Marko 14 – CCL & TNCV

The Word of God in Contemporary Chichewa

Marko 14:1-72

Yesu Adzozedwa ku Betaniya

1Tsopano panali patatsala masiku awiri okha kuti tsiku la Paska ndi Phwando la Buledi wopanda yisiti lifike, ndipo akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo ankafunafuna mpata woti amugwire Yesu ndi kumupha. 2Iwo anati, “Koma osati nthawi yaphwando, chifukwa anthu angachite chiwawa.”

3Pamene Iye anali mʼBetaniya, atakhala pa tebulo akudya mʼnyumba ya munthu wodziwika kuti Simoni wakhate, anabwera mayi ndi botolo la mafuta onunkhira amtengo wapamwamba opangidwa ndi nadi. Anaphwanya botololo nakhuthula mafutawo pa mutu wa Yesu.

4Ena mwa iwo amene analipo, anakwiya nati kwa wina ndi mnzake, “Chifukwa chiyani akuwononga mafuta onunkhirawa? 5Akanatheka kugulitsidwa ndi ndalama zambiri zoposa malipiro a pa chaka ndipo ndalamazo ndi kupatsa osauka.” Ndipo anamudzudzula iye mwaukali.

6Yesu anati, “Musiyeni, chifukwa chiyani mukumuvutitsa? Wandichitira Ine chinthu chabwino. 7Anthu osauka mudzakhala nawo nthawi zonse, ndipo mukhoza kuwathandiza nthawi iliyonse mungafune. Koma simudzakhala ndi Ine nthawi zonse. 8Wachita zimene akanatha. Wathira mafuta onunkhira pa thupi langa nthawi isanakwane kukonzekera kuyikidwa kwanga mʼmanda. 9Zoonadi, ndikuwuzani kuti kulikonse kumene Uthenga Wabwino udzalalikidwa pa dziko lonse, zimene wachitazi zidzanenedwa pomukumbukira iye.”

10Kenaka Yudasi Isikarioti, mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anapita kwa akulu a ansembe kuti akamupereke Yesu. 11Iwo anakondwa pakumva zimenezi ndipo analonjeza kumupatsa iye ndalama. Ndipo ankadikira mpata wabwino woti amupereke.

Mgonero wa Ambuye

12Pa tsiku loyamba la Phwando la Buledi wopanda yisiti, nthawi imene mwa mwambo inali ya kupha mwana wankhosa wa Paska, ophunzira a Yesu anafunsa Iye kuti, “Mufuna tipite kuti kumene tikakonzekere kuti mukadyere Paska?”

13Pamenepo anatumiza awiri mwa ophunzira ake, nawawuza kuti, “Pitani mu mzinda, ndipo mukakumana ndi mwamuna wonyamula mtsuko wa madzi. Kamutsatireni iye. 14Kawuzeni mwini nyumba imene iye akalowemo kuti, ‘Aphunzitsi akufunsa: kodi chili kuti chipinda changa cha alendo, kumene ndidyere Paska ndi ophunzira anga?’ 15Iye adzakuonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokhala kale ndi zonse ndi chokonzedwa kale. Katikonzereni ife Paska kumeneko.”

16Ophunzirawo anachoka, napita mu mzindawo ndipo anakapeza zinthu monga mmene Yesu anawawuzira. Choncho anakakonza Paska.

17Ndipo kutada Yesu anafika ndi khumi ndi awiriwo. 18Pamene ankadya pa tebulo Iye anati, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti mmodzi wa inu adzandipereka, mmodzi amene akudya ndi Ine.”

19Iwo anamva chisoni, ndipo mmodzi ndi mmodzi anati kwa Iye, “Kodi ndine?”

20Iye anayankha kuti, “Ndi mmodzi mwa khumi ndi awirinu, amene akusunsa buledi mʼmbale pamodzi ndi Ine. 21Mwana wa Munthu adzapita monga momwe zinalembedwera za Iye. Koma tsoka kwa munthu amene adzapereka Mwana wa Munthu! Kukanakhala bwino kwa iye akanapanda kubadwa.”

22Pamene ankadya, Yesu anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema nagawira ophunzira ake nanena kuti, “Tengani, ili ndi thupi langa.”

23Kenaka anatenga chikho, nayamika nachipereka kwa iwo ndipo onse anamweramo.

