Aisraeli apita ku Mizipa. Tsono Aisraeli anati, “Tiwuzeni, zinthu zoyipa izi zinachitika bwanji.”

4Choncho Mlevi uja, mwamuna wa mkazi wophedwa uja anayankha nati, “Ine ndinapita ku Gibeya mʼdziko la Benjamini pamodzi ndi mzikazi wanga kuti tikagone kumeneko. 5Usiku anthu a ku Gibeya anandiwukira, nazinga nyumba munali ine. Ankafuna kundipha ndipo anagona ndi mzikazi wanga momukakamiza mpaka anafa. 6Ine ndinatenga mzikazi wangayo ndi kumudula nthulinthuli ndikuzitumiza kwa fuko lililonse la Aisraeli. Anthu amenewa, zedi achita chinthu chonyansa kwambiri mʼdziko lino la Israeli. 7Ndi zimenezotu inu Aisraeli nonse; yankhulaponi mawu ndi kupereka maganizo anu.”

8Anthu onse anayimirira ngati munthu mmodzi nanena kuti, “Palibe mmodzi wa ife amene apite ku nyumba kwake. Palibe amene abwerere ku nyumba kwake. 9Koma tsopano chimene ife tichite ndi dziko la Gibeya ndi ichi: Tidzapita kukamenyana nawo potsatira zimene maere anene. 10Mʼmafuko onse a Aisraeli tidzasankha anthu khumi pa anthu 100 aliwonse: ndiye kuti anthu 100 pa anthu 1,000 aliwonse kapena anthu 1,000 pa anthu 10,000 aliwonse. Anthu amenewa adzasonkhanitsa zakudya za ankhondo, ndipo ankhondowo adzapita kukalipsira anthu a ku Geba mʼdziko la Benjamini chifukwa chochita chinthu chonyansa chotere mʼdziko la Israeli.” 11Choncho anthu a ku Israeli anasonkhana pamodzi nagwirizana chimodzi, kukalimbana ndi mzindawo.

12Mafuko a Israeli anatumiza anthu kwa fuko lonse la Benjamini kukafunsa kuti, “Kodi zoyipa zachitika pakati panuzi ndi zotani? 13Tsono tikuti mutipatse anthu achabechabe a ku Gibeya kuti tiwaphe kuti tichotse chinthu choyipachi mʼdziko la Israeli.”

Koma fuko la Benjamini silinafune kumvera zimene ananena Aisraeli anzawo. 14Mʼmalo mwake, Abenjaminiwo anatuluka mʼmizinda yawo ku Gibeya kukamenyana ndi Aisraeli. 15Tsiku limenelo Abenjamini anasonkhanitsa kuchokera ku mizinda yawo ankhondo 26,000 amalupanga awo, osawerengera anthu ena 700 a ku Gibeya amene anasankhidwa. 16Mwa onsewa panali ankhondo 70 amanzere amene aliyense anali wodziwa kulasa ngakhale tsitsi limodzi ndi mwala osaphonya.

17Aisraeli, kupatula fuko la Benjamini, anasonkhanitsa anthu 400,000 a malupanga, onse odziwa bwino nkhondo.

18Ndipo Aisraeli ananyamuka kupita ku Beteli kukafunsira kwa Mulungu. Iwo anati, “Ndani mwa ife amene angayambe kukamenyana ndi fuko la Benjamini?”

Yehova anayankha kuti, “Fuko la Yuda ndilo liyambe.”

19Mmawa mwake Israeli ananyamuka nakamanga msasa moyangʼanana ndi Gibeya. 20Aisraeli anapita kukachita nkhondo ndi fuko la Benjamini ndipo anandandalika ankhondo awo moyangʼanana ndi Gibeya. 21A fuko la Benjamini anatuluka ku Gibeya ndipo tsiku limenelo anapha Aisraeli 22,000 ku nkhondoko. 22Koma ankhondo a Israeli analimbikitsananso mtima ndipo anasonkhanitsanso kachiwiri ankhondo awo pa malo pamene anawandandalika poyamba paja. 23Aisraeli anapita kukalira pamaso pa Yehova mpaka madzulo. Iwo anafunsa Yehova kuti, “Kodi tipitenso kukamenyana ndi a fuko la Benjamini abale athu?”

Yehova anayankha kuti, “Pitani mukalimbane nawo.”

24Ndipo Aisraeli anayandikiranso pafupi ndi fuko la Benjamini tsiku lachiwiri lake kuti amenyane nawo. 25Pa tsiku lachiwiri lomwelo Abenjamini anatulukanso mu mzinda wa Gibeya ndipo anaphanso ankhondo 18,000. Onse amene anawaphawo anali odziwa kugwiritsa ntchito bwino malupanga.

