Mphotho ya Kumvera
1“ ‘Musadzipangire mafano ndipo musayimike chifanizo chosema kapena mwala woti mudzipembedza. Musayike mwala wosema mʼdziko mwanu kuti muziwugwadira. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
2“ ‘Muzisunga Masabata anga ndipo muzilemekeza malo anga wopatulika. Ine ndine Yehova.
3“ ‘Mukamayenda motsata malangizo anga ndi kumvera mosamalitsa malamulo anga, 4ndidzakupatsani mvula pa nyengo yake. Nthaka yanu idzabala zokolola zake, ndipo mitengo ya mʼmunda idzabala zipatso zake. 5Mudzakhala mukupuntha tirigu mpaka nthawi yothyola mphesa, ndipo mudzakhala mukuthyola mphesa mpaka nthawi yodzala. Mudzadya chakudya chanu mpaka kukhuta ndipo mudzakhala mʼdziko lanu mwamtendere.
6“ ‘Ndidzabweretsa mtendere mʼdziko lanu, ndipo muzidzagona popanda wokuopsezani. Ndidzachotsa nyama zakuthengo zoopsa mʼdziko mwanu, ndipo mʼdzikomo simudzakhala nkhondo. 7Mudzapirikitsa adani anu, ndipo mudzawagonjetsa ndi lupanga pamaso panu. 8Anthu asanu mwa inu adzapirikitsa anthu 100, ndipo anthu 100 mwa inu adzathamangitsa anthu 10,000, ndipo adani anuwo mudzawagonjetsa ndi lupanga.
9“ ‘Ndidzakukumbukirani ndi kukupatsani ana ambiri ndi kukuchulukitsani. Ndidzasunga pangano langa ndi inu. 10Mudzakhala mukudyabe chakudya chogonera ndipo mudzachotse chakudyacho mʼnkhokwe kuti mupezemo malo woyika chakudya china chatsopano. 11Ndidzakhala pakati panu, ndipo sindidzayipidwa nanu. 12Ine ndidzayendayenda pakati panu ndipo ndidzakhala Mulungu wanu. Inu mudzakhala anthu anga. 13Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto kuti musakhalenso akapolo a Aigupto. Ndinadula mipiringidzo ya goli lanu ndi kukuthandizani kuti muziyenda momasuka.
Chilango Chakusamvera
14“ ‘Koma mukadzapanda kundimvera ndi kuphwanya malamulo anga onsewa, 15ndipo ngati mudzanyoza malangizo anga ndi kunyansidwa ndi malamulo anga, ndi kulephera kumvera zonse zimene ndakulamulani, ndi kuswa pangano langa, 16Ine ndidzakuchitirani izi: ndidzabweretsa zoopsa zadzidzidzi monga chifuwa chachikulu chowondetsa ndiponso malungo amene adzawononga maso ndi kufowoketsa moyo wanu. Mudzangovutika kudzala mbewu zanu chifukwa adani anu adzazidya. 17Ndidzakufulatirani, kotero kuti adani anu adzakugonjetsani. Odana nanu adzakulamulirani ndipo inu muzidzagothawa popanda wokupirikitsani.
18“ ‘Ngati simudzandimvera mutaona zonsezi, ndidzakulanganinso mochulukitsa kasanu ndi kawiri chifukwa cha kuchimwa kwanu. 19Ndidzathyola mphamvu zanu zimene mukunyadirazo, ndipo ndidzasandutsa mitambo kuti ikhale yowuma ngati chitsulo, ndiponso nthaka yanu kuti ikhale ngati mkuwa. 20Mphamvu zanu zidzapita pachabe chifukwa nthaka yanu sidzabala kanthu, ngakhale mitengo yake sidzabala zipatso zake.
21“ ‘Ngati mudzapitirira kutsutsana nane ndi kukana kundimvera, ndidzachulukitsa masautso anu kasanu ndi kawiri molingana ndi machimo anu. 22Ndidzabweretsa zirombo zolusa pakati panu, ndipo zidzakulandani ana anu ndi kuwononga ngʼombe zanu. Choncho zidzachepetsa chiwerengero chanu kotero kuti mʼnjira mwanu simudzapita anthu.
