Machitidwe a Atumwi 13 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Machitidwe a Atumwi 13:1-52

Barnaba ndi Saulo Atumidwa ndi Mpingo

1Mu mpingo wa ku Antiokeya munali aneneri ndi aphunzitsi awa: Barnaba, Simeoni, Lukia wa ku Kurene, Manayeni (amene analeredwa pamodzi ndi mfumu Herode), ndiponso Saulo. 2Iwo pamene ankapembedza Ambuye ndi kusala kudya, Mzimu Woyera anati, “Mundipatulire Barnaba ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndinawayitanira.” 3Ndipo atasala kudya ndi kupemphera anasanjika manja awo pa iwo nawatumiza.

Ku Kupro

4Barnaba ndi Saulo motumidwa ndi Mzimu Woyera, anapita ku Selukeya ndipo kuchokera kumeneko anakwera sitima ya pamadzi kupita ku Kupro. 5Pamene anafika ku Salamisi, analalikira Mawu a Mulungu mʼMasunagoge a Ayuda. Iwo anali ndi Yohane monga wowatumikira.

6Iwo anayenda pa chilumba chonse mpaka anafika ku Pafo, kumeneko anapezanako ndi Myuda, wamatsenga amene analinso mneneri wonama dzina lake Barayesu. 7Iyeyu, amathandiza mkulu wa boma, Sergio Paulo. Mkulu wa bomayu, munthu wanzeru, anayitana Barnaba ndi Saulo chifukwa anafuna kumva Mawu a Mulungu. 8Koma Elima wamatsengayo, (Elima tanthauzo lake ndi wamatsenga), anatsutsana nawo ndipo anafuna kumuletsa mkulu wa bomayo kuti asakhulupirire. 9Koma Saulo, amenenso amatchedwa Paulo, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera anamuyangʼanitsitsa Elima ndipo anati, 10“Iwe ndiwe mwana wa mdierekezi ndiponso mdani wa chilungamo! Ndiwe wodzaza ndi chinyengo cha mtundu uliwonse ndi kuchenjera konse. Kodi sudzaleka kupotoza njira zolungama za Ambuye? 11Tsopano dzanja la Ambuye likukutsutsa iwe. Udzakhala wosaona ndipo kwa kanthawi sudzatha kuona kuwala kwa dzuwa.”

Nthawi yomweyo khungu ndi mdima zinamugwera ndipo anafunafuna munthu woti amugwire dzanja kuti amutsogolere. 12Pamene mkulu wa bomayo anaona zimene zinachitika anakhulupirira pakuti anadabwa ndi chiphunzitso cha Ambuye.

Antiokeya wa ku Pisidiya

13Kuchokera ku Pafo, Paulo ndi anzake anayenda pa sitima ya pamadzi kupita ku Perga wa ku Pamfiliya, kumeneko Yohane anawasiya nabwerera ku Yerusalemu. 14Kuchokera ku Perga anapita ku Pisidiya wa ku Antiokeya. Pa tsiku la Sabata analowa mʼsunagoge, nakhala pansi. 15Atawerenga mawu a mʼMalamulo ndi Aneneri, akulu a sunagoge anawatumizira mawu ndi kuti, “Abale ngati muli ndi mawu olimbikitsa nawo anthuwa, nenani.”

16Atayimirira, Paulo anakweza dzanja lake ndi kuti, “Inu Aisraeli ndiponso inu a mitundu ina amene mumapembedza Mulungu, tandimverani! 17Mulungu wa Aisraeli anasankha makolo athu ndipo anawapatsa chuma chambiri pamene amakhala ku Igupto. Anawatulutsa mʼdzikomo ndi dzanja lake lamphamvu. 18Ndipo Iye anapirira khalidwe lawo mʼchipululu kwa zaka makumi anayi. 19Mulungu anawagonjetsera mitundu isanu ndi iwiri ya ku Kanaani ndipo anapereka dzikolo kwa Israeli kuti likhale lawo. 20Izi zonse zinatenga zaka 450.

