Nehemiya 7 – CCL & KLB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Nehemiya 7:1-73

1Khoma linamangidwa ndipo zitseko zinayikidwa. Pambuyo pake alonda a Nyumba ya Mulungu, oyimba nyimbo ndiponso Alevi anasankhidwa. 2Kenaka ine ndinasankha mʼbale wanga Hanani pamodzi ndi Hananiya woyangʼanira nsanja yankhondo kukhala olamulira Yerusalemu chifukwa iyeyu anali munthu odalirika ndi woopa Mulungu kuposa anthu ena. 3Ine ndinawawuza kuti, “Musalole kuti zipata za Yerusalemu zitsekulidwe mpaka dzuwa litatentha, ndipo alonda asanaweruke aonetsetse kuti atseka zitseko ndi kuzipiringidza. Musankhe alonda pakati pa anthu okhala mu Yerusalemu, ena akhale pa malo pawo ndi ena akhale moyangʼanana ndi nyumba zawo.”

Mndandanda wa Anthu Oyamba Kubwera Kuchokera ku Ukapolo

4Tsono mzinda wa Yerusalemu unali wotambasuka ndiponso waukulu koma munali anthu ochepa ndipo nyumba zinali zisanamangidwe. 5Ndipo Mulungu wanga anayika mu mtima mwanga maganizo oti ndisonkhanitse anthu olemekezeka, akuluakulu ndi anthu onse kuti alembetse mayina mwa mabanja awo. Ndinapeza buku limene munalembedwa mayina a mabanja a iwo amene anayamba kubwera kuchokera ku ukapolo. Izi ndi zimene ndinazipeza zitalembedwa mʼmenemo:

6Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerera kuchokera ku ukapolo amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawatenga ukapolo. Iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wa makolo ake. 7Anabwera pamodzi ndi atsogoleri awa: Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu ndi Baana.

Tsono chiwerengero cha anthu a ku Israeli chinali chotere:

8Zidzukulu za Parosi 2,1729Zidzukulu za Sefatiya 37210Zidzukulu za Ara 65211Zidzukulu za Pahati-Mowabu (kudzera mu mʼbado wa Yesuwa ndi Yowabu) 2,81812Zidzukulu za Elamu 1,25413Zidzukulu za Zatu 84514Zidzukulu za Zakai 76015Zidzukulu za Binuyi 64816Zidzukulu za Bebai 62817Zidzukulu za Azigadi 2,32218Zidzukulu za Adonikamu 66719Zidzukulu za Abigivai 2,06720Zidzukulu za Adini 65521Zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya) 9822Zidzukulu za Hasumu 32823Zidzukulu za Bezayi 32424Zidzukulu za Harifu 11225Zidzukulu za Gibiyoni 95.

26Anthu a ku Betelehemu ndi Netofa18827Anthu a ku Anatoti 12828Anthu a ku Beti-Azimaveti 4229Anthu a ku Kiriati Yeyarimu Kefira ndi Beeroti 74330Anthu a ku Rama ndi Geba 62131Anthu a ku Mikimasi 12232Anthu a ku Beteli ndi Ai 12333Anthu a ku Nebo winayo 5234Ana a Elamu wina 1,25435Zidzukulu za Harimu 32036Zidzukulu za Yeriko 34537Zidzukulu za Lodi, Hadidi ndi Ono72138Zidzukulu za Senaya 3,930.

39Ansembe anali awa:

A banja la Yedaya (ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa) 97340Zidzukulu za Imeri 1,05241Zidzukulu za Pasi-Huri 1,24742Zidzukulu za Harimu 1,017.

43Alevi anali awa:

A banja la Yesuwa ndi Kadimieli, ndiye kuti zidzukulu za Hodaviya 74.

44Anthu oyimba:

   Zidzukulu za Asafu 148.

45Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa:

Zidzukulu za   Salumu, Ateri, Talimoni, Hatita ndi Sobai 138.

46Anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu anali awa:

Zidzukulu za   Ziha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti,47Zidzukulu Kerosi, zidzukulu za Siya, zidzukulu za Padoni48Zidzukulu za Lebana za Hagaba, ndi za Salimayi,49Zidzukulu za Hanani, zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari,50Zidzukulu za Reyaya, zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nehoda,51Zidzukulu za Gazamu, zidzukulu za Uza, zidzukulu za Paseya,52Zidzukulu za Besai, zidzukulu za Meunimu, zidzukulu za Nefusimu,53Zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri,54Zidzukulu za Baziliti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa,55Zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema56Zidzukulu za Neziya, ndi zidzukulu za Hatifa.

