Mateyu 6 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mateyu 6:1-34

Zopereka Zachifundo

1“Samalani kuti musachite ntchito zanu zolungama pamaso pa anthu kuti akuoneni. Popeza ngati mutero simudzalandira mphotho yochokera kwa Atate anu akumwamba.

2“Pamene mupereka zachifundo, musachite modzionetsera monga amachita achiphamaso mʼmasunagoge ndi pa misewu kuti atamidwe ndi anthu. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwowo alandiriratu mphotho yawo yonse. 3Koma pamene mupereka zachifundo, dzanja lanu lamanzere lisadziwe chimene dzanja lanu lamanja likuchita, 4kotero kuti kupereka kwanu kukhale mwachinsinsi. Ndipo Atate anu amene amaona zochitika mwachinsinsi, adzakupatsani mphotho.

Za Kupemphera

5“Pamene mupemphera, musakhale ngati achiphamaso, chifukwa iwo amakonda kupemphera choyimirira mʼmasunagoge ndi pa mphambano za mʼmisewu kuti anthu awaone. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwo alandiriratu mphotho yawo yonse. 6Koma pamene mupemphera, lowani mʼchipinda chanu chamʼkati, ndi kutseka chitseko ndipo mupemphere kwa Atate anu amene saoneka. Ndipo Atate anu, amene amaona zochitika mseri, adzakupatsani mphotho. 7Ndipo pamene mukupemphera, musamabwerezabwereza monga akunja, pakuti iwo amaganiza kuti adzamveka chifukwa chochulutsa mawu. 8Musakhale ngati iwo chifukwa Atate anu amadziwa zimene musowa musanapemphe.

9“Chifukwa chake pempherani motere:

“ ‘Atate athu akumwamba,

dzina lanu lilemekezedwe,

10Ufumu wanu ubwere,

chifuniro chanu chichitike

pansi pano monga kumwamba.

11Mutipatse chakudya chathu chalero.

12Mutikhululukire mangawa athu,

monga ifenso tawakhululukira amangawa athu.

13Ndipo musatitengere kokatiyesa;

koma mutipulumutse kwa woyipayo.’

14Ngati inu mukhululukira anthu pamene akuchimwirani, Atate anu akumwamba adzakukhululukirani. 15Koma ngati inu simukhululukira anthu zolakwa zawo, Atate anunso sadzakukhululukirani machimo anu.

Kusala Kudya

16“Pamene mukusala kudya, musaonetse nkhope yachisoni monga achita achiphamaso, pakuti iwo amasintha nkhope zawo kuonetsa anthu kuti akusala kudya. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwo alandiriratu mphotho yawo yonse. 17Koma pamene ukusala kudya, samba mʼmaso nudzole mafuta kumutu, 18kuti usaonekere kwa anthu kuti ukusala kudya koma kwa Atate ako ali mseri; ndipo Atate ako amene amaona za mseri adzakupatsa mphotho.

Za Chuma cha Kumwamba

19“Musadziwunjikire chuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri zimawononga ndi pamene mbala zimathyola ndi kuba. 20Koma mudziwunjikire chuma kumwamba kumene njenjete ndi dzimbiri siziwononga ndipo mbala sizithyola ndi kuba. 21Pakuti kumene kuli chuma chako, mtima wako udzakhala komweko.

Diso Nyale ya Thupi

22“Diso ndi nyale ya thupi. Ngati maso ako ali bwino, thupi lako lonse lidzakhala mʼkuwala. 23Koma ngati maso ako sali bwino, thupi lako lonse lidzakhala mu mdima. Koma ngati kuwala kuli mwa iwe ndi mdima, ndiye kuti mdimawo ndi waukulu bwanji!

24“Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri. Pakuti pena adzamuda mmodzi ndi kukonda winayo kapena adzagwira ntchito mokhulupirika kwa mmodzi, nadzanyoza winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa chuma pa nthawi imodzi.

Musade Nkhawa

25“Nʼchifukwa chake ndikuwuzani kuti musadere nkhawa za moyo wanu kuti mudzadya chiyani kapena mudzamwa chiyani; kapenanso za thupi lanu kuti mudzavala chiyani. Kodi moyo suposa chakudya? Kodi thupi siliposa zovala? 26Onani mbalame zamlengalenga sizifesa kapena kukolola kapena kusunga mʼnkhokwe komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Kodi inu simuziposa kwambiri? 27Kodi ndani wa inu podandaula angathe kuwonjeza ora limodzi pa moyo wake?

