Maliro 1 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Maliro 1:1-22

1Haa! Mzinda uja wasiyidwa wokhawokha,

umene kale unali wodzaza ndi anthu!

Kale unali wotchuka pakati pa mitundu ya anthu!

Tsopano wasanduka ngati mkazi wamasiye.

Kale unali mfumukazi ya onse pa dziko lapansi,

tsopano wasanduka kapolo.

2Ukulira mowawidwa mtima usiku wonse,

misozi ili pa masaya pake.

Mwa abwenzi ake onse,

palibe ndi mmodzi yemwe womutonthoza.

Abwenzi ake onse amuchitira chiwembu;

onse akhala adani ake.

3Yuda watengedwa ku ukapolo,

kukazunzika ndi kukagwira ntchito yolemetsa.

Iye akukhala pakati pa anthu a mitundu ina;

ndipo alibe malo opumulira.

Onse omuthamangitsa iye amupitirira,

ndipo alibe kwina kothawira.

4Misewu yopita ku Ziyoni ikulira,

chifukwa palibe ndi mmodzi yemwe akubwera ku maphwando ake.

Zipata zake zonse zili pululu,

ansembe akubuwula.

Anamwali ake akulira,

ndipo ali mʼmasautso woopsa.

5Adani ake asanduka mabwana ake;

odana naye akupeza bwino.

Yehova wamubweretsera mavuto

chifukwa cha machimo ake ambiri.

Ana ake atengedwa ukapolo

pamaso pa mdani.

6Ulemerero wonse wa mwana wamkazi wa Ziyoni

wachokeratu.

Akalonga ake ali ngati mbawala

zosowa msipu;

alibe mphamvu zothawira

owathamangitsa.

7Pa masiku a masautso ndi kuzunzika kwake,

Yerusalemu amakumbukira chuma chonse

chimene mʼmasiku amakedzana chinali chake.

Anthu ake atagwidwa ndi adani ake,

panalibe aliyense womuthandiza.

Adani ake ankamuyangʼana

ndi kumuseka chifukwa cha kuwonongeka kwake.

8Yerusalemu wachimwa kwambiri

ndipo potero wakhala wodetsedwa.

Onse amene ankamulemekeza pano akumunyoza,

chifukwa aona umaliseche wake.

Iye mwini akubuwula

ndipo akubisa nkhope yake.

9Uve wake umaonekera pa zovala zake;

iye sanaganizire za tsogolo lake.

Nʼchifukwa chake kugwa kwake kunali kwakukulu;

ndipo analibe womutonthoza.

“Inu Yehova, taonani masautso anga,

pakuti mdani wapambana.”

10Adani amulanda

chuma chake chonse;

iye anaona mitundu ya anthu achikunja ikulowa mʼmalo ake opatulika,

amene Inu Mulungu munawaletsa

kulowa mu msonkhano wanu.

11Anthu ake onse akubuwula

pamene akufunafuna chakudya;

asinthanitsa chuma chawo ndi chakudya

kuti akhale ndi moyo.

“Inu Yehova, taonani ndipo ganizirani,

chifukwa ine ndanyozeka.”

12“Kodi zimenezi mukuziyesa zachabe, inu nonse mukudutsa?

Yangʼanani ndipo muone.

Kodi pali mavuto ofanana ndi

amene andigwerawa,

amene Ambuye anandibweretsera

pa tsiku la ukali wake?

13“Anatumiza moto kuchokera kumwamba,

unalowa mpaka mʼmafupa anga.

Anayala ukonde kuti ukole mapazi anga

ndipo anandibweza.

Anandisiya wopanda chilichonse,

wolefuka tsiku lonse.

14“Wazindikira machimo anga onse

ndipo ndi manja ake anawaluka pamodzi.

Machimowa afika pakhosi panga,

ndipo Ambuye wandithetsa mphamvu.

Iye wandipereka

kwa anthu amene sindingalimbane nawo.

15“Ambuye wakana

anthu anga onse amphamvu omwe ankakhala nane:

wasonkhanitsa gulu lankhondo kuti lilimbane nane,

kuti litekedze anyamata anga;

mʼmalo ofinyira mphesa Ambuye wapondereza

anamwali a Yuda.

16“Chifukwa cha zimenezi ndikulira

ndipo maso anga adzaza ndi misozi.

Palibe aliyense pafupi woti anditonthoze,

palibe aliyense wondilimbitsa mtima.

Ana anga ali okhaokha

chifukwa mdani watigonjetsa.

17“Ziyoni wakweza manja ake,

koma palibe aliyense womutonthoza.

Yehova walamula kuti abale ake

a Yakobo akhale adani ake;

Yerusalemu wasanduka

chinthu chodetsedwa pakati pawo.

18“Yehova ndi wolungama,

koma ndine ndinawukira malamulo ake.

Imvani inu anthu a mitundu yonse;

onani masautso anga.

Anyamata ndi anamwali anga

agwidwa ukapolo.

19“Ndinayitana abwenzi anga

koma anandinyenga.

Ansembe ndi akuluakulu anga

anafa mu mzinda

pamene ankafunafuna chakudya

kuti akhale ndi moyo.

20“Inu Yehova, onani mmene ine ndavutikira!

Ndikuzunzika mʼkati mwanga,

ndipo mu mtima mwanga ndasautsidwa

chifukwa ndakhala osamvera.

Mʼmisewu anthu akuphedwa,

ndipo ku mudzi kuli imfa yokhayokha.

21“Anthu amva kubuwula kwanga,

koma palibe wonditonthoza.

Adani anga onse amva masautso anga;

iwo akusangalala pa zimene Inu mwachita.

Lifikitseni tsiku limene munalonjeza lija

kuti iwonso adzakhale ngati ine.

22“Lolani kuti ntchito zawo zoyipa zifike pamaso panu;

muwalange

ngati mmene mwandilangira ine

chifukwa cha machimo anga onse.

Ndikubuwula kwambiri

ndipo mtima wanga walefuka.”