Luka 1 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Luka 1:1-80

Mawu Oyamba

1Ambiri anayesa kufotokoza nkhani ya zimene zinakwaniritsidwa pakati pathu, 2monga mmene zinaperekedwera kwa ife ndi iwo amene anaona poyambirira ndi atumiki a mawu. 3Popeza inenso ndafufuza mosamalitsa chilichonse kuyambira pachiyambi, zandikomera kukulemberani mwatsatanetsatane inu wolemekezeka Tiofilo, 4kuti mudziwe bwinobwino zoona za zinthu zimene mwaphunzitsidwa.

Aneneratu za Kubadwa kwa Yohane Mʼbatizi

5Mʼmasiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kunali wansembe dzina lake Zakariya wa gulu la ansembe la Abiya; mkazi wake Elizabeti analinso wa fuko la Aaroni. 6Onse awiri anali olungama pamaso pa Mulungu, ndipo amasunga malamulo ndi malangizo onse a Ambuye osalakwa konse. 7Koma analibe ana chifukwa Elizabeti anali wosabereka; ndipo onse anali okalamba.

8Nthawi yogwira ntchito yotumikira ansembe a gulu la Zekariya, Zekariya ankatumikira ngati wansembe pamaso pa Mulungu, 9Zakariyayo anasankhidwa mwa maere, monga mwa mwambo wa unsembe, kupita mʼNyumba ya Ambuye kukafukiza lubani. 10Ndipo nthawi yofukiza lubani itafika, gulu lonse lopembedza linkapemphera kunja.

11Kenaka mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye, atayimirira ku dzanja lamanja la guwa lofukizira. 12Zakariya ataona mngeloyo, anadzidzimuka ndipo anagwidwa ndi mantha. 13Koma mngeloyo anati kwa iye: “Usachite mantha, Zakariya; pemphero lako lamveka. Mkazi wako Elizabeti adzakuberekera iwe mwana wamwamuna ndipo udzamutche dzina loti Yohane. 14Ndipo adzakhala chimwemwe ndi chisangalalo kwa iwe, ndipo ambiri adzasangalala chifukwa cha kubadwa kwake, 15chifukwa adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye. Iye sadzamwa vinyo kapena chakumwa choledzeretsa, ndipo adzazadzidwa ndi Mzimu Woyera kuyambira pa kubadwa. 16Iye adzabweretsanso Aisraeli ambiri kwa Ambuye Mulungu wawo. 17Ndipo iye adzabwera Ambuye asanabwere mu mzimu ndi mphamvu ya Eliya. Adzatembenuzira mitima ya abambo kwa ana awo ndi osamvera ku nzeru ya olungama, kuthandiza anthu kuti akonzekere kubwera kwa Ambuye.”

18Zakariya anamufunsa mngeloyo kuti, “Kodi ndingatsimikize bwanji zimenezi? Ine ndine wokalamba ndipo mkazi wanga ali ndi zaka zambiri.”

19Mngeloyo anayankha kuti, “Ine ndine Gabrieli. Ndimayima pamaso pa Mulungu, ndipo ndatumidwa kwa iwe kudzakuwuza uthenga wabwinowu. 20Ndipo kuyambira tsopano sudzatha kuyankhula kufikira izi zitachitika chifukwa sunakhulupirire mawu awa, amene adzakwaniritsidwe pa nthawi yake yoyenera.”

21Pa nthawiyi, anthu ankadikira Zakariya ndipo anadabwa chifukwa anatenga nthawi yayitali ali mʼNyumba ya Mulungu. 22Atatuluka sanathe kuyankhulana nawo. Anazindikira kuti anaona masomphenya mʼNyumbamo, chifukwa ankasonyeza zizindikiro kwa iwo koma sankatha kuyankhula.

23Nthawi yake yotumikira itatha, anabwerera kwawo. 24Zitatha izi, mkazi wake Elizabeti anakhala ndi pakati ndipo anadzibisa kwa miyezi isanu. 25Iye anati, “Ambuye wandichitira izi, kuti mʼmasiku ano wandionetsera kukoma mtima kwake ndi kuchotsa manyazi anga pakati pa anthu.”

Aneneratu za Kubadwa kwa Yesu

26Mwezi wachisanu ndi chimodzi, Mulungu anatuma mngelo Gabrieli ku Nazareti, mudzi wa ku Galileya, 27kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi Yosefe, wa fuko la Davide. Dzina la namwaliyo linali Mariya. 28Mngeloyo anafika kwa iye nati, “Moni, inu amene Ambuye wakukomerani mtima kwambiri! Ambuye ali ndi inu.”

29Mariya anavutika kwambiri ndi mawu awa ndipo anadabwa ndi kulonjera kotere. 30Koma mngeloyo anati kwa iye, “Usachite mantha Mariya, pakuti wapeza chisomo pamaso Mulungu. 31Udzakhala woyembekezera ndipo udzabala mwana wamwamuna ndipo udzamupatse dzina loti Yesu. 32Iye adzakhala wamkulu ndipo adzatchedwa Mwana wa Wammwambamwamba. Ambuye Mulungu adzamupatsa Iye mpando waufumu wa abambo ake Davide, 33ndipo adzalamulira pa nyumba ya Yakobo ku nthawi zonse; ufumu wake sudzatha.”

34Mariya anafunsa mngeloyo kuti, “Izi zingatheke bwanji popeza ine sindidziwa mwamuna?”

35Mngelo anayankha kuti, “Mzimu Woyera adzabwera pa iwe ndipo mphamvu ya Wammwambamwamba idzakuphimba, ndipo Woyerayo amene adzabadwe adzatchedwa Mwana wa Mulungu. 36Ngakhale Elizabeti mʼbale wako adzakhala ndi mwana mu ukalamba wake ndipo iye amene amati ndi wosabereka, uno mwezi wake wachisanu ndi chimodzi. 37Pakuti palibe chinthu chosatheka ndi Mulungu.”

