Levitiko 26 – CCL & ASCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Levitiko 26:1-46

Mphotho ya Kumvera

1“ ‘Musadzipangire mafano ndipo musayimike chifanizo chosema kapena mwala woti mudzipembedza. Musayike mwala wosema mʼdziko mwanu kuti muziwugwadira. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

2“ ‘Muzisunga Masabata anga ndipo muzilemekeza malo anga wopatulika. Ine ndine Yehova.

3“ ‘Mukamayenda motsata malangizo anga ndi kumvera mosamalitsa malamulo anga, 4ndidzakupatsani mvula pa nyengo yake. Nthaka yanu idzabala zokolola zake, ndipo mitengo ya mʼmunda idzabala zipatso zake. 5Mudzakhala mukupuntha tirigu mpaka nthawi yothyola mphesa, ndipo mudzakhala mukuthyola mphesa mpaka nthawi yodzala. Mudzadya chakudya chanu mpaka kukhuta ndipo mudzakhala mʼdziko lanu mwamtendere.

6“ ‘Ndidzabweretsa mtendere mʼdziko lanu, ndipo muzidzagona popanda wokuopsezani. Ndidzachotsa nyama zakuthengo zoopsa mʼdziko mwanu, ndipo mʼdzikomo simudzakhala nkhondo. 7Mudzapirikitsa adani anu, ndipo mudzawagonjetsa ndi lupanga pamaso panu. 8Anthu asanu mwa inu adzapirikitsa anthu 100, ndipo anthu 100 mwa inu adzathamangitsa anthu 10,000, ndipo adani anuwo mudzawagonjetsa ndi lupanga.

9“ ‘Ndidzakukumbukirani ndi kukupatsani ana ambiri ndi kukuchulukitsani. Ndidzasunga pangano langa ndi inu. 10Mudzakhala mukudyabe chakudya chogonera ndipo mudzachotse chakudyacho mʼnkhokwe kuti mupezemo malo woyika chakudya china chatsopano. 11Ndidzakhala pakati panu, ndipo sindidzayipidwa nanu. 12Ine ndidzayendayenda pakati panu ndipo ndidzakhala Mulungu wanu. Inu mudzakhala anthu anga. 13Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto kuti musakhalenso akapolo a Aigupto. Ndinadula mipiringidzo ya goli lanu ndi kukuthandizani kuti muziyenda momasuka.

Chilango Chakusamvera

14“ ‘Koma mukadzapanda kundimvera ndi kuphwanya malamulo anga onsewa, 15ndipo ngati mudzanyoza malangizo anga ndi kunyansidwa ndi malamulo anga, ndi kulephera kumvera zonse zimene ndakulamulani, ndi kuswa pangano langa, 16Ine ndidzakuchitirani izi: ndidzabweretsa zoopsa zadzidzidzi monga chifuwa chachikulu chowondetsa ndiponso malungo amene adzawononga maso ndi kufowoketsa moyo wanu. Mudzangovutika kudzala mbewu zanu chifukwa adani anu adzazidya. 17Ndidzakufulatirani, kotero kuti adani anu adzakugonjetsani. Odana nanu adzakulamulirani ndipo inu muzidzagothawa popanda wokupirikitsani.

18“ ‘Ngati simudzandimvera mutaona zonsezi, ndidzakulanganinso mochulukitsa kasanu ndi kawiri chifukwa cha kuchimwa kwanu. 19Ndidzathyola mphamvu zanu zimene mukunyadirazo, ndipo ndidzasandutsa mitambo kuti ikhale yowuma ngati chitsulo, ndiponso nthaka yanu kuti ikhale ngati mkuwa. 20Mphamvu zanu zidzapita pachabe chifukwa nthaka yanu sidzabala kanthu, ngakhale mitengo yake sidzabala zipatso zake.

21“ ‘Ngati mudzapitirira kutsutsana nane ndi kukana kundimvera, ndidzachulukitsa masautso anu kasanu ndi kawiri molingana ndi machimo anu. 22Ndidzabweretsa zirombo zolusa pakati panu, ndipo zidzakulandani ana anu ndi kuwononga ngʼombe zanu. Choncho zidzachepetsa chiwerengero chanu kotero kuti mʼnjira mwanu simudzapita anthu.

