Habakuku 2 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Habakuku 2:1-20

1Ndidzakhala pa malo anga aulonda,

ndi kuyima pa mitumbira ya nkhondo;

ndidzadikira kuti ndimve zimene Iye adzandiwuze,

ndi yankho limene ndidzapatsidwe pa madandawulo anga.

Yankho la Yehova

2Tsono Yehova anandiyankha, nati:

“Lemba masomphenyawa

ndipo uwalembe mooneka bwino pa mapale

kuti wowerenga awawerenge mosavuta.

3Pakuti masomphenyawa akudikira nthawi yake;

masomphenyawa akunena zamʼtsogolo

ndipo sizidzalephera kuchitika.

Ngakhale achedwe kukwaniritsidwa, uwayembekezere;

zidzachitika ndithu ndipo sadzachedwa.

4“Taona, mdani wadzitukumula;

zokhumba zake sizowongoka,

koma wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.

5Ndithu, wasokonezeka ndi vinyo;

ndi wodzitama ndiponso wosakhazikika.

Pakuti ngodzikonda ngati manda,

ngosakhutitsidwa ngati imfa,

wadzisonkhanitsira mitundu yonse ya anthu

ndipo wagwira ukapolo anthu a mitundu yonse.

6“Kodi onse ogwidwawo sadzamunyoza ndi kumunyogodola ponena kuti,

“Tsoka kwa amene amadzikundikira katundu amene si wake

ndipo amadzilemeretsa ndi chuma cholanda!

Kodi izi zidzachitika mpaka liti?

7Kodi angongole ako sadzakuwukira mwadzidzidzi?

Kodi sadzadzuka ndi kukuchititsa mantha?

Pamenepo iwe udzalandidwa kalikonse.

8Pakuti unafunkha mitundu yambiri ya anthu,

mitundu ina imene inatsala idzakufunkha iweyo.

Pakuti wakhetsa magazi a anthu;

wawononga mayiko ndi mizinda ndi aliyense wokhala mʼmenemo.

9“Tsoka kwa amene amalemera ndi chuma chochipeza mwachinyengo,

kukweza malo ake okhalapo,

kuthawa mavuto!

10Wakonzekera kuwononga mitundu yambiri ya anthu,

kuchititsa manyazi nyumba yako yomwe ndi kuwononga moyo wako.

11Mwala pa khoma udzafuwula,

ndipo mitanda ya matabwa idzavomereza zimenezi.

12“Tsoka kwa amene amanga mzinda pokhetsa magazi

ndi kukhazikitsa mzinda pochita zoyipa!

13Kodi Yehova Wamphamvuzonse sanatsimikize

kuti ntchito za anthu zili ngati nkhuni pa moto,

ndi kuti mitundu ya anthu imadzitopetsa popanda phindu?

14Pakuti dziko lapansi lidzadzaza ndi chidziwitso cha ulemerero wa Yehova,

monga momwe madzi amadzazira nyanja.

15“Tsoka kwa amene amamwetsa anzake zakumwa zoledzeretsa,

kutsanula mʼbotolo mpaka ataledzera,

kuti aone umaliseche wawo.

16Udzachita manyazi mʼmalo mokhala ndi ulemerero.

Tsopano ino ndi nthawi yako! Imwa mpaka umaliseche wako uwonekere!

Chikho chochokera mʼdzanja lamanja la Yehova chikubwera kwa iwe,

ndipo manyazi adzaphimba ulemerero wako.

17Udzathedwa nzeru ndi chiwawa chimene unachita ku Lebanoni,

ndiponso udzachita mantha ndi nyama zimene unaziwononga.

Pakuti wakhetsa magazi a anthu;

wawononga mayiko ndi mizinda ndi aliyense wokhala mʼmenemo.

18“Kodi fano lili ndi phindu lanji, poti analisema ndi munthu,

kapena chifanizo chimene chimaphunzitsa mabodza?

Pakuti munthu amene walipanga amakhulupirira ntchito ya manja ake;

amapanga mafano amene samatha kuyankhula.

19Tsoka kwa amene amawuza mtengo kuti, ‘Khala wamoyo!’

Kapena mwala wopanda moyo kuti, ‘Dzuka!’

Kodi zimenezi zingathe kulangiza?

Ndi zokutidwa ndi golide ndi siliva;

mʼkati mwake mulibe mpweya.

20Koma Yehova ali mʼNyumba yake yopatulika;

dziko lonse lapansi likhale chete pamaso pake.”