24Iye anawawuza kuti, “Awa ndi magazi anga a pangano amene akhetsedwa chifukwa cha ambiri. 25Zoonadi, ndikuwuzani kuti sindidzamwanso kuchokera ku chipatso cha mphesa mpaka tsikulo pamene ndidzamwa chatsopano mu ufumu wa Mulungu.”

26Atayimba nyimbo, anapita ku phiri la Olivi.

Yesu Aneneratu zakuti Petro Adzamukana

27Yesu anati, “Nonse mudzandithawa, pakuti kwalembedwa:

“ ‘Kantha Mʼbusa,

ndipo nkhosa zidzabalalika.’

28Koma ndikadzauka, ndidzatsogola kupita ku Galileya.”

29Petro anati, “Ngakhale onse adzakuthaweni, ine sindidzatero.”

30Yesu anayankha kuti, “Zoona ndikukuwuza kuti lero lino, usiku uno, tambala asanalire kawiri, iweyo udzandikana katatu.”

31Koma Petro ananenetsa kuti, “Ngakhale kutakhala kufa nanu, ine sindidzakukanani.” Ndipo ena onse ananena chimodzimodzi.

Mu Getsemani

32Ndipo anapita ku malo otchedwa Getsemani, ndipo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Khalani pano pamene Ine ndi kupemphera.” 33Iye anatenga Petro, Yakobo ndi Yohane, ndipo anayamba kumva chisoni kwambiri ndi kuvutika mu mtima. 34Iye anawawuza kuti, “Moyo wanga wagwidwa ndi chisoni chofa nacho. Khalani pano ndipo musagone.”

35Atapita patsogolo pangʼono, anagwa pansi ndi kupemphera kuti ngati ndi kotheka oralo limupitirire. 36Iye anati, “Abba, Atate, zinthu zonse ndi zotheka ndi Inu. Chotsereni chikhochi. Komabe chitani zimene Inu mukufuna, osati zimene Ine ndikufuna.”

37Kenaka anabwerera kwa ophunzira ake ndipo anawapeza akugona, Iye anati kwa Petro, “Simoni, kodi uli mtulo? Kodi simukanatha kukhala maso kwa ora limodzi? 38Khalani tcheru ndi kupemphera kuti musalowe mʼmayesero. Mzimu ukufuna, koma thupi ndi lofowoka.”

39Kenakanso anachoka ndi kukapemphera chimodzimodzi. 40Iye atabwerera, anawapezanso akugona, chifukwa mʼmaso mwawo munadzaza tulo. Iwo sanadziwe choti anene kwa Iye.

41Atabweranso kachitatu, anawafunsa kuti, “Kodi mukugonabe ndi kupumula? Pakwana! Nthawi yafika. Taonani, Mwana wa Munthu akuperekedwa mʼmanja mwa anthu ochimwa. 42Nyamukani! Tiyeni tizipita! Uyu wondipereka Ine wafika!”

Amugwira Yesu

43Iye akuyankhulabe, Yudasi, mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anatulukira. Anali ndi gulu la anthu litanyamula malupanga ndi zibonga, otumidwa ndi akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo, ndi akuluakulu.

44Tsopano womupereka anapangana chizindikiro ndi iwo kuti: “Amene ndikapsompsone ndi iyeyo; mukamugwire ndi kumutenga ali womangidwa.” 45Atapita kwa Yesu nthawi yomweyo, Yudasi anati, “Aphunzitsi,” ndipo anapsompsona. 46Anthu anamugwira Yesu ndi kumumanga. 47Kenaka mmodzi wa iwo amene anayima pafupipo anatulutsa lupanga lake nakhapa wantchito wa wamkulu wa ansembe, nʼkudula khutu lake.

48Yesu anati, “Kodi Ine ndikutsogolera gulu lowukira, kuti mubwera ndi malupanga ndi zibonga kudzandigwira? 49Tsiku ndi tsiku ndinali ndi inu, kuphunzitsa mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, koma inu simunandigwire. Koma malemba ayenera kukwaniritsidwa.” 50Pamenepo ophunzira ake onse anathawa namusiya yekha.

51Mnyamata wamngʼono amene anangofundira nsalu yokha, wopanda chovala ankamutsatira Yesu. Atamugwira, 52anathawa wamaliseche kusiya nsalu yake mʼmbuyo.

