Mateyu 8 – CCL & NIV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mateyu 8:1-34

Yesu Achiritsa Wakhate

1Iye atatsika ku phiri kuja, anthu ambirimbiri anamutsata. 2Ndipo munthu wakhate anadza kwa Yesu namugwadira nati, “Ambuye, ngati mufuna, mukhoza kundiyeretsa.”

3Yesu anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo nati, “Ndikufuna, yeretsedwa!” Nthawi yomweyo anachiritsidwa khate lake. 4Ndipo Yesu anati kwa iye, “Taona, usawuze wina aliyense. Koma upite kwa mkulu wa ansembe ukadzionetse wekha ndi kupereka mphatso imene Mose analamulira, kuti ukhale umboni kwa iwo.”

Chikhulupiriro cha Kenturiyo

5Yesu atalowa mʼKaperenamu, Kenturiyo anabwera kwa Iye napempha chithandizo, 6nati, “Ambuye, wantchito wanga ali chigonere ku nyumba, sakuthanso kuyenda, akumva kuwawa kwambiri.”

7Ndipo Yesu anati kwa iye, “Ine ndibwera kudzamuchiritsa.”

8Kenturiyo uja anayankha kuti, “Ambuye, ndine wosayenera kuti Inu mukalowe mʼnyumba mwanga. Koma mungonena mawu ndipo wantchito wanga adzachiritsidwa. 9Pakuti inenso ndili pansi pa ulamuliro ndipo ndili ndi asilikali amene ndiwalamulira. Ndikalamulira mmodzi kuti, ‘Pita,’ amapita; ndi kwa wina kuti, ‘Bwera,’ amabwera. Ndikawuza wantchito wanga kuti, ‘Chita ichi,’ iye amachita.”

10Yesu atamva zimenezi, anadabwa ndipo anati kwa omutsatira, “Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti sindinapeze wina aliyense mu Israeli wachikhulupiriro chachikulu chotere. 11Ndikuwuzani kuti ambiri adzabwera kuchokera kummawa ndi kumadzulo, nadzakhala nawo pa phwando pamodzi ndi Abrahamu, Isake ndi Yakobo mu ufumu wakumwamba. 12Koma eni ake ufumuwo adzaponyedwa ku mdima wakunja kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.”

13Pamenepo Yesu anati kwa Kenturiyo, “Pita! Zichitike monga momwe wakhulupirira.” Ndipo wantchito wake anachira pa nthawi yomweyo.

Yesu Achiritsa Anthu Ambiri

14Ndipo Yesu atalowa mʼnyumba ya Petro, anaona mpongozi wake wa Petro ali gone akudwala malungo. 15Ndipo Yesu anakhudza dzanja lake ndipo pomwepo anachira nayamba kumutumikira.

16Itafika nthawi yamadzulo, anthu anabweretsa kwa Iye anthu ambiri ogwidwa ndi ziwanda ndipo anatulutsa ziwandazo ndi mawu okha, nachiritsa odwala onse. 17Uku kunali kukwaniritsa zimene ananena mneneri Yesaya kuti,

“Iye anatenga zofowoka zathu,

nanyamula nthenda zathu.”

Za Kutsatira Yesu

18Yesu ataona gulu la anthu litamuzungulira, analamula kuti awolokere kutsidya lina la nyanja. 19Ndipo mphunzitsi wa malamulo anabwera kwa Iye nati, “Aphunzitsi, ine ndidzakutsatani kulikonse kumene muzipita.”

20Yesu anayankha kuti, “Nkhandwe zili ndi mapanga ndi mbalame zamlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa Munthu alibe malo ogona ngakhale potsamira mutu wake.”

21Wophunzira wina anati kwa Iye, “Ambuye, mundilole ndiyambe ndakayika maliro a abambo anga.”

22Koma Yesu anamuwuza kuti, “Nditsate Ine ndipo uwaleke akufa ayikane akufa okhaokha.”

Yesu Aletsa Namondwe

23Iye atalowa mʼbwato, ophunzira ake anamutsatira. 24Ndipo taonani mwadzidzidzi mphepo yayikulu yamkuntho inawomba pa nyanjapo, kotero kuti bwatolo linayamba kumizidwa ndi mafunde. Koma Yesu anali mtulo. 25Ophunzira ake anapita namudzutsa nati, “Ambuye! Tipulumutseni! Tikumira!”

26Iye anawayankha kuti, “Inu achikhulupiriro chochepa, chifukwa chiyani mukuchita mantha?” Ndipo anayimirira nadzudzula mphepoyo ndi mafunde ndipo panali bata lalikulu.

27Ndipo ophunzirawo anadabwa nafunsa kuti, “Ndi munthu wotani uyu? Kuti ngakhale mphepo ndi mafunde zimvera Iye!”

