Ezekieli 15 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 15:1-8

Yerusalemu, Mtengo Wamphesa Wosabereka

1Yehova anayankhulanso nane kuti, 2“Iwe mwana wa munthu, kodi mtengo wamphesa umapambana bwanji mtengo wina uliwonse? Nthambi zake zimapambana bwanji nthambi ina iliyonse. 3Mtengo umene uja nʼkupangira chiyani? Kodi anthu angathe kupangira chikhomo chokolekapo zinthu zawo? 4Taonani, ndi nkhuni chabe zosonkhera moto. Ukaponyedwa pa moto monga nkhuni ndi kuyaka mbali zonse ndi kusanduka makala, kodi ungagwiritsidwe ntchito ina iliyonse? 5Ngati pamene unali wosapsa sukanatheka kuwugwiritsa ntchito, nanga bwanji utapserera ndi moto, adzawugwiritsa ntchito bwanji?

6“Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti, ‘Mtengo wamphesa ndidzawuponya mʼmoto monga ndimachitira ndi mitengo ina ya ku nkhalango. Momwemonso ndidzachita ndi anthu a ku Yerusalemu. 7Ndidzawalanga pamenepo ngakhale iwo atuluka pa moto, motowo udzawatenthabe. Ndipo pamene ndidzatsutsana nawo, mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. 8Ine ndidzasandutsa dziko kukhala chipululu chifukwa anthu akhala osakhulupirika, akutero Ambuye Yehova.’ ”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

以西结书 15:1-8

葡萄树的比喻

1耶和华对我说: 2“人子啊,葡萄木比林中其他木材更好吗? 3葡萄木有什么用呢?能用它制造挂钩挂东西吗? 4它只能用来当柴烧。如果火已经烧了它的两头,中间也烧黑了,它还有什么用呢? 5它完好无损的时候,尚且不能用来制造工具,被火烧后岂不更没用了吗? 6所以,主耶和华说,我怎样把林中的葡萄树丢在火中当柴烧,也必照样丢弃耶路撒冷的居民。 7我必严惩他们。他们纵然火里逃生,仍要被火烧灭。我严惩他们的时候,他们便知道我是耶和华。 8我必使他们的土地荒凉,因为他们对我不忠。这是主耶和华说的。”