Ezekieli 37 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 37:1-28

Chigwa cha Mafupa Owuma

1Dzanja la Yehova linali pa ine, ndipo Mzimu wa Yehova unandinyamula nʼkukandikhazika pakati pa chigwa. Chigwacho chinali chodzaza ndi mafupa. 2Yehova anandiyendetsa uku ndi uku pakati pa mafupawo. Mafupawo anali ochuluka kwambiri mʼchigwa monsemo ndipo anali owuma kwambiri. 3Tsono Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi mafupa amenewa angakhalenso ndi moyo?”

Ndinayankha kuti, “Inu Ambuye Yehova, Inuyo nokha ndiye mukudziwa.”

4Pamenepo anandiwuza kuti, “Lengeza kwa mafupa amenewa ndi kuwawuza kuti amve mawu a Ine Yehova! 5Uwawuze kuti zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena kwa mafupa ndi izi: Ndidzawuzira mpweya mwa inu, ndipo mudzakhalanso ndi moyo. 6Ndidzakupatsani mitsempha ndi mnofu. Ndiponso ndidzakukutani ndi khungu. Pambuyo pake ndidzawuzira mpweya mwa inu ndipo mudzakhalanso ndi moyo. Pamenepo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

7Ndipo ndinanenera monga anandilamulira. Ndipo pamene ndinkanenera, ndinamva gobedegobede, ndipo mafupa aja anayamba kulumikizana, fupa ku fupa linzake. 8Ine ndinayangʼana, ndipo mitsempha ndi mnofu zinabwera pa mafupawo ndipo khungu linaphimba pamwamba pake, koma munalibe mpweya mwa iwo.

9Tsono Yehova anandiwuza kuti, “Nenera kwa mpweya, nenera iwe mwana wa munthu ndi kuwuza mpweya mawu a Ine Ambuye Yehova kuti, ‘Bwera kuno iwe mpweya. Bwera kuchokera ku mbali zonse zinayi ndi kudzawuzira anthu ophedwawa kuti akhalenso ndi moyo.’ 10Choncho ndinanenera monga anandilamulira ndipo mpweya unalowa mwa iwo; apo anthu akufawo anakhala ndi moyo, nayimirira ndipo linali gulu lalikulu lankhondo.”

11Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, mafupa awa ndi nyumba yonse ya Israeli. Iwo amanena kuti, ‘Mafupa athu awuma ndipo chiyembekezo chathu chatayika, ife tawonongeka!’ 12Nʼchifukwa chake nenera ndi kuwawuza kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Inu anthu anga, ndidzafukula manda anu, ndipo ndidzakutulutsanimo ndi kukubwezerani ku dziko la Israeli. 13Ndipo inu, anthu anga, mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pamene ndidzafukula manda anu ndikukutulutsanimo. 14Ine ndidzayika Mzimu wanga mwa inu ndipo mudzakhalanso ndi moyo. Pambuyo pake ndidzakulowetsani mʼdziko lanulanu. Choncho mudzadziwa kuti Ambuye Yehova ndayankhula zimenezi, ndipo ndidzazichitadi. Ndikutero Ine Yehova!’ ”

Dziko Limodzi Kutsogoleredwa ndi Mfumu Imodzi

15Yehova anandiyankhula kuti: 16“Iwe mwana wa munthu, tenga ndodo ndipo ulembepo kuti, ‘Ndodo ya Yuda ndi Aisraeli oyanjana nawo.’ Utengenso ndodo ina ndipo ulembepo kuti, ‘Ndodo ya Efereimu, ndiye kuti fuko la Yosefe ndi Aisraeli onse oyanjana nawo.’ 17Ulumikize ndodo ziwirizi kuti zikhale ndodo imodzi mʼdzanja lako.

18“Anthu a mtundu wako akadzakufunsa tanthauzo la zimenezi 19iwe udzawawuze mawu awa a Ine Ambuye Yehova akuti, ‘Ine ndidzatenga ndodo ya Yosefe imene ili mʼdzanja la Efereimu, ndi ya mafuko a Aisraeli oyanjana naye, ndi kuyilumikiza ku ndodo ya Yuda, kuti zikhale ndodo imodzi, ndipo zidzakhaladi ndodo imodzi mʼdzanja langa!’ 20Ndodo ziwiri zimene udzalembepozo zikadzakhala mʼmanja mwako pamaso pa anthu onse, 21udzawawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzawachotsa Aisraeli pakati pa anthu a mitundu ina kumene anapita ku ukapolo. Ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku mbali zonse ndi kubwera nawo ku dziko lawolawo. 22Ndidzawasandutsa mtundu umodzi mʼdzikomo, pa mapiri a Israeli. Padzakhala mfumu imodzi yowalamulira, ndipo sadzakhalanso mitundu iwiri kapena kugawikana maufumu awiri. 23Sadzadziyipitsanso ndi mafano awo, kapena ndi zinthu zawo zonyansa, kapenanso ndi ntchito zawo zoyipa zilizonse. Ndidzawapulumutsa ku machimo awo onse ndi kuwayeretsa. Choncho adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo.