Yesu ku Bwalo la Milandu

53Anamutengera Yesu kwa mkulu wa ansembe, ndipo akulu a ansembe, akuluakulu ndi aphunzitsi amalamulo anasonkhana pamodzi. 54Petro anamutsatira ali patali, mpaka ku bwalo la mkulu wa ansembe. Kumeneko anakhala pansi ndi alonda namawotha moto.

55Akulu a ansembe ndi onse olamulira a Ayuda ankafunafuna umboni womutsutsa Yesu kuti amuphe, koma sanapeze wina uliwonse. 56Ambiri anamunenera Iye maumboni abodza, koma maumboni awo sanagwirizane.

57Kenaka ena anayimirira namunenera umboni wonama womutsutsa Iye kunena kuti, 58“Tamumva akunena kuti, ‘Ndidzawononga Nyumba ya Mulungu iyi yopangidwa ndi anthu ndipo mʼmasiku atatu ndidzamanga ina, osati yopangidwa ndi munthu.’ ” 59Ngakhale iwonso umboni wawo sunagwirizane.

60Kenaka mkulu wa ansembe anayimirira pakati pawo namufunsa Yesu kuti, “Kodi suyankha? Kodi umboni uwu ndi wotani umene anthu akukuchitira?” 61Koma Yesu anakhala chete ndipo sanayankhe.

Mkulu wa ansembe anabwereza kumufunsa Iye kuti, “Kodi ndiwe Khristu Mwana wa Wodalitsikayo?”

62Yesu anati, “Ndine, ndipo mudzaona Mwana wa Munthu atakhala kudzanja lamanja la Wamphamvuzonse ndipo akubwera mʼmitambo ya kumwamba.”

63Mkulu wa ansembe anangʼamba zovala zaunsembe zake. Iye anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani tikufuna mboni zinanso? 64Mwamva mwanowo. Muganiza chiyani?”

Onse anavomereza kuti ndi woyenera imfa. 65Kenaka ena anayamba kumulavulira malovu; anamumanga mʼmaso, namumenya ndi zibakera ndipo anati, “Nenera!” Ndipo asilikali anamutenga namumenya.

Petro Akana Yesu

66Petro ali chakumunsi kwa bwalo la milandu, mmodzi wa atsikana a ntchito a mkulu wa ansembe anabwera. 67Ataona Petro akuwotha moto, anamuyangʼanitsitsa.

Iye anati, “Iwenso unali pamodzi ndi Mnazareti, Yesu.”

68Koma iye anakana nati, “Sindikudziwa kapena kumvetsetsa zimene ukuyankhula.” Ndipo anachoka napita ku chipata.

69Pamene mtsikana wantchitoyo anamuona iye, anatinso kwa iwo amene anayimirira pomwepo, “Munthu uyu ndi mmodzi mwa iwo.” 70Anakananso kachiwiri.

Patapita kanthawi pangʼono, amene anayimirira pafupi anati kwa Petro, “Zoonadi ndiwe mmodzi wa iwo, pakuti ndiwe mu Galileya.”

71Iye anayamba kudzitemberera, nalumbira kuti, “Sindimudziwa munthu ameneyu.”

72Nthawi yomweyo tambala analira kachiwiri. Pamenepo Petro anakumbukira mawu amene Yesu ananena anamuwuza kuti, “Tambala asanalire kawiri, iwe udzandikana katatu.” Ndipo iye anasweka mtima nayamba kulira.

Thai New Contemporary Version

มาระโก 14:1-72

พระเยซูทรงรับการชโลมที่เบธานี

(มธ.26:2-16; ลก.22:1-6)

1อีกสองวันจะถึงเทศกาลปัสกาและเทศกาลขนมปังไม่ใส่เชื้อ พวกหัวหน้าปุโรหิตกับธรรมาจารย์กำลังหาอุบายที่จะจับพระเยซูมาฆ่า 2เขาพูดกันว่า “แต่อย่าลงมือช่วงเทศกาลเลยมิฉะนั้นประชาชนจะก่อการจลาจล”

3ที่หมู่บ้านเบธานีขณะพระเยซูทรงนั่งรับประทานอาหารอยู่ที่โต๊ะอาหารในบ้านของซีโมนคนโรคเรื้อน หญิงคนหนึ่งถือขวดน้ำมันหอมราคาแพงมากมา น้ำมันหอมนั้นทำจากเครื่องหอมบริสุทธิ์ นางเปิดขวดและรินน้ำมันหอมลงบนพระเศียรของพระองค์