26Tsono Aisraeli onse, gulu lonse la ankhondo, anapita ku Beteli kukalira pamaso pa Yehova. Anakhala pansi nasala zakudya tsiku lonse mpaka madzulo. Anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pamaso pa Yehova. 27Bokosi la Chipangano cha Yehova linali kumeneko. 28Finehasi mwana wa Eliezara mwana wa Aaroni ndiye ankatumikira nthawi imeneyo. Tsono Aisraeli anafunsa Yehova kuti, “Kodi tipitenso kukachita nkhondo ndi mʼbale athu Abenjamini, kapena ayi?”

Yehova anayankha kuti, “Pitaninso chifukwa mawa ndidzawapereka mʼmanja mwanu.”

29Choncho Aisraeli anayika anthu obisalira mozungulira Gibeya. 30Tsiku lachitatu anapita kukamenyana ndi Benjamini ndipo anayika ankhondo mʼmalo mwawo kuti amenyane ndi Gibeya monga anachitira poyamba. 31Abenjamini anatuluka kukamenyana nawo anthuwo ndipo anapita kutali ndi mzindawo. Iwo anayamba kupha Aisraeli monga poyamba paja, kotero kuti anapha anthu pafupifupi makumi atatu. Mitembo ya ena inali mu misewu yayikulu yopita ku Beteli ndi ku Gibeya, ndipo ina inali kwina poyera.

32Abenjamini ankanena kuti, “Tikuwagonjetsa monga poyamba.” Koma Aisraeli ankanena kuti, “Tiyeni tithawe kuti apite ku msewu chapatali ndi mzinda wawo.”

33Choncho Aisraeli onse anachoka mʼmalo mwawo ndi kukandanda ku Baala-Tamara, ndipo Aisraeli obisalira aja anatuluka mʼmalo awo kummawa kwa Geba. 34Aisraeli osankhidwa 10,000 ndiwo anabwera kudzalimbana ndi mzinda wa Gibeya. Nkhondoyo inafika poyipa kwambiri mwakuti Abenjamini samadziwa kuti zoopsa zili pafupi kuwagwera. 35Tsono Yehova anagonjetsa Abenjamini pamaso pa Israeli motero kuti Aisraeli anapha ankhondo a Abenjamini 25,100 tsiku limenelo. 36Choncho Abenjamini anaona kuti agonjetsedwa.

Paja Aisraeli anathawa fuko la Benjamini chifukwa ankadalira anthu amene anawayika kuti abisalire mzinda wa Gibeya. 37Tsono anthu amene anabisala aja anachita changu kuwuthira nkhondo mzinda wa Gibeyawo. Ndipo anapha anthu onse a mu mzindawo ndi lupanga. 38Chizindikiro chimene Aisraeli anapangana ndi anthu obisalira aja chinali chakuti obisalira aja akangofukiza utsi wambiri ngati mtambo mu mzindamo, 39ndiye kuti Aisraeli enawo abwerere ku nkhondo.

Pa nthawiyo nʼkuti Abenjamini atayamba kale kumenya Aisraeliwo kwambiri ndi kupha pafupifupi anthu makumi atatu. Ndipo iwo ankanena kuti, “Ndithu tawapha monga poyamba paja.” 40Koma pamene utsi wa chizindikiro uja unayamba kukwera tolotolo mmwamba kuchoka mu mzindamo, Abenjamini anayangʼana mʼmbuyo ndipo anangoona utsi mu mzinda onse uli tolotolo kukwera mmwamba. 41Kenaka Aisraeli anabwerera ndipo Abenjamini anachita mantha, chifukwa anaona kuti zoopsa zili pafupi kuwagwera. 42Choncho anathawa pamaso pa Aisraeli kudzera njira ya ku chipululu, koma nkhondo inawapeza. Ndipo anaphedwa kumeneko ndi Aisraeli amene anachokera mu mzindamo. 43Anawazungulira Abenjaminiwo, nawathamangitsa ndi kuwagonjetseratu osawachitira chifundo mpaka ku dera la kummawa kwa Gibeya. 44Abenjamini 18,000 olimba mtima anaphedwa. 45Koma ena anatembenuka nathawira ku chipululu ku thanthwe la Rimoni. Mwa iwowa Aisraeli anapha Abenjamini 5,000 mʼmisewu yayikulu. Anawapitikitsabe Abenjaminiwo mpaka kufika ku Gidomu ndi kuphanso ena 2,000.

