Mʼndandanda wa Ayuda amene Anabwerera
1Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerako ku ukapolo, amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anawagwira ukapolo ndi kupita nawo ku Babuloni (iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wake. 2Iwo anabwerera pamodzi ndi Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Seruya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu ndi Baana).
Chiwerengero cha anthu aamuna a Israeli chinali chotere:
3Zidzukulu za Parosi | 2,172 |
4zidzukulu za Sefatiya | 372 |
5zidzukulu za Ara | 775 |
6zidzukulu za Pahati-Mowabu (zochokera kwa Yesuwa ndi Yowabu) | 2,812 |
7zidzukulu za Elamu | 1,254 |
8zidzukulu za Zatu | 945 |
9zidzukulu za Zakai | 760 |
10zidzukulu za Bani | 642 |
11zidzukulu za Bebai | 623 |
12zidzukulu za Azigadi | 1,222 |
13zidzukulu za Adonikamu | 666 |
14zidzukulu za Bigivai | 2,056 |
15zidzukulu za Adini | 454 |
16zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya) | 98 |
17zidzukulu za Bezayi | 323 |
18zidzukulu za Yora | 112 |
19zidzukulu za Hasumu | 223 |
20zidzukulu za Gibari | 95. |
21Anthu a ku Betelehemu | 123 |
22Anthu aamuna a ku Netofa | 56 |
23Anthu aamuna a ku Anatoti | 128 |
24Anthu aamuna a ku Azimaveti | 42 |
25Anthu aamuna a ku Kiriati Yearimu, Kefira ndi Beeroti | 743 |
26Anthu aamuna a ku Rama ndi Geba | 621 |
27Anthu aamuna a ku Mikimasi | 122 |
28Anthu aamuna a ku Beteli ndi Ai | 223 |
29Anthu aamuna a ku Nebo | 52 |
30Anthu aamuna a ku Magaibisi | 156 |
31Anthu aamuna a ku Elamu wina | 1,254 |
32Anthu aamuna a ku Harimu | 320 |
33Anthu aamuna a ku Lodi, Hadidi ndi Ono | 725 |
34Anthu aamuna a ku Yeriko | 345 |
35Anthu aamuna a ku Sena | 3,630. |
36Ansembe anali awa:
Zidzukulu za Yedaya (kudzera mu banja la Yesuwa) | 973 |
37Zidzukulu za Imeri | 1,052 |
38Zidzukulu za Pasuri | 1,247 |
39Zidzukulu za Harimu | 1,017. |
40Alevi anali awa:
Zidzukulu za Yesuwa ndi Kadimieli (kudzera mwa ana a Hodaviya) | 74. |
41Anthu oyimba nyimbo anali awa:
42Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa:
Zidzukulu za Salumu, zidzukulu za Ateri, zidzukulu za Talimoni, zidzukulu za Akubu, zidzukulu za Hatita ndi zidzukulu za Sobai | 139. |
43Otumikira ku Nyumba ya Mulungu anali awa:
Zidzukulu za |
Ziha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti, |
44zidzukulu za Kerosi, zidzukulu za Siyaha, Padoni, |
45zidzukulu za Lebana, zidzukulu za Hagaba, zidzukulu za Akubu, |
46zidzukulu za Hagabu, zidzukulu za Salimayi, zidzukulu za Hanani, |
47zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari, zidzukulu za Reaya, |
48zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nekoda, zidzukulu za Gazamu, |
49zidzukulu za Uza, zidzukulu za Peseya, zidzukulu za Besai, |
50zidzukulu za Asina, zidzukulu za Meunimu, Nefusimu, |
51zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri, |
52zidzukulu za Baziruti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa, |
53zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema, |
54zidzukulu za Neziya ndi zidzukulu za Hatifa. |
55Zidzukulu za antchito a Solomoni zinali izi:
Zidzukulu za |
Sotai, zidzukulu za Hasofereti, zidzukulu za Peruda, |
56zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli, |
57zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu, |
zidzukulu za Pokereti, Hazebayimu ndi Ami. |
58Chiwerengero cha onse otumikira ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za Solomoni chinali | 392. |
59Anthu ali mʼmunsiwa anabwera kuchokera ku mizinda ya Teli-Mela, Teli-Harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri, ngakhale samatha kutsimikiza kuti mafuko awo analidi Aisraeli enieni kapena ayi:
60Zidzukulu za Delaya, zidzukulu za Tobiya, ndi zidzukulu za Nekoda. Onse pamodzi anali | 652. |
61Ndi ena pakati pa ansembe anali awa:
Zidzukulu za |
Hobiya, Hakozi, ndi Barizilai (Zidzukulu za Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai. Barizilai ameneyu ndi uja anakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi ndipo ankadziwika ndi dzina la bambo wawoyo.) |
62Amenewa anafufuza mayina awo mʼbuku lofotokoza mbiri ya mafuko awo, koma mayinawo sanawapezemo, choncho anawachotsa pa unsembe ngati anthu odetsedwa pa zachipembedzo. 63Bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo mpaka atapezeka wansembe wodziwa kuwombeza ndi Urimu ndi Tumimu.
64Chiwerengero cha anthu onse pamodzi chinali 42,360, 65kuwonjezera pamenepo, panalinso antchito awo aamuna ndi aakazi okwanira 7,337. Analinso ndi amuna ndi akazi oyimba nyimbo okwanira 200. 66Anali ndi akavalo 736, nyulu 245, 67ngamira 435 ndi abulu 6,720.
68Atafika ku Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu, ena mwa atsogoleri a mabanja anapereka zopereka zaufulu zothandizira kumanganso Nyumba ya Mulungu pamalo pake pakale. 69Anapereka kwa msungichuma wa ntchitoyo molingana ndi mmene aliyense chuma chake chinalili: golide wa makilogalamu 500, siliva makilogalamu 2,800 ndi zovala za ansembe zokwanira 100.
70Ansembe, Alevi, oyimba nyimbo, alonda ndi antchito a ku Nyumba ya Yehova pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmidzi ya makolo awo.