4บางคนที่นั่นไม่พอใจ ต่างพูดกันว่า “ทำให้น้ำมันหอมเสียไปเปล่าๆ ทำไม? 5ถ้านำไปขายคงจะได้เงินมากกว่าค่าจ้างคนงานทั้งปี14:5 ภาษากรีกว่ามากกว่า 300 เดนาริอันซึ่ง 1 เดนาริอันมีค่าเท่ากับค่าแรง 1 วัน จะได้เอาเงินไปให้คนยากจน” และพวกเขาตำหนินางอย่างรุนแรง

6พระเยซูตรัสว่า “อย่ายุ่งกับนาง ไปกวนใจนางทำไม? หญิงคนนี้ได้ทำสิ่งดีงามให้เรา 7ท่านจะมีคนยากจนอยู่กับท่านเสมอและท่านสามารถช่วยพวกเขาได้ทุกเวลาตามที่ท่านต้องการ แต่เราจะไม่ได้อยู่กับท่านเสมอไป 8หญิงคนนี้ทำเท่าที่นางทำได้ นางรินน้ำหอมลงบนกายของเราเป็นการเตรียมสำหรับพิธีศพของเราไว้ล่วงหน้า 9เราบอกความจริงแก่ท่านว่าไม่ว่าข่าวประเสริฐจะเผยแผ่ไปที่ใดๆ ทั่วโลก สิ่งที่นางได้ทำก็จะถูกเล่าขานไปเป็นการระลึกถึงนาง”

10แล้วยูดาสอิสคาริโอทหนึ่งในสาวกสิบสองคนก็ไปพบพวกหัวหน้าปุโรหิตเพื่อจะมอบพระเยซูให้คนเหล่านั้น 11พวกหัวหน้าปุโรหิตฟังแล้วก็ดีใจ และสัญญาจะให้เงินแก่ยูดาส เขาจึงจ้องหาโอกาสที่จะมอบพระองค์แก่พวกนั้น

พระเยซูเสวยปัสกากับเหล่าสาวก

(มธ.26:17-30; ลก.22:7-23)

12วันแรกของเทศกาลขนมปังไม่ใส่เชื้อซึ่งตามธรรมเนียมจะถวายแกะปัสกา เหล่าสาวกของพระเยซูมาทูลถามพระองค์ว่า “พระองค์ทรงประสงค์ให้จัดเตรียมปัสกาสำหรับเสวยที่ไหน?”

13พระองค์จึงทรงส่งสาวกสองคนไปพร้อมทั้งตรัสว่า “จงเข้าไปในเมือง จะมีชายคนหนึ่งทูนหม้อน้ำมาพบท่าน จงตามคนนั้นไป 14จงบอกเจ้าของบ้านที่ชายคนนั้นเดินเข้าไปว่า ‘พระอาจารย์ตรัสถามว่าห้องรับรองแขกที่พระองค์จะเสวยปัสการ่วมกับเหล่าสาวกอยู่ที่ไหน?’ 15เขาจะพาไปดูห้องใหญ่ชั้นบนซึ่งตกแต่งเตรียมไว้เรียบร้อยแล้ว จงเตรียมปัสกาให้เราที่นั่น”

16สาวกทั้งสองก็เข้าไปในเมืองและได้พบสิ่งต่างๆ ตามที่พระเยซูตรัส เขาจึงเตรียมปัสกา

17พอพลบค่ำพระเยซูเสด็จมาพร้อมกับสาวกทั้งสิบสองคน 18ขณะที่นั่งรับประทานอาหารอยู่ที่โต๊ะอาหารพระเยซูตรัสว่า “เราบอกความจริงแก่ท่านว่าคนหนึ่งในพวกท่านจะทรยศเรา คือผู้ที่กำลังรับประทานอาหารกับเรา”

19เหล่าสาวกก็เสียใจและทูลพระองค์ทีละคนว่า “ไม่ใช่ข้าพระองค์แน่ใช่ไหม?”

