Nahumu 3 – The Word of God in Contemporary Chichewa CCL

The Word of God in Contemporary Chichewa

Nahumu 3:1-19

Tsoka la Ninive

1Tsoka kwa mzinda wopha anthu,

mzinda wodzaza ndi mabodza,

mzinda wodzaza ndi anthu olanda zinthu anzawo,

mu mzinda mʼmene simusowa anthu osautsidwa nthawi zonse!

2Kulira kwa zikwapu,

mkokomo wa mikombero,

kufuwula kwa akavalo

ndiponso phokoso la magaleta!

3Kuthamanga kwa anthu okwera pa akavalo,

kungʼanima kwa malupanga

ndi kunyezimira kwa mikondo!

Anthu ambiri ophedwa,

milumilu ya anthu akufa,

mitembo yosawerengeka,

anthu akupunthwa pa mitemboyo.

4Zonsezi ndi chifukwa cha zilakolako za mkazi wachiwerewere,

wokopa anthu uja, mkazi wochita zamatsenga,

amene anakopa mitundu ya anthu ndi zachiwerewere zake,

ndiponso anthu a mitundu ina ndi zaufiti zake.

5Yehova Wamphamvuzonse akuti,

“Ine ndikutsutsana nawe.

Ndidzakuvula chovala chako.

Anthu a mitundu ina ndidzawaonetsa umaliseche wako

ndipo udzachita manyazi pamaso pa maufumu onse.

6Ndidzakuthira zonyansa,

ndidzakuchititsa manyazi

ndiponso kukusandutsa chinthu choseketsa.

7Onse amene adzakuona adzakuthawa ndipo adzati,

‘Ninive wasanduka bwinja,

adzamulira ndani?’

Kodi ndingamupeze kuti munthu woti nʼkukutonthoza?”

8Kodi ndiwe wopambana Tebesi,

mzinda wokhala mʼmbali mwa Nailo,

wozunguliridwa ndi madzi?

Mtsinjewo unali chitetezo chake,

madziwo anali linga lake.

9Mphamvu zake zinali Kusi ndi Igupto,

Puti ndi Libiya anali ena mwa abwenzi ake.

10Komabe anthu a ku Tebesi anagwidwa

ndipo anapita ku ukapolo.

Ana ake anawaphwanyitsa pansi

mʼmisewu yonse ya mu mzindamo.

Anachita maere ogawana anthu ake otchuka,

ndipo anthu ake onse amphamvu

anamangidwa ndi maunyolo.

11Iwenso Ninive udzaledzera;

udzabisala

ndipo udzafunafuna malo othawirako kuopa mdani.

12Malo ako onse otetezedwa ali ngati mitengo ya mkuyu

yokhala ndi zipatso zoyambirira kucha;

pamene agwedeza mitengoyo,

nkhuyuzo zimagwera mʼkamwa mwa wofuna kuzidya.

13Tayangʼana ankhondo ako,

onse ali ngati akazi!

Zipata za dziko lako zatsekukira adani ako;

moto wapsereza mipiringidzo yake.

14Tungani madzi woti mudzamwe nthawi ya kuzunguliridwa kwanu,

limbitsani chitetezo chanu!

Pondani dothi,

ikani mʼchikombole,

konzani khoma la njerwa!

15Kumeneko moto udzakupserezani;

lupanga lidzakukanthani

ndipo lidzakuwonongani ngati likuwononga ziwala.

Chulukanani ngati ziwala,

chulukanani ngati dzombe!

16Mwachulukitsa chiwerengero cha anthu a malonda anu

mpaka kupambana nyenyezi za mlengalenga,

koma iwo ngati dzombe akuwononga dziko

ndipo kenaka akuwuluka nʼkuchoka.

17Akalonga ako ali ngati dzombe,

akuluakulu ako ali ngati gulu la dzombe

limene lamatirira pa khoma nthawi yozizira,

koma pamene dzuwa latuluka limawuluka,

ndipo palibe amene amadziwa komwe lapita.

18Iwe mfumu ya ku Asiriya,

abusa ako agona tulo;

anthu ako olemekezeka amwalira.

Anthu ako amwazikira ku mapiri

popanda ndi mmodzi yemwe wowasonkhanitsa.

19Palibe chimene chingachize bala lako;

chilonda chako sichingapole.

Aliyense amene amamva za iwe

amawomba mʼmanja chifukwa cha kugwa kwako,

kodi alipo amene sanazilawepo

nkhanza zako zosatha?