Oweruza 19 – CCL & AKCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Oweruza 19:1-30

Mlevi ndi Mzikazi Wake

1Pa nthawi imeneyo ku Israeli kunalibe mfumu.

Mlevi wina ankakhala kutali ku dziko lamapiri la Efereimu. Iyeyu anatenga mzikazi wa ku Betelehemu, mʼdziko la Yuda. 2Tsiku lina mzikazi uja anakwiyira mwamuna wake ndipo anamuchokera kupita kwa abambo ake ku Betelehemu mʼdziko la Yuda. Anakakhala kumeneko miyezi inayi. 3Mwamuna wake anamulondola kuti akayankhule naye mofatsa kumupempha kuti abwerere. Iye anali ndi antchito ake ndi abulu ake awiri. Anafika ku nyumba kwa mkazi uja ndipo iye anamulowetsa mʼnyumba ya abambo ake. Abambo aja atamuona mnyamata uja anamulandira mwachimwemwe. 4Mpongozi wake, yemwe anali abambo a mtsikanayo, anamupempha kuti aswere. Choncho anakhalako masiku atatu. Ankadya, kumwa ndi kugona komweko.

5Tsiku lachinayi anadzuka mʼmamawa kukonzekera kuti azipita kwawo, koma abambo ake a mtsikanayo anawuza mkamwini wawo uja kuti, “Yambani mwadya chakudya, ndipo kenaka mutha kupita.” 6Choncho onse awiri anakhala pansi ndi kudya ndi kumwa pamodzi. Atadya, abambo a mtsikanayo anati, “Chonde mugonenso konkuno musangalale.” 7Ndipo pamene mwamunayo anakonzeka kuti azipita, apongozi ake anamuwumirizanso kuti asapite. Choncho anagona komweko usiku umenewo. 8Mmawa wa tsiku lachisanu, atadzuka kuti azipita abambo ake a mtsikanayo anamuwuza kuti, “Yambani mwadya chakudya ndipo mutandale mpaka madzulo.” Choncho awiriwo anadya pamodzi.

9Pambuyo pake munthu uja pamodzi ndi mzikazi wake ndiponso mtumiki anakonzeka kuti azipita. Koma abambo a mtsikana uja anatinso kwa iye, “Onani tsopano kukuda. Gonani konkuno pakuti tsiku latha kale. Gonani ndipo musangalale. Mawa mudzuka mʼmamawa ndi kumapita kwanu.” 10Koma munthuyo sanafune kugonanso tsiku limenelo. Choncho ananyamuka kumapita, ndipo anakafika ku malo oyangʼanana ndi Yebusi (ndiye kuti Yerusalemu). Iyeyo anali atatenga abulu ake awiri okhala ndi zokhalira zake, ndipo mzikazi wake uja anali naye limodzi.

11Akuyandikira ku Yebusi nʼkuti kutada ndithu. Tsono mtumiki uja anawuza mbuye wake kuti, “Tiyeni, tipatukire ku mzinda wa Ayebusiwa ndipo tigone.”

12Mbuye wake anamuyankha kuti, “Ayi, tisapatukire ku mzinda wa alendo, anthu amene sali Aisraeli. Koma tipitirire mpaka ku Gibeya.” 13Tsono anamuwuza mtumiki wake uja kuti, “Tiye tipite ku amodzi a malo awa, ku Gibeya kapena ku Rama ndipo tikagone kumeneko.” 14Choncho nayenda ulendo wawo, ndipo dzuwa linawalowera akuyandikira ku Gibeya mʼdziko la Benjamini. 15Ndipo anapatukira kumeneko kuti alowe mu mzinda wa Gibeya kukagona usiku umenewo. Anakalowa mu mzindamo ndi kukakhala pabwalo popeza panalibe munthu amene anawalandira ku nyumba kwake kuti akagone.

16Pambuyo pake anangoona munthu wina wokalamba akuchokera ku ntchito ya ku munda kwake madzulo. Iyeyu anali wa ku dziko la mapiri ku Efereimu, koma ankakhala ku Gibeya. Koma anthu a kumeneko anali a fuko la Benjamini. 17Munthu wokalamba uja anakweza maso ndipo anaona munthu wa paulendo uja atakhala pabwalo la mzindawo, ndipo anamufunsa kuti, “Kodi mukupita kuti? Nanga mukuchokera kuti?”

18Iye anayankha kuti, “Tikuchokera ku Betelehemu ku dziko la Yuda ndipo tikupita kutali ku dziko lamapiri la Efereimu kumene ndimakhala. Ndinapita ku Betelehemu mʼdziko la Yuda ndipo tsopano ndikubwerera kwathu. Koma palibe aliyense amene wanditengera ku nyumba yake. 19Tili ndi udzu ndi chakudya cha abulu athu. Tilinso ndi buledi ndi vinyo wokwanira ifeyo: ine, mdzakazi wanuyu, ndi mtumiki amene ali nafeyu. Palibe chimene tikusowa.”