“Zitatha izi, Mulungu anawapatsa oweruza mpaka nthawi ya mneneri Samueli. 21Kenaka anthu anapempha kuti awapatse mfumu, ndipo anawapatsa Sauli mwana wa Kisi, wa fuko la Benjamini amene analamulira zaka makumi anayi. 22Mulungu atamuchotsa Sauli, anayika Davide kukhala mfumu yawo. Mulungu anamuchitira umboni kuti, ‘Ndapeza Davide mwana wa Yese munthu wa pamtima panga; iye adzachita zonse zimene ine ndikufuna kuti iye achite.’

23“Kuchokera mwa zidzukulu za munthu ameneyu, Mulungu anawutsa Yesu kukhala Mpulumutsi wa Aisraeli, monga analonjezera. 24Yesu asanabwere, Yohane analalikira kwa anthu onse Aisraeli za kutembenuka mtima ndi ubatizo. 25Pamene Yohane amatsiriza ntchito yake anati: ‘Mukuganiza kuti ine ndine yani? Ine sindine ameneyo ayi, koma Iye akubwera pambuyo panga, amene ine sindine woyenera kumasula zingwe za nsapato zake.’

26“Abale, ana a Abrahamu, ndiponso inu a mitundu ina amene mumaopa Mulungu, Iye watumiza uthenga wachipulumutsowo kwa ife. 27Anthu a ku Yerusalemu ndi atsogoleri awo sanazindikire Yesu, komabe pomuweruza Yesu anakwaniritsa mawu a Aneneri amene amawerengedwa Sabata lililonse. 28Ngakhale sanapeze chifukwa choti afe, anapempha Pilato kuti amuphe. 29Atachita zonse zimene zinalembedwa za Iye, iwo anamuchotsa pa mtengo ndipo anamuyika mʼmanda. 30Koma Mulungu anamuukitsa, 31ndipo kwa masiku ambiri anaonekera kwa amene anayenda naye kuchokera ku Galileya mpaka ku Yerusalemu. Iwowa tsopano ndi mboni zake kwa anthu a Israeli.

32“Ife tikukuwuzani Uthenga Wabwino; umene Mulungu analonjeza makolo athu. 33Iye wakwaniritsa zimenezi kwa ife ana awo, poukitsa Yesu kuchokera kwa akufa. Monga zinalembedwa mu Salimo lachiwiri kuti,

“Iwe ndiwe mwana wanga;

lero ine ndakhala Atate ako.”

34Zakuti Mulungu anamuukitsa kuti asawole konse, zinanenedwa mʼmawu awa:

“ ‘Ine, ndidzakupatsa madalitso opatulika ndi odalirika amene ndinalonjeza Davide.’

35Nʼchifukwa chakenso zinalembedwa mu Salimo lina kuti,

“ ‘Simudzalekerera woyera wanu kuti awole.’

36“Pakuti pamene Davide anatsiriza kutumikira Mulungu mu mʼbado wake, anamwalira, iye anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake ndipo thupi lake linawola. 37Koma amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa sanawole ayi.

38“Nʼchifukwa chake, abale anga, dziwani kuti mwa Yesu chikhululukiro cha machimo chikulalikidwa. 39Kudzera mwa Iye aliyense amene akhulupirira, alungamitsidwa kuchoka ku tchimo lililonse limene silingachoke ndi Malamulo a Mose. 40Samalani kuti zimene aneneri akunena zisakuchitikireni inu:

41“ ‘Onani, inu anthu onyoza,

dabwani ndipo wonongekani,

chifukwa ine ndidzachita china chake mʼmasiku anu,

inu simudzazikhulupirira

ngakhale wina atakufotokozerani!’ ”

42Pamene Paulo ndi Barnaba amatuluka mʼSunagoge, anthu anawapempha kuti adzapitirize kuyankhula zinthu zimenezi Sabata linalo. 43Atatha mapemphero, Ayuda ambiri ndi anthu odzipereka otembenukira ku Chiyuda anatsatira Paulo ndi Barnaba, iwo anayankhula ndi anthuwo ndipo anawapempha kuti apitirire mʼchisomo cha Mulungu.

