Ezekieli 46 – CCL & BDS

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 46:1-24

1“Ambuye Yehova akuti, Chipata chakummawa cha bwalo lamʼkati chizikhala chotseka pa masiku asanu ndi limodzi ogwira ntchito, koma chizitsekulidwa pa tsiku la sabata ndi pa tsiku la chikondwerero cha mwezi watsopano. 2Mfumu izilowa podzera mʼkhonde la mʼkati la chipata pochokera kunja, nʼkudzayima pafupi ndi nsanamira yapakhomo. Ansembe apereke nsembe yake yopsereza ndi nsembe yake yachiyanjano. Mfumuyo ipembedze pa chiwundo cha pa chipatacho kenaka nʼkutuluka. Koma chipatacho asachitseke mpaka madzulo. 3Anthu a mʼdziko azipembedza pamaso pa Yehova pa khomo la chipata chimenechi pa masiku a sabata ndi pa tsiku la mwezi watsopano. 4Nsembe yopsereza imene mfumu iyenera kupereka kwa Yehova ikhale motere: pa tsiku la Sabata izipereka ana ankhosa aamuna asanu ndi mmodzi wopanda chilema, ndiponso nkhosa yayima yopanda chilema. 5Pamodzi ndi nkhosa yayimuna, mfumu izipereka nsembe ya chakudya yokwanira efa imodzi. Pamodzi ndi ana ankhosa, mfumu izipereka monga ikufunira kutero. Iperekenso hini imodzi ya mafuta pa efa iliyonse ya tirigu. 6Pa tsiku la mwezi watsopano mfumuyo ipereke mwana wangʼombe wamwamuna, ana ankhosa asanu ndi mmodzi ndiponso nkhosa yayimuna, zonsezi zopanda chilema. 7Ipereke efa imodzi ya tirigu pa ngʼombe yayimuna iliyonse ndiponso efa ina pa nkhosa yayimuna iliyonse. Pa ana ankhosa ipereke tirigu monga ikufunira kutero. Pamodzi ndi efa ya tirigu, ipereke hini imodzi ya mafuta. 8Pamene mfumu ikulowa, izidzera mʼkhonde lamʼkati la chipata chakummawa, izitulukiranso pomwepo.

9“Anthu a mʼdzikomo akabwera kudzapembedza Yehova pa masiku a chikondwerero, ngati munthu alowera pa chipata chakumpoto atulukire chipata chakummwera. Munthu wolowera chipata chakummwera, atulukire chipata chakumpoto. Munthu asatulukire pomwe walowera, koma atulukire pa chipata choyangʼanana nacho. 10Mfumu izidzakhala pakati pawo. Anthu akamadzalowa mfumu idzalowa nawo. Anthu akamadzatuluka mfumu idzatuluka nawo.

11“Pa masiku achikondwerero ndi pa masiku ena osankhidwa, zopereka za chakudya zikhale zokwanira efa imodzi pamodzi ndi ngʼombe yayimuna iliyonse, efa imodzinso ndi nkhosa yayimuna, koma pa mwana wankhosa apereke monga angathere. Iperekenso hini imodzi ya mafuta pa efa iliyonse. 12Pamene mfumu ikufuna kupereka chopereka chaufulu kwa Yehova, kaya ndi nsembe yopsereza kapena zopereka za chiyanjano, ayitsekulire chipata chakummawa. Iyo ipereke nsembe yopsereza kapena zopereka zake za chiyanjano monga imachitira pa tsiku la Sabata. Kenaka ituluke ndipo mfumuyo itatuluka, atseke chitsekocho.

13“Tsiku lililonse nthawi ya mmawa azipereka kwa Yehova mwana wankhosa wa chaka chimodzi. 14Pamodzi ndi nyamayo aziperekanso mmawa uliwonse chopereka cha chakudya chokwanira chimodzi mwa zigawo zisanu ndi chimodzi za efa. Aziperekanso chimodzi mwa zigawo zitatu za hini ya mafuta okandira ufa wosalala. Chopereka cha chakudya chimenechi chiziperekedwa kwa Yehova nthawi zonse mwa lamulo. 15Motero azipereka mwana wankhosa ndi chopereka cha chakudya ndi mafuta mmawa uliwonse kuti zikhale nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku.