57Zidzukulu za antchito a Solomoni:

Zidzukulu za   Sotai, zidzukulu za Sofereti, zidzukulu za Perida58zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli,59zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu   zidzukulu za Pokereti-Hazebaimu ndi zidzukulu Amoni.60Anthu onse ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za antchito a Solomoni analipo 392.

61Ali munsiwa anachokera ku Teli-Mela, Teri-Harisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, koma sanathe kunena mwa tchutchutchu kuti makolo awo kapena mafuko awo analidi Aisraeli kapena ayi.

62Zidzukulu za   Delaya, zidzukulu za Tobiya ndi zidzukulu za Nekoda 642.

63Ndiponso ena pakati pa ansembe anali awa:

zidzukulu za

Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai (munthu amene anakwatira mwana wamkazi wa Barizilai wa ku Giliyadi ndipo amatchedwa dzina limenelo).

64Iwowa anafufuzafufuza mayina awo mʼbuku la mibado ya mabanja awo ndipo sanapeze mayina awo kotero anachotsedwa pa unsembe nawerengedwa ngati odetsedwa pa chipembedzo. 65Choncho bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo chakudya china chilichonse choperekedwa kwa Mulungu mpaka patapezeka wansembe wodziwa kugwiritsa bwino ntchito ya Urimu ndi Tumimu.

66Chiwerengero chonse cha anthuwa chinali 42,360. 67Kuwonjezera pamenepa panali antchito awo aamuna ndi aakazi 7,337 ndiponso anthu aamuna ndi aakazi oyimba nyimbo okwanira 245. 68Panali akavalo 736, abulu angʼonoangʼono 245. 69Ngamira zawo zinalipo 435 ndipo abulu analipo 6,720.

70Atsogoleri ena a mabanja anapereka mphatso zothandizira ntchito. Bwanamkubwa anapereka ku thumba losungira chuma, ndalama zagolide za makilogalamu asanu ndi atatu, mabeseni makumi asanu ndi zovala za ansembe 530. 71Atsogoleri ena amabanja anapereka ku thumba losungira chuma ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndiponso ndalama za siliva zokwana makilogalamu 1,250. 72Anthu ena onse otsala anapereka ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndalama za siliva zokwana makilogalamu 140, ndiponso zovala za ansembe 67.

73Choncho ansembe, Alevi, alonda a Nyumba ya Mulungu, anthu oyimba nyimbo, ena mwa anthu wamba, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmizinda yawo.

Ezara Awerenga Malamulo

Pofika mwezi wachisanu ndi chiwiri Aisraeli onse anali atakhazikika mʼmizinda yawo.

Korean Living Bible

느헤미야 7:1-73

1성벽 건축 공사를 마치고 성문을 단 다음에 나는 성전 문지기와 성가대원과 레위 사람들에게 업무를 할당하고

2내 동생 하나니와 요새의 지휘관 하나냐에게 예루살렘을 다스릴 책임을 맡게 하였다. 하나냐는 그 누구보다도 성실하고 하나님을 두려워하는 사람이었다.

3그리고 나는 그들에게 해가 높이 떠오를 때까지는 예루살렘 성문을 열지 말며 문지기가 문을 지키고 있을 때 성문을 닫고 빗장을 지르도록 지시하였다. 나는 또 그들에게 예루살렘 주민들 가운데 경계병을 세워 각자 자기 초소와 자기 집 앞을 경계하게 하라고 지시하였다.

귀환자들의 명단

4예루살렘은 크고 넓은 성이었으나 거기에 사는 사람이 많지 않아 아직 집을 많이 짓지 않았다.

5그래서 하나님이 내 마음을 감동시키셔서 백성들과 지도자들을 모아 각 집안별로 등록하도록 하셨다. 그때 나는 차 귀환자들의 명단을 발견했는데 거기에는 이렇게 적혀 있었다:

6바빌로니아의 느부갓네살왕에게 포로로 잡혀갔던 수많은 사람들이 예루살렘과 유다와 그들의 각 성으로 돌아왔다.

