Estere 2 – CCL & NASV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Estere 2:1-23

Mfumu Ikwatira Estere

1Pambuyo pake mtima wa Ahasiwero utatsika, Ahasiwero anakumbukira Vasiti ndi zimene anachita Vasitiyo. Anakumbukiranso lamulo lomukhudza limene anasindikiza. 2Tsono anyamata a mfumu amene ankamutumikira anati, “Mfumu, akufunireni anamwali okongola. 3Mfumu isankhe oyangʼanira pa chigawo chilichonse cha ufumu wake kuti abwere nawo pamodzi anamwali onse okongola ku nyumba yosungira akazi ku Susa. Hegai, mdindo wofulidwa wa mfumu, amene amayangʼanira amayi, akhale wosamalira anamwaliwa ndipo aziwapatsa mafuta odzola. 4Ndipo namwali amene mfumu yakondwera naye akhale mfumukazi mʼmalo mwa Vasiti.” Mfumu inakondwera ndi uphunguwu, ndipo inachita momwemo.

5Myuda wina wa fuko la Benjamini, dzina lake Mordekai, mwana wa Yairi, mwana wa Simei, mwana wa Kisi, anali mu mzinda wa Susa. 6Iyeyu anali mmodzi mwa anthu amene anatengedwa ukapolo ndi Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni kuchokera ku Yerusalemu pamodzi ndi Yekoniya mfumu ya Yuda. 7Mordekai nʼkuti atalera Hadasa, amene ankatchedwanso Estere, mwana wamkazi wa amalume ake chifukwa analibe abambo kapena amayi. Mtsikanayu anali wokongola ndi wooneka bwino ndipo Mordekai ankamutenga ngati mwana wake weniweni pamene abambo ndi amayi ake anamwalira.

8Lamulo la mfumu atalilengeza ndi kubwera nawo pamodzi anamwali ambiri ku mzinda wa Susa kuti akasamalidwe ndi Hegai, Estere nayenso anatengedwa kupita naye ku nyumba ya mfumu kuti akasamalidwe ndi Hegai woyangʼanira nyumba yosungiramo akazi uja. 9Hegai anasangalatsidwa naye namwaliyo ndipo anamukomera mtima. Mosataya nthawi anamupatsa mafuta ake odzola ndi chakudya chapadera. Anamusankhiranso anamwali asanu ndi awiri a ku nyumba ya mfumu kuti azimutumikira, ndipo iye pamodzi ndi anamwali omutumikira aja anawapatsa malo abwino koposa mʼnyumba yosungira akazi.

10Estere sanawulule mtundu wake ndi abale ake chifukwa Mordekai anamuletsa kutero. 11Tsiku ndi tsiku Mordekai ankayendayenda pafupi ndi bwalo la nyumba yosungiramo akazi ija kuti adziwe za moyo wa Estere ndi kuti zinthu zikumuyendera bwanji.

12Tsono nthawi inkafika kuti namwali aliyense akaonekere kwa mfumu Ahasiwero, pakutha pa miyezi khumi ndi iwiri yomwe inakhazikitsidwa kuti amayi azidzikongoletsa. Pa miyezi isanu ndi umodzi ankadzola mafuta a mure ndipo pa miyezi isanu ndi umodzi inayo ankadzola zonunkhira ndi zokongoletsa. 13Ndipo namwali ankapita kwa mfumu motere: Ankaloledwa kutenga chilichonse angafune mʼnyumba yosungiramo akazi kupita nacho ku nyumba ya mfumu. 14Ankalowa madzulo kwa mfumu ndi kutuluka mmawa kupita ku nyumba ina yosungira akazi yomwe ankayangʼanira ndi Saasigazi, mdindo wofulidwa wa mfumu amene amayangʼanira akazi a mfumu. Namwali sankabwerera kwa mfumu pokhapokha amukomere mtima ndi kumuyitana potchula dzina lake.

15Tsono inafika nthawi kuti Estere, mwana wamkazi wa Abihaili amenenso analeredwa ndi Mordekai amalume ake, alowe kwa mfumu. Iye sanapemphe kanthu kalikonse, koma anatenga zokhazo zimene ananena Hegai mdindo wofulidwa wa mfumu woyangʼanira nyumba yosungiramo akazi. Ndipo aliyense amene anamuona Estere, anasangalatsidwa naye. 16Anapita naye kwa mfumu Ahasiwero ku nyumba ya ufumu pa mwezi wa khumi, mwezi wa Tebete, chaka cha chisanu ndi chiwiri cha ufumu wake.

17Ndipo mfumu inamukonda Estere koposa wina aliyense wa akazi aja, kotero inamukonda ndi kumukomera mtima koposa wina aliyense wa anamwali aja. Choncho anamumveka chipewa chaufumu pa mutu pake nakhala mfumukazi mʼmalo mwa Vasiti. 18Ndipo mfumu inakonza phwando lalikulu, phwando la Estere, kukonzera anthu olemekezeka ndi nduna zake zonse. Analamuliranso kuti anthu mʼzigawo zonse asapereke msonkho ndipo anapereka mphatso monga mwakukoma mtima kwa mfumu.

