Luka 7 – CCL & NIRV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Luka 7:1-50

Chikhulupiriro cha Kenturiyo

1Yesu atamaliza kunena zonsezi pamaso pa anthu amene ankamvetsera, analowa mu Kaperenawo. 2Kumeneko wantchito wa Kenturiyo, amene amamukhulupirira kwambiri, anadwala ndipo anali pafupi kufa. 3Kenturiyo anamva za Yesu ndipo anatumiza ena a akulu Ayuda kwa Iye kuti abwere adzachiritse wantchito wakeyo. 4Iwo atafika kwa Yesu, anamudandaulira kwambiri, nati, “Munthuyu ayenera kuthandizidwa 5chifukwa amakonda mtundu wathu ndipo anatimangira sunagoge wathu.” 6Pamenepo Yesu anapita nawo.

Iye sanali patali ndi nyumba pamene Kenturiyo anatumiza anzake kuti akamuwuze kuti, “Ambuye, musadzivutitse, pakuti ndine wosayenera kuti mulowe mʼnyumba mwanga. 7Nʼchifukwa chake sindinadziyenereze ndi pangʼono pomwe kuti ndibwere kwa inu. Koma nenani mawu, ndipo wantchito wanga adzachira. 8Pakuti ndili pansi paulamuliro, ndiponso ndili ndi asilikali pansi panga. Ndikamuwuza uyu kuti, ‘Pita,’ iye amapita; ndi uyo kuti, ‘Bwera,’ amabwera. Ndikamuwuza wantchito wanga kuti, ‘Chita ichi,’ amachita.”

9Yesu atamva izi, anadabwa naye, ndipo anatembenukira gulu la anthu limene limamutsatira nati, “Ndikukuwuzani kuti, sindinapeze chikhulupiriro chachikulu ngati ichi mu Israeli.” 10Kenaka anthu amene anatumidwawo anabwerera ku nyumba ndipo anakamupeza wantchitoyo atachira.

Yesu Aukitsa Mwana wa Mayi Wamasiye

11Zitangotha izi, Yesu anapita ku mudzi wa Naini ndipo ophunzira ake ndi gulu lalikulu la anthu linapita naye pamodzi. 12Akufika pa chipata cha mudziwo, anakumana ndi anthu amene ankatuluka ndi munthu wakufa amene anali mwana yekhayo wa mkazi wamasiye. Gulu lalikulu la anthu a mʼmudziwo linali naye. 13Ambuye atamuona mayiyo, mtima wawo unagwidwa naye chifundo ndipo anati, “Usalire.”

14Kenaka anapita nakakhudza chithatha cha maliro ndipo amene anachinyamulawo anayima. Iye anati, “Mnyamata, ndikukuwuza kuti, dzuka!” 15Wakufayo anakhala tsonga ndi kuyamba kuyankhula, ndipo Yesu anamupereka mnyamatayo kwa amayi ake.

16Onse anachita mantha kwambiri nalemekeza Mulungu. Iwo anati, “Mneneri wamkulu waonekera pakati pathu. Mulungu wabwera kudzathandiza anthu ake.” 17Mbiriyi inafalikira ku Yudeya konse ndi ku madera ozungulira.

Yesu ndi Yohane Mʼbatizi

18Ndipo ophunzira a Yohane anamuwuza Yohaneyo zinthu zonsezi. Atayitana awiri a ophunzirawo, 19anawatumiza kwa Ambuye kukafunsa kuti, “Kodi ndinu anayenera kubwerayo, kapena tiyembekezere wina?”

20Anthuwo atafika kwa Yesu anati, “Yohane Mʼbatizi watituma kwa Inu kuti tidzafunse kuti, ‘Kodi ndinu anayenera kubwerayo, kapena tiyembekezere wina?’ ”

21Pa nthawi yomweyo, Yesu anachiritsa ambiri amene ankavutika, odwala ndi amene anali mizimu yoyipa, ndiponso anapenyetsa anthu osaona. 22Ndipo Iye anawayankha otumidwawo kuti, “Bwererani ndi kukamuwuza Yohane zimene mwaona ndi kumva: Osaona akuona, olumala akuyenda, akhate akuchiritsidwa, osamva akumva, akufa akuukitsidwa, ndipo Uthenga Wabwino ukulalikidwa kwa osauka. 23Odala munthu amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.”

24Anthu otumidwa ndi Yohane aja atachoka, Yesu anayamba kuyankhula ndi gulu la anthu za Yohaneyo kuti, “Kodi munkapita ku chipululu kukaona chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo? 25Ngati si choncho, munkapita kukaona chiyani? Munthu wovala zovala zabwino? Ayi, ovala zovala zodula ndi okhala moyo wapamwamba ali mʼnyumba zaufumu. 26Koma inu munkapita kukaona chiyani? Mneneri? Inde, Ine ndikukuwuzani, woposa mneneri. 27Uyu ndi amene malemba akunena za Iye kuti,

“ ‘Ine ndidzatuma mthenga wanga patsogolo panu,

amene adzakonza njira yanu.’

