Masalimo 51 – CCL & NASV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 51:1-19

Salimo 51

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Pamene Mneneri Natani anabwera kwa iye atachita chigololo ndi Batiseba.

1Mundichitire chifundo, Inu Mulungu,

molingana ndi chikondi chanu chosasinthika;

molingana ndi chifundo chanu chachikulu

mufafanize mphulupulu zanga.

2Munditsuke zolakwa zanga zonse

ndipo mundiyeretse kuchotsa tchimo langa.

3Pakuti ndikudziwa mphulupulu zanga,

ndipo tchimo langa lili pamaso panga nthawi zonse.

4Motsutsana ndi Inu, Inu nokha, ndachimwa

ndipo ndachita zoyipa pamaso panu,

Kotero kuti inu mwapezeka kuti ndinu wolungama

pamene muyankhula ndi pamene muweruza.

5Zoonadi ine ndinali wochimwa pomwe ndimabadwa,

wochimwa kuyambira pa nthawi imene amayi anga anakhala woyembekezera ine.

6Zoonadi inu mumafuna choonadi mu ziwalo zamʼkati mwanga;

mumandiphunzitsa nzeru mʼkati mwanga mwenimweni.

7Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera,

munditsuke ndipo ndidzayera kuposa matalala

8Mundilole ndimve chimwemwe ndi chisangalalo,

mulole kuti mafupa amene mwawamphwanya akondwere.

9Mufulatire machimo anga

ndi kufafaniza zolakwa zanga zonse.

10Mulenge mʼkati mwanga mtima woyera Inu Mulungu

ndi kukonzanso mzimu wokhazikika mwa ine.

11Musandichotse pamaso panu

kapena kuchotsa Mzimu wanu Woyera mwa ine.

12Bwezeretsani mwa ine chimwemwe cha chipulumutso chanu

ndipo mundipatse mzimu wofuna kumvera kuti undilimbitse.

13Pamenepo ndidzaphunzitsa anthu amphulupulu njira zanu

kuti ochimwa adzabwerere kwa inu.

14Mundipulumutse ku tchimo lokhetsa magazi, Inu Mulungu,

Mulungu wa chipulumutso changa,

ndipo lilime langa lidzayimba zachilungamo chanu.

15Inu Ambuye tsekulani milomo yanga,

ndipo pakamwa panga padzalengeza matamando anu.

16Inu simusangalatsidwa ndi nsembe wamba.

Ndikanapereka nsembe yopsereza, Inu simukondwera nayo.

17Nsembe za Mulungu ndi mzimu wosweka;

mtima wosweka ndi wachisoni

Inu Mulungu simudzawunyoza.

18Mwa kukoma mtima kwanu mupange Ziyoni kuti alemere;

mumange makoma a Yerusalemu.

19Kotero kudzakhala nsembe zachilungamo,

nsembe yonse yopsereza yokondweretsa Inu;

ndipo ngʼombe zazimuna zidzaperekedwa pa guwa lanu la nsembe.

New Amharic Standard Version

መዝሙር 51:1-19

መዝሙር 51

የኀጢአት ኑዛዜ

ለመዘምራን አለቃ፤ ዳዊት ወደ ቤርሳቤህ ከገባ በኋላ፣ ነቢዩ ናታን ወደ እርሱ በመጣ ጊዜ፤ የዳዊት መዝሙር።

1እግዚአብሔር ሆይ፤ እንደ ቸርነትህ መጠን፣

ምሕረት አድርግልኝ፤

እንደ ርኅራኄህም ብዛት፣

መተላለፌን ደምስስ።

2በደሌን ፈጽሞ ዕጠብልኝ፤

ከኀጢአቴም አንጻኝ።

3እኔ መተላለፌን ዐውቃለሁና፤

ኀጢአቴም ዘወትር በፊቴ ነው።

4በውሳኔህ ትክክል፣

በምትሰጠው ፍርድም ንጹሕ ትሆን ዘንድ፣

አንተን፣ በርግጥ አንተን ብቻ በደልሁ፤

በፊትህም ክፉ ነገር አደረግሁ።

5ስወለድ ጀምሮ በደለኛ፣

ገና እናቴም ስትፀንሰኝ ኀጢአተኛ ነኝ።

6እነሆ፤ እውነትን ከሰው ልብ ትሻለህ፤51፥6 በዕብራይስጡ የዚህ ሐረግ ትርጕም በትክክል አይታወቅም።

ስለዚህ ጥልቅ ጥበብን በውስጤ አስተምረኝ።51፥6 አስተምረህኛል ወይም ትፈልጋለህ ተብሎ መተርጐም ይቻላል።

7በሂሶጵ እርጨኝ፤ እኔም እነጻለሁ፤

ዕጠበኝ፤ ከበረዶም ይልቅ ነጭ እሆናለሁ።

8ሐሤትንና ደስታን አሰማኝ፤

ያደቀቅሃቸው ዐጥንቶቼም ደስ ይበላቸው።

9ፊትህን ከኀጢአቴ መልስ፤

በደሌንም ሁሉ ደምስስልኝ።

10አምላኬ ሆይ፤ ንጹሕ ልብ ፍጠርልኝ፤

ቀና የሆነውንም መንፈስ በውስጤ አድስ።

11ከፊትህ አትጣለኝ፤

ቅዱስ መንፈስህንም ከእኔ ላይ አትውሰድ።

12የማዳንህን ደስታ መልስልኝ፤

በእሽታ መንፈስም ደግፈህ ያዘኝ።

13እኔም ለሕግ ተላላፊዎች መንገድህን አስተምራለሁ፤

ኀጢአተኞችም ወደ አንተ ይመለሳሉ።

14የድነቴ አምላክ እግዚአብሔር ሆይ፤

ደም ከማፍሰስ አድነኝ፤

አንደበቴም ስለ ጽድቅህ በእልልታ ይዘምራል።

15ጌታ ሆይ ከንፈሮቼን ክፈት፤

አፌም ምስጋናህን ያውጃል።

16መሥዋዕትን ብትወድድ ኖሮ ባቀረብሁልህ ነበር፤

የሚቃጠል መሥዋዕትም ደስ አያሰኝህም።

17እግዚአብሔር የሚቀበለው መሥዋዕት የተሰበረ መንፈስ ነው፤51፥17 ወይም አምላክ ሆይ፤ የእኔ መሥዋዕት የተሰበረ

እግዚአብሔር ሆይ፤

አንተ የተሰበረውንና የተዋረደውን ልብ አትንቅም።

18በበጎ ፈቃድህ ጽዮንን አበልጽጋት፤

የኢየሩሳሌምንም ቅጥሮች ሥራ።

19የጽድቅ መሥዋዕት፣ የሚቃጠል መሥዋዕትና

ሙሉ የሚቃጠል መሥዋዕት ያን ጊዜ ደስ ያሰኙሃል፤

ኰርማዎች በመሠዊያህ ላይ የሚሠዉትም ያን ጊዜ ነው።