Kubwera kwa Mzimu Woyera
1Litafika tsiku la chikondwerero cha Pentekosite, onse anali pamodzi. 2Mwadzidzidzi kunamveka mkokomo kuchokera kumwamba ngati wa mphepo yamphamvu, ndipo inadzaza nyumba yonse imene amakhala. 3Iwo anaona zinthu zokhala ngati malilime amoto ogawikana ndipo anakhala pa aliyense wa iwo. 4Ndipo onse anadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kuyankhula mu ziyankhulo zina, monga Mzimu Woyerayo anawayankhulitsa.
5Ayuda woopa Mulungu ochokera ku mayiko onse a dziko lapansi ankakhala mu Yerusalemu nthawi imeneyi. 6Utamveka mkokomo uja, gulu la anthu linasonkhana. Anthuwo anadabwa chifukwa aliyense anawamva atumwiwo akuyankhula ziyankhulo zosiyanasiyana. 7Mothedwa nzeru anafunsana kuti, “Kodi anthu onse amene akuyankhulawa si Agalileya? 8Nanga bwanji aliyense wa ife akuwamva iwo mu chinenero cha kwawo? 9Apanti, Amedi ndi Aelami; okhala ku Mesopotamiya, ku Yudeya ndi ku Kapadokiya, ku Ponto ndi ku Asiya, 10ku Frugiya ndi Pamfiliya, ku Igupto ndi ku madera a ku Libiya kufupi ndi ku Kurene; alendo ochokera ku Roma, 11Ayuda ndi otsatira chipembedzo cha Chiyuda onse pamodzi; Akrete ndi Aarabu, ife tonse tikuwamva akuyankhula za ntchito zodabwitsa za Mulungu mu ziyankhulo zathu.” 12Modabwa ndi mothedwa nzeru anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Zimenezi zikutanthauzanji?”
13Koma ena anawaseka nati, “Aledzera vinyo watsopano.”
Uthenga wa Petro
14Koma Petro anayimirira pamodzi ndi atumwi khumi ndi mmodziwo ndipo anakweza mawu ake nayankhula kwa gulu la anthu nati: “Ayuda anzanga, ndi nonse amene muli mu Yerusalemu, mvetsetsani izi ndipo tcherani khutu ku zimene ndikunena. 15Kunena zoona, anthu awa sanaledzere ayi, monga momwe mukuganizira, pakuti ino ndi 9 koloko mmawa! 16Koma izi ndi zimene ananena Mneneri Yoweli kuti:
17“ ‘Mulungu akuti, mʼmasiku otsiriza
ndidzakhuthulira Mzimu wanga pa anthu onse.
Ana anu aamuna ndi aakazi adzanenera,
anyamata anu adzaona masomphenya,
nkhalamba zanu zidzalota maloto.
18Ngakhalenso pa antchito anga aamuna ndi aakazi,
ndidzakhuthulira Mzimu wanga masiku amenewo,
ndipo iwo adzanenera.
19Ndipo ndidzaonetsa zodabwitsa mlengalenga
ndi zizindikiro pa dziko lapansi pano,
ndizo magazi, moto ndi utsi watolotolo.
20Dzuwa lidzadetsedwa
ndipo mwezi udzaoneka ngati magazi
lisanafike tsiku lalikulu ndi laulemerero la Ambuye.
21Ndipo aliyense amene adzayitana
pa dzina la Ambuye adzapulumuka.’
22“Inu Aisraeli mverani mawu awa; Yesu wa ku Nazareti anali munthu amene anaperekedwa kwa inu ndi Mulungu. Ndipo Mulungu anakutsimikizirani zimenezi ndi zamphamvu, zodabwitsa ndi zizindikiro zimene anachita mwa Iye pakati panu, monga inu mukudziwa. 23Yesu ameneyu anaperekedwa kwa inu mwa kufuna ndi kudziwiratu kwa Mulungu; ndipo inu mothandizidwa ndi anthu oyipa, munamupha Iye pomupachika pa mtanda. 24Koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa, kumumasula Iye ku zowawa za imfa, chifukwa kunali kosatheka kuti agwiridwe ndi imfa. 25Pakuti Davide ananena za Iye kuti,
“ ‘Ndinaona Ambuye pamaso panga nthawi zonse.
