Nyimbo ya Solomoni 7 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Nyimbo ya Solomoni 7:1-13

1Iwe namwali waufumu, mapazi ako ngokongola

mu nsapato wavalazo!

Ntchafu zako nʼzowumbika bwino ngati miyala yamtengowapatali,

ntchito ya manja ya mmisiri waluso.

2Mchombo wako uli ngati chikho chowumbika bwino

chimene nthawi zonse ndi chodzaza ndi vinyo.

Chiwuno chako ndi choningʼa ngati mtolo wa tirigu

utazunguliridwa ndi maluwa okongola.

3Mawere ako akuoneka ngati ana awiri a mbawala,

ngati mphoyo zamapasa.

4Khosi lako lili see! ngati nsanja ya mnyanga wa njovu.

Maso ako ali ngati mayiwe a ku Hesiboni,

amene ali pafupi ndi chipata cha Bati Rabimu.

Mphuno yako ili ngati nsanja ya ku Lebanoni,

yoyangʼana ku Damasiko.

5Mutu wako uli bwinobwino nengʼaa ngati phiri la Karimeli.

Tsitsi lako lili ngati nsalu yakuda yaufumu;

mfumu yakopeka ndi maonekedwe ake okongola.

6Ndiwe wokongola kwambiri ndiponso wosangalatsa,

iwe wokondedwa, namwali wokondweretsawe!

7Msinkhu wako uli ngati mtengo wa mgwalangwa,

ndipo mawere ako ali ngati phava la zipatso.

8Ndinati, “Ndikwera mtengo wa mgwalangwa;

ndidzathyola zipatso zake.”

Mawere ako ali ngati maphava a mphesa,

fungo la mpweya wako lili ngati ma apulosi,

9ndipo pakamwa pako pali ngati vinyo wokoma kwambiri.

Mkazi

Tsono vinyo ameneyu amuthirire wachikondi wanga,

ayenderere bwino pa milomo yake ndi mano ake.

10Wokondedwayo ine ndine wake,

ndipo chilakolako chake chili pa ine.

11Bwera wachikondi wanga, tiye tipite ku madera a ku midzi,

tikagone ku midzi.

12Tiye tilawirire mmamawa kupita ku minda ya mpesa,

tikaone ngati mitengo ya mpesa yayamba kuphukira,

ngati maluwa ake ayamba kuoneka,

komanso ngati makangadza ayamba kuonetsa maluwa.

Kumeneko ndidzakuonetsa chikondi changa.

13Mitengo ya mankhwala a chisulo ikupereka fungo lake labwino,

ndipo pa khomo pathu pali zipatso zonse zokoma,

zatsopano ndi zakale zomwe,

zimene ndakusungira wokondedwa wanga.