24“ ‘Mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yawo, motero onsewa adzakhala ndi mʼbusa mmodzi. Iwo adzatsatira malamulo anga ndipo adzasamalira kusunga malangizo anga. 25Iwo adzakhala mʼdziko limene ndinalipereka kwa mtumiki wanga Yakobo, dziko limene makolo anu ankakhalamo. Iwo ndi ana awo pamodzi ndi zidzukulu zawo adzakhala kumeneko ndipo Davide adzakhala mfumu yawo kwa muyaya. 26Ndidzachita nawo pangano lamtendere; lidzakhala pangano lamuyaya. Ndidzawakhazikitsa ndi kuwachulukitsa, ndipo ndidzayika malo anga opatulika pakati pawo kwamuyaya. 27Nyumba yanga yokhalamo idzakhala pakati pawo; Ine ndidzakhala Mulungu wawo, ndipo iwo adzakhala anthu anga. 28Pamenepo anthu a mitundu ina adzadziwa kuti Ine Yehova ndiye amene ndimasandutsa Israeli kukhala woyera, pamene malo anga opatulika adzakhala pakati pawo kwamuyaya!’ ”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

以西结书 37:1-28

枯骨复活

1耶和华的灵降在我身上,把我带到一个山谷,那里遍地都是骸骨。 2祂领我环绕那些骸骨走了一圈,我见到谷中枯干的骸骨相当多。 3祂对我说:“人子啊,这些骸骨能复活吗?”我说:“主耶和华啊,只有你知道。” 4祂又对我说:“你对这些骸骨发预言说,‘枯骨啊,你们要听耶和华说的话! 5主耶和华说,我要使气息进入你们里面,你们就必复活过来。 6我必给你们加上筋,使你们长出肉,再包上皮,将气息放在你们里面,你们就复活了。这样,你们就知道我是耶和华。’”

7于是,我便按耶和华的吩咐向枯骨发预言,我正说预言的时候,忽然有震动的声音,骨头便连在了一起。 8我又发现骨头上有了筋,长了肉,包上了皮,只是还没有气息。 9耶和华对我说:“人子啊,你要向风37:9 ”希伯来文又作“灵”,“气息”。说预言,告诉风,主耶和华这样说,‘风啊,从四方吹来,吹在这些被杀的人身上,使他们复活。’” 10于是,我便按耶和华的吩咐说预言,气息就进入他们里面,他们便复活了,并且站立起来,成为一支大军。

11耶和华对我说:“人子啊,这些骸骨就是所有的以色列人,他们说,‘我们骨头枯干,希望幻灭,彻底完了。’ 12你要说预言,告诉他们,‘主耶和华说,我的子民啊,我要打开你们的坟墓,领你们出来,我要领你们返回以色列13我的子民啊,当我这样做的时候,你们就知道我是耶和华。 14我要把我的灵放在你们里面,叫你们复活,安居在自己的土地上,那时你们就知道我耶和华言出必行。这是耶和华说的。’”

15耶和华对我说: 16“人子啊,你拿一根杖来,写上‘犹大和他的以色列同伴’,然后再拿另一根杖,写上‘约瑟,即以法莲,与他的以色列同伴’。 17然后把这两根杖连成一根,拿在手中。 18当你的同胞问你这是什么意思时, 19你就告诉他们,主耶和华这样说,‘我要把约瑟和他的以色列同伴的杖,就是以法莲手中的杖,与犹大的杖在我手中连成一根。’ 20你要拿着这两根写着字的杖让他们看, 21告诉他们,主耶和华这样说,‘我要把以色列的百姓从他们分散的各国招聚起来,领他们回归故土。 22我要使他们在以色列的土地和群山上成为一国,只有一位王统治他们,不再分为两个国家。 23他们不会再因祭拜偶像、行可憎之事而玷污自己,我要从他们犯罪的地方把他们救出来,洗净他们的罪。他们要做我的子民,我要做他们的上帝。

24“‘我的仆人大卫要做王治理他们,成为他们唯一的牧人。他们必恪守我的典章,谨遵我的律例。 25他们要安居在我赐给我仆人雅各的土地上,就是你们祖先居住的地方。他们世世代代都要居住在那里,我仆人大卫要永远做他们的王。 26我要与他们订立永存的平安之约,使他们安居,人丁兴旺。我的圣所要永远设立在他们当中。 27我要住在他们中间。我要做他们的上帝,他们要做我的子民。 28各国的人看见我的圣所永远设立在他们当中,便会知道是我耶和华使以色列圣洁了。’”