Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Genesis 17:1-27

Pangano la Mdulidwe

1Pamene Abramu anali ndi zaka 99, Yehova anamuonekera nati, “Ine ndine Mulungu Wamphamvuzonse. Ukhale munthu wochita zolungama nthawi zonse. 2Ndipo Ine ndikulonjeza kuti ndidzakupatsa zidzukulu zambiri.”

3Pomwepo Abramu anadziponya pansi ndipo Mulungu anati kwa iye, 4“Pangano langa ndi iwe ndi ili: Udzakhala kholo la mitundu yambiri ya anthu. 5Sudzatchedwanso Abramu; dzina lako lidzakhala Abrahamu, chifukwa ndakusandutsa kukhala kholo la mitundu yambiri ya anthu. 6Ndidzakupatsa zidzukulu zambiri motero kuti mitundu yambiri ya anthu idzatuluka mwa iwe. Mafumunso adzatuluka mwa iwe. 7Pangano langa ndi iwe pamodzi ndi zidzukulu za mibado ya mʼtsogolo lidzakhala la muyaya. Ndidzakhala Mulungu wako ndi Mulungu wa zidzukulu zako. 8Dziko lonse la Kanaani, limene iwe ukukhala tsopano, ndalipereka kwa iwe ndi kwa zidzukulu zako kuti likhale chuma chanu mpaka muyaya. Ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wa zidzukulu zako.”

9Kenaka Mulungu anati kwa Abrahamu, “Koma iwe pamodzi ndi zidzukulu zako zobwera pambuyo pako mʼmibado ya mʼtsogolomo, sungani pangano langali. 10Iwe pamodzi ndi zidzukulu zako zobwera pambuyo pako muzisunga pangano ili loti mwamuna aliyense pakati panupa azichita mdulidwe. 11Kuyambira tsopano muzichita mdulidwe ndipo ichi chidzakhala chizindikiro cha pangano langa ndi iwe. 12Kuyambira tsopano mpaka mibado ya mʼtsogolomo mwana wamwamuna aliyense pakati panu amene wakwana masiku asanu ndi atatu ayenera kuchita mdulidwe. Awa ndi ana obadwa mʼbanja lako, kapena akapolo ochita kugula ndi ndalama, mlendo osakhala wa mʼmbumba yako. 13Achite mdulidwe ndithu mwana wamwamuna aliyense, mbadwa ngakhale kapolo wochita kugula ndi ndalama, ndipo ichi chidzakhala chizindikiro pa thupi lanu cha pangano langa lamuyaya. 14Mwamuna aliyense amene adzakhala wosachita mdulidwe adzachotsedwa pakati pa anthu ake chifukwa sanasunge pangano langa.”

15Mulungu anatinso kwa Abrahamu, “Sarai mkazi wako, sudzamutchanso Sarai; dzina lake lidzakhala Sara. 16Ndidzamudalitsa ndipo adzakubalira mwana wamwamuna. Ndidzamudalitsa kuti akhale mayi wa mitundu ya anthu; mafumu a anthuwo adzachokera mwa iye.”

17Abrahamu anadzigwetsa pansi pamaso pa Yehova, Iye anaseka nati, “Kodi munthu wa zaka 100 nʼkubala mwana? Kodi Sara adzabereka mwana pa msinkhu wa zaka makumi asanu ndi anayi?” 18Ndipo Abrahamu anati kwa Mulungu, “Bwanji mumudalitse Ismaeli.”

19Koma Mulungu anati, “Ayi, koma mkazi wako Sara adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha Isake. Ndidzasunga pangano langa losatha ndi iyeyu komanso ndi zidzukulu zobwera pambuyo pake. 20Koma za Ismaeli, ndamva. Ndidzamudalitsadi, ndipo adzakhala ndi zidzukulu zambiri. Iye adzakhala kholo la mafumu khumi ndi awiri ndipo mwa iye mudzatuluka mtundu waukulu wa anthu. 21Koma ndidzasunga pangano langali ndi Isake amene Sara adzakubalira pofika nthawi ngati ino chaka chamawa.” 22Atatha kuyankhula, Mulungu anamuchokera Abrahamu.

23Tsono Abrahamu anachita mdulidwe mwana wake Ismaeli ndi onse amene anali mʼbanja lake, mbadwa ngakhale kapolo ochita kugula ndi ndalama, monga mmene Mulungu analamulira. 24Abrahamu anali ndi zaka 99 pamene anachita mdulidwe, 25ndipo mwana wake Ismaeli anali ndi zaka khumi ndi zitatu; 26Onse, Abrahamu ndi mwana wake Ismaeli, anachita mdulidwe tsiku limodzi. 27Aliyense wamwamuna wa pa banja pa Abrahamu, kuphatikizapo iwo amene anabadwira pa banja pomwepo kapena akapolo ogula ndi ndalama kwa alendo, anachita mdulidwe.

Священное Писание (Восточный перевод), версия для Таджикистана

Начало 17:1-27

Обряд обрезания – знак священного соглашения

1Когда Иброму было девяносто девять лет, Вечный явился ему и сказал:

– Я – Бог Всемогущий; ходи передо Мной и будь непорочен. 2Я заключу священное соглашение между Мной и тобой и дам тебе многочисленное потомство.

3Ибром поклонился до самой земли, и Всевышний сказал ему:

4– Вот Моё священное соглашение с тобой. Ты будешь отцом многих народов. 5Ты больше не будешь называться Ибромом («превознесённый отец»): твоё имя будет Иброхим («отец множества»), потому что Я сделал тебя отцом множества народов. 6Я сделаю тебя очень плодовитым; от тебя Я произведу народы, и от тебя произойдут цари. 7Я заключу Моё священное соглашение с тобой и твоими потомками17:7 Букв.: «семенем». в грядущих поколениях как вечное священное соглашение: Я Бог, Которому будешь поклоняться ты и твои потомки. 8Всю землю Ханона, где ты сейчас пришелец, Я отдам в вечное владение тебе и твоим потомкам; и они будут Мне поклоняться.

9Всевышний сказал Иброхиму:

– Ты же должен соблюдать Моё священное соглашение, ты и потомки твои после тебя в грядущих поколениях. 10Вот Моё священное соглашение с тобой и твоими потомками после тебя, которое ты должен соблюдать: каждый младенец мужского пола да будет обрезан. 11Каждому должно быть сделано обрезание крайней плоти, и это будет знаком священного соглашения между Мной и вами. 12Каждый ваш младенец мужского пола должен быть обрезан, когда ему исполнится восемь дней: и тот, кто рождён в твоём доме, и тот, кто не из твоего потомства, а куплен за деньги у чужеземца. 13И рождённый в твоём доме, и купленный за деньги должен быть обрезан, и на теле вашем будет знак Моего вечного священного соглашения. 14Необрезанный младенец мужского пола, у которого не была обрезана крайняя плоть, будет исторгнут из своего народа: он нарушил священное соглашение со Мной.

15Ещё Всевышний сказал Иброхиму:

– Что до Сары, жены твоей, ты больше не будешь называть её Сарой: её имя будет Соро («княгиня»). 16Я благословлю её и дам тебе сына от неё. Я благословлю её так, что она станет матерью народов; цари народов произойдут от неё.

17Иброхим поклонился до самой земли и подумал, рассмеявшись: «Родится ли сын у человека, которому сто лет? Родит ли ребёнка Соро, которой уже девяносто?» 18И он сказал Всевышнему:

– Хотя бы Исмоил был жив и благословлён Тобой!

19Всевышний сказал:

– Именно твоя жена Соро родит тебе сына, и ты назовёшь его Исхок («он смеётся»). Я заключу Моё священное соглашение с ним как вечное соглашение для его потомков после него. 20Что до Исмоила, то Я услышал тебя: Я непременно благословлю его, Я сделаю его плодовитым и сильно размножу его. Он будет отцом двенадцати правителей, и Я произведу от него великий народ. 21Но Моё священное соглашение Я заключу с Исхоком, которого Соро родит тебе к этому времени в следующем году.

22Закончив говорить с Иброхимом, Всевышний поднялся от него. 23В тот же самый день Иброхим взял своего сына Исмоила и всех, кто был рождён в его доме или куплен за деньги, всех людей мужского пола в доме, и обрезал их, как сказал ему Всевышний. 24Иброхиму было девяносто девять лет, когда он был обрезан, 25а его сыну Исмоилу было тринадцать; 26Иброхим и его сын Исмоил оба были обрезаны в тот же день. 27И все мужчины в доме Иброхима, включая тех, кто был рождён в его доме или куплен у чужеземца, были обрезаны вместе с ним.