44Pa Sabata linalo pafupifupi anthu onse a mu mzindawo anasonkhana kudzamva Mawu a Ambuye. 45Pamene Ayuda anaona gulu la anthu, anachita nsanje ndipo anayankhula zamwano kutsutsana ndi zimene Paulo amanena.

46Ndipo Paulo ndi Barnaba anawayankha molimba mtima kuti, “Ife tinayenera kuyankhula Mawu a Mulungu kwa inu poyamba. Popeza inu mwawakana ndi kudziyesa nokha osayenera moyo wosatha, ife tsopano tikupita kwa anthu a mitundu ina. 47Pakuti izi ndi zimene Ambuye anatilamula ife:

“ ‘Ine ndakuyika iwe ukhale kuwunika kwa anthu a mitundu ina,

kuti ukafikitse chipulumutso ku malekezero a dziko lapansi!’ ”

48Anthu a mitundu ina atamva izi, anakondwa ndipo analemekeza Mawu Ambuye; ndipo onse amene anawasankha kuti alandire moyo osatha anakhulupirira.

49Mawu a Ambuye anafalikira mʼchigawo chonse. 50Koma Ayuda anawutsa mitima ya akazi otchuka opembedza Mulungu ndi akulu a mu mzindamo. Iwo anabweretsa mazunzo kwa Paulo ndi Barnaba ndipo anawathamangitsa mʼchigawo chawo. 51Tsono iwo anasasa fumbi la ku mapazi awo powatsutsa, ndipo anapita ku Ikoniya. 52Ndipo ophunzira anadzazidwa ndi chimwemwe ndiponso ndi Mzimu Woyera.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

使徒行傳 13:1-52

巴拿巴和掃羅接受差遣

1安提阿教會中有幾位先知和教師,就是巴拿巴、綽號「黑人」的希緬古利奈路求、與分封王希律一同長大的馬念以及掃羅2一天,他們正在敬拜主、禁食的時候,聖靈對他們說:「要為我把巴拿巴掃羅分別出來,好讓他們做我呼召他們去做的事。」 3於是,他們禁食禱告並把手按在巴拿巴掃羅身上,然後差遣他們出去。

4二人受聖靈差遣,下到西流基,從那裡乘船去塞浦路斯5他們到了撒拉米,就在當地的猶太會堂傳講上帝的道。約翰·馬可作他們的助手。

6他們走遍全島,遠至帕弗,在那裡遇見一個冒充先知的猶太術士巴·耶穌7這人和當地的士求·保羅總督常有來往。士求·保羅是個聰明人,他邀請了巴拿巴掃羅來,要聽上帝的道。 8希臘名字叫以呂馬的那個術士反對使徒,試圖攔阻總督信主。 9又名保羅掃羅被聖靈充滿,盯著他說: 10「你這魔鬼的兒子,充滿了詭詐和邪惡,是一切正義之敵,到現在還想歪曲主的正道嗎? 11現在主要親手懲罰你,使你瞎眼,暫時不見天日!」

他頓覺眼前一片漆黑,只好四處摸索,求人領他走路。 12總督看見所發生的事,對主的道感到驚奇,就信了。

保羅傳揚基督

13保羅和同伴從帕弗乘船到旁非利亞別加約翰·馬可在那裡離開他們回耶路撒冷去了。 14他們由別加繼續前行,來到彼西底區的安提阿。在安息日那天,他們進了會堂坐下來。 15讀完律法書和先知書後,會堂主管派人告訴他們:「弟兄們,如果你們有什麼勸勉眾人的話,請講。」

