Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezara 1:1-11

Koresi Athandiza Ayuda Kubwerera Kwawo

1Mʼchaka choyamba cha ufumu wa Koresi mfumu ya Perisiya, pofuna kukwaniritsa zimene anayankhula kudzera mwa Yeremiya, Yehova anayika maganizo mu mtima mwa Koresi mfumu ya Perisiya kuti alengeze mʼdziko lake lonse ndi mawu apakamwa ngakhalenso ochita kulemba.

2Iye anati, “Koresi mfumu ya Perisiya ikunena kuti,

“ ‘Yehova, Mulungu wakumwamba wandipatsa maufumu onse a dziko lapansi, ndipo wandipatsa udindo woti ndimumangire Nyumba ku Yerusalemu mʼdziko la Yuda. 3Aliyense wa inu amene ali wa Yehova, Mulungu wakeyo akhale naye. Tsono aliyense wa inu apite ku Yerusalemu, mʼdziko la Yuda kuti akamange Nyumba ya Yehova, Mulungu wa Israeli. Iyeyu ndi Mulungu amene ali mu Yerusalemu. 4Ndipo kumalo kulikonse kumene otsalawo akukhala, athandizidwe ndi eni dzikolo powapatsa siliva, golide, katundu ndi ziweto ndi zopereka za ufulu zoti akapereke ku Nyumba ya Yehova imene ili ku Yerusalemu.’ ”

5Choncho atsogoleri a mabanja afuko la Yuda ndi la Benjamini komanso ansembe ndi Alevi, aliyense amene Mulungu anawutsa mtima wake, anayamba kukonzeka kupita kukamanga Nyumba ya Yehova imene ili ku Yerusalemu. 6Onse oyandikana nawo anawathandiza powapatsa ziwiya za siliva ndi zagolide, kuphatikizaponso katundu ndi ziweto, ndiponso mphatso zamtengo wapatali, kuwonjezera pa zopereka zaufulu zija. 7Nayenso mfumu Koresi anatulutsa ziwiya za mʼNyumba ya Yehova zimene Nebukadinezara anazitenga kuzichotsa ku Yerusalemu ndi kuziyika mʼnyumba ya milungu yake. 8Koresi, mfumu ya ku Perisiya inatulutsa ziwiyazi ndi kuzipereka kwa Miteridati, msungichuma amene anaziwerenga pamaso pa Sesibazara nduna yayikulu ya dziko la Yuda.

9Chiwerengerochi chinali motere:

Mabeseni agolide 30mabeseni asiliva1,000a zopereka2910timiphika tagolide 230timiphika tasiliva 410ziwiya zina 1,000.

11Ziwiya zonse zagolide ndi siliva pamodzi zinalipo 5,400. Zonsezi ndi zimene Sezi-Bazara anabwera nazo pamene otengedwa ukapolo aja ankabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku Babuloni.

New Russian Translation

Ездра 1:1-11

Указ Кира о возвращении пленников

(2 Пар. 36:22-23)

1В первый год правления Кира1:1 Кир II Великий, основатель Персидского государства Ахменидов, правил с 558 по 530 гг. до н. э. В 539 г. покорил Вавилон и Месопотамию. Кир погиб во время похода в Центральную Азию от руки сакской царицы Тамирис., царя Персии, чтобы исполнилось слово Господа, которое возвестил Иеремия1:1 См. Иер. 29:10-14., Господь побудил Кира, царя Персии, объявить по всему своему царству и записать такой указ:

2«Так говорит Кир, царь Персии:

Господь, Бог небес, отдал мне все царства земли и поручил мне построить Ему дом в Иерусалиме, в Иудее. 3Всякий из вас, кто принадлежит к Его народу, – да будет с ним его Бог! – может отправляться в Иерусалим, в Иудею, и строить дом Господа, Бога Израиля, Бога, Который в Иерусалиме. 4И пусть жители тех мест, где сейчас живут уцелевшие иудеи, снабдят их серебром и золотом, имуществом и скотом и добровольными пожертвованиями для Божьего дома в Иерусалиме».

5И главы семейств из родов Иуды и Вениамина со священниками и левитами – всякий, кого побудил Бог, – стали собираться, чтобы пойти и отстроить дом Господа в Иерусалиме. 6Все их соседи помогли им серебряными и золотыми вещами, имуществом и скотом, и дорогими дарами, не считая всех добровольных пожертвований. 7Сам царь Кир вынес утварь дома Господа, которую Навуходоносор1:7 Царь Навуходоносор II, самый великий царь Нововавилонской империи, правил с 605 по 562 гг. до н. э. забрал из Иерусалима и положил в доме своего бога1:7 Или: «своих богов».. 8Кир, царь Персии, вверил их хранителю сокровищницы Митредату, который по счету выдал их Шешбацару, вождю Иудеи.

9Вот их опись:

золотых блюд 30;

серебряных блюд 1 000;

ножей1:9 Так в одном из древних переводов; смысл этого места в еврейском тексте неясен. 29;

10золотых чаш 30;

одинаковых серебряных чаш 410;

других предметов 1 000.

11Всего золотых и серебряных предметов было пять тысяч четыреста. Когда переселенцы отправлялись из Вавилона в Иерусалим, Шешбацар взял все это с собой.