Eksodo 40 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Eksodo 40:1-38

Adzutsa Chihema

1Kenaka Yehova anati kwa Mose, 2“Imika chihema, tenti ya msonkhano, tsiku loyamba la mwezi. 3Uyikemo bokosi la umboni ndipo uphimbe bokosilo ndi katani. 4Ulowetsemo tebulo ndi kuyika zimene zimakhala pamenepo. Kenaka ulowetse choyikapo nyale ndipo uyikepo nyale zake. 5Uyike guwa lofukiza la golide patsogolo pa bokosi la umboni ndipo uyike katani ya pa chipata cha chihema.

6“Uyike guwa lansembe yopsereza patsogolo pa chipata cha chihema, tenti ya msonkhano. 7Uyike beseni pakati pa tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe ndipo uyikemo madzi. 8Upange bwalo lozungulira chihemacho ndipo uyike katani ya pa chipata cha bwalolo.

9“Utenge mafuta wodzozera ndipo udzoze chihema ndi chilichonse chili mʼmenemo ndipo zidzakhala zoyeretsedwa. 10Kenaka udzoze guwa lansembe lopsereza ndi ziwiya zake zonse. Ulipatule guwalo ndipo lidzakhala loyera kwambiri. 11Udzoze beseni ndi miyendo yake ndipo uzipatule.

12“Ubwere ndi Aaroni ndi ana ake pa chipata cha tenti ya msonkhano ndipo uwasambitse ndi madzi. 13Kenaka umuveke Aaroni zovala zopatulika, umudzoze ndi kumupatula kotero kuti athe kunditumikira monga wansembe. 14Ubweretse ana ake ndipo uwaveke minjiro. 15Uwadzoze monga momwe unadzozera abambo awo, kotero kuti anditumikire monga ansembe. Kudzozedwako kudzakhala unsembe wawo pa mibado ndi mibado” 16Mose anachita zonse monga Yehova anamulamulira.

17Kotero anayimika chihema tsiku loyamba la mwezi woyamba mʼchaka chachiwiri. 18Nthawi imene Mose anayimika chihema, anayika matsinde mʼmalo ake, kuyimitsa maferemu, kulowetsa mitanda ndi kuyika nsichi. 19Kenaka anayika tenti pamwamba pa chihema ndipo anayika chophimba pa tenti monga momwe Yehova analamulira Mose.

20Iye anatenga miyala ya umboni nayika mʼbokosi lija ndi kuyika chivundikiro pamwamba pake. 21Kenaka analowetsa bokosilo mʼchihema ndipo anapachika katani ndi kubisa bokosi la umboni monga momwe Yehova analamulira iye.

22Mose anayika tebulo mu tenti ya msonkhano kumpoto kwa chihema, kunja kwa katani, 23ndipo anayikapo buledi pamaso pa Yehova, monga momwe Yehova analamulira Mose.

24Iye anayikanso choyikapo nyale mu tenti ya msonkhano moyangʼanana ndi tebulo mbali yakummwera kwa chihema. 25Ndipo anayikapo nyale zija pamaso pa Yehova, monga Yehova analamulira Mose.

26Mose anayika guwa la golide mu tenti ya msonkhano patsogolo pa katani 27ndipo anapserezapo lubani wonunkhira monga Yehova anamulamulira. 28Kenaka anayika katani ya pa chipata cha chihema.

29Iye anayika guwa lansembe yopsereza pafupi ndi chipata cha chihema, tenti ya msonkhano, ndipo anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe ya ufa monga Yehova anamulamulira.

30Iye anayika beseni pakati pa tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe ndipo anathiramo madzi wosamba, 31ndipo Mose, Aaroni ndi ana ake amasamba manja ndi mapazi awo. 32Iwo amasamba nthawi zonse akamalowa mu tenti ya msonkhano kapena kuyandikira guwa lansembe monga Yehova analamulira Mose.

33Kenaka Mose anamanga bwalo kuzungulira chihema ndi guwa lansembe ndipo anayika katani ya pa chipata cha bwalo. Kotero Mose anamaliza ntchito.

Ulemerero wa Yehova

34Kenaka mtambo unaphimba tenti ya msonkhano, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza mʼchihemacho. 35Mose sanathe kulowa mu tenti ya msonkhano chifukwa mtambo unali utakhazikika pa chihemacho, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza mʼchihemacho.

36Pa maulendo awo onse, mtambo ukachoka pamwamba pa chihema, Aisraeli ankasamukanso pamene analipo. 37Koma ngati mtambo sunachoke, iwo sankasamukanso mpaka tsiku limene udzachoke. 38Kotero mtambo wa Yehova unkakhala pamwamba pa chihema usana, ndi mtambo wamoto umakhala usiku, pamaso pa nyumba yonse ya Israeli pa masiku onse aulendo wawo.