Ezekieli 33 – CCL & NSP

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 33:1-33

Ezekieli Akhala Mlonda

1Yehova anandiyankhula nati: 2“Iwe mwana wa munthu awuze anthu a mtundu wako kuti, ‘Paja zimati ndikatumiza nkhondo mʼdziko anthu a mʼdzikomo amasankha munthu mmodzi pakati pawo kuti akhale mlonda. 3Tsono iyeyo amati akaona nkhondo ikubwera amaliza lipenga kuti achenjeze anthuwo. 4Wina aliyense akamva lipenga koma osasamala, mdani uja akabwera nʼkumupha, ndiye kuti wadziphetsa yekha. 5Iye anamva kulira kwa lipenga koma sanalabadire. Ndiye kuti wadziphetsa yekha. Akanasamala kuchenjeza kwa mlonda akanapulumuka. 6Koma ngati mlondayo aona lupanga likubwera ndipo osawomba lipengalo kuchenjeza anthu, ndipo lupanga libwera ndi kuchotsa moyo wa mmodzi mwa iwo, munthu ameneyo adzafa chifukwa cha tchimo lake, koma ndidzamuyimba mlandu mlondayo chifukwa cha imfa ya mnzakeyo.’

7“Tsono iwe mwana wa munthu, ndakuyika kuti ukhale mlonda wa Aisraeli. Choncho imva mawu amene ndikuyankhula ndipo uwachenjeze. 8Ndikawuza munthu woyipa kuti, ‘Iwe munthu woyipa, udzafa ndithu,’ ndipo iwe osayankhula kumuchenjeza kuti aleke njira zake, munthu wochimwayo adzafa chifukwa cha tchimo lake, koma Ine ndidzakuyimba mlandu chifukwa cha imfa yake. 9Koma ngati uchenjeza munthu woyipa kuti aleke njira zake, ndipo iye osatero, adzafa chifukwa cha tchimo lake, koma iwe udzapulumutsa moyo wako.

10“Iwe mwana wa munthu, akumbutse Aisraeli mawu awo akuti, ‘Ife talemedwa ndi zolakwa zathu ndi machimo athu, ndipo tikuwonda chifukwa cha zimene tachita. Kodi tingakhale ndi moyo bwanji?’ ” 11Uwawuze kuti, Ine Ambuye Yehova ndikuti: “Pali Ine wamoyo, sindikondwera ndi imfa ya munthu woyipa. Ndimakondwera ndikamaona munthu woyipa akuleka zoyipa zake kuti akhale ndi moyo. Tembenukani! Tembenukani, siyani makhalidwe anu oyipa! Muferanji, Inu Aisraeli?

12“Tsono iwe mwana wa munthu, awuze anthu a mtundu wako kuti, ‘Ngati munthu wolungama achimwa, ndiye kuti ntchito zake zabwino zija sizidzamupulutsa. Koma wochimwa akaleka ntchito zake zoyipazo, sadzalangidwa konse. Ndithu ngati munthu wolungama ayamba kuchimwa sadzatha kukhala ndi moyo chifukwa cha ntchito zake zabwino zija.’ 13Ngati ndiwuza munthu wolungama kuti adzafa ndithu, koma iyeyo nʼkumadalira ntchito zake zabwino zimene anachita kale ndi kuyamba kuchimwa, ndiye kuti ntchito zake zabwinozo zidzayiwalika. Iye adzafa chifukwa cha machimo ake. 14Ndipo ngati ndiwuza munthu woyipa kuti, ‘Udzafa ndithu,’ tsono iye nʼkutembenuka kuleka machimo ake ndi kuyamba kuchita zimene Yehova afuna, 15monga kubweza chimene anatenga ngati chikole cha ngongole, kubweza chimene anaba, kutsatira malamulo omwe amapereka moyo ndi kuleka kuchita zoyipa, iye adzakhala ndithu ndi moyo; sadzafa. 16Ndidzakhululuka machimo ake onse anachita. Iye wachita zimene ndi zolungama ndi zoyenera ndipo iye adzakhala ndi moyo ndithu.

