Estere 6 – CCL & JCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Estere 6:1-14

Mordekai Apatsidwa Ulemu

1Usiku umenewo mfumu inalephera kugona tulo; Choncho inayitanitsa buku limene amalembamo mbiri ya zamakedzana kuti amuwerengere. 2Anapeza kuti mʼbukumo munalembedwa zoti Mordekai anawulula kuti Bigitana ndi Teresi, awiri mwa adindo ofulidwa a mfumu amene ankalondera pa khomo la chipinda cha mfumu ndiwo anakonza chiwembu chofuna kupha mfumu Ahasiwero.

3Mfumu inafunsa kuti, “Kodi Mordekai anamupatsa ulemu ndi ukulu wotani chifukwa cha chinthu chimene anachitachi?”

Atumiki ake anamuyankha kuti, “Palibe chimene chinachitika kwa iye.”

4Mfumu inati, “Kodi ndani ali mʼbwalomo?” Tsono Hamani anali atangolowa kumene mʼbwalo lakunja la nyumba yaufumu kuti akawuze mfumu zomukhomera Mordekai pa mtanda umene anamukonzera.

5Atumiki ake anamuyankha kuti, “Hamani ndiye wayima mu bwalo.”

“Mulowetseni,” Mfumu inalamulira.

6Hamani atalowa, mfumu inamufunsa kuti, “Kodi timuchitire ulemu otani munthu amene mfumu ikondweretsedwa naye?”

Tsono Hamani anaganiza mu mtima kuti, “Kodi palinso ndani amene mfumu ingamulemekeze kuposa ine?” 7Choncho Hamani anayankha mfumuyo kuti, “Munthu amene mfumu ifuna kumuchitira ulemu, imuchitire izi: 8Anthu abwere ndi chovala cha ufumu ndi kavalo amene mfumu imakwerapo wokhala ndi chizindikiro chaufumu pamutu pake. 9Ndipo mupereke chovala cha ufumucho ndi kavalo kwa mmodzi wa akalonga a mfumu a ulemu kwambiri. Ameneyu amuveke chovalacho munthu amene mfumu yakondweretsedwa naye. Akavekedwa chovalachi amuyendetse mʼmisewu yonse ya mzinda atakwera pa kavalo wa mfumu. Kalongayu azifuwula patsogolo pa munthuyu kuti ‘Ichi ndi chimene mfumu yachita kwa munthu amene yafuna kumuchitira ulemu!’ ”

10Mfumu inalamulira Hamani kuti, “Pita msanga, katenge chovala cha ufumu ndi kavalo ndipo uchite monga wanenera kwa Mordekai Myuda, amene amakhala pa chipata cha mfumu. Usasiyeko china chilichonse chimene wanena.”

11Choncho Hamani anatenga chovala ndi kavalo. Anamuveka Mordekai chovalacho ndipo anamuyendetsa mʼmisewu yonse ya mu mzinda atakwera pa kavalo, akufuwula kuti, “Ichi ndi chimene mfumu yachita kwa munthu amene yafuna kumuchitira ulemu!”

12Pambuyo pake Mordekai anabwerera ku chipata cha mfumu. Koma Hamani anapita msanga ku nyumba kwake, akulira, atafundira mutu wake. 13Hamani anawuza Zeresi mkazi wake ndi abwenzi ake onse zonse zinamuchitikira.

Anthu ake anzeru ndi mkazi wake Zeresi anamuwuza kuti, “Popeza kuti Mordekai ndi Myuda amene mwayamba kale kugonja pamaso pake, ndiye kuti palibe chimene mungachitepo. Mudzagwa ndithu pamaso pake.” 14Pamene anthuwa amayankhula nayebe, adindo a mfumu ofulidwa anabwera kudzamutenga Hamani mofulumira kupita naye ku phwando limene Estere anakonza.

Japanese Contemporary Bible

エステル 記 6:1-14

6

栄誉を受けるモルデカイ

1-2さてその夜のこと、王はどうしても寝つくことができませんでした。しばらく読書でもしようかと、書庫から王国の記録文書を持って来させました。読み進むうち、ある項目に目が行きました。門の警備に当たっていた役人ビグタンとテレシュが企てた、王の暗殺未遂事件のところです。計画が未然に防げたのはモルデカイの手柄だとありました。

3王は、そばにいた者に尋ねました。「このモルデカイに何かほうびを取らせたか。」「何も取らせてはおりません。」 4「誰か外庭で勤務についている者はいないか。」王がこう言った時、例の絞首台にモルデカイをつるす許可を得ようと、ハマンが城の外庭にさしかかりました。 5家来は答えました。「ハマン様がお見えです。」「ちょうどよい。ここへ呼べ。」

6ハマンが来ると、王はさっそく話を切り出しました。「ほうびを取らせたい者がいるのだが、どんな栄誉を与えたらよいものか。」ハマンは心のうちで思いました。「きっと私のことだ。私以外に、陛下が栄誉を与えたいと思う者などいるはずがないではないか。」 7-8そこで、わくわくしながら意見を述べました。「陛下ご着用の王衣、それにご愛馬と王冠をお取りそろえください。 9そして、最も身分の高い貴族の一人にその人の世話をさせてください。つまり陛下の服を着せ、ご愛馬に乗せ、くつわを取らせて通りを引いて行かせるのです。その時、その者に『陛下のお心にかなう人は、このような栄誉を受けるのだ!』と皆に聞こえるように言わせてはいかがでしょう。」 10「名案だ!」 王は思わずひざを打ちました。「大至急、王衣を持って来させ、私の馬を引いて来て、そのとおりにしてくれ。栄誉を受けるのは宮廷務めのユダヤ人モルデカイだ。今言ったことを、そっくりそのまま実行するのだ。」

11ハマンはしぶしぶモルデカイに王衣を着せ、王の愛馬に乗せ、くつわを取って通りを引き歩きながら、「王のお心にかなう人は、このような栄誉を受けるのだ!」と叫びました。 12モルデカイは勤務に戻りましたが、おさまらないのはハマンです。何とも言えないみじめな気持ちで家に逃げ帰りました。 13妻のゼレシュや取り巻きたちに事の次第を話すと、一同は頭をかかえるばかりでした。「まずいですね。モルデカイがユダヤ人だと陛下に知れた以上、あの男を亡き者にする計画は台無しです。それどころか、いつまでもモルデカイを目の敵にしていたら、かえって命取りになります。」

14皆があれこれ知恵をしぼり、善後策を講じている最中に、王の使いが来て、エステルの設けた宴へ出向くようモルデカイをせき立てました。