16“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ngati kalonga apereka mphatso chigawo cha cholowa chake kwa mmodzi mwa ana ake, mphatsoyo idzakhala ya ana akewo. Idzakhala yawo chifukwa ndi cholowa chawo. 17Koma ngati ipereka mphatso yotere kuchokera pa cholowa chake kwa mmodzi mwa antchito ake, mphatsoyo idzakhala ya wantchitoyo mpaka chaka chaufulu. Pambuyo pake idzabwereranso kwa kalongayo chifukwa cholowa chake ndi cha ana ake. 18Kalonga asalande cholowa chilichonse cha anthu, kuwachotsa mʼdera lawo la dziko. Iye apereke kwa ana ake cholowa chawo chochokera pa chuma chakechake, kuti pasapezeke ndi mmodzi yemwe mwa anthu anga wolandidwa chuma chake.’ ”

19Kenaka munthu uja anandidzeretsa pa khomo la pambali pa chipata nandilowetsa ku zipinda za ansembe zoyangʼana kumpoto. Ndipo ndinaona kumeneko malo chakumadzulo kwa zipindazo. 20Munthuyo anandiwuza kuti, “Awa ndi malo amene ansembe adzaphikirapo nsembe yopepesera kupalamula ndi nsembe yopepesera machimo. Kumenekonso azidzawotcherako chopereka cha chakudya. Sadzatuluka nazo zoyerazi mʼbwalo lakunja kuopa kuti angapatsireko kuyera anthu ena.”

21Pambuyo pake anandilowetsa mʼbwalo lakunja napita nane ku ngodya zinayi za bwalolo. Ndipo ndinaona mʼkati mwa ngodya iliyonse bwalo lina. 22Motero pa ngodya zinayi za bwalo panalinso mabwalo ena angʼonoangʼono. Mabwalo amenewa anali ofanana. Mulitali mwake munali mamita makumi awiri ndipo mulifupi mwake munali mamita khumi ndi asanu. 23Kuzungulira mabwalo anayi angʼonoangʼono aja panali mpanda wamiyala, ndi malo asonkhapo moto omangidwa mʼmunsi mwa mpandawo mozungulira. 24Munthuyo anandiwuza kuti, “Izi ndi zipinda zophikiramo. Mʼmenemu anthu otumikira ku Nyumba ya Mulungu adzaphikiramo nyama za nsembe za anthu.”

La Bible du Semeur

Ezéchiel 46:1-24

Les sabbats et les nouvelles lunes

1Voici ce que déclare le Seigneur, l’Eternel : La porte orientale du parvis intérieur restera fermée les six jours de travail. Mais le sabbat et le jour de la nouvelle lune, elle sera ouverte. 2Le prince, venant de l’extérieur, entrera par le portique de la porte46.2 Rituellement purifiée (45.19). De là, le prince pouvait suivre les sacrifices offerts sur le grand autel du parvis intérieur, mais il ne lui était pas permis de pénétrer dans ce parvis. et se tiendra près du montant de la porte. Les prêtres offriront son holocauste et ses sacrifices de communion. Il se prosternera sur le seuil de la porte, puis se retirera, et la porte ne sera plus refermée avant le soir. 3Les gens du peuple se prosterneront devant l’Eternel à l’entrée de cette porte, les jours de sabbat et lors des nouvelles lunes.

4Le sabbat, le prince offrira à l’Eternel en holocauste six agneaux sans défaut et un bélier sans défaut. 5Il présentera comme offrande quinze kilogrammes de grains avec le bélier, et ce qu’il voudra donner comme offrande accompagnant les agneaux. L’offrande d’huile sera de trois litres et demi par quinze kilogrammes de grains46.5 Littéralement : un épha de grains avec le bélier… un hîn d’huile par épha de grains.. 6Le jour de la nouvelle lune, il offrira un jeune taureau sans défaut, six agneaux et un bélier sans défaut. 7Il joindra comme offrande quinze kilogrammes de grains pour le taureau et autant pour le bélier et, pour les agneaux, ce qu’il aura à disposition, plus trois litres et demi d’huile par quinze kilogrammes de grains46.7 Littéralement : un épha de grains pour le taureau et un épha pour le bélier… plus un hîn d’huile par épha de grains..