23“ ‘Mukadzapanda kutembenukira kwa Ine ngakhale nditakulangani motere, ndi kumachitabe zotsutsana ndi Ine, 24Ine mwini ndidzalimbana nanu, ndipo ndidzakulangani mochulukitsa kasanu ndi kawiri chifukwa cha machimo anu. 25Ndipo ndidzabweretsa lupanga pa inu ndi kukulangani chifukwa chophwanya pangano langa. Mukadzasonkhana mʼmizinda yanu, ndidzatumiza miliri pakati panu ndipo ndidzakuperekani mʼmanja mwa adani anu. 26Ndikadzachepetsa buledi wanu, akazi khumi adzaphika buledi wawo mu uvuni umodzi, ndipo adzakugawirani bulediyo pangʼonopangʼono. Choncho mudzadya koma wosakhuta.

27“ ‘Mukadzapanda kundimvera ngakhale nditakulangani motere, ndi kumatsutsanabe ndi Ine, 28pamenepo ndidzalimbana nanu mwaukali, ndipo Ine mwini ndidzakulangani mochulukitsa kasanu ndi kawiri chifukwa cha kuchimwa kwanu. 29Mudzadya ana anu aamuna ndiponso mudzadya ana anu aakazi. 30Ine ndidzawononga malo anu opembedzera mafano a ku mapiri. Ndidzagwetsa maguwa anu ofukizira lubani, ndipo ndidzawunjika pamodzi mitembo ya mafano anu wopanda moyowo, ndipo ndidzanyansidwa nanu. 31Ndidzasandutsa mizinda yanu kukhala mabwinja ndi kuwononga malo anu wopatulika. Sindidzakondweranso ndi fungo lokoma la zopereka zanu. 32Ndidzawononga dziko kotero kuti adani anu mʼmenemo adzadabwa. 33Ndidzakubalalitsani pakati pa mitundu ina ya anthu ndipo ndidzasolola lupanga langa ndi kukupirikitsani. Dziko lanu lidzawonongedwa, ndipo mizinda yanu idzasanduka mabwinja. 34Nthawi imeneyo nthaka idzasangalalira kuyipumitsa kwake nthawi yonse imene idzakhala yosalimidwa, pamene inu mudzakhala muli mʼdziko la adani anu. Pa nthawi imeneyo dziko lidzapumula ndi kukondwerera kulipumuza kwake. 35Nthawi zonse pamene dzikolo lidzakhala lopanda anthu, nthaka idzapumula. Mpumulo umenewu udzakhala umene nthakayo sinapumulepo pa nthawi zimene inu munkapumula muli mʼdzikomo.

36“ ‘Kunena za amene adzatsale, ndidzayika mantha mʼmitima mwawo mʼdziko la adani awo kotero kuti adzathawa ngakhale mtswatswa wa tsamba lowuluka ndi mphepo. Adzathawa ngati akuthawa lupanga, ndipo adzagwa pansi ngakhale padzakhale wopanda kuwapirikitsa. 37Iwo adzaphunthwitsana ngati akuthawa nkhondo, ngakhale padzakhale popanda wowapirikitsa. Choncho simudzatha kuyima pamaso pa adani anu. 38Mudzatheratu pakati pa mitundu ya anthu. Dziko la adani anu lidzakudyani. 39Ngakhale iwo amene adzatsale adzatheratu mʼdziko la adani awo chifukwa cha machimo awo ndi machimo a makolo awo.

40“ ‘Tsono adzawulula machimo awo ndi machimo a makolo awo, kusakhulupirika kwawo ndi mayendedwe awo otsutsana nane, 41zomwe zinandipangitsa kuwafulatira ndi kuwapereka mʼmanja mwa adani awo. Ndipo mitima yawo yowumayo ikadzadzichepetsa ndi kuvomera kulangidwa chifukwa cha machimo awo, 42Ine ndidzakumbukira pangano langa ndi Yakobo, pangano langa ndi Isake, pangano langa ndi Abrahamu. Ndidzakumbukiranso dzikolo. 43Pakuti adzasiya dziko lawo lopanda anthu, nthaka idzakondwerera zaka zake zoyipumuza pamene iwo kudzakhala kulibe. Koma adzalangidwa chifukwa cha machimo awo popeza anakana malamulo anga ndipo mitima yawo inkayipidwa nawo malangizo anga. 44Komabe ngakhale adzachite zonsezi ali mʼdziko la adani awo, Ine sindidzawakana kapena kuyipidwa nawo kwakuti nʼkuwawononga kwathunthu ndi kuthetsa pangano langa ndi iwo. Ine ndine Yehova Mulungu wawo. 45Koma powachitira chifundo, ndidzakumbukira pangano langa ndi makolo awo amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto mitundu ina ikuona kuti Ine ndikhale Mulungu wawo. Ine ndine Yehova.’ ”

46Amenewa ndi malamulo ndi malangizo amene Yehova anawayika pakati pa Iye mwini ndi Aisraeli pa Phiri la Sinai kudzera mwa Mose.