Mordekai Awulula Chiwembu

19Anamwali atasonkhanitsidwa pamodzi, Mordekai anakhala pansi pa chipata cha mfumu. 20Koma Estere anali asanawululebe za mtundu wake ndi anthu a pa banja lake monga momwe analamulira Mordekai, chifukwa anapitirira kutsata malangizo a Mordekai monga ankachitira pamene ankamulera.

21Pa nthawi imene Mordekai ankalondera pa chipata cha mfumu, Bigitana ndi Teresi, awiri mwa adindo ofulidwa amfumu, olondera pa khomo la nyumba yake, anayipidwa mtima ndipo anakonza chiwembu chofuna kupha mfumu Ahasiwero. 22Koma Mordekai atazindikira za chiwembuchi anawuza mfumukazi Estere ndipo iye anakawuza mfumu mʼmalo mwa Mordekai. 23Ndipo pamene anafufuza za chiwembuchi kuti zinali zoona, adindo awiriwa anaphedwa monyongedwa. Zinthu izi zinalembedwa mʼbuku la Mbiri ndi kusungidwa ndi Mfumu.

New Amharic Standard Version

አስቴር 2:1-23

አስቴር ንግሥት ሆነች

1ከዚህ በኋላ ንጉሡ ጠረክሲስ ቍጣው ሲበርድለት አስጢንን፣ ያደረገችውን ነገርና በእርሷም ላይ ያስተላለፈውን ዐዋጅ ዐሰበ። 2ከዚያም የንጉሡ የቅርብ አገልጋዮች እንዲህ የሚል ሐሳብ አቀረቡ፤ “ለንጉሡ ቈንጆ ልጃገረዶች ይፈለጉለት፤ 3እነዚህን ሁሉ ቈንጆ ልጃገረዶች በሱሳ ግንብ ወደሚገኘው ልዩ የሴቶች መኖሪያ ቦታ እንዲያመጡ፣ ንጉሡ በግዛቱ በሚገኙት አውራጃዎቹ ሁሉ ባለ ሥልጣኖችን ይሹም፤ እነርሱም የሴቶች የበላይ ኀላፊ በሆነው በንጉሡ ጃንደረባ በሄጌ ኀላፊነት ሥር ይሁኑ፤ የውበትም እንክብካቤ ይደረግላቸው። 4ከዚያም ንጉሡን ደስ የምታሰኘው ልጃገረድ በአስጢን ፈንታ ንግሥት ትሁን።” ምክሩ ንጉሡን ደስ አሰኘው፤ በተባለውም መሠረት አደረገ።

5በዚህ ጊዜ ከብንያም ነገድ የቂስ ልጅ፣ የሰሜኢ ልጅ፣ የኢያዕር ልጅ መርዶክዮስ የሚባል አንድ አይሁዳዊ በሱሳ ግንብ ይኖር ነበር፤ 6እርሱም የባቢሎን ንጉሥ ናቡከደነፆር ከማረካቸው ከይሁዳ ንጉሥ ከኢኮንያን2፥6 በዕብራይስጥ፣ ኢኮንያን የሚለው ስም ኢዮአቄም ከሚለው ጋር አንድ ዐይነት ነው። ጋር ከኢየሩሳሌም በምርኮ ከተወሰዱት አንዱ ነበር። 7መርዶክዮስ አንዲት ሀደሳ የምትባል የአጎቱ ልጅ ነበረችው፤ አባትና እናት ስላልነበራት፣ ያሳደጋት እርሱ ነበር። አስቴር ተብላ የምትጠራው ይህች ልጃገረድ በተክለ ሰውነቷም ሆነ በመልኳ እጅግ ውብ ነበረች። አባቷና እናቷ ከሞቱ በኋላ መርዶክዮስ እንደ ራሱ ልጅ አድርጎ ወሰዳት።

8የንጉሡ ትእዛዝና ዐዋጅ በወጣ ጊዜ፣ ብዙ ልጃገረዶች ወደ ሱሳ ግንብ ተወስደው ለጠባቂው ለሄጌ ተሰጡ፤ አስቴርም ወደ ንጉሡ ቤተ መንግሥት ተወስዳ፣ ለሴቶቹ ጠባቂ ለሄጌ በዐደራ ተሰጠች። 9ልጃገረዲቱም ደስ አሰኘችው፤ በእርሱም ዘንድ መወደድን አተረፈች፤ እርሱም የውበት መንከባከቢያዋንና የተለየ ምግብ ወዲያውኑ ሰጣት። ከቤተ መንግሥቱ የተመረጡ ሰባት ደንገጡሮችን በመመደብም እርሷንና ደንገጡሮቿን ምርጥ ወደ ሆነው የሴቶች መጠበቂያ አዛወረ።