Les règles pour le prince

8Quand le prince viendra, il entrera par le portique de la porte et sortira par le même chemin. 9Et quand les gens du peuple viendront devant l’Eternel lors des fêtes cultuelles, ceux qui entreront par la porte nord pour se prosterner, sortiront par la porte sud, et ceux qui entreront par la porte sud, sortiront par la porte nord. On ne repassera pas la porte par laquelle on sera entré, on sortira par la porte opposée. 10Le prince sera au milieu de son peuple, entrant et sortant en même temps qu’eux.

11Lors des fêtes et des solennités, l’offrande sera de quinze kilogrammes de grains par taureau et par bélier, et, pour les agneaux, ce qu’il voudra donner ; avec chaque mesure de quinze kilogrammes de grains, on offrira trois litres et demi d’huile46.11 Littéralement : un épha par taureau et par bélier… avec chaque épha de grains, on offrira un hîn d’huile..

12Quand le prince offrira à l’Eternel un holocauste ou un sacrifice de communion en offrande volontaire, on lui ouvrira la porte orientale, et il offrira son holocauste et son sacrifice de communion comme il le fait le jour du sabbat. Puis il sortira, et on refermera la porte derrière lui.

13On offrira chaque jour en holocauste à l’Eternel un agneau d’un an sans défaut. On l’offrira chaque matin. 14On y ajoutera chaque matin comme offrande deux kilogrammes et demi de fine farine que l’on pétrira avec un bon litre d’huile46.14 Littéralement : un sixième d’épha de fine farine et le tiers d’un hîn d’huile pour la mouiller.. C’est une offrande pour l’Eternel. Ce sont les lois fixées pour toujours pour le sacrifice perpétuel. 15On offrira chaque matin l’agneau, l’offrande et l’huile, c’est l’holocauste perpétuel.

Les droits du prince sur son patrimoine

16Voici ce que déclare le Seigneur, l’Eternel : Quand le prince fera une donation à l’un de ses fils, elle appartiendra à ce fils et passera comme patrimoine héréditaire à ses enfants. 17Mais lorsqu’il fera à l’un de ses serviteurs un don pris sur son patrimoine, ce don appartiendra au serviteur jusqu’à l’année de la libération46.17 Voir Lv 25.8-55. puis il reviendra au prince. Ainsi son patrimoine restera la propriété de ses fils. 18Le prince ne prendra rien sur le patrimoine du peuple en le dépouillant de ses propriétés ; c’est seulement de son propre domaine qu’il donnera des parts à ses fils, afin que personne de mon peuple ne soit dispersé loin de sa propriété46.18 Comme ce fut le cas pour Achab qui déposséda Naboth de sa vigne (1 R 21.3-16)..

Les cuisines du Temple

19Après cela, le personnage me fit pénétrer, par l’entrée qui est à côté de la porte nord, dans les salles saintes réservées aux prêtres. Tout au fond, du côté ouest, il y avait un emplacement 20et le personnage me dit que les prêtres y feraient cuire la viande des sacrifices de culpabilité et des sacrifices pour le péché, ainsi que les offrandes, afin de ne pas emporter ces aliments sur le parvis extérieur où leur contact pourrait rendre saints des membres du peuple.

21Puis il me fit sortir vers le parvis extérieur et me fit passer auprès des quatre coins du parvis, et je vis que dans chaque angle du parvis, il y avait une courette 22fermée46.22 fermée: terme hébreu de sens incertain., de quarante coudées de long sur trente coudées de large. Les quatre courettes avaient les mêmes dimensions. 23Chacune était entourée d’une enceinte, à la base de laquelle on avait aménagé des fourneaux tout autour. 24L’homme me dit : Voici les cuisines où les serviteurs du Temple feront cuire la viande des sacrifices offerts par le peuple.