20Munthu wokalambayo anati, “Mtendere ukhale nanu. Ine ndikuthandizani pa zosowa zanu zonse, koma musagone pabwalo usiku uno.” 21Choncho anapita nawo ku nyumba yake, ndipo anawapatsa abulu ake chakudya. Alendo aja anasamba mapazi awo, nalandira chakudya ndi chakumwa.

22Pamene ankadya mosangalala, anangoona anthu ena achabechabe a mu mzindawo azungulira nyumba ija nʼkumamenya chitseko. Tsono anawuza mwini nyumbayo, munthu wokalamba uja kuti, “Mutulutse munthu amene wabwera mʼnyumba yakoyu kuti tigone naye.”

23Koma mwini nyumba uja anatuluka ku bwalo nawawuza kuti, “Ayi, abale anga musachite zoyipa zotere. Popeza munthu uyu walowa mʼnyumba mwanga muno, musachite chinthu chonyansa chotere. 24Onani, pano pali mwana wanga wamkazi wosadziwa mwamuna pamodzi ndi mzikazi wa mlendoyu. Ndikutulutsirani amenewa tsopano ndipo atengeni ndi kuchita nawo chomwe chikukomerani. Koma musachite chinthu chonyansa ndi munthuyu.”

25Koma anthuwo sanafune kumumvera. Choncho mlendo uja anagwira mzikazi wake namutulutsa kuja kumene kunali iwo. Tsono iwowo anagona naye ndi kuchita naye zonyansa usiku wonse mpaka mmawa. Mʼbandakucha anamulola kuti apite. 26Ndipo mmawa kukucha mzikazi uja anabwerera nakagwa pansi pa khomo pa nyumba imene mwamuna wake anali, ndipo anakhala pomwepo mpaka kunayera.

27Mwamuna wake anadzuka mʼmamawa, natsekula chitseko cha nyumba kuti atuluke ndi kumapita. Koma anangoona mzikazi wake uja ali thapsa pa khomo la nyumbayo, manja ake ali pa khonde. 28Iye anati kwa mkaziyo, “Dzuka tizipita.” Koma sanayankhe kanthu. Kenaka anamukweza pa bulu wake ndipo ananyamuka kumapita kwawo.

29Atafika ku nyumba yake, anatenga mpeni, nagwira mzikazi wake uja ndi kuduladula thupi lake nthuli khumi ndi ziwiri. Kenaka anazitumiza ku zigawo zonse za Israeli. 30Aliyense amene anaona zimenezi ankanena kuti, “Zoterezi sizinaonekepo kuyambira pamene Aisraeli anatuluka mʼdziko la Igupto mpaka lero lino. Ganizirani bwino chinthu chimenechi ndipo tiwuzeni zoyenera kuchita!”

Akuapem Twi Contemporary Bible

Atemmufo 19:1-30

Lewini Ne Ne Mpena

1Saa bere no na Israel nni ɔhene. Na ɔbarima bi a ofi Lewi abusuakuw mu te Efraim bepɔw asase no so akyirikyiri baabi. Da bi, ɔde ɔbea bi fi Betlehem a ɛwɔ Yuda baa fie sɛ ne mpena. 2Nanso ɔbea no anni no nokware enti ɔsan kɔɔ nʼagya fi wɔ Betlehem. Asram anan akyi no, 3ne kunu no faa ɔsomfo ne afurum foforo kaa ne ho kɔɔ Betlehem sɛ ɔde rekɔdɛfɛdɛfɛ no na wasan nʼakyi aba. Oduu ɔbea no agya fi no, ɔde no kɔɔ ofi no mu maa nʼagya no gyee no fɛw so. 4Ɔbea no agya ka kyerɛɛ no se ɔntena nkyɛ kakra. Enti odii nnansa, didi, nom, daa hɔ.

5Ne nnannan so no, ɔbarima no sɔree anɔpa, pɛɛ sɛ ɔkɔ. Nanso ɔbea no agya ka kyerɛɛ no se, “Didi ansa na woakɔ.” 6Enti wɔn baanu no tenaa ase didi, nomee. Afei, ɔbea no agya ka kyerɛɛ no se, “Mesrɛ wo, da anadwo yi na gye wʼani.” 7Ɔbarima no sɔree sɛ anka ɔrekɔ, nanso nʼase no hyɛɛ no sɛ ɔntena. Enti ɔpenee so daa hɔ anadwo no. 8Nnaanum so anɔpa no, ɔsɔree bio a ɔpɛɛ sɛ ɔkɔ. Nanso bio, ɔbea no agya kae se, “Didi ansa, na awia mu kakra no wubetumi akɔ.” Enti wɔsan didii bio.