Ogwidwa ndi Ziwanda a ku Gadara

28Ndipo atafika ku mbali ina ya dera la Gadara, anakumana ndi anthu awiri ogwidwa ndi ziwanda akuchokera ku manda. Iwowa anali woopsa kwambiri kotero kuti panalibe munthu akanatha kudzera njira imeneyo. 29Ndipo iwo anafuwulira kwa Yesu nati, “Mukufuna chiyani kwa ife, Inu Mwana wa Mulungu? Kodi mwabwera kuno kudzatizunza nthawi yake isanafike?”

30Ndipo patali pake panali gulu la nkhumba zimene zimadya. 31Ndipo ziwandazo zinamupempha Yesu kuti, “Ngati mutitulutsa ife mutitumize mu nkhumba izo.”

32Iye anati kwa ziwandazo, “Pitani!” Ndipo pamenepo zinatuluka ndi kukalowa mʼnkhumbazo ndipo nkhumba zonse zinathamangira mʼnyanja ndi kufera momwemo. 33Koma amene amaziweta anathawa nalowa mʼmudzi nafotokoza zonse, kuphatikizapo zimene zinachitika ndi anthu ogwidwa ndi ziwanda aja. 34Ndipo anthu onse a mʼmudziwo anatuluka kukakumana ndi Yesu. Ndipo atamuona Iye, anamupempha kuti achoke mʼdera lawo.

New International Version

Matthew 8:1-34

Jesus Heals a Man With Leprosy

1When Jesus came down from the mountainside, large crowds followed him. 2A man with leprosy8:2 The Greek word traditionally translated leprosy was used for various diseases affecting the skin. came and knelt before him and said, “Lord, if you are willing, you can make me clean.”

3Jesus reached out his hand and touched the man. “I am willing,” he said. “Be clean!” Immediately he was cleansed of his leprosy. 4Then Jesus said to him, “See that you don’t tell anyone. But go, show yourself to the priest and offer the gift Moses commanded, as a testimony to them.”

The Faith of the Centurion

5When Jesus had entered Capernaum, a centurion came to him, asking for help. 6“Lord,” he said, “my servant lies at home paralyzed, suffering terribly.”

7Jesus said to him, “Shall I come and heal him?”

8The centurion replied, “Lord, I do not deserve to have you come under my roof. But just say the word, and my servant will be healed. 9For I myself am a man under authority, with soldiers under me. I tell this one, ‘Go,’ and he goes; and that one, ‘Come,’ and he comes. I say to my servant, ‘Do this,’ and he does it.”

10When Jesus heard this, he was amazed and said to those following him, “Truly I tell you, I have not found anyone in Israel with such great faith. 11I say to you that many will come from the east and the west, and will take their places at the feast with Abraham, Isaac and Jacob in the kingdom of heaven. 12But the subjects of the kingdom will be thrown outside, into the darkness, where there will be weeping and gnashing of teeth.”

13Then Jesus said to the centurion, “Go! Let it be done just as you believed it would.” And his servant was healed at that moment.

Jesus Heals Many

14When Jesus came into Peter’s house, he saw Peter’s mother-in-law lying in bed with a fever. 15He touched her hand and the fever left her, and she got up and began to wait on him.

16When evening came, many who were demon-possessed were brought to him, and he drove out the spirits with a word and healed all the sick. 17This was to fulfill what was spoken through the prophet Isaiah:

“He took up our infirmities

and bore our diseases.”8:17 Isaiah 53:4 (see Septuagint)

The Cost of Following Jesus

18When Jesus saw the crowd around him, he gave orders to cross to the other side of the lake. 19Then a teacher of the law came to him and said, “Teacher, I will follow you wherever you go.”

20Jesus replied, “Foxes have dens and birds have nests, but the Son of Man has no place to lay his head.”

21Another disciple said to him, “Lord, first let me go and bury my father.”

22But Jesus told him, “Follow me, and let the dead bury their own dead.”

Jesus Calms the Storm

23Then he got into the boat and his disciples followed him. 24Suddenly a furious storm came up on the lake, so that the waves swept over the boat. But Jesus was sleeping. 25The disciples went and woke him, saying, “Lord, save us! We’re going to drown!”

26He replied, “You of little faith, why are you so afraid?” Then he got up and rebuked the winds and the waves, and it was completely calm.

27The men were amazed and asked, “What kind of man is this? Even the winds and the waves obey him!”

Jesus Restores Two Demon-Possessed Men

28When he arrived at the other side in the region of the Gadarenes,8:28 Some manuscripts Gergesenes; other manuscripts Gerasenes two demon-possessed men coming from the tombs met him. They were so violent that no one could pass that way. 29“What do you want with us, Son of God?” they shouted. “Have you come here to torture us before the appointed time?”

30Some distance from them a large herd of pigs was feeding. 31The demons begged Jesus, “If you drive us out, send us into the herd of pigs.”

32He said to them, “Go!” So they came out and went into the pigs, and the whole herd rushed down the steep bank into the lake and died in the water. 33Those tending the pigs ran off, went into the town and reported all this, including what had happened to the demon-possessed men. 34Then the whole town went out to meet Jesus. And when they saw him, they pleaded with him to leave their region.