Asante Twi Contemporary Bible

3 Mose 26:1-46

Osetie So Akatua

1“ ‘Monnyɛ abosom. Monnsisi ahoni anaa aboɔ mma mo ho. Mommfa aboɔ a wɔatwa nsisi mo asase so sɛ morebɛkoto wɔn. Mene Awurade mo Onyankopɔn.

2“ ‘Ɛsɛ sɛ modi me Homeda, na mode anidie ma me kronkronbea. Mene Awurade.

3“ ‘Sɛ modi me mmara no nyinaa so a, 4daa mɛtɔ osuo ama mo ama mo nnɔbaeɛ ayɛ yie abu so, na mo nnua nso bɛso aba a ɛbɛkyɛre wɔ nnua no so. 5Na sɛ ɛduru odua berɛ so bio koraa a, mo borɔdɔma bɛkɔ so abere. Mobɛdidi amee na moatena asase no so asomdwoeɛ mu,

6“ ‘Ɛfiri sɛ, mɛma mo asomdwoeɛ, na mɛma mo ada a monnsuro hwee. Mɛpam mmoa bɔne afiri mo ho. 7Mobɛpam mo atamfoɔ; na wɔbɛwuwu wɔ mo asekan ano. 8Mo mu baanum bɛka ɔha agu, na mo mu ɔha aka ɔpedu agu! Mo atamfoɔ bɛtotɔ wɔ akofena ano wɔ mo anim.

9“ ‘Mɛhwɛ mo so na mama mo adɔre, na madi apam a me ne mo pameeɛ no so. 10Mo nnɔbaeɛ bɛbu so a sɛ otwa berɛ foforɔ duru so a, morenhunu deɛ mode bɛyɛ. 11Na mɛtena mo mu, na meremmu mo animtiaa. 12Me ne mo bɛnante, na mayɛ mo Onyankopɔn, na moayɛ me nkurɔfoɔ. 13Mene Awurade mo Onyankopɔn a ɔde mo firi Misraim asase so baeɛ sɛ ɔmpɛ sɛ moyɛ nkoa bio no. Mabubu mo nkɔnsɔnkɔnsɔn mu, na mɛma mo anante animuonyam so.

14“ ‘Na sɛ moantie me, anni mʼasɛm so, 15na mopo me mmara a, 16deɛ mɛyɛ mo nie: Mɛma mo akoma atutu na mama nsamanwa ayɛ mo, na atiridiinini abɔ mo. Mo ani bɛtutu, na mo nkwa so ahwan. Mobɛdua nnɔbaeɛ agu kwa, ɛfiri sɛ, mo atamfoɔ na wɔbɛdie. 17Mɛyi mʼani afiri mo so, na moadwane afiri mo atamfoɔ anim. Wɔn a wɔtan mo bɛdi mo so. Mobɛdwane ɛberɛ a obiara mpam mo.

18“ ‘Na sɛ mokɔ so yɛ asoɔden a, mɛtwe mo aso mmɔho nson a emu yɛ den wɔ mo bɔne no ho. 19Mɛsɛe mo ahantan tumi no na mayɛ mo soro sɛ dadeɛ ne mo fam sɛ kɔbere. 20Mobɛsɛe mo ahoɔden kwa, na mo asase nnya nnɔbaeɛ biara, na ɛso nnua nso renso aba.

21“ ‘Na sɛ tie ara na monntie me a, mo bɔne enti, mede ɔyaredɔm mmɔho nson bɛgu mo so. 22Mɛma nkekaboa abɛkunkum mo mma na wɔakunkum mo anantwie, na mate mo dodoɔ so, na mo akwan bɛda mpan a obi mfa so bio.