28“Ndipo bwanji inu mudera nkhawa za zovala? Onani makulidwe a maluwa akutchire. Sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu. 29Ndikukuwuzani kuti angakhale Solomoni mu ulemerero wake sanavale mofanana ndi limodzi la maluwa amenewa. 30Ngati umu ndi mmene Mulungu avekera udzu wa kutchire umene ulipo lero ndipo mawa uponyedwa ku moto, kodi sadzakuvekani koposa? Aa! Inu a chikhulupiriro chochepa! 31Chifukwa chake musadere nkhawa ndi kuti, ‘Tidzadya chiyani?’ kapena ‘Tidzamwa chiyani?’ kapena ‘Tidzavala chiyani?’ 32Pakuti anthu akunja amazifuna zinthu zonsezi ndipo Atate anu akumwamba adziwa kuti musowa zimenezi. 33Koma muyambe mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake ndipo zinthu zonsezi zidzapatsidwa kwa inu. 34Chifukwa chake musadere nkhawa ndi za mawa, popeza tsiku lililonse lili ndi zovuta zake zokwanira.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

马太福音 6:1-34

论周济穷人

1“你们要小心,行善的时候不可张扬,故意叫人看见,否则就不能得你们天父的赏赐了。

2“因此,周济穷人的时候,不要大吹大擂,像那些伪君子在会堂和街市上所行的一样,以博取人们的赞赏。我实在告诉你们,他们得到的赏赐仅此而已。 3你们周济穷人的时候,右手所做的别叫左手知道, 4要不声不响地去做。这样,鉴察隐秘事的天父必赏赐你们。

论祷告

5“你们祷告时,不要像伪君子那样。他们喜欢站在会堂里和十字路口上公开祷告,故意让人看见。我实在告诉你们,他们得到的赏赐不过是人的赞赏。 6你们祷告的时候,要进入内室,关上门,向你们肉眼看不见的父祈祷,鉴察隐秘事的父必赏赐你们。

7“你们祷告时不可像外族人那样喋喋不休,他们以为长篇大论,就必蒙上帝垂听。 8不可像他们那样,因为在你们祷告以前,你们的父已经知道你们的需要了。

9“你们应当这样祷告,

“‘我们天上的父,

愿人们都尊崇你的圣名,

10愿你的国度降临,

愿你的旨意在地上成就,就像在天上成就一样。

11求你今天赐给我们日用的饮食。

12饶恕我们的罪,

就像我们饶恕了得罪我们的人。

13不要让我们遇见诱惑,

救我们脱离那恶者。

因为国度、权柄、荣耀都是你的,直到永远。阿们!’

14“如果你们饶恕别人的过犯,你们的天父也必饶恕你们的过犯。 15如果你们不饶恕别人的过犯,你们的天父也不会饶恕你们的过犯。

论禁食

16“你们禁食的时候,不要像伪君子那样愁眉苦脸,因为他们故意蓬头垢面,好让别人知道他们在禁食。我实在告诉你们,他们得到的赏赐不过是人的赞赏。 17你禁食的时候要梳头洗脸, 18不叫人们看出你在禁食,只让你肉眼看不见的父知道,鉴察隐秘事的父必赏赐你。

论积财

19“不要为自己在世上积攒财宝,世上有虫子咬,会生锈,又有贼闯进来偷。 20你们要把财宝积攒在天上,天上没有虫子咬,不会生锈,也没有贼闯进来偷。 21要知道,你的财宝在哪里,你的心也在哪里。

22“眼睛是身上的灯。如果你的眼睛明亮,全身都光明; 23要是你的眼睛昏花6:23 昏花”或作“邪恶”。,全身就黑暗。如果你里面的光黑暗了,那黑暗是多么大啊!

24“一个人不能服侍两位主人,因为他不是恨这位、爱那位,就是重这位、轻那位。你们不能又事奉上帝,又崇拜金钱。

不要忧虑衣食

25“所以我告诉你们,不要为生活忧虑,如吃什么、喝什么,也不要为身体忧虑,如穿什么。难道生命不比饮食重要吗?身体不比穿着重要吗?

26“你们看天上的飞鸟,它们不种,不收,也不在仓里积存粮食,你们的天父尚且养活它们,难道你们还不如飞鸟贵重吗? 27你们谁能用忧虑使自己多活片刻呢?

28“何必为穿着忧虑呢?你们看看野地的百合花是如何生长的,它们既不劳苦,也不纺织。 29但我告诉你们,就连所罗门王最显赫时的穿戴还不如一朵百合花! 30你们的信心太小了!野地里的草今天还在,明天就丢在炉中化为灰烬,上帝还这样装扮它们,何况你们呢? 31所以,你们不要忧虑‘吃什么?喝什么?穿什么?’ 32因为这些都是外族人的追求,你们的天父知道你们的需要。

33“你们要先寻求上帝的国和祂的义,这一切都会赐给你们。 34所以,不要为明天忧虑,因为明天自有明天的忧虑,一天的难处一天担就够了。