20พระเยซูตรัสว่า “เขาเป็นหนึ่งในสาวกสิบสองคน เป็นคนที่หยิบอาหารจุ่มในชามเดียวกับเรา 21บุตรมนุษย์จะต้องไปตามที่มีเขียนไว้แต่วิบัติแก่ผู้นั้นที่ทรยศบุตรมนุษย์! ถ้าเขาไม่ได้เกิดมาก็ยังจะดีกับตัวเขาเองมากกว่า”

พิธีมหาสนิท

(มธ.26:26-29; ลก.22:15-20; 1คร.11:23-26)

22ขณะรับประทานอาหารพระเยซูทรงหยิบขนมปัง ทรงขอบพระคุณพระเจ้าแล้วหักส่งให้เหล่าสาวกพร้อมทั้งตรัสว่า “จงรับไปรับประทานเถิด นี่เป็นกายของเรา”

23แล้วพระองค์ทรงหยิบถ้วย ทรงขอบพระคุณพระเจ้าและยื่นให้กับพวกเขา และพวกเขาทุกคนก็ดื่ม

24พระองค์ตรัสกับพวกเขาว่า “นี่คือโลหิตของเราอันเป็นโลหิตแห่งพันธสัญญา14:24 สำเนาต้นฉบับบางสำเนาว่าพันธสัญญาใหม่ซึ่งหลั่งรินเพื่อคนเป็นอันมาก 25เราบอกความจริงแก่ท่านว่าเราจะไม่ดื่มน้ำจากผลองุ่นนี้อีกจนกว่าจะถึงวันนั้นที่เราดื่มใหม่ในอาณาจักรของพระเจ้า”

26เมื่อร้องเพลงสรรเสริญแล้วพวกเขาก็ออกไปยังภูเขามะกอกเทศ

พระเยซูทรงทำนายว่าเปโตรจะปฏิเสธพระองค์

(มธ.26:31-35)

27พระเยซูตรัสแก่เหล่าสาวกว่า “พวกท่านจะทิ้งเราไปกันหมด เพราะมีเขียนไว้ว่า

“ ‘เราจะฟาดฟันคนเลี้ยงแกะ

และแกะจะกระจัดกระจายไป’14:27 ศคย. 13:7

28แต่หลังจากที่เราเป็นขึ้นเราจะไปยังกาลิลีก่อนหน้าท่าน”

29เปโตรประกาศว่า “ถึงใครๆ ทิ้งพระองค์ไปหมดแต่ข้าพระองค์จะไม่ทิ้งพระองค์”

30พระเยซูตรัสตอบว่า “เราบอกความจริงแก่ท่านว่าวันนี้คืนนี้ก่อนไก่ขันสองหน14:30 สำเนาต้นฉบับเก่าแก่บางสำเนาไม่มีคำว่าสองหนท่านเองจะปฏิเสธเราสามครั้ง”

31แต่เปโตรยังยืนยันแข็งขันว่า “ถึงแม้ข้าพระองค์ต้องตายกับพระองค์ ข้าพระองค์จะไม่มีวันปฏิเสธพระองค์” แล้วสาวกที่เหลือก็พูดแบบเดียวกัน

เกทเสมนี

(มธ.26:36-46; ลก.22:40-46)

32พวกเขามายังที่แห่งหนึ่งเรียกว่าเกทเสมนี พระเยซูตรัสกับเหล่าสาวกว่า “จงนั่งอยู่ที่นี่ขณะที่เราไปอธิษฐาน” 33พระองค์ทรงพาเปโตร ยากอบ และยอห์นไปกับพระองค์ด้วย ทรงเศร้าโศกและเป็นทุกข์ยิ่งนัก 34พระองค์ตรัสกับพวกเขาว่า “จิตวิญญาณของเราท่วมท้นด้วยความเศร้าโศกทุกข์หนักแทบจะตาย จงเฝ้าระวังอยู่ที่นี่”

35พระองค์ทรงดำเนินเลยไปอีกหน่อยหนึ่งแล้วซบลงที่พื้นและทรงอธิษฐานว่าหากเป็นไปได้ขอให้ชั่วโมงนั้นผ่านพ้นไปจากพระองค์ 36พระองค์ทรงทูลว่า “อับบา14:36 เป็นภาษาอาราเมค หมายถึงพ่อ พระบิดาเจ้าข้า ทุกสิ่งเป็นไปได้สำหรับพระองค์ ขอทรงเอาถ้วยนี้ไปจากข้าพระองค์ อย่างไรก็ตามอย่าให้เป็นไปตามใจของข้าพระองค์แต่ขอให้เป็นไปตามพระประสงค์ของพระองค์”

