Masalimo 1 – The Word of God in Contemporary Chichewa CCL

The Word of God in Contemporary Chichewa

Masalimo 1:1-6

BUKU LOYAMBA

Masalimo 1–41

Salimo 1

1Wodala munthu

amene satsatira uphungu wa anthu ochimwa,

kapena kuyima mʼnjira ya anthu oyipa,

kapena kukhala mʼmagulu a anthu onyoza.

2Koma chikondwerero chake chili mʼmalamulo a Yehova

ndipo mʼmalamulo akewo amalingaliramo usana ndi usiku.

3Iye ali ngati mtengo wodzalidwa mʼmbali mwa mitsinje ya madzi,

umene umabereka zipatso zake pa nyengo yake

ndipo masamba ake safota.

Chilichonse chimene amachita amapindula nacho.

4Sizitero ndi anthu oyipa!

Iwo ali ngati mungu

umene umawuluzidwa ndi mphepo.

5Kotero anthu oyipa sadzatha kuyima pa chiweruzo,

kapena anthu ochimwa mu msonkhano wa anthu olungama.

6Pakuti Yehova amayangʼanira mayendedwe a anthu olungama,

koma mayendedwe a anthu oyipa adzawonongeka.