16保羅站起來向大家揮手示意,說:「各位以色列同胞和各位敬畏上帝的外族朋友們,請聽我說。 17以色列的上帝揀選了我們的祖先,讓他們在埃及寄居期間人丁興旺成為大族,後來祂伸出臂膀帶領他們離開埃及18他們在曠野漂泊的那四十年間,上帝一直照顧、容忍他們。 19後來上帝又滅了迦南境內的七族,把土地分給他們作產業。 20前後歷時約四百五十年。之後,上帝又為他們設立士師,直到撒母耳先知的時代。

21「後來,他們求上帝為他們立一位王,上帝就選立便雅憫支派中基士的兒子掃羅為王,執政四十年。 22之後,上帝廢掉掃羅,選立大衛作王,並為他作證說,『我找到了耶西的兒子大衛,他是合我心意的人,他必遵行我一切的旨意。』 23上帝照自己的應許,從大衛的後裔中為以色列人立了一位救主,就是耶穌。 24在耶穌還未公開露面以前,約翰已經勸告以色列人要悔改,接受洗禮。 25約翰在工作快要完成的時候說,『你們以為我是誰?我不是基督。在我之後來的那位,我連給祂解鞋帶也不配。』

26「弟兄們,各位亞伯拉罕的子孫和敬畏上帝的外族人啊,這救恩之道原是傳給我們的。 27可是耶路撒冷的人和他們的官長不知道耶穌是基督,雖然每個安息日都誦讀先知的信息,卻把基督判死罪。這正應驗了先知們的話。 28他們雖然找不到判祂死罪的理由,卻強求彼拉多將祂處死。 29祂受死的記載全部應驗之後,有人把祂從十字架上取下來,安放在石墓裡。 30但上帝卻使祂從死裡復活。 31之後有許多天,那些從加利利跟隨祂上耶路撒冷的人都看見過祂,他們如今在百姓中都是祂的見證人。 32我們要報給你們一個好消息,上帝給我們祖先的應許, 33祂藉著使耶穌復活已為我們做子孫的成就了。正如詩篇第二篇所說,

『你是我的兒子,

我今日成為你父親。』

34聖經曾這樣記載上帝使祂從死裡復活、永不朽壞的事,

『我必將應許大衛的聖潔、

可靠的恩福賜給你們。』

35又在詩篇上說,

『你必不讓你的聖者身體朽壞。』

36大衛在世時遵行上帝的旨意,最後死了,葬在他祖先那裡,肉身也朽壞了。 37然而,上帝使之復活的那位卻沒有朽壞。 38所以,弟兄們,你們應該知道,赦罪的信息是藉著耶穌傳給你們的。 39你們靠遵行摩西律法不能被稱為義人,只有信靠耶穌才能被稱為義人。 40你們要當心,免得先知說的話應驗在你們身上,

41『藐視真理的人啊,看吧!

你們要在驚懼中滅亡,

因為我要在你們的時代行一件事,

即使有人告訴你們,

你們也不會信。』」

42保羅巴拿巴離開會堂時,會堂裡的人請求他們下一個安息日再來講道。 43許多猶太人和誠心改信猶太教的外族人都跟隨保羅巴拿巴,二人就與他們談論,勸勉他們要堅定不移地信靠上帝的恩典。

44到了下一個安息日,幾乎全城的人都聚集起來,要聽上帝的道。 45猶太人看見那麼多人聚集,充滿嫉妒,便反駁保羅所講的,誹謗他。 46保羅巴拿巴毫不畏懼地說:「上帝的道本該先傳給你們,你們既然拒絕接受,認為自己不配得永生,我們現在就把這道傳給外族人。 47因為主這樣吩咐我們,

『我已使你成為外族人的光,

好把救恩帶到地極。』」

48外族人聽後,非常歡喜,頌讚主的道。凡被選定得永生的人都信了主。 49主的道傳遍了那個地方。

50猶太人煽動虔誠的貴婦和城中顯要迫害保羅巴拿巴,將二人趕出城去。 51保羅巴拿巴便當眾跺掉腳上的塵土13·51 表示兩不相干,參見馬太福音10·14,去了以哥念52門徒滿心喜樂,被聖靈充滿。