17“Komabe anthu a mtundu wako akunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Ayi, koma makhalidwe awo ndiwo ali osalungama. 18Ngati munthu wolungama atembenuka ndi kuleka ntchito zake zolungama ndi kuyamba kuchita zoyipa, adzafa nazo. 19Ndipo ngati munthu woyipa atembenuka ndi kuleka ntchito zake zoyipa ndi kuyamba kuchita zolungama ndi zoyenera, iye adzakhala ndi moyo pochita zimenezo. 20Koma Inu Aisraeli, mukunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Ayi, inu Aisraeli, Ine ndidzaweruza aliyense wa inu potsata ntchito zake.”

Mbiri ya Kuwonongeka kwa Yerusalemu

21Pa tsiku lachisanu la mwezi wakhumi, chaka chakhumi ndi chiwiri cha ukapolo wathu, munthu wina amene anapulumuka ku Yerusalemu anabwera kudzandiwuza kuti, “Mzinda wagwa!” 22Tsono madzulo ake munthuyo asanafike, dzanja la Yehova linali pa ine. Koma mmawa mwake munthuyo atabwera Yehova anatsekula pakamwa panga, motero kuti sindinakhalenso wosayankhula.

23Ndipo Yehova anandiyankhula kuti: 24“Iwe mwana wa munthu, anthu amene akukhala mʼmizinda ya mabwinja ya dziko la Israeli akunena kuti, ‘Abrahamu anali munthu mmodzi yekha, ndipo anamupatsa dziko lonse. Koma ife tilipo ambiri, motero tsono dzikolo ndi lathu.’ 25Choncho iwe uwawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti, ‘Inu mumadya nyama ili ndi magazi ake, ndipo mumapembedza mafano ndi kukhetsa magazi, kodi tsono inu nʼkulandira dzikoli? 26Mumadalira lupanga lanu, mumachita zinthu zonyansa, ndipo aliyense wa inu amachita chigololo ndi mkazi wa mnzake. Kodi inu nʼkulandira dzikoli?’

27“Uwawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti, ‘Ndithu pali Ine wamoyo, anthu amene anatsala mʼmizinda ya mabwinja adzaphedwa ndi lupanga, amene ali ku midzi ndidzawapereka kuti adzadyedwe ndi zirombo zakuthengo, ndipo amene ali mʼmalinga ndi mʼmapanga adzafa ndi mliri. 28Ndidzalisandutsa chipululu dzikolo, ndipo mphamvu zake zimene amanyadira zidzatheratu, ndipo mapiri a Yerusalemu adzasanduka chipululu, kotero kuti palibe amene adzatha kudutsako. 29Ndikadzasandutsa dzikolo chipululu chifukwa cha zonyansa zimene ankachita, pamenepo ndiye adzadziwa kuti ndine Yehova.’

30“Koma kunena za iwe, mwana wa munthu, anthu a mtundu wako akumayankhula za iwe akakhala pa makoma a mzinda ndi pa makomo a nyumba zawo. Akumawuzana kuti, ‘Tiyeni tikamve uthenga umene wachokera kwa Yehova.’ 31Anthu anga amabwera kwa iwe, monga momwe amachitira nthawi zonse anthu anga, ndipo amakhala pansi pamaso pako kumvetsera mawu ako. Koma zimene akumvazo sazichita. Zokamba zawo zimaonetsa chikondi, koma mitima yawo imakhala pa phindu lawo. 32Kunena zoona, kwa iwowo sindiwe kanthu konse, ndiwe munthu wamba chabe womangoyimba nyimbo zachikondi ndi liwu lokoma poyimba zeze. Kumva amamva mawu ako koma sawagwiritsa ntchito.

33“Koma zonsezi zikadzachitika, ndipo zidzachitika ndithu, pamenepo adzadziwa kuti mneneri anali pakati pawo.”

New Serbian Translation

Књига пророка Језекиља 33:1-33

Одговорност пророка

1Дође ми опет реч Господња: 2„Сине човечији, говори својим сународницима. Реци им: ’Ако доведем мач на неку земље, а народ земље узме једног човека из својих крајева и поставе га за чувара, 3и ако он види да мач долази на ту земљу, па затруби у трубу и опомене народ, 4али се онај који чује глас трубе не да опоменути, а мач дође и покоси га, његова ће крв пасти на његову главу. 5Пошто је чуо глас трубе, а није се дао опоменути, његова ће крв бити на њему. Да се дао опоменути, спасао би себи живот. 6Ако чувар види да мач долази, а не затруби у трубу, те народ не буде опоменут, а дође мач и покоси једног од њих, тај ће платити животом за своју кривицу, али ћу одговорност за његову крв тражити од чувара.’