Chifukwa Iye ali kudzanja langa lamanja,
Ine sindidzagwedezeka.
26Chifukwa chake mtima wanga ndi wokondwa ndipo lilime langa likukondwera;
thupi langanso lidzakhala ndi chiyembekezo.
27Chifukwa simudzasiya moyo wanga kumalo a anthu akufa, ku manda,
kapena kulekerera Woyerayo kuti awole.
28Inu munandidziwitsa ine njira zamoyo;
Inu mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu.’
29“Abale, ine ndikuwuzani motsimikiza kuti kholo lathu Davide anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda, ndipo manda ake alipo lero lino. 30Koma iye anali mneneri ndipo anadziwa kuti Mulungu analonjeza ndi lumbiro kuti adzayika mmodzi wa zidzukulu zake pa mpando waufumu. 31Davide ataoneratu zimene zinali mʼtsogolo anayankhula za kuuka kwa Khristu, kuti Iye sanasiyidwe mʼmanda, ndipo thupi lake silinawole. 32Mulungu wamuukitsa Yesu ameneyu, ndipo ife ndife mboni za zimenezi. 33Khristu anakwezedwa kukhala kudzanja lamanja la Mulungu, nalandira Mzimu Woyera amene Atate anamulonjeza, ndipo watipatsa ife zimene mukuona ndi kumvazi. 34Pakuti si Davide anakwera kumwamba koma iye akuti,
“ ‘Ambuye anawuza Ambuye anga kuti:
Khala kudzanja langa lamanja
35mpaka nditasandutsa adani ako
kukhala chopondapo mapazi ako.’
36“Nʼchifukwa chake, Aisraeli onse adziwe ndithu kuti, Yesu amene inu munamupachika, Mulungu wamuyika kukhala Ambuye ndiponso Mpulumutsi.”
37Anthu atamva zimenezi, anatsutsika kwambiri mu mtima ndipo anati kwa Petro ndi atumwi enawo, “Abale, kodi ife tichite chiyani?”
38Petro anawayankha kuti, “Lapani ndipo mubatizidwe aliyense wa inu, mʼdzina la Yesu Khristu kuti machimo anu akhululukidwe. Ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. 39Pakuti lonjezoli ndi lanu ndi ana anu ndiponso la onse amene ali kutali, ndi iwo onse amene Ambuye Mulungu wathu adzawayitane.”
40Petro anawachenjeza ndi mawu ena ambiri, ndipo anawadandaulira iwo kuti, “Mudzipulumutse ku mʼbado owonongeka uno.” 41Iwo amene anawulandira uthenga wake anabatizidwa ndipo tsiku lomwelo miyoyo pafupifupi 3,000 inawonjezedwa ku gulu lawo.
Kuyanjana kwa Okhulupirira
42Iwo ankasonkhana pamodzi kuphunzitsidwa ndi atumwi, pachiyanjano, pachakudya ndi popemphera. 43Aliyense ankachita mantha chifukwa cha zodabwitsa ndi zizindikiro zambiri zimene atumwi ankachita. 44Okhulupirira onse anali pamodzi ndipo aliyense ankapereka zinthu zake kuti zikhale za onse. 45Ankagulitsa minda yawo ndi katundu wawo, ndi kugawira kwa aliyense molingana ndi zosowa zake. 46Tsiku ndi tsiku ankasonkhana pamodzi pa bwalo la pa Nyumba ya Mulungu. Ankadya pamodzi mʼnyumba zawo mwasangala ndi mtima woona. 47Ankayamika Mulungu ndipo anthu onse ankawakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankawonjezera ena pa chiwerengero cha olandira chipulumutso.