Genesis 3 – CCL & SNC

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Genesis 3:1-24

Kuchimwa kwa Munthu

1Ndipo njoka inali yochenjera kuposa nyama yakuthengo iliyonse imene Yehova Mulungu anapanga. Njokayo inati kwa mkaziyo, “Kodi Mulungu ananenadi kuti, ‘Inu musadye zipatso za mtengo uliwonse mʼmundamu?’ ”

2Mkaziyo anati kwa njokayo, “Tikhoza kudya zipatso za mʼmitengo ya mʼmundawu, 3koma Mulungu anati, ‘Musadye zipatso za mu mtengo umene uli pakati pa munda, ndipo musadzawukhudze kuti mungadzafe.’ ”

4“Ndithudi simudzafa,” inatero njokayo kwa mkaziyo. 5“Pakuti Mulungu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye zipatso za mu mtengowo, maso anu adzatsekuka, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wodziwa zabwino ndi zoyipa.”

6Pamene mkaziyo anaona kuti mtengowo unali wabwino kudya ndi wokongola ndi kuti unali wopatsa nzeru, anatengako zipatso zake nadya. Zina anamupatsako mwamuna wake amene anali naye pomwepo ndipo naye anadyanso. 7Kenaka maso awo anatsekuka, ndipo anazindikira kuti anali maliseche. Choncho anasoka masamba a mkuyu nadzipangira zovala.

8Kenaka munthu uja ndi mkazi wake anamva mtswatswa wa Yehova Mulungu akuyendayenda mʼmundamo madzulo a tsikulo, ndipo iwo anabisala pamaso pa Yehova Mulungu pakati pa mitengo ya mʼmundamo. 9Yehova Mulungu anayitana munthu uja kuti, “Uli kuti?”

10Iye anayankha, “Ndinakumvani mʼmundamo, ndipo ndimaopa chifukwa ndinali maliseche; choncho ndinabisala.”

11Ndipo anamufunsa, “Ndani anakuwuza kuti uli maliseche? Kodi wadya zipatso za mtengo umene ndinakulamulira kuti usadye?”

12Koma munthu uja anati, “Mkazi amene munandipatsa kuti ndizikhala nayeyu anandipatsako chipatso cha mtengowo ndipo ndinadya.”

13Tsono Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, “Wachitachi nʼchiyani?”

Mkaziyo anati, “Njoka inandinamiza, ndipo ndinadya.”

14Choncho Yehova Mulungu anati kwa njokayo, “Popeza wachita zimenezi,

“Ndiwe wotembereredwa kuposa ziweto zonse

ndi nyama zakuthengo zonse.

Udzayenda chafufumimba

ndipo udzadya fumbi

masiku onse a moyo wako.

15Ndipo ndidzayika chidani

pakati pa iwe ndi mkaziyo,

pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake;

Iye adzaphwanya mutu wako

ndipo iwe udzaluma chidendene chake.”

16Kwa mkaziyo Iye anati,

“Ndidzachulukitsa ululu wako kwambiri pamene uli ndi pakati;

ndipo udzamva ululu pa nthawi yako yobereka ana.

Udzakhumba mwamuna wako,

ndipo adzakulamulira.”

17Ndipo kwa Adamu Mulungu anati, “Chifukwa wamvera mkazi wako ndipo wadya zipatso za mu mtengo umene ndinakulamulira kuti, ‘Usadye.’

“Nthaka yatembereredwa chifukwa cha iwe,

movutikira udzadya zochokera mʼnthakamo

masiku onse a moyo wako.

18Mʼnthakamo mudzamera minga ndi nthula

ndipo udzadya zomera zakuthengo.

19Kuti upeze chakudya udzayenera

kukhetsa thukuta,

mpaka utabwerera ku nthaka

pakuti unachokera kumeneko;

pakuti ndiwe fumbi

ku fumbi komweko udzabwerera.”

20Munthu uja anatcha mkazi wake Hava, chifukwa iyeyu adzakhala mayi wa anthu onse amoyo.