37แล้วพระองค์ทรงกลับมาหาสาวกเหล่านั้นและพบว่าพวกเขานอนหลับอยู่จึงตรัสกับเปโตรว่า “ซีโมน ท่านหลับอยู่หรือ? จะคอยเฝ้าระวังอยู่สักชั่วโมงเดียวไม่ได้เชียวหรือ? 38จงเฝ้าระวังและอธิษฐานเพื่อท่านจะไม่ตกเข้าไปอยู่ในการทดลอง จิตวิญญาณพร้อมแล้วก็จริงแต่กายยังอ่อนกำลัง”

39แล้วพระองค์เสด็จไปอธิษฐานอย่างเดียวกันอีกครั้งหนึ่ง 40เมื่อเสด็จกลับมาก็พบว่าพวกเขายังคงหลับอยู่เพราะเขาง่วงมากจนลืมตาไม่ขึ้น พวกเขาไม่รู้จะทูลพระองค์ว่าอย่างไร

41เมื่อทรงกลับมาเป็นครั้งที่สามพระองค์ตรัสกับพวกเขาว่า “พวกท่านยังนอนหลับพักผ่อนอยู่อีกหรือ? พอเถอะ! ถึงเวลาแล้ว ดูเถิด บุตรมนุษย์กำลังจะถูกทรยศให้ตกอยู่ในมือของคนบาปแล้ว 42ลุกขึ้น! ไปกันเถิด! ผู้ทรยศเรามาแล้ว!”

พระเยซูถูกจับกุม

(มธ.26:47-56; ลก.22:47-50; ยน.18:3-11)

43พระองค์ตรัสยังไม่ทันขาดคำ ยูดาสหนึ่งในสาวกสิบสองคนก็ปรากฏตัวขึ้น มีคนกลุ่มใหญ่ถือดาบถือกระบองมากับเขาด้วย พวกหัวหน้าปุโรหิต ธรรมาจารย์ และเหล่าผู้อาวุโสเป็นผู้ส่งคนเหล่านี้มา

44ผู้ทรยศได้ตกลงเรื่องอาณัติสัญญาณกับพวกเขาว่า “ผู้ที่เราจูบคือผู้นั้น ให้จับกุมและคุมตัวเขาไป” 45ยูดาสตรงเข้ามาหาพระเยซูทันทีและทูลว่า “รับบี!” แล้วจูบพระองค์ 46พวกนั้นจึงจับกุมพระเยซู 47แล้วคนหนึ่งซึ่งยืนอยู่ใกล้ๆ ก็ชักดาบออกมาฟันหูบ่าวของมหาปุโรหิตขาด

48พระเยซูตรัสว่า “เราก่อการกบฏหรือ? ท่านจึงได้ถือดาบถือกระบองมาจับเรา 49ทุกวันเราอยู่กับพวกท่าน สั่งสอนอยู่ในลานพระวิหารท่านก็ไม่มาจับกุมเรา แต่จะต้องเป็นจริงตามพระคัมภีร์” 50แล้วทุกคนก็ทิ้งพระองค์และหนีกันไปหมด

51ชายหนุ่มคนหนึ่งมีแต่ผ้าลินินห่มกายได้ติดตามพระเยซูไป เมื่อคนเหล่านั้นจับกุมเขา 52เขาก็สลัดผ้าทิ้งแล้วหนีไปทั้งๆ ที่เปลือยกาย

ต่อหน้าสภาแซนเฮดริน

(มธ.26:57-68; ลก.22:67-71; ยน.18:12,13,19-24)

53พวกเขานำพระเยซูมาพบมหาปุโรหิต ขณะนั้นพวกหัวหน้าปุโรหิต ธรรมาจารย์ และเหล่าผู้อาวุโสมาชุมนุมกันอยู่ 54เปโตรตามพระเยซูมาห่างๆ จนถึงลานบ้านของมหาปุโรหิต เขาก็เข้าไปนั่งผิงไฟกับพวกยามพระวิหาร

55พวกหัวหน้าปุโรหิตและทั้งสภาแซนเฮดรินพยายามค้นหาหลักฐานมามัดตัวพระเยซูเพื่อจะได้ประหารพระองค์ แต่พวกเขาไม่พบเลย 56มีหลายคนเป็นพยานเท็จปรักปรำพระองค์ แต่คำให้การของพวกเขาไม่สอดคล้องกัน