9Awia no, ɔbarima no ne ne mpena no ne ne somfo boaboaa wɔn ho pɛɛ sɛ wɔkɔ. Nanso nʼase no ka kyerɛɛ no se, “Muntie! Ade reyɛ asa. Montena na munnye mo ani anadwo yi. Ɔkyena mubetumi asi mu anɔpahema.”

10Nanso afei de, ɔbarima no pɛɛ sɛ ɔbɛkɔ. Enti ɔfaa ne mfurum abien a wɔahyehyɛ wɔn no ne ne mpena no, na wɔde wɔn ani kyerɛɛ Yebus (a ɛyɛ Yerusalem). 11Bere a woduu Yebus no na ade reyɛ asa, na ɔsomfo no ka kyerɛɛ ne wura no se, “Ade reyɛ asa, enti momma yɛnna Yebusifo kuropɔn yi mu anadwo yi.”

12Ne wura no buae se, “Dabi, yɛrentumi ntena ananafo kuropɔn a Israelfo nni mu yi mu. Yɛbɛtoa so akɔ Gibea. 13Yebenya nnabea anadwo yi wɔ Gibea anaa Rama.” 14Enti wɔtoaa so. Wɔrebedu kurow Gibea a ɛwɔ Benyamin asase so no, na owia rekɔtɔ. 15Ɛhɔ na wɔdaa anadwo no. Wɔdaa kurow no abɔnten kɛse so, na obiara amfa wɔn ankɔ fie ankɔsom wɔn hɔho.

16Anwummere no, akwakoraa bi fii nʼafum baa fie. Na ofi Efraim bepɔw asase so, nanso na ɔte Gibea wɔ Benyamin asase so. 17Bere a ohuu akwantufo yi sɛ wɔtete kurow no abɔnten kɛse so no, obisaa wɔn faako a wofi ne nea wɔrekɔ.

18Ɔbarima no buaa no se, “Yefi Betlehem a ɛwɔ Yuda na yɛrekɔ Efraim bepɔw asase no so; kurow bi a ɛwɔ akyirikyiri, na yɛrekɔ Awurade Hyiadan. Nanso obiara amfa yɛn ankɔ ne fi ankɔma yɛn nnabea, 19ɛwɔ mu sɛ yɛwɔ nea ehia yɛn biara. Yɛwɔ sare ne aduan a yɛde bɛma yɛn mfurum; yenhia hwee.”

20Akwakoraa no kae se, “Mommra me fi. Mɛma mo biribiara a ebehia mo. Na anadwo yi de, ɛnsɛ sɛ moda abɔnten kɛse so ha.” 21Enti ɔfaa wɔn de wɔn kɔɔ ne fi, na ɔmaa wɔn mfurum no aduan. Wɔhohoroo wɔn nan ase wiei no, wɔbɔɔ mu didii.

22Bere a wɔregye wɔn ani no, kurow no mu nnipa bɔnefo bi betwaa ofi no ho hyiae. Wofii ase pempem ɔpon no teɛteɛɛ mu guu akwakoraa no so se, “Fa ɔbarima a wabɛsoɛ wo no ma yɛn sɛnea yebetumi ne no ada.”

23Akwakoraa no fi ba bɛkasa kyerɛɛ wɔn se, “Dabi, anuanom, monnyɛ bɔne a ɛte saa. Saa ɔbarima yi yɛ me hɔho na sɛ moyɛ saa a, ɛbɛyɛ animguase. 24Me babea ɔbabun ne ɔbarima yi mpena ni. Mede wɔn bɛma mo. Na nea mopɛ biara no monyɛ wɔn. Na mo ne saa ɔbarima yi nyɛ saa animguasede yi.”

25Nanso wɔantie no. Enti Lewini no faa ne mpena no piaa no fii adi. Na kurow no mu mmarima no faa no nnidiso nnidiso kosii adekyee. Ahemadakye no na wogyaw no ma ɔkɔe. 26Ɔbea no koduu ofi a ne kunu no te mu no pon ano ara pɛ na ɔtɔɔ mum. Ɔdaa hɔ ara kosii sɛ anim tetewee.

27Bere a ne kunu buee ɔpon no sɛ ɔrepue pɛ na ohuu sɛ ɔda hɔ. Na nʼanim butuw hɔ a ne nsa gu apongua no so. 28Ohuu no no, ɔkae se, “Sɔre! Ma yɛnkɔ!” Nanso wammua. Enti ɔde no too nʼafurum no so de no kɔɔ fie.

29Oduu fie no, ɔtwee afoa de twitwaa ne mpena no mu asinasin dumien. Na ɔde sin baako biara kɔɔ Israel mmusuakuw dumien no mu. 30Na obiara a ohuu saa aninyanne yi kae se, “Efi bere a Israel fii Misraim no, obi nnii saa amumɔyɛsɛm yi bi da. Adɛn nti na ɛnsɛ sɛ yɛkasa na yɛyɛ ho biribi?”