Nahumu 1 – CCL & PCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Nahumu 1:1-15

1Uthenga wonena za Ninive. Buku la masomphenya a Nahumu wa ku Elikosi.

Mkwiyo wa Yehova pa Ninive

2Yehova ndi Mulungu wansanje

ndiponso wobwezera;

Yehova amabwezera ndipo ndi waukali.

Yehova amabwezera adani ake

ndipo ukali wake umakhala nthawi zonse pa adani akewo.

3Yehova sakwiya msanga koma ndi wa mphamvu yayikulu;

ndipo sadzalola kuti munthu

wolakwa asalangidwe.

Iye amayenda mʼkamvuluvulu ndi mʼnamondwe,

ndipo mitambo ndi fumbi la ku mapazi ake.

4Amalamulira nyanja ndipo imawuma;

amawumitsa mitsinje yonse.

Zomera za ku Basani ndi Karimeli zimawuma

ndipo maluwa a ku Lebanoni amafota.

5Mapiri amagwedera pamaso pake

ndipo zitunda zimasungunuka.

Dziko lapansi limanjenjemera pamaso pake,

dziko lonse ndi zonse zokhala mʼmenemo.

6Ndani angathe kuyima pamaso pake Iye akalusa?

Ndani angapirire mkwiyo wake woopsa?

Ukali wake ukuyaka ngati moto;

matanthwe akunyeka pamaso pake.

7Yehova ndi wabwino,

ndiye kothawirako nthawi ya masautso.

Amasamalira amene amamudalira,

8koma ndi madzi achigumula choopsa

Iye adzawononga adani ake (Ninive);

adzapirikitsira adani ake ku malo a mdima.

9Chiwembu chilichonse chimene akukonzekera kumuchitira Yehova

adzachiwononga kotheratu;

msautso sudzabweranso kachiwiri.

10Iwo adzakodwa mu ziyangoyango za minga

ndipo adzaledzera ndi vinyo wawo;

adzatenthedwa ngati ziputu zowuma.

11Kwa iwe, Ninive, kunachokera munthu wa cholinga choyipa,

wofuna kuchitira Yehova chiwembu,

amene amapereka uphungu woyipa.

12Yehova akuti,

“Ngakhale Asiriyawo ali ndi abwenzi,

kaya iwowo ndi ambiri,

koma adzawonongedwa ndi kutheratu.

Ngakhale ndinakuzunza iwe Yuda,

sindidzakuzunzanso.

13Tsopano ndidzathyola goli lake pa khosi lako

ndipo ndidzadula maunyolo ako.”

14Yehova walamulira za iwe, Ninive kuti,

“Sudzakhala ndi zidzukulu

zimene zidzadziwike ndi dzina lako.

Ndidzawononga zifanizo zosema ndi mafano owumba

amene ali mʼnyumba ya milungu yako.

Ine ndidzakukumbira manda

chifukwa ndiwe woyipitsitsa.”

15Taonani, pa phiripo,

mapazi a munthu amene akubweretsa nkhani yabwino,

amene akulengeza za mtendere!

Inu anthu a ku Yuda, chitani madyerero anu

ndipo kwaniritsani malumbiro anu.

Anthu oyipa sadzakuthiraninso nkhondo;

iwo adzawonongedwa kotheratu.

Persian Contemporary Bible

ناحوم 1:1-15

انتقام خداوند از نينوا

1خداوند اين رؤيا را که دربارهٔ نينوا است به ناحوم القوشی نشان داد: 2خداوند غيور است و از کسانی که با وی مخالفت ورزند، انتقام می‌گيرد و با خشم شديد آنان را مجازات می‌کند. 3خداوند دير خشمگين می‌شود ولی گناه را هرگز بی‌سزا نمی‌گذارد. قدرت او عظيم است و آن را می‌توان در گردبادهای وحشتناک و طوفانهای شديد مشاهده کرد. ابرها خاک زير پای او هستند! 4به فرمان خداوند درياها و رودها خشک می‌شوند، چراگاههای سبز و خرم باشان و کرمل از بين می‌روند و جنگلهای سرسبز لبنان طراوت و خرمی خود را از دست می‌دهند. 5در حضور او کوهها می‌لرزند، تپه‌ها ناپديد می‌شوند، زمين متلاشی می‌گردد و ساکنانش نابود می‌شوند.

6کيست که بتواند در برابر خشم خدا ايستادگی کند؟ غضب او مانند آتش فرو می‌ريزد و کوهها در برابر خشم او خرد می‌شوند.

7خداوند نيکوست و در روز بلا و سختی پناهگاه می‌باشد. او از کسانی که به او توکل می‌کنند مراقبت می‌نمايد، 8ولی دشمنان خود را با سيلابی شديد از بين می‌برد و آنها را به ظلمت مرگ روانه می‌کند.

9ای نينوا، چرا به فکر مخالفت با خداوند هستی؟ او با يک ضربه تو را از پای در خواهد آورد، به طوری که ديگر نخواهی توانست مقاومت کنی. 10او دشمنانش را مثل خارهای به هم پيچيده به داخل آتش می‌اندازد و آنها همچون کاه در شعله‌های آتش سوخته شده دود می‌شوند. 11اين پادشاه تو کيست که جرأت می‌کند بر ضد خداوند توطئه کند؟ 12خداوند می‌فرمايد: «سپاه آشور هر قدر هم قوی و بزرگ باشد، محو و نابود خواهد شد.

«ای قوم من، به اندازه کافی شما را تنبيه کرده‌ام! 13اينک زنجيرهای شما را پاره می‌کنم و شما را از قيد اسارت پادشاه آشور آزاد می‌سازم.»

14خداوند به پادشاه آشور می‌فرمايد: «نسل تو را از بين می‌برم تا نام و نشانی از تو باقی نماند. بتها و بتخانه‌های تو را نابود می‌کنم و قبرت را می‌کنم، چون بر اثر گناه فاسد شده‌ای.»

خبر سقوط نينوا

15ببينيد، قاصدی از کوهها سرازير شده، خبر خوش پيروزی را ندا می‌دهند. ای يهودا، عيدهای خود را برگزار نما و نذرهای خود را به خدا وفا کن، چون دشمن، ديگر هرگز برنمی‌گردد. او برای هميشه ريشه کن شده است!