Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Estere 1:1-22

Vasiti Mkazi wa Mfumu Achotsedwa

1Izi ndi zimene zinachitika pa nthawi ya ufumu wa Ahasiwero, amene analamulira zigawo 127 kuyambira ku India mpaka ku Kusi. 2Pa nthawi imeneyi nʼkuti mfumu Ahasiwero atakhazikika pa mpando wake wa ufumu mu mzinda wa Susa, 3ndipo mʼchaka chachitatu cha ufumu wake anakonza phwando la olemekezeka ndi nduna zake. Atsogoleri a nkhondo a ku Peresiya ndi Mediya, anthu olemekezeka pamodzi ndi nduna za mʼzigawo zonse anasonkhana kwa iye.

4Pa nthawi yomweyi kwa masiku 180 a phwando mfumu inkaonetsa kulemera kwa ulemerero wa ufumu wake ndiponso kukongola ndi kukula kwa ufumu wake. 5Atatha masiku amenewa, kwa masiku ena asanu ndi awiri mfumu inakonzanso phwando la anthu onse okhala mu mzinda wa Susa kuyambira anthu olemekezeka mpaka anthu wamba ku bwalo la munda la nyumba yake yaufumu. 6Bwalo la mundali analikongoletsa ndi makatani a nsalu zoyera ndi za mtundu wamtambo zimene anazimangirira ndi zingwe za nsalu zoyera ndi zapepo ku mphete za siliva zimene anazikoloweka pa nsanamira za maburo. Anayika mipando yopumirapo yagolide ndi siliva pabwalo la miyala yoyala yamtengowapatali yofiira, ya marabulo, ndi yonyezimira. 7Anapereka zakumwa mʼchikho zagolide zamitundumitundu, ndipo vinyo waufumu anali wochuluka kwambiri monga mwa kukoma mtima kwa mfumu. 8Monga mwa lamulo la mfumu aliyense anamwa mʼmene anafunira, pakuti mfumu inawuza otumikira ake kuti apatse aliyense monga mwa kukonda kwake.

9Mkazi wa mfumu Vasiti nayenso anakonzera phwando amayi ku nyumba ya ufumu ya mfumu Ahasiwero.

10Pa tsiku la chisanu ndi chiwiri, pamene mfumu Ahasiwero inaledzera ndi vinyo, inalamula adindo ofulidwa asanu ndi awiri amene ankamutumikira: Mehumani, Bizita, Haribona, Bigita, Abagita, Zetara, ndi Karikasi 11kuti abwere naye mfumukazi Vasiti pamaso pa mfumu atavala chipewa chaufumu. Cholinga cha mfumu chinali choti adzamuonetse kwa anthu onse ndi olemekezeka, chifukwa anali wokongola kwambiri. 12Koma antchito atapereka uthenga wa mfumu kwa mfumukazi, Vasiti anakana kubwera. Tsono mfumu inakwiya ndi kupsa mtima.

13Mfumu inayankhula ndi anthu anzeru ndi ozindikira choyenera kuchita popeza chinali chikhalidwe chake kufunsa uphungu kwa akatswiri pa nkhani za malamulo ndi kuweruza kolungama. 14Anthu amene ankakhala pafupi ndi mfumu anali awa: Karisena, Setara, Adimata, Tarisisi, Meresi, Marisena ndi Memukani, olemekezeka asanu ndi awiri a ku Peresiya ndi Medina amene ankaloledwa mwapadera kuonana ndi mfumu ndipo anali pamwamba kwambiri mu ufumuwo.

15Mfumu inafunsa kuti, “Kodi titani naye mfumukazi Vasiti mwa lamulo, popeza sanamvere lamulo la ine mfumu Ahasiwero limene adindo ofulidwa anakamuwuza?”

16Ndipo Memukani anayankha pa maso pa mfumu ndi olemekezeka anzake kuti, “Mfumukazi Vasiti sanalakwire mfumu yokha, koma walakwiranso olemekezeka onse ndi anthu onse okhala mʼzigawo zonse za mfumu Ahasiwero. 17Pakuti amayi onse adzadziwa zimene wachita mfumukazi ndipo kotero adzapeputsa amuna awo ndi kunena kuti, ‘Mfumu Ahasiwero analamulira kuti abwere naye mfumukazi Vasiti kwa iye koma sanapite.’ 18Lero lomwe lino amayi olemekezeka a ku Peresiya ndi Mediya amene amva zimene wachita mfumukazi adzaganiza zochita chimodzimodzi kwa nduna zonse za mfumu. Ndipo kupeputsana ndi kukongola zidzapitirira.”

19“Choncho, ngati chikukomerani mfumu, lamulirani kuti Vasiti asadzaonekerenso pamaso pa mfumu Ahasiwero. Lamuloli lilembedwe mʼmabuku a malamulo a Aperezi ndi Amedi kuti lisadzasinthike. Pamalo pa Vasiti ngati mfumukazi payikidwepo mkazi wina amene ali bwino kuposa iye. 20Ndipo lamulo la mfumuli lilengezedwa mʼdziko lake lonse ngakhale lili lalikulu, amayi onse adzapereka ulemu kwa amuna awo, amuna olemekezeka mpaka amuna wamba.”