10መርዶክዮስ እንዳትናገር አዝዟት ስለ ነበር፣ አስቴር የየት አገር ሰውና የእነማን ወገን እንደ ሆነች አልገለጸችም። 11መርዶክዮስም አስቴር እንዴት እንደ ሆነችና ምንስ እንዳጋጠማት ለማወቅ፣ በየዕለቱ በሴቶች መጠበቂያ አደባባይ አጠገብ ወዲያና ወዲህ ይመላለስ ነበር።

12አንዲት ልጃገረድ ወደ ንጉሥ ጠረክሲስ ዘንድ ለመግባት ተራዋ ከመድረሱ በፊት ስድስት ወር በከርቤ ዘይት፣ ስድስት ወር ደግሞ ልዩ ልዩ ሽቱ በመቀባትና በተለያዩ የፊት ቀለሞች በመዋብ በአጠቃላይ ዐሥራ ሁለት ወር መቈየት ነበረባት፤ 13ወደ ንጉሡ ዘንድ የምትገባውም በዚህ ሁኔታ ሲሆን፣ ሴቶቹ ከሚኖሩበት ስፍራ ወደ ንጉሡ ቤተ መንግሥት ስትሄድ፣ መውሰድ የምትፈልገው ማናቸውም ነገር ይሰጣት ነበር። 14ሲመሽ ወደዚያው ትሄዳለች፤ ሲነጋም የቁባቶች ኀላፊ በሆነው በንጉሡ ጃንደረባ በሻአሽጋዝ ጥበቃ ሥር ወደሚገኘው ወደ ሌላው የሴቶች መጠበቂያ ቤት ትመለሳለች፤ ደስ የተሰኘባት ካልሆነችና በስሟም ካልጠራት ዳግመኛ ወደ ንጉሡ ዘንድ አትገባም።

15መርዶክዮስ እንደ ልጁ አድርጎ ያሳደጋት የአጎቱ የአቢካኢል ልጅ አስቴር ወደ ንጉሡ ዘንድ የምትሄድበት ተራ በደረሰ ጊዜ የሴቶች ልዩ ጥበቃ ቤት ኀላፊ የሆነው ሄጌ የነገራትን እንጂ፣ ሌላ ምንም አልጠየቀችም። አስቴር በሚያዩዋት ሁሉ ዘንድ ሞገስ አገኘች። 16በነገሠ በሰባተኛው ዓመት ቴቤት በተባለው በዐሥረኛው ወር ወደ ንጉሥ ጠረክሲስ ቤተ መንግሥት ተወሰደች።

17በዚህ ጊዜ ንጉሡ ከሌሎቹ ሴቶች ሁሉ ይበልጥ አስቴርን ወደዳት፤ ከሌሎቹ ደናግልም ሁሉ ይልቅ በእርሱ ዘንድ ሞገስንና መወደድን አገኘች። ስለዚህ የእቴጌነት ዘውድ በራሷ ላይ ጫነላት፤ በአስጢንም ፈንታ ንግሥት አደረጋት። 18ንጉሡም ስለ አስቴር ክብር ለመኳንንቱና ለሹማምቱ ሁሉ ታላቅ ግብዣ አደረገ፤ በዓሉም በየአውራጃዎቹ ሁሉ እንዲከበር ዐወጀ፤ በንጉሣዊ ልግስናውም ስጦታ አደረገ።

መርዶክዮስ በንጉሡ ላይ የተጠነሰሰውን ሤራ ደረሰበት

19ደናግሉ ለሁለተኛ ጊዜ ተሰብስበው ሳለ፣ መርዶክዮስ በንጉሡ በር ተቀምጦ ነበር። 20አስቴር ግን ልክ መርዶክዮስ እንደ ነገራት የማን ወገንና የየት አገር ሰው እንደ ሆነች ደብቃ ነበር፤ ይህ የሆነበት ምክንያት መርዶክዮስ በሚያሳድጋት ጊዜ ታደርግ እንደ ነበረው ሁሉ፣ አሁንም ምክሩን ትከተል ስለ ነበር ነው።

21መርዶክዮስ በንጉሡ በር ተቀምጦ ሳለ፣ በሩን ከሚጠብቁት ከንጉሡ የጦር አለቆች ሁለቱ ገበታና ታራ ተቈጡ፤ ንጉሥ ጠረክሲስንም ለመግደል ዶለቱ። 22መርዶክዮስም አድማውን ስለ ደረሰበት፣ ለንግሥት አስቴር ገለጠላት፤ እርሷም ይህን ከመርዶክዮስ ማግኘቷን ለንጉሡ ገልጣ ነገረችው። 23ነገሩ ሲጣራም እውነት ሆኖ ተገኘ፤ ሁለቱም ሹማምት በስቅላት ሞት ተቀጡ። ይህ ሁሉ በንጉሡ ፊት በታሪክ መዝገብ ተጻፈ።