38Mariya anayankha kuti, “Ine ndine mtumiki wa Ambuye. Zikhale kwa ine monga mwanenera.”

Mariya Acheza kwa Elizabeti

39Nthawi imeneyo anakonzeka ndipo anapita mofulumira ku mudzi wa ku mapiri a dziko la Yudeya, 40kumene anakalowa mʼnyumba ya Zakariya nalonjera Elizabeti. 41Elizabeti atamva moni wa Mariya, mwana anatakataka mʼmimba mwake, ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera. 42Anafuwula ndi mawu akulu kuti, “Ndiwe wodala pakati pa akazi, ndipo ndi wodala mwana amene udzabereke! 43Koma nʼchifukwa chiyani andikomera mtima kuti amayi a Ambuye anga abwere kwa ine? 44Nthawi yomwe ndinamva mawu akulonjera kwanu, mwana anatakataka mʼmimba mwanga chifukwa cha chimwemwe. 45Wodala iye amene wakhulupirira kuti chimene Ambuye wanena kwa iye chidzakwaniritsidwa!”

Nyimbo ya Mariya

46Ndipo Mariya anati:

“Moyo wanga ulemekeza Ambuye.

47Ndipo mzimu wanga ukondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga,

48pakuti wakumbukira

kudzichepetsa kwa mtumiki wake.

Kuyambira tsopano mibado yonse idzanditcha wodala,

49pakuti Wamkuluyo wandichitira ine zinthu zazikulu,

dzina lake ndi loyera.

50Chifundo chake chifikira kwa iwo amene amuopa Iye

kufikira mibadomibado.

51Iye wachita zamphamvu ndi dzanja lake;

Iye anabalalitsa iwo amene ali onyada mʼmaganizo awo.

52Iye anachotsa olamulira pa mipando yawo yaufumu,

koma wakweza odzichepetsa.

53Iye wakhutitsa a njala ndi zinthu zabwino

koma anachotsa olemera wopanda kanthu.

54Iye anathandiza mtumiki wake Israeli,

pokumbukira chifundo chake.

55Kwa Abrahamu ndi zidzukulu zake ku nthawi zonse

monga ananena kwa makolo athu.”

56Mariya anakhala ndi Elizabeti pafupifupi miyezi itatu ndipo kenaka anabwerera kwawo.

Kubadwa kwa Yohane Mʼbatizi

57Itakwana nthawi yoti Elizabeti abereke, anabereka mwana wamwamuna. 58Anansi ndi abale ake anamva kuti Ambuye anamuchitira chifundo chachikulu ndipo anakondwera naye pamodzi.

59Pa tsiku lachisanu ndi chitatu anabwera ndi mwana kuti adzachitidwe mdulidwe, ndipo anafuna kumupatsa dzina la abambo ake Zakariya, 60koma amayi ake anayankhula nati, “Ayi, atchulidwe kuti Yohane.”

61Iwo anati kwa iye, “Palibe mmodzi mwa abale ake amene ali ndi dzina limeneli.”

62Pamenepo anapanga zizindikiro kwa abambo ake kuti adziwe dzina limene akanakonda kumutcha mwanayo. 63Iye anapempha poti alembepo, ndipo chodabwitsa kwa aliyense analemba kuti, “Dzina lake ndi Yohane.” 64Nthawi yomweyo pakamwa pake panatsekuka ndi lilime lake linamasuka ndipo anayamba kuyankhula, nayamika Mulungu. 65Anansi onse anachita mantha kwambiri, ndipo ku madera onse a kumapiri a Yudeya, anthu anayankhula zinthu zonsezi. 66Aliyense amene anamva izi anadabwa nazo nafunsa kuti, “Kodi mwana uyu adzakhala wotani?” Pakuti dzanja la Ambuye lili pa iye.

Nyimbo ya Zakariya

67Abambo ake, Zakariya, anadzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo ananenera kuti,

68“Alemekezeke Ambuye, Mulungu wa Israeli

chifukwa wabwera ndi kuwombola anthu ake.

69Iye wakweza nyanga yachipulumutso kwa ife

mu nyumba ya mtumiki wake Davide.

70(Monga mmene ananenera kudzera mwa aneneri oyera),

71chipulumutso kuchoka kwa adani athu

ndi kuchoka mʼdzanja la onse otida,

72kuonetsa chifundo kwa makolo athu

ndi kukumbukira pangano lake loyera,

73lumbiro limene analumbira kwa kholo lathu Abrahamu:

74kutilanditsa ife mʼdzanja la adani athu,

ndi kutipanga ife timutumikire Iye mopanda mantha,

75mʼchiyero ndi mʼchilungamo masiku athu onse.

76“Ndipo iwe mwana wanga udzatchedwa mneneri wa Wammwambamwamba;

pakuti udzapita patsogolo pa Ambuye kukonza njira yake,

77kupatsa anthu ake chidziwitso cha chipulumutso

kudzera mwa chikhululukiro cha machimo awo,

78chifukwa cha chifundo chachikulu cha Mulungu wathu,

ndipo kuwala kwa dzuwa kudzafikira ife kuchokera kumwamba,

79kuwalira iwo okhala mu mdima

ndi mu mthunzi wa imfa,

kutsogolera mapazi athu mu njira yamtendere.”

80Ndipo mwanayo anakula nakhala wamphamvu mu mzimu; ndipo anakhala ku chipululu mpaka pamene anaonekera poyera mu Israeli.