23“ ‘Mukadzapanda kutembenukira kwa Ine ngakhale nditakulangani motere, ndi kumachitabe zotsutsana ndi Ine, 24Ine mwini ndidzalimbana nanu, ndipo ndidzakulangani mochulukitsa kasanu ndi kawiri chifukwa cha machimo anu. 25Ndipo ndidzabweretsa lupanga pa inu ndi kukulangani chifukwa chophwanya pangano langa. Mukadzasonkhana mʼmizinda yanu, ndidzatumiza miliri pakati panu ndipo ndidzakuperekani mʼmanja mwa adani anu. 26Ndikadzachepetsa buledi wanu, akazi khumi adzaphika buledi wawo mu uvuni umodzi, ndipo adzakugawirani bulediyo pangʼonopangʼono. Choncho mudzadya koma wosakhuta.
27“ ‘Mukadzapanda kundimvera ngakhale nditakulangani motere, ndi kumatsutsanabe ndi Ine, 28pamenepo ndidzalimbana nanu mwaukali, ndipo Ine mwini ndidzakulangani mochulukitsa kasanu ndi kawiri chifukwa cha kuchimwa kwanu. 29Mudzadya ana anu aamuna ndiponso mudzadya ana anu aakazi. 30Ine ndidzawononga malo anu opembedzera mafano a ku mapiri. Ndidzagwetsa maguwa anu ofukizira lubani, ndipo ndidzawunjika pamodzi mitembo ya mafano anu wopanda moyowo, ndipo ndidzanyansidwa nanu. 31Ndidzasandutsa mizinda yanu kukhala mabwinja ndi kuwononga malo anu wopatulika. Sindidzakondweranso ndi fungo lokoma la zopereka zanu. 32Ndidzawononga dziko kotero kuti adani anu mʼmenemo adzadabwa. 33Ndidzakubalalitsani pakati pa mitundu ina ya anthu ndipo ndidzasolola lupanga langa ndi kukupirikitsani. Dziko lanu lidzawonongedwa, ndipo mizinda yanu idzasanduka mabwinja. 34Nthawi imeneyo nthaka idzasangalalira kuyipumitsa kwake nthawi yonse imene idzakhala yosalimidwa, pamene inu mudzakhala muli mʼdziko la adani anu. Pa nthawi imeneyo dziko lidzapumula ndi kukondwerera kulipumuza kwake. 35Nthawi zonse pamene dzikolo lidzakhala lopanda anthu, nthaka idzapumula. Mpumulo umenewu udzakhala umene nthakayo sinapumulepo pa nthawi zimene inu munkapumula muli mʼdzikomo.
36“ ‘Kunena za amene adzatsale, ndidzayika mantha mʼmitima mwawo mʼdziko la adani awo kotero kuti adzathawa ngakhale mtswatswa wa tsamba lowuluka ndi mphepo. Adzathawa ngati akuthawa lupanga, ndipo adzagwa pansi ngakhale padzakhale wopanda kuwapirikitsa. 37Iwo adzaphunthwitsana ngati akuthawa nkhondo, ngakhale padzakhale popanda wowapirikitsa. Choncho simudzatha kuyima pamaso pa adani anu. 38Mudzatheratu pakati pa mitundu ya anthu. Dziko la adani anu lidzakudyani. 39Ngakhale iwo amene adzatsale adzatheratu mʼdziko la adani awo chifukwa cha machimo awo ndi machimo a makolo awo.
40“ ‘Tsono adzawulula machimo awo ndi machimo a makolo awo, kusakhulupirika kwawo ndi mayendedwe awo otsutsana nane, 41zomwe zinandipangitsa kuwafulatira ndi kuwapereka mʼmanja mwa adani awo. Ndipo mitima yawo yowumayo ikadzadzichepetsa ndi kuvomera kulangidwa chifukwa cha machimo awo, 42Ine ndidzakumbukira pangano langa ndi Yakobo, pangano langa ndi Isake, pangano langa ndi Abrahamu. Ndidzakumbukiranso dzikolo. 43Pakuti adzasiya dziko lawo lopanda anthu, nthaka idzakondwerera zaka zake zoyipumuza pamene iwo kudzakhala kulibe. Koma adzalangidwa chifukwa cha machimo awo popeza anakana malamulo anga ndipo mitima yawo inkayipidwa nawo malangizo anga. 44Komabe ngakhale adzachite zonsezi ali mʼdziko la adani awo, Ine sindidzawakana kapena kuyipidwa nawo kwakuti nʼkuwawononga kwathunthu ndi kuthetsa pangano langa ndi iwo. Ine ndine Yehova Mulungu wawo. 45Koma powachitira chifundo, ndidzakumbukira pangano langa ndi makolo awo amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto mitundu ina ikuona kuti Ine ndikhale Mulungu wawo. Ine ndine Yehova.’ ”
46Amenewa ndi malamulo ndi malangizo amene Yehova anawayika pakati pa Iye mwini ndi Aisraeli pa Phiri la Sinai kudzera mwa Mose.