23“ ‘Na sɛ yei antumi ansesa mo, na mokɔ so tia mʼapɛdeɛ a, 24me nso, mɛtia mo apɛdeɛ, na me ara mʼankasa mɛtwe mo aso mprɛnson wɔ mo bɔne ho. 25Menam ɔko so bɛbu mʼapam so ako atia mo de atua mo so ka. Mobɛdwane akɔ mo nkuro mu, na mede nyarewa bɛtoa mo wɔ hɔ. Na mo atamfoɔ bɛdi mo so. 26Mɛsɛe mo nnuane a mobɛnya nyinaa kɔsi sɛ mpo, fononoo baako burodo a ɛbɛto no na mmusuakuo edu bɛdi. Aduane kakra a mobɛdi no akyi, ɛkɔm bɛde mo.

27“ ‘Na sɛ mokɔ so yɛ asoɔden a, 28mo bɔne enti, me bo bɛfu mo na matwe mo aso a emu yɛ den mmɔho nson. 29Mobɛwe mo mmammarima ne mo mmammaa ɛnam. 30Mɛsɛe mo sorɔnsorɔmmea. Mɛtwitwa mo aduhwam afɔrebukyia agu, na mahyehyɛ mo afunu wɔ mo ahoni a ɛnni nkwa no so; na mɛpo mo. 31Mɛma mo nkuro ayɛ amamfo na masɛe baabi a mosom nyinaa, na mapo mo ohwam afɔrebɔ no. 32Ampa ara, mɛma mo asase so ada mpan na mo atamfoɔ atena so, na deɛ mɛyɛ mo no ayɛ mo nwanwa. 33Mɛbɔ mo apete aman no a morekɔ so nyinaa, na mede ɔko asɛe mo. Mo asase bɛda mpan na wɔasɛe mo nkuro. 34Akyire no, asase no bɛda hɔ ahome de asi mfeɛ dodoɔ a moamma anhome no anan; ɛbɛda hɔ wɔ mmerɛ a mowɔ atamfoɔ nsam wɔ wɔn nsase so no nyinaa. Na asase no ahome, na anya ne home nna nso. 35Ɛberɛ a asase no da mpan nyinaa, ɛbɛnya home a moamma annya wɔ Homeda dodoɔ a motenaa soɔ no.

36“ ‘Wɔn a wɔgyaa wɔn hɔ a wɔnwuiɛ no nso, mɛma wɔatwe wɔn akɔ akyirikyiri nsase so sɛ ɔko mu nneduafoɔ ne nkoa. Ɛhɔ na wɔbɛtena daa wɔ ehu mu. Wɔte sɛ mframa rebɔ ahahan koraa a, wɔbɛdwane te sɛ deɛ obi a ɔkura akofena repam wɔn; wɔbɛhwehwe ase wɔ ɛberɛ a obi mpam wɔn. 37Obiara rempamo wɔn nanso ehu enti, wɔbɛsuntisunti wɔn ho wɔn ho te sɛ deɛ wɔredwane afiri akono a wɔnni tumi biara a wɔde bɛgyina wɔn atamfoɔ anim no. 38Mobɛyera wɔ aman mu, na mo atamfoɔ asɛe mo. 39Wɔn a wɔbɛka no, wɔn bɔne enti, wɔn ho bɛyera wɔn wɔ atamfoɔ nsase so, bɔne a wɔn agyanom yɛeɛ no enti.

40“ ‘Nanso akyire no, me nkurɔfoɔ bɛka wɔn bɔne ne wɔn agyanom bɔne. Wɔbɛka sɛdeɛ wɔdii me hwammɔ na wɔtiaa me no. 41Sɛ me nso metia wɔn te sɛ deɛ ɛsɛ na mede wɔn kɔ wɔn atamfoɔ asase so a, afei, wɔn akomaden no ano bɛbrɛ ase, na wɔbɛtua wɔn bɔne so ka. 42Afei, mɛkae apam a me ne Yakob, Isak ne Abraham ayɛ, na mɛkae asase no. 43Asase no da hɔ dinn no, ɛbɛdi ne homeda. Nanso akyire no, wɔbɛnya wɔn asotwe sɛ wɔanni me nhyehyɛeɛ so na wɔtiaa me mmara. 44Na deɛ wɔyɛɛ no nyinaa akyi no, merensɛe wɔne mʼapam no korakora, ɛfiri sɛ, mene Awurade wɔn Onyankopɔn. 45Mɛkae tete apam a me ne wɔn agyanom a meyii wɔn firii Misraim, ɛberɛ a amanaman nyinaa rehwɛ no, yɛeɛ no. Me Awurade ne wɔn Onyankopɔn.’ ”

46Yeinom ne mmara ne ahyɛdeɛ a Awurade nam Mose so de maa Israelfoɔ no wɔ Sinai Bepɔ so no.