21Yehova Mulungu anapangira Adamu ndi mkazi wake zovala zachikopa ndipo anawaveka. 22Ndipo Yehova Mulungu anati, “Tsopano munthu uyu wasanduka mmodzi wa ife, wodziwa zabwino ndi zoyipa. Iyeyu asaloledwe kutambasula dzanja ndi kutengako zipatso za mu mtengo wopatsa moyo uja kuti angakhale ndi moyo mpaka muyaya.” 23Kotero Yehova Mulungu anatulutsa Adamu Mʼmunda wa Edeni kuti azilima mʼnthaka imene anachokera. 24Atamuthamangitsa munthu uja, Yehova anayika Akerubi mbali ya kummawa kwa Munda wa Edeni ndi lupanga lamoto limene limayendayenda ponsepo, kuteteza njira ya ku mtengo wopatsa moyo.

Slovo na cestu

1 Mojžíšova 3:1-24

1Had pak byl nejchytřejší ze všech živočichů polních, kteréž byl učinil Hospodin Bůh. A ten řekl ženě: Tak-liž jest, že vám Bůh řekl: Nebudete jísti z každého stromu rajského? 2I řekla žena hadu: Ovoce stromů rajských jíme; 3Ale o ovoci stromu, kterýž jest u prostřed ráje, řekl Bůh: Nebudete ho jísti, aniž se ho dotknete, abyste nezemřeli. 4I řekl had ženě: Nikoli nezemřete smrtí! 5Ale ví Bůh, že v kterýkoli den z něho jísti budete, otevrou se oči vaše; a budete jako bohové, vědouce dobré i zlé. 6Viduci tedy žena, že dobrý jest strom k jídlu i příjemný očima, a k nabytí rozumnosti strom žádostivý, vzala z ovoce jeho a jedla; dala také i muži svému s sebou, a on jedl. 7Tedy otevříny jsou oči obou dvou, a poznali, že jsou nazí; i navázali lístí fíkového a nadělali sobě věníků. 8A v tom uslyšeli hlas Hospodina Boha chodícího po ráji k větru dennímu; i skryl se Adam a žena jeho před tváří Hospodina Boha, u prostřed stromoví rajského. 9I povolal Hospodin Bůh Adama, a řekl jemu: Kdež jsi? 10Kterýžto řekl: Hlas tvůj slyšel jsem v ráji a bál jsem se, že jsem nahý; protož skryl jsem se. 11I řekl Bůh: Kdožť oznámil, že jsi nahý? Nejedl-lis ale z toho stromu, z něhožť jsem jísti zapověděl? 12I řekl Adam: Žena, kterouž jsi mi dal, aby byla se mnou, ona mi dala z stromu toho, a jedl jsem. 13I řekl Hospodin Bůh ženě: Což jsi to učinila? I řekla žena: Had mne podvedl, i jedla jsem. 14Tedy řekl Hospodin Bůh hadu: Že jsi to učinil, zlořečený budeš nade všecka hovada a nade všecky živočichy polní; po břiše svém plaziti se budeš, a prach žráti budeš po všecky dny života svého. 15Nad to, nepřátelství položím mezi tebou a mezi ženou, i mezi semenem tvým a semenem jejím; ono potře tobě hlavu, a ty potřeš jemu patu. 16Ženě pak řekl: Velice rozmnožím bolesti tvé a počínání tvá, s bolestí roditi budeš děti, a pod mocí muže tvého bude žádost tvá, a on panovati bude nad tebou. 17Adamovi také řekl: Že jsi uposlechl hlasu ženy své, a jedl jsi z stromu toho, kterýžť jsem zapověděl, řka: Nebudeš jísti z něho; zlořečená země pro tebe, s bolestí jísti budeš z ní po všecky dny života svého. 18Trní a bodláčí tobě ploditi bude, i budeš jísti byliny polní. 19V potu tváři své chléb jísti budeš, dokavadž se nenavrátíš do země, poněvadž jsi z ní vzat. Nebo prach jsi a v prach se navrátíš. 20Dal pak byl Adam jméno ženě své Eva, proto že ona byla mátě všech živých. 21I zdělal Hospodin Bůh Adamovi a ženě jeho oděv kožený, a přioděl je. 22Tedy řekl Hospodin Bůh: Aj, člověk učiněn jest jako jeden z nás, věda dobré i zlé; pročež nyní, aby nevztáhl ruky své, a nevzal také z stromu života, a jedl by, i byl by živ na věky, vyžeňme jej. 23I vypustil jej Hospodin Bůh z zahrady Eden, aby dělal zemi, z níž vzat byl. 24A tak vyhnal člověka a osadil zahradu Eden cherubíny k východní straně s mečem plamenným blýskajícím se, aby ostříhali cesty k stromu života.