7이들과 함께 온 지도자들은 스룹바벨, 예수아, 느헤미야, 아사랴, 라아먀, 나하마니, 모르드개, 빌산, 미스베렛, 비그왜, 느훔, 바아나였다. 그리고 이 귀환자들의 인원을 각 자손별로 나열하면 다음과 같다:

8바로스 자손 2,172명,

9스바댜 자손 372명,

10아라 자손 652명,

11예수아와 요압 계통의 바핫 – 모압 자손 2,818명,

12엘람 자손 1,254명,

13삿두 자손 845명,

14삭개 자손 760명,

15빈누이 자손 648명,

16브배 자손 628명,

17아스갓 자손 2,322명,

18아도니감 자손 667명,

19비그왜 자손 2,067명,

20아딘 자손 655명,

21히스기야 계통의 아델 자손 98명,

22하숨 자손 328명,

23베새 자손 324명,

24하립 자손 112명,

25기브온 사람 95명,

26베들레헴과 느도바 사람 188명,

27아나돗 사람 128명,

28벧 – 아스마 사람 42명,

29기럇 – 여아림과 그비라와 브에롯 사람 743명,

30라마와 게바 사람 621명,

31믹마스 사람 122명,

32벧엘과 아이 사람 123명,

33느보 사람 52명,

34다른 엘람 사람 1,254명,

35하림 사람 320명,

36여리고 사람 345명,

37로드와 하딧과 오노 사람 721명,

38스나아 사람 3,930명,

39제사장 중에서는 예수아 계통의 여다야 자손 973명,

40임멜 자손 1,052명,

41바스훌 자손 1,247명,

42하림 자손 1,017명,

43레위 사람 중에서는 호다위야 계통의 예수아와 갓미엘 자손 74명,

44성가대원인 아삽 자손 148명,

45살룸과 아델과 달몬과 악굽과 하디다와 소배의 자손인 성전 문지기 138명이었다.

46그리고 7:46 원문에는 ‘느디님 사람들’성전 봉사자들은 시하, 하수바, 답바옷,

47게로스, 시아, 바돈,

48르바나, 하가바, 살매,

49하난, 깃델, 가할,

50르아야, 르신, 느고다,

51갓삼, 웃사, 바세아,

52베새, 므우님, 7:52 또는 ‘느비스심’느부심,

53박북, 하그바, 할훌,

547:54 또는 ‘바슬릿’바슬룻, 므히다, 하르사,

55바르고스, 시스라, 데마,

56느시야, 하디바 – 이상 모든 사람들의 자손들이었다.

57솔로몬왕 신하들의 자손들 중에서 돌아온 사람들은 소대 자손, 소베렛 자손, 브리다 자손,

58야알라 자손, 다르곤 자손, 깃델 자손,

59스바댜 자손, 핫딜 자손, 보게렛 – 하스바임 자손, 7:59 또는 ‘아미’아몬 자손들이었다.

60이와 같이 성전 봉사자들과 솔로몬왕 신하들의 자손들 중에서 돌아온 사람들은 모두 392명이었다.

61이때 페르시아의 델 – 멜라, 델 – 하르사, 그룹, 7:61 또는 ‘앗단’앗돈, 임멜 지방에서 예루살렘으로 돌아온 다른 집단도 있었으나 그들이 실제로 이스라엘 자손이라는 확실한 증거가 없었다.

62이들은 들라야와 도비야와 느고다 자손들로 모두 642명이었다.

63그리고 제사장들 중에서 호바야 자손과 학고스 자손, 그리고 길르앗 사람 바르실래의 딸과 결혼하여 처갓집 이름을 딴 바르실래의 자손들도 예루살렘으로 돌아왔는데

64그들도 족보에서 그 신원이 밝혀지지 않았다. 그래서 이들은 부정한 자로 취급을 받아 제사장 직분을 수행하지 못했으며

65유다 지도자는 제사장이 7:65 어떤문제에대해서대제사장이가부간에하나님의뜻을물어보고자사용했던두가지도구.우림과 둠밈으로 하나님의 판결을 물어 그들이 실제로 제사장인지 아닌지 밝혀낼 때까지는 제사장이 먹는 거룩한 음식을 먹지 말라고 명령하였다.

66-67이상과 같이 유다로 돌아온 사람들은 노예 7,337명과 남녀 성가대원 7:66-67 스2:64-65에는 ‘200명’245명 외에 42,360명이었다.

68-69또 그들은 말 736마리, 노새 245마리, 낙타 435마리, 당나귀 6,720마리도 함께 끌고 왔다.

70그리고 많은 사람들이 성전을 재건하기 위해서 예물을 바쳤다. 그들의 지도자들이 바친 것은 금 7:70 히 ‘1,000 다릭’8.4킬로그램과 대접 50개와 제사장복 530벌이었고

71족장들이 바친 것은 7:71 히 ‘금 20,000다릭, 은 2,200미나’금 168킬로그램과 은 약 1,256킬로그램이었으며

72그 밖에 백성들이 바친 것은 7:72 히 ‘금 20,000다릭, 은 2,000미나’금 168킬로그램과 은 1,142킬로그램과 제사장복 67벌이었다.

73이렇게 해서 제사장, 레위 사람, 성전 문지기, 성가대원, 그 밖의 모든 백성들이 각자 자기 성에 정착하였다.