Eksodo 11 – CCL & BDS

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Eksodo 11:1-10

Mliri wa Imfa ya Ana Oyamba Kubadwa

1Tsopano Yehova anati kwa Mose, “Ine ndidzalanga Farao pamodzi ndi Aigupto onse ndi mliri umodzi wotsiriza. Zikadzachitika izi iye adzakulolani kuti mutuluke mʼdziko lino. Ndithu pamene azidzakutulutsani adzachita ngati akukuyingitsani. 2Awuze anthu kuti mwamuna aliyense ndi mkazi aliyense apemphe kwa mnansi wake ziwiya zasiliva ndi golide.” 3Tsono Yehova anachititsa Aigupto kuti akomere mtima Aisraeli. Komanso Mose anali wotchuka kwambiri mʼdziko la Igupto, pamaso pa nduna za Farao ndi anthu onse.

4Tsono Mose anawuza Farao kuti, “Pakati pa usiku, Yehova adzayenda pakati pa anthu a ku Igupto. 5Ndipo mwana aliyense wamwamuna wachisamba adzafa, kuyambira mwana wamwamuna wa Farao amene amakhala pa mpando waufumu, mpaka mwana wamwamuna wachisamba wa mdzakazi wake amene ali naye pa mtondo, komanso ana oyamba a ziweto. 6Kudzakhala kulira kwakukulu mʼdziko lonse la Igupto, kumene sikunachitikepo ndipo sikudzachitikanso. 7Koma pakati pa Aisraeli, ngakhale galu sadzawuwa munthu aliyense kapena chiweto!” Kotero mudzadziwa kuti Yehova ndiye wasiyanitsa pakati pa Igupto ndi Israeli. 8Nduna zanu zonse zidzabwera kwa ine, kugwada pamaso panga ndi kunena kuti, “Pita iwe ndi anthu ako onse amene akukutsatirawa! Zimenezi zikadzachitika ine ndidzachoka.” Ndipo Mose anachoka kwa Farao atakwiya kwambiri.

9Yehova ananena kwa Mose kuti, “Farao