Mlaliki 1 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mlaliki 1:1-18

Zapansipano Nʼzopandapake

1Mawu a Mlaliki, mwana wa Davide, mfumu ya ku Yerusalemu:

2“Zopandapake! Zopandapake!”

atero Mlaliki.

“Zopandapake kotheratu!

Zopandapake.”

3Kodi munthu amapindulanji pa ntchito zake zonse

zimene amasautsidwa nazo pansi pano?

4Mibado imabwera ndipo mibado imapita,

koma dziko lapansi limakhalapobe nthawi zonse.

5Dzuwa limatuluka ndipo dzuwa limalowa

ndipo limapita mwamsanga kumene limatulukira.

6Mphepo imawombera cha kummwera

ndi kukhotera cha kumpoto;

imawomba mozungulirazungulira,

kumangobwererabwerera komwe yachokera.

7Mitsinje yonse imakathira ku nyanja,

koma nyanjayo sidzaza;

kumene madziwo amachokera,

amabwereranso komweko.

8Zinthu zonse ndi zotopetsa,

kutopetsa kwake ndi kosaneneka.

Maso satopa ndi kuona

kapena khutu kukwaniritsidwa ndi kumva.

9Zomwe zinalipo kale zidzakhalaponso,

zomwe zinachitika kale zidzachitikanso.

Ndiye kuti chatsopano palibiretu pansi pano.

10Kodi chilipo chinthu chimene wina anganene kuti,

“Taona! Ichi ndiye chatsopano?”

Chinalipo kale, kalekale;

chinalipo ife kulibe.

11Anthu akale sakumbukiridwa,

ngakhale amene adzabwera mʼtsogolomu

sadzakumbukiridwa ndi iwo

amene adzabwere pambuyo pawo.

Nzeru Nʼzopandapake

12Ine, Mlalikine, ndinali mfumu ya Israeli mu Yerusalemu. 13Ndinayika mtima wanga pophunzira ndi kufunafuna mwa nzeru zinthu zonse zimene zimachitika pansi pa thambo. Ndi ntchito yolemetsa ndithu imene Mulungu anayipereka kwa anthu! 14Ine ndaona zinthu zonse zochitika pansi pano; zinthu zonsezo ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.

15Chinthu chokhota sichingathe kuwongoledwa;

chimene palibe sichingathe kuwerengedwa.

16Ine ndinaganiza mu mtima mwanga, “Taona, ine ndakula ndi kukhala wa nzeru zochuluka kupambana aliyense amene analamulirapo Yerusalemu ndisanabadwe; ndaphunzira nzeru zochuluka ndi luntha.” 17Ndipo ndinadzipereka kuti ndithe kumvetsa kuti nzeru nʼchiyani, misala nʼchiyani, uchitsiru nʼchiyani, koma ndinazindikira ichi, kuti kuteronso nʼkungodzivuta chabe.

18Pakuti nzeru zochuluka zimabweretsa chisoni chochulukanso:

chidziwitso chochuluka, zowawa zochulukanso.