7Тебе сам, сине човечији, поставио за чувара дому Израиљевом. Кад чујеш реч из мојих уста, пренеси им моју опомену. 8Кад кажем опакоме: ’Заиста ћеш умрети’, а ти му не кажеш ништа како би га опоменуо да се окане свог опаког пута, опаки ће свакако умрети због своје кривице, али ћу одговорност за његову смрт тражити од тебе. 9Али ако опоменеш опаког да се врати са свог пута, а он се не врати са свог пута, умреће за своју кривицу. Ти ћеш, пак, спасти себи живот.

10А ти, сине човечији, реци дому Израиљеву: ’Ви говорите: наши преступи и греси нас терете, и због њих пропадамо. Како ћемо опстати!’ 11Реци им: ’Живота ми мога – говори Господ Бог – није мени мило да опаки умре, него да се врати са свог пута и живи. Вратите се! Вратите се са својих злих путева! Зашто да изгинете, доме Израиљев?’

12Ти, сине човечији, реци својим сународницима: ’Праведника неће спасти његова праведност када згреши, нити ће опакост довести опакога до његове пропасти када се окане своје опакости. Праведник неће остати у животу кад згреши.’ 13Кад кажем праведнику да ће живети, али се он поузда у своју праведност, па згреши, сва његова праведност неће се памтити; умреће због неправде коју је починио. 14А ако кажем опакоме: ’Заиста ћеш умрети!’ – и он се окане свог греха, па почне да чини право и правду; 15ако опаки врати залог и врати што је опљачкао, држи се заповести живота и не чини неправду, заиста ће живети, неће умрети. 16Ни један од греха које је починио му се неће памтити. Чинио је право и правду, заиста ће живети.

17Ипак, твоји сународници кажу: ’Пут Господњи није праведан.’ Не, њихови путеви нису праведни! 18Кад се праведник одврати од своје праведности и стане да чини неправду, умреће због ње. 19А ако се опаки окане своје опакости и почне да чини право и правду, живеће због њих. 20А ви кажете: ’Пут Господњи није праведан.’ Доме Израиљев, свакоме ћу од вас судити по његовим путевима!“

Пад Јерусалима

21У дванаестој години нашег изгнанства, петога дана десетог месеца, дошао ми је један бегунац из Јерусалима и рекао ми: „Град је пао!“ 22А увече, пре него што је бегунац дошао, на мене се спустила рука Господња. Господ ми је отворио уста пре него што је овај дошао ујутро. И пошто су ми се отворила уста, више нисам ћутао.

23Тада ми дође реч Господња: 24„Сине човечији, они што живе у оним рушевинама у Израиљевој земљи говоре: ’Аврахам је био један једини кад је примио земљу у посед, а нас је много. Нама је земља дана у посед.’ 25Зато им реци: ’Говори Господ Бог: ето, ви једете месо с крвљу, дижете очи према својим идолима и проливате крв, а хоћете да поседујете земљу? 26Ослањате се на свој мач, чините гадости, и свако од вас скрнави жену свог ближњег. Зар ви да поседујете земљу?’

27Овако им реци: ’Говори Господ Бог: живота ми мога, они који живе у рушевинама изгинуће од мача, оне који су напољу даћу зверима за храну, а они који су у склоништима и пећинама помреће од заразе. 28Тако ћу земљу претворити у крајњу пустош, па ће нестати понос њене силе. Горе ће Израиљеве опустети, и више нико тамо неће пролазити. 29И знаће да сам ја Господ, када претворим земљу у крајњу пустош због гадости које су починили.’

30Сине човечији, твоји сународници говоре о теби уз зидове и код кућних врата. Говоре један другом: ’Дођите и послушајте реч која је дошла од Господа!’ 31Долазе к теби као кад народ долази на сабор; мој народ седа испред тебе и слуша твоје речи, али их не извршава; пријају им у устима, а срце им иде за непоштеним добитком. 32Ти си за њих као певач умилног гласа, који пева љубавне песме и вешто свира; слушају твоје речи, али их не извршавају.

33Али кад ово дође, а ево, већ долази, тада ће знати да је пророк био међу њима.“