28Ine ndikukuwuzani kuti pakati pa obadwa kuchokera mwa mkazi palibe wina wamkulu kuposa Yohane; komabe amene ali wamngʼono mu ufumu wa Mulungu ndi wamkulu kuposa iye.”

29Anthu onse, ngakhale amisonkho, atamva mawu a Yesu, anavomereza kuti njira ya Mulungu ndi yolondola, chifukwa anabatizidwa ndi Yohane. 30Koma Afarisi ndi akatswiri amalamulo anakana cholinga cha Mulungu kwa iwo okha, chifukwa sanabatizidwe ndi Yohane.

31“Kodi ndingawafanizire chiyani anthu a mʼbado uno? Ali ngati chiyani? 32Ali ngati ana amene akukangana pa msika, ena akufunsa anzawo kuti,

“ ‘Ife tinakuyimbirani chitoliro,

koma inu simunavine.

Tinakuyimbirani nyimbo zamaliro,

koma inu simunalire.’

33Pakuti Yohane Mʼbatizi sanabwere kudzadya buledi kapena kumwa vinyo, koma inu mumati, ‘Ali ndi chiwanda.’ 34Mwana wa Munthu anabwera nadya ndi kumwa, ndipo inu mukuti, ‘Ali ndi dyera komanso ndi woledzera, bwenzi la amisonkho ndi ochimwa.’ 35Ndipo nzeru zimaoneka zolondola mwa ana ake onse.”

Yesu Adzozedwa ndi Mayi Wochimwa

36Tsopano mmodzi mwa Afarisi anayitana Yesu kuti akadye naye ku nyumba kwake ndipo anapita nakakhala pa tebulo. 37Mayi amene amakhala moyo wauchimo mu mzindawo atadziwa kuti Yesu akudya ku nyumba ya Mfarisiyo, anabweretsa botolo la mafuta onunkhira a alabasta. 38Iye anayimirira kumbuyo kwa Yesu pa mapazi ake akulira, nayamba kumadontheza misozi pa mapazi ake. Ndipo iye anapukuta mapaziwo ndi tsitsi lake, nawapsompsona ndi kuwathira mafuta onunkhirawo.

39Mfarisiyo anamuyitanayo ataona izi, anati mu mtima mwake, “Ngati munthuyu akanakhala mneneri, akanadziwa kuti akumukhudzayo ndi mayi otani, kuti ndi wochimwa.”

40Yesu anamuyankha iye kuti, “Simoni, ndili ndi kanthu koti ndikuwuze.”

Iye anati, “Ndiwuzeni Aphunzitsi.”

41“Anthu awiri anakongola ndalama kwa munthu wina wokongoletsa ndalama: mmodzi ndalama zokwana 500 ndi winayo ndalama makumi asanu. 42Panalibe mmodzi mwa iwo anali ndi ndalama zobwezera, ndipo iye anawakhululukira ngongole zawo. Tsopano ndi ndani mwa awiriwa adzamukonde koposa?”

43Simoni anayankha kuti, “Ndikuganiza kuti ndi amene anamukhululukira ngongole yayikulu.”

Yesu anati, “Wayankha molondola.”

44Kenaka anatembenukira kwa mayiyo nati kwa Simoni, “Ukumuona mayiyu? Ine ndabwera mʼnyumba yako. Iwe sunandipatse madzi otsukira mapazi anga, koma iyeyu wanyowetsa mapazi anga ndi misozi yake ndi kuwapukuta ndi tsitsi lake. 45Iwe sunandipsompsone, koma mayiyu, kuyambira pamene Ine ndalowa, sanaleke kupsompsona mapazi anga. 46Iwe sunadzoze mutu wanga mafuta, koma iye wadzoza mapazi anga mafuta onunkhira. 47Tsono, ndikukuwuza iwe, machimo ake amene ndi ambiri akhululukidwa, monga chaonetsera chikondi chake chachikulu. Koma iye amene wakhululukidwa zochepa amakonda pangʼono.”

48Kenaka anati kwa mayiyo, “Machimo ako akhululukidwa.”

49Alendo enawo anayamba kumanena mʼmitima mwawo kuti, “Uyu ndi ndani amene akhululukiranso machimo?”

50Yesu anati kwa mayiyo, “Chikhulupiriro chako chakupulumutsa. Pita mu mtendere.”

New International Reader’s Version

Luke 7:1-50

A Roman Commander Has Faith

1Jesus finished saying all these things to the people who were listening. Then he entered Capernaum. 2There the servant of a Roman commander was sick and about to die. His master thought highly of him. 3The commander heard about Jesus. So he sent some elders of the Jews to him. He told them to ask Jesus to come and heal his servant. 4They came to Jesus and begged him, “This man deserves to have you do this. 5He loves our nation and has built our synagogue.” 6So Jesus went with them.

When Jesus came near the house, the Roman commander sent friends to him. He told them to say, “Lord, don’t trouble yourself. I am not good enough to have you come into my house. 7That is why I did not even think I was fit to come to you. But just say the word, and my servant will be healed. 8I myself am a man who is under authority. And I have soldiers who obey my orders. I tell this one, ‘Go,’ and he goes. I tell that one, ‘Come,’ and he comes. I say to my servant, ‘Do this,’ and he does it.”

