Chenjezo kwa Ansembe
1“Tsono chenjezo ili ndi la inu, inu ansembe.” 2Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ngati simumvera, ndipo ngati simulemekeza dzina langa mʼmitima mwanu, ndidzakutembererani ndipo madalitso onse munawalandira ndidzawatemberera. Ndithu, ndawatemberera kale, chifukwa simunalemekeze Ine mʼmitima mwanu.”
3“Ine ndidzalanga zidzukulu zanu chifukwa cha inu; ndidzakupakani kumaso ndowe za nsembe zanu zachikondwerero, ndipo ndidzakutayani pamodzi ndi ndowezo.” 4Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Apo mudzadziwa kuti Ine ndatumiza chenjezoli kuti pangano langa ndi Levi lipitirire. 5Ine ndinali naye pa pangano, pangano lopatsa moyo ndi mtendere, ndipo ndinamupatsa zimenezi kuti azindiopa, ndipo anandiopadi ndi kulemekeza dzina langa. 6Pakamwa pake pankatuluka malangizo woona, ndipo pa milomo yake sipanapezeke chinyengo. Iye anayenda nane mwamtendere ndi molungama mtima, ndipo anabweza anthu ambiri mʼnjira zawo zauchimo.
7“Pakuti wansembe ayenera kukhala ndi chidziwitso, ndipo anthu ayenera kufunafuna malangizo kuchokera kwa iye, popeza iye ndi mthenga wa Yehova Wamphamvuzonse. 8Koma inu mwasiya njira yanga ndipo mwapunthwitsa anthu ambiri ndi ziphunzitso zanu; mwayipitsa pangano langa ndi Levi,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. 9“Choncho Ine ndachititsa kuti munyozedwe ndi kuchititsidwa manyazi pamaso pa anthu onse, chifukwa simunatsate njira zanga koma mwakhala mukuonetsa kukondera pa nkhani za malamulo.”
Kusakhulupirika kwa Yuda
10Kodi sitili naye Atate mmodzi tonsefe? Kodi anatilenga si Mulungu mmodzi? Chifukwa chiyani tikudetsa pangano la makolo athu posamakhulupirirana wina ndi mnzake?
11Yuda waleka kukhulupirika. Chinthu chonyansa chachitika mu Israeli ndi mu Yerusalemu: Yuda wayipitsa malo opatulika amene Yehova amawakonda, pokwatira mkazi wopembedza mulungu wachilendo. 12Ndipo wina aliyense wochita zimenezi, kaya munthuyo ndi wotani, Yehova amuchotse ku banja la Yakobo, ngakhale atabweretsa zopereka kwa Yehova Wamphamvuzonse.
13China chimene mumachita ndi ichi: Mumakhathamiritsa guwa lansembe la Yehova ndi misozi. Mumalira ndi kufuwula kwambiri chifukwa Iye amakana kuyangʼana nsembe zanu, kapena kulandira mokondwera nsembe za mʼmanja mwanu. 14Inu mukufunsa kuti, “Chifukwa chake nʼchiyani?” Chifukwa chake nʼchakuti Yehova ndi mboni ya pangano limene unachita ndi mkazi wa unyamata wako, chifukwa sunakhulupirike kwa iye, ngakhale kuti iyeyo ndiye mnzako, ndi mkazi wako mwapangano.
15Kodi Yehova sanawalenge iwo ngati munthu mmodzi? Ndi ake mʼthupi ndi mu mzimu. Nʼchifukwa chiyani ali mmodzi? Chifukwa Iye amafuna ana opembedza Mulungu. Motero samala moyo wako wauzimu, ndipo usakhale wosakhulupirika kwa mkazi wa unyamata wako.
16Yehova Mulungu wa Israeli akuti, “Ndimadana ndi kulekana ukwati. Ndimadana ndi munthu wochita zankhanza zotere kwa mkazi wake,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
Choncho tetezani mzimu wanu, ndipo musakhale osakhulupirika.
Tsiku la Chiweruzo
17Mwamutopetsa Yehova ndi zoyankhula zanu.
Inu mukufunsa kuti, “Kodi tamutopetsa bwanji?”
Mwamutopetsa ponena kuti, “Aliyense amene amachita zoyipa ndi wabwino pamaso pa Yehova ndipo iye amakondwera naye” kapena pofunsa kuti, “Ali kuti Mulungu woweruza mwachilungamo?”
Додатне опомене свештеницима
1Свештеници, ево сада и за вас заповести: 2Ако не послушате, ако срцем не жудите да имену моме дате славу – каже Господ над војскама – проклетство ћу послати на вас. Проклећу и благослове ваше, како сам их и проклео, јер нисте срцем жудили.
3Ево, покараћу вам потомке, а вама ћу лица замазати изнутрицама, отпацима ваших празничних жртава, да вас такве одведу. 4И тада ћете знати да сам ја овако заповедио за вас, да би важио мој савез са Левијем – каже Господ над војскама. 5А мој савез са њим је био у животу и миру који сам му дао да би ме поштовао. И он ми је част одавао и страховао од мог имена. 6Поучавао је истинит Закон и није говорио неправду. Живео је са мном спокојно и праведно и многе је одвратио од греха.
7Јер би уста свештеника требало да чувају знање, да људи од њега траже поуку јер је он гласник Господа над војскама. 8Али ви сте скренули са тог пута па сте многе саплели да крше Закон и Левијев савез – каже Господ над војскама. 9Зато сам вас учинио презреним и пониженим пред свим народима, јер се нисте држали мојих путева и гледали сте ко је ко у стварима Закона.“
Кршење савеза разводом
10Немамо ли сви ми једног оца? Није ли нас један Бог створио? Зашто изневеравамо једни друге и скрнавимо савез својих отаца?
11Јуда је неверан, а у Израиљу и у Јерусалиму је почињена гадост, зато што је Јуда оскрнавио Господње Светилиште које је он волео и оженио ћерку туђинског бога. 12Нека Господ из Јаковљевих шатора истреби сваког ко то чини, и ко је будан и ко одговара, и ко приноси жртву Господу над војскама.
13А и ово још радите: сузама заливате жртвеник Господњи, вапите и стењете. Зато се он не осврће на жртве и не ужива у вашим приносима. 14А ви питате: „Зашто?“ Зато што је Господ сведок између тебе и жене из младости твоје којој си неверан, а она ти је пријатељ и законита жена.
15Зар их он није створио као једно? Није ли у њему остатак духа? А чему једно? Тежи Божијем потомству. Зато чувајте помно дух свој и не варајте жену из младости своје.
16„Човек што мрзи жену своју и разводи се – каже Господ, Бог Израиљев – злоставља ону коју би требало да штити – говори Господ над војскама.“
Зато чувајте помно дух свој и не будите неверни.
Кршење савеза неправдом
17Додијали сте Господу својим изјавама.
Али ви питате: „Како смо то додијали?“
Тако што говорите: „Пред Господом је добар свако ко зло чини. Он ужива у таквима.“ Или: „Где је тај Бог правде?“