46Pa tsiku limenelo Abenjamini olimba mtima okhala ndi malupanga okwana 25,000 anafa. 47Koma anthu 700 anabwerera ndi kuthawira ku chipululu ku thanthwe la Rimoni kumene anakhalako miyezi inayi. 48Aisraeli anabwerera kukamenyana ndi Abenjamini otsala ndi kuwapha ndi lupanga kuphatikizapo ziweto ndi zonse anali nazo. Ndipo anayatsa moto mizinda yonse anayipeza.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

士師記 20:1-48

討伐基比亞

1於是,從別示巴以及基列的全體以色列人萬眾一心,來到米斯巴,聚集在耶和華面前。 2以色列各支派的首領都參加了這次上帝子民的聚會,當時有四十萬持刀的步兵。 3便雅憫人也聽見以色列人聚集在米斯巴的消息。以色列人問那個利未人:「請告訴我們,這件邪惡的事是怎麼發生的。」 4利未人,就是被害女子的丈夫說:「我和我的妾到便雅憫基比亞住宿。 5那天晚上,基比亞人包圍我們住宿的房子,要殺死我。他們把我的妾蹂躪致死。 6我就把她的屍體切成塊,送到以色列的各個地區,讓以色列人都知道基比亞人做了邪惡、無恥的事。 7以色列人啊,你們看該怎麼處理吧!」

8眾人起來異口同聲地說:「我們誰也不回帳篷,誰也不回家。 9現在我們要抽籤去攻打基比亞10我們要從各支派中抽出十分之一的人負責運糧,等軍隊到達基比亞後,就可以討伐在以色列做出這種卑鄙之事的基比亞人。」 11於是,以色列人團結一致,一起去攻打那城。

12他們派人去對便雅憫各地的人說:「你們中間怎麼發生了這種邪惡的事! 13現在把那些基比亞的無賴交出來,我們要處死他們,從以色列剷除罪惡。」便雅憫人卻充耳不聞, 14還從各城聚集到基比亞以色列人打仗。 15便雅憫人從各城召集了兩萬六千刀兵,還從基比亞召集了七百精兵。 16軍中有七百精兵善用左手甩石,毫髮不差。 17其他十一個以色列支派則召集了四十萬善戰的刀兵。

18以色列人到伯特利去求問上帝,說:「我們當中哪個支派應當先去攻打便雅憫人呢?」耶和華說:「猶大支派。」

19第二天清早,以色列人就在基比亞附近安營, 20擺開陣勢,準備攻打便雅憫人。 21便雅憫人從基比亞出來,當天殺了以色列軍兩萬二千人。 22以色列人重整士氣,仍在第一天列陣的地方列陣。 23列陣之前,他們在耶和華面前一直哀哭到晚上。他們求問耶和華,說:「我們應該再去攻打我們的同胞便雅憫人嗎?」耶和華說:「可以去。」

24第二天,以色列人前去攻打便雅憫人。 25便雅憫人從基比亞出來迎戰,又殺了以色列軍一萬八千刀兵。 26以色列全軍來到伯特利,坐在耶和華面前哀哭,那天他們一直禁食到晚上,又在耶和華面前獻上燔祭和平安祭。 27-28那時,上帝的約櫃就在那裡,亞倫的孫子、以利亞撒的兒子非尼哈任祭司。以色列人求問耶和華,說:「我們應該再去攻打我們的同胞便雅憫人嗎?還是退兵?」耶和華說:「去攻打吧,因為明天我必把他們交在你們手中。」

29以色列人在基比亞周圍設下伏兵。 30第三天,以色列人又像前兩次一樣在基比亞列陣,攻打便雅憫人。 31便雅憫人前來迎戰,被以色列人誘到城外。他們又像前兩次一樣擊殺以色列人,大約三十名以色列人死在通往基比亞伯特利的兩條路上。 32便雅憫人說:「我們又打敗他們了。」但以色列人已經商議好,用詐敗的方法誘敵離城到大路上來。 33以色列全軍在巴力·他瑪列陣反攻,埋伏在基比亞西面的以色列人也衝了出來。 34有一萬以色列精兵從正面攻打基比亞,戰事非常激烈。便雅憫人大禍臨頭了仍懵然不知。 35耶和華幫助以色列人戰勝了便雅憫人。那天,以色列人殺了便雅憫兩萬五千一百刀兵。 36便雅憫人這才意識到自己戰敗了。

原來以色列人在便雅憫人面前詐敗,因為他們已在基比亞附近設下伏兵。 37那些伏兵迅速衝進基比亞,殺了全城的人。 38以色列人和伏兵已有約定,伏兵在城內點起一股濃煙時, 39以色列人便轉身殺回。便雅憫人殺了詐敗的以色列軍大約三十人,以為像以前一樣打敗了他們。 40這時基比亞城已濃煙滾滾,便雅憫人回頭觀望,只見全城濃煙四起。 41以色列人轉身殺了回來,便雅憫人大驚失色,知道大禍臨頭了。 42他們從以色列人面前轉身逃往曠野,卻無法逃脫。以色列人從各城出來夾攻他們。 43以色列人圍攻便雅憫人,一路追殺他們直到基比亞的東邊。 44便雅憫人共死了一萬八千名勇士。 45餘下的人都逃往曠野的臨門岩,沿途有五千人被殺。以色列人追殺他們,一直追到基頓,又消滅了他們兩千人。 46那天,便雅憫人共死了兩萬五千名英勇的刀兵, 47只有六百人逃到了臨門岩,在那裡住了四個月。 48以色列人回師便雅憫境內,將各城的男女老少以及牲畜全部殺死,又放火燒毀所有的城邑。