9When Jesus heard this, he was amazed at the commander. Jesus turned to the crowd that was following him. He said, “I tell you, even in Israel I have not found anyone whose faith is so strong.” 10Then the men who had been sent to Jesus returned to the house. They found that the servant was healed.

Jesus Raises a Widow’s Son From the Dead

11Some time later, Jesus went to a town called Nain. His disciples and a large crowd went along with him. 12He approached the town gate. Just then, a dead person was being carried out. He was the only son of his mother. She was a widow. A large crowd from the town was with her. 13When the Lord saw her, he felt sorry for her. So he said, “Don’t cry.”

14Then he went up and touched the coffin. Those carrying it stood still. Jesus said, “Young man, I say to you, get up!” 15The dead man sat up and began to talk. Then Jesus gave him back to his mother.

16The people were all filled with wonder and praised God. “A great prophet has appeared among us,” they said. “God has come to help his people.” 17This news about Jesus spread all through Judea and the whole country.

Jesus and John the Baptist

18John’s disciples told him about all these things. So he chose two of them. 19He sent them to the Lord. John told them to ask him, “Are you the one who is supposed to come? Or should we look for someone else?”

20The men came to Jesus. They said, “John the Baptist sent us to ask you, ‘Are you the one who is supposed to come? Or should we look for someone else?’ ”

21At that time Jesus healed many people. They had illnesses, sicknesses and evil spirits. He also gave sight to many who were blind. 22So Jesus replied to the messengers, “Go back to John. Tell him what you have seen and heard. Blind people receive sight. Disabled people walk. Those who have skin diseases are made ‘clean.’ Deaf people hear. Those who are dead are raised to life. And the good news is announced to those who are poor. 23Blessed is anyone who does not give up their faith because of me.”

24So John’s messengers left. Then Jesus began to speak to the crowd about John. He said, “What did you go out into the desert to see? Tall grass waving in the wind? 25If not, what did you go out to see? A man dressed in fine clothes? No. Those who wear fine clothes and have many expensive things are in palaces. 26Then what did you go out to see? A prophet? Yes, I tell you, and more than a prophet. 27He is the one written about in Scripture. It says,

“ ‘I will send my messenger ahead of you.

He will prepare your way for you.’ (Malachi 3:1)

28I tell you, no one more important than John has ever been born. But the least important person in God’s kingdom is more important than John is.”

29All the people who heard Jesus’ words agreed that God’s way was right. Even the tax collectors agreed. These people had all been baptized by John. 30But the Pharisees and the authorities on the law did not accept for themselves God’s purpose. So they had not been baptized by John.

31Jesus went on to say, “What can I compare today’s people to? What are they like? 32They are like children sitting in the market and calling out to each other. They say,

“ ‘We played the flute for you.

But you didn’t dance.

We sang a funeral song.

But you didn’t cry.’

33That is how it has been with John the Baptist. When he came to you, he didn’t eat bread or drink wine. And you say, ‘He has a demon.’ 34But when the Son of Man came, he ate and drank as you do. And you say, ‘This fellow is always eating and drinking far too much. He’s a friend of tax collectors and sinners.’ 35All who follow wisdom prove that wisdom is right.”

A Sinful Woman Pours Perfume on Jesus

36One of the Pharisees invited Jesus to have dinner with him. So he went to the Pharisee’s house. He took his place at the table. 37There was a woman in that town who had lived a sinful life. She learned that Jesus was eating at the Pharisee’s house. So she came there with a special jar of perfume. 38She stood behind Jesus and cried at his feet. And she began to wet his feet with her tears. Then she wiped them with her hair. She kissed them and poured perfume on them.

39The Pharisee who had invited Jesus saw this. He said to himself, “If this man were a prophet, he would know who is touching him. He would know what kind of woman she is. She is a sinner!”

40Jesus answered him, “Simon, I have something to tell you.”

“Tell me, teacher,” he said.

41“Two people owed money to a certain lender. One owed him 500 silver coins. The other owed him 50 silver coins. 42Neither of them had the money to pay him back. So he let them go without paying. Which of them will love him more?”

43Simon replied, “I suppose the one who owed the most money.”

“You are right,” Jesus said.

44Then he turned toward the woman. He said to Simon, “Do you see this woman? I came into your house. You did not give me any water to wash my feet. But she wet my feet with her tears and wiped them with her hair. 45You did not give me a kiss. But this woman has not stopped kissing my feet since I came in. 46You did not put any olive oil on my head. But she has poured this perfume on my feet. 47So I tell you this. Her many sins have been forgiven. She has shown that she understands this by her great acts of love. But whoever has been forgiven only a little loves only a little.”

48Then Jesus said to her, “Your sins are forgiven.”

49The other guests began to talk about this among themselves. They said, “Who is this who even forgives sins?”

50Jesus said to the woman, “Your faith has saved you. Go in peace.”