21Mfumu ndi nduna zake anakondwera ndi uphungu uwu, kotero mfumu inachita monga momwe ananenera Memukani. 22Mfumu inatumiza makalata ku madera onse a ufumu wake, chigawo chilichonse mʼzilembo zawo ndi ku mtundu uliwonse mʼchiyankhulo chawochawo kulengeza kuti mwamuna ayankhule chilichonse chimene chikumukomera.

Persian Contemporary Bible

استر 1:1‏-22

ملكه وشتی بركنار می‌شود

1‏-3خشايارشا، پادشاه پارس، بر سرزمين پهناوری سلطنت می‌كرد كه از هند تا حبشه را در بر می‌گرفت و شامل ۱۲۷ استان بود.

او در سال سوم سلطنت خود، در كاخ سلطنتی شوش جشن بزرگی بر پا نمود و تمام بزرگان و مقامات مملكتی را دعوت كرد. فرماندهان لشكر پارس و ماد همراه با اميران و استانداران در اين جشن حضور داشتند. 4در طی اين جشن كه شش ماه طول كشيد، خشايارشا تمام ثروت و شكوه و عظمت سلطنت خود را به نمايش گذاشت.

5پس از پايان جشن، خشايارشا برای تمام كسانی كه در شوش زندگی می‌كردند، فقير و غنی، ميهمانی هفت روزه‌ای در باغ كاخ سلطنتی ترتيب داد. 6محل ميهمانی با پرده‌هايی از كتان سفيد و آبی تزيين شده بود. اين پرده‌ها با ريسمانهای سفيد و ارغوانی كه داخل حلقه‌های نقره‌ای قرار داشتند از ستونهای مرمر آويزان بود. تختهای طلا و نقره روی سنگفرشهايی از سنگ سماک، مرمر، صدف مرواريد و فيروزه قرار داشت. 7از كرم پادشاه، شراب شاهانه فراوان بود و در جامهای طلايی كه شكلهای گوناگون داشت، صرف می‌شد. 8پادشاه به پيشخدمتهای دربار دستور داده بود ميهمانان را در نوشيدن آزاد بگذارند، پس ايشان به دلخواه خود، هر قدر كه می‌خواستند شراب می‌نوشيدند.

9در همان هنگام، ملكه وشتی هم برای زنان دربار ضيافتی ترتيب داده بود.

10در آخرين روز ميهمانی، پادشاه كه از باده‌نوشی سرمست شده بود، هفت خواجهٔ حرمسرا يعنی مهومان، بزتا، حربونا، بغتا، ابغتا، زاتر و كركس را كه خادمان مخصوص او بودند احضار كرد. 11او به آنان دستور داد ملكه وشتی را كه بسيار زيبا بود با تاج ملوكانه به حضورش بياورند تا زيبايی او را به مقامات و مهمانانش نشان دهد. 12اما وقتی خواجه‌سرایان فرمان پادشاه را به ملكه وشتی رساندند، او از آمدن سرباز زد. پادشاه از اين موضوع بسيار خشمناک شد؛ 13‏-14اما پيش از آنكه اقدامی كند، اول از مشاوران خود نظر خواست، چون بدون مشورت با آنها كاری انجام نمی‌داد. مشاوران او مردانی دانا و آشنا به قوانين و نظام دادگستری پارس بودند و پادشاه به قضاوت آنها اعتماد داشت. نام اين دانشمندان كرشنا، شيتار، ادماتا، ترشيش، مرس، مرسنا و مموكان بود. اين هفت نفر جزو مقامات عالی رتبهٔ پارس و ماد و از اميران ارشد مملكتی بودند. 15خشايارشا از ايشان پرسيد: «در مورد ملكه وشتی چه بايد كرد؟ زيرا از فرمان پادشاه كه به او ابلاغ شده، سر باز زده است. قانون چه مجازاتی برای چنين شخصی تعيين كرده است؟»

16مموكان خطاب به پادشاه و اميران دربار گفت: «ملكه وشتی نه فقط به پادشاه بلكه به اميران دربار و تمام مردم مملكت اهانت كرده است. 17هر زنی كه بشنود ملكه وشتی چه كرده است، او نيز از دستور شوهرش سرپيچی خواهد كرد. 18وقتی زنانِ اميرانِ دربارِ پارس و ماد بشنوند كه ملكه چه كرده، آنان نيز با شوهرانشان چنين خواهند كرد و اين بی‌احترامی و سركشی به همه جا گسترش خواهد يافت. 19بنابراين، اگر پادشاه صلاح بدانند، فرمانی صادر كنند تا در قوانين ماد و پارس كه هرگز تغيير نمی‌كند ثبت گردد و بر طبق آن فرمان، ملكه وشتی ديگر به حضور پادشاه شرفياب نشود. آنگاه زن ديگری كه بهتر از او باشد به جای وی به عنوان ملكه انتخاب شود. 20وقتی اين فرمان در سراسر اين سرزمين پهناور اعلام شود آنگاه در همه جا شوهران، هر مقامی كه داشته باشند، مورد احترام زنانشان قرار خواهند گرفت.»

21پيشنهاد مموكان مورد پسند پادشاه و اميران دربار واقع شد و خشايارشا مطابق صلاحديد او عمل كرد 22و به تمام استانها، هر يک به خط و زبان محلی، نامه فرستاده، اعلام داشت كه هر مرد بايد رئيس خانهٔ خود باشد.