57แล้วมีบางคนยืนขึ้นเป็นพยานเท็จกล่าวหาพระองค์ว่า 58“พวกเราได้ยินเขากล่าวว่า ‘เราจะทำลายวิหารนี้ซึ่งสร้างขึ้นด้วยน้ำมือมนุษย์ แล้วในสามวันจะสร้างอีกวิหารหนึ่งขึ้นซึ่งไม่ได้สร้างด้วยมือมนุษย์’ ” 59ถึงกระนั้นคำพยานของพวกเขาก็ขัดกันเอง

60มหาปุโรหิตจึงยืนขึ้นต่อหน้าที่ประชุมและถามพระเยซูว่า “ท่านจะไม่ตอบอะไรหรือ? ท่านจะว่าอย่างไรกับข้อกล่าวหาของพยานเหล่านี้?” 61แต่พระเยซูทรงนิ่งอยู่ ไม่ได้ตรัสตอบ

มหาปุโรหิตจึงถามพระองค์อีกครั้งว่า “ท่านคือพระคริสต์14:61 หรือพระเมสสิยาห์ พระบุตรขององค์ผู้ทรงเป็นที่สรรเสริญหรือ?”

62พระเยซูตรัสว่า “เราเป็น และท่านจะเห็นบุตรมนุษย์นั่งอยู่เบื้องขวาพระหัตถ์ขององค์ผู้ทรงฤทธิ์และเสด็จมาบนหมู่เมฆแห่งฟ้าสวรรค์”

63มหาปุโรหิตจึงฉีกเสื้อของตนและพูดว่า “เราจะต้องหาพยานอีกทำไม? 64ท่านทั้งหลายได้ยินเขาพูดหมิ่นประมาทแล้ว ท่านคิดเห็นอย่างไร?”

พวกเขาทั้งหมดเห็นพ้องกันว่าพระองค์ควรรับโทษถึงตาย 65แล้วบางคนก็ถ่มน้ำลายรดพระองค์ พวกเขาเอาผ้าปิดพระเนตร ต่อยพระองค์ แล้วพูดว่า “ทายมาสิ!” พวกยามก็นำพระองค์ไปและทุบตีพระองค์

เปโตรปฏิเสธพระเยซู

(มธ.26:69-75; ลก.22:56-62; ยน.18:16-18,25-27)

66ขณะเปโตรอยู่ข้างล่างที่ลานบ้าน มีสาวใช้คนหนึ่งของมหาปุโรหิตผ่านมา 67เมื่อนางเห็นเปโตรผิงไฟอยู่ก็จ้องมองและพูดว่า

“เจ้าก็อยู่กับเยซูชาวนาซาเร็ธด้วย”

68แต่เปโตรปฏิเสธว่า “เจ้าพูดอะไรข้าไม่รู้เรื่อง” แล้วออกไปที่ทางเข้า14:68 สำเนาต้นฉบับเก่าแก่บางสำเนาเพิ่มข้อความว่าแล้วไก่ก็ขัน

69สาวใช้คนนั้นเห็นเขาที่นั่นก็พูดกับคนที่ยืนอยู่แถวนั้นอีกว่า “คนนี้ก็เป็นคนหนึ่งในพวกนั้น” 70เปโตรปฏิเสธอีก

ครู่หนึ่งต่อมาคนที่ยืนใกล้ๆ พูดกับเปโตรว่า “ใช่แน่ๆ เจ้าเป็นคนหนึ่งในพวกนั้นเพราะเจ้าเป็นชาวกาลิลี”

71เปโตรจึงเริ่มสบถสาบานเป็นการใหญ่ว่า “ข้าไม่รู้จักคนที่พวกเจ้าพูดถึง”

72ทันใดนั้นไก่ก็ขันเป็นครั้งที่สอง14:72 สำเนาต้นฉบับเก่าแก่บางสำเนาไม่มีข้อความว่าครั้งที่สอง เปโตรจึงนึกขึ้นได้ที่พระเยซูตรัสกับเขาไว้ว่า “ก่อนไก่ขันสองหน14:72 สำเนาต้นฉบับเก่าแก่บางสำเนาไม่มีข้อความว่าสองหนท่านจะปฏิเสธเราสามครั้ง” เปโตรก็ร้องไห้ออกมาด้วยความเสียใจ