รางวัลของการเชื่อฟัง
1“ ‘เจ้าอย่าสร้างรูปเคารพ หรือทำแบบจำลอง หรือตั้งศิลาศักดิ์สิทธิ์สำหรับตัวเจ้าและอย่าวางหินสลักในดินแดนของเจ้าเพื่อกราบไหว้ เราคือพระยาห์เวห์พระเจ้าของเจ้า
2“ ‘จงถือรักษาสะบาโตของเรา และยำเกรงสถานนมัสการของเรา เราคือพระยาห์เวห์
3“ ‘หากเจ้าปฏิบัติตามกฎหมายของเรา และใส่ใจเชื่อฟังคำสั่งของเรา 4เราจะให้ฝนตกต้องตามฤดูกาล แผ่นดินจะให้พืชผลอุดมและต้นไม้จะออกผล 5ช่วงเวลานวดข้าวจะเนิ่นนานถึงฤดูเก็บผลองุ่น และฤดูเก็บผลองุ่นจะเนิ่นนานไปถึงฤดูหว่าน เจ้าจะได้รับประทานอย่างอิ่มหนำ และอาศัยอยู่อย่างปลอดภัยในแผ่นดินของเจ้า
6“ ‘เราจะให้ความสงบสุขในแผ่นดินนั้น ยามนอนเจ้าจะไม่ต้องหวาดผวา เราจะขับไล่สัตว์ร้ายออกไปจากแผ่นดินนั้น และดาบจะไม่แผ้วพานแผ่นดินของเจ้าเลย 7เจ้าจะรุกไล่ศัตรูของเจ้า คนเหล่านั้นจะล้มตายด้วยคมดาบต่อหน้าเจ้า 8พวกเจ้าห้าคนจะรุกไล่ศัตรูนับร้อย พวกเจ้าร้อยคนจะรุกไล่ศัตรูนับหมื่น ศัตรูทั้งหลายจะล้มตายด้วยคมดาบต่อหน้าเจ้า
9“ ‘เราจะดูแลเจ้าด้วยความโปรดปรานและให้เจ้ามีลูกเต็มบ้านมีหลานเต็มเมือง และเราจะรักษาพันธสัญญาของเราที่ให้ไว้กับเจ้า 10เจ้าจะยังคงกินพืชผลจากการเก็บเกี่ยวในปีที่แล้ว เมื่อต้องขยับขยายจัดที่สำหรับพืชผลรุ่นใหม่ 11เราจะตั้งที่พำนัก26:11 หรือพลับพลาของเราท่ามกลางพวกเจ้า และเราจะไม่ชิงชังพวกเจ้า 12เราจะดำเนินอยู่ท่ามกลางพวกเจ้า เป็นพระเจ้าของเจ้า เจ้าจะเป็นประชากรของเรา 13เราคือพระยาห์เวห์พระเจ้าของเจ้า ผู้นำเจ้าทั้งหลายออกมาจากอียิปต์ เพื่อเจ้าจะไม่ต้องเป็นทาสของชาวอียิปต์อีกต่อไป เราได้ทำลายแอกของเจ้า และช่วยให้เจ้าก้าวเดินไปอย่างสง่าผ่าเผย
โทษของการไม่เชื่อฟัง
14“ ‘แต่หากเจ้าไม่ฟังเรา ไม่ปฏิบัติตามคำสั่งเหล่านี้ 15และหากเจ้าปฏิเสธกฎหมายของเรา และชิงชังบทบัญญัติของเรา ไม่ได้ทำตามคำสั่งของเราซึ่งเป็นการละเมิดพันธสัญญาของเรา 16แล้วเราจะทำกับเจ้าอย่างนี้คือ เราจะนำความหวาดหวั่นพรั่นพรึงมาอย่างฉับพลัน โรคต่างๆ และความเจ็บไข้ที่ทำลายสายตาของเจ้า และทำให้ชีวิตของเจ้าทรุดโทรมไปมาเหนือเจ้า เจ้าจะหว่านพืชโดยเปล่าประโยชน์ เพราะศัตรูของเจ้าจะมากิน 17เราจะตั้งตนเป็นปฏิปักษ์กับเจ้า เพื่อเจ้าจะพ่ายแพ้ต่อหน้าศัตรู บรรดาผู้เกลียดชังเจ้าจะปกครองเจ้า เจ้าจะวิ่งหนีแม้ขณะที่ไม่มีใครไล่ตาม
18“ ‘และหากเจ้ายังไม่ยอมเชื่อฟัง เราจะลงโทษเจ้าหนักขึ้นเจ็ดเท่า ให้สมกับบาปของเจ้า 19เราจะทำลายความเย่อหยิ่งอย่างดื้อด้านของเจ้า และทำให้ท้องฟ้าเหนือเจ้าเป็นเช่นเหล็กและแผ่นดินเบื้องล่างเจ้าเป็นดั่งทองสัมฤทธิ์ 20เจ้าจะเสียเหงื่อลงแรงโดยเปล่าประโยชน์เพราะแผ่นดินจะไม่ให้พืชผล ต้นไม้ในที่ดินก็จะไม่ออกผล
21“ ‘หากเจ้ายังคงขัดขืนต่อต้านและไม่ยอมฟังเรา เราจะทวีความทุกข์ยากขึ้นอีกเจ็ดเท่า ให้สาสมกับบาปของเจ้า 22เราจะส่งสัตว์ร้ายมาเล่นงานเจ้าและพวกมันจะปล้นเอาลูกหลานของเจ้าไป จะทำลายฝูงสัตว์ของเจ้าและจะทำให้จำนวนคนของเจ้าลดลงจนถนนหนทางเริศร้าง
23“ ‘หากเราทำกับเจ้าถึงขนาดนี้แล้ว เจ้ายังไม่ยอมรับการดัดนิสัยจากเรา แต่ยังคงขัดขืนต่อต้านเรา 24เราเองจะต่อสู้กับเจ้า และจะให้เจ้าทุกข์ทรมานเพราะบาปของตนหนักยิ่งขึ้นอีกเจ็ดเท่า 25และเราจะนำดาบมายังเจ้าเพื่อแก้แค้นที่พันธสัญญาของเราถูกละเมิด เมื่อเจ้าถอยหนีเข้าไปยังเมืองต่างๆ ของเจ้า เราจะส่งโรคระบาดร้ายแรงมาท่ามกลางพวกเจ้า และเจ้าจะตกอยู่ในมือของศัตรู 26เราจะทลายแหล่งเสบียงของเจ้า ถึงขนาดหญิงสิบคนใช้เตาเพียงเตาเดียวอบขนมให้พวกเจ้า และต้องชั่งอาหารแบ่งกันกิน เจ้าจะกินแต่ไม่อิ่ม
27“ ‘หากถึงขนาดนี้แล้วเจ้ายังไม่ฟังเรา แต่ยังคงขัดขืนต่อต้านเรา 28เราจะต่อสู้กับเจ้าด้วยพระพิโรธ และเราเองจะลงโทษบาปของเจ้าหนักยิ่งขึ้นเจ็ดเท่า 29เจ้าจะกินเนื้อลูกชายลูกสาวของตัวเอง 30เราจะทลายแท่นบูชาบนที่สูงของเจ้า จะโค่นแท่นเผาเครื่องหอมของเจ้า ทิ้งซากศพของเจ้าไว้บนรูปเคารพที่ไม่มีชีวิตของพวกเจ้า และเราจะชิงชังพวกเจ้า 31เราจะทำให้นครต่างๆ ของเจ้าเริศร้าง และทำลายสถานนมัสการของเจ้า เราจะไม่นิยมยินดีในกลิ่นหอมที่น่าพอใจจากเครื่องบูชาของเจ้า 32เราจะทิ้งให้แผ่นดินเริศร้างจนศัตรูของเจ้าที่เข้ามาพักอาศัยตกใจ 33เราจะทำให้พวกเจ้ากระจัดกระจายไปท่ามกลางชนชาติต่างๆ เราจะชักดาบออกจากฝักรุกไล่เจ้า ดินแดนของเจ้าจะถูกทิ้งร้างและเมืองต่างๆ จะถูกทำลาย 34แล้วแผ่นดินจะได้ชื่นชมกับปีสะบาโตของมันตลอดช่วงที่ถูกทิ้งร้างซึ่งเจ้าตกอยู่ในดินแดนของศัตรู แผ่นดินจะได้พักสงบและชื่นชมกับสะบาโตของมัน 35ตลอดช่วงที่ถูกทิ้งร้าง แผ่นดินจะได้พักสงบ ชดเชยกับที่ไม่ได้หยุดพักในช่วงสะบาโตขณะที่เจ้าอาศัยอยู่ในแผ่นดิน
36“ ‘สำหรับพวกที่เหลืออยู่ เราจะทำให้จิตใจของพวกเขาหวาดหวั่นขวัญผวาในแดนของศัตรูถึงขนาดเสียงใบไม้ถูกลมพัดปลิวก็ทำให้พวกเขาหนีไป เขาจะวิ่งราวกับหนีเตลิดจากคมดาบ และเขาจะล้มลงแม้ไม่มีใครไล่ตาม 37เขาจะสะดุดล้มทับกันราวกับหนีเตลิดจากคมดาบแม้ไม่มีใครรุกไล่พวกเขา ดังนั้นเจ้าจะไม่สามารถยืนหยัดต่อหน้าศัตรูของเจ้า 38เจ้าจะพินาศในหมู่ประชาชาติทั้งหลาย และถูกกลืนหายไปในดินแดนของศัตรู 39คนที่เหลืออยู่จะเสื่อมโทรมไปในดินแดนของศัตรูเพราะบาปของพวกเขา และเพราะบาปของบรรพบุรุษของพวกเขา
40“ ‘แต่หากพวกเขาสารภาพบาปของตนและบาปของบรรพบุรุษที่พวกเขาขัดขืนต่อต้านเรา 41ซึ่งทำให้เราเป็นศัตรูกับเขา จนเราส่งพวกเขาไปยังดินแดนของเหล่าศัตรู ตราบจนจิตใจที่ไม่ได้เข้าสุหนัตของเขาถ่อมลงและพวกเขาชดใช้บาปของตน 42เมื่อนั้นเราจะระลึกถึงพันธสัญญาของเราที่ให้ไว้กับยาโคบ อิสอัค และอับราฮัม และจะระลึกถึงแผ่นดินนั้น 43เพราะแผ่นดินนั้นจะชื่นชมกับสะบาโตของมันขณะที่ถูกทิ้งร้างอยู่ พวกเขาจะชดใช้บาปของตนที่ได้ละทิ้งบทบัญญัติของเราและเกลียดชังกฎหมายของเรา 44แต่กระนั้นเมื่อเขาอยู่ในดินแดนของศัตรู เราจะไม่ปฏิเสธหรือเกลียดชังพวกเขาจนถึงกับทำลายล้างพวกเขาให้หมดสิ้น ซึ่งเป็นการละเมิดพันธสัญญาของเรากับพวกเขา เราคือพระยาห์เวห์พระเจ้าของพวกเขา 45แต่เพื่อเห็นแก่พวกเขา เราจะระลึกถึงพันธสัญญาที่ให้ไว้กับบรรพบุรุษของพวกเขาซึ่งเราได้พาออกมาจากอียิปต์ต่อหน้าประชาชาติทั้งหลาย เพื่อเป็นพระเจ้าของพวกเขา เราคือพระยาห์เวห์’ ”
46ทั้งหมดนี้คือกฎหมาย บทบัญญัติ และกฎระเบียบ ซึ่งองค์พระผู้เป็นเจ้าทรงตั้งไว้ระหว่างพระองค์เองกับชนอิสราเอลผ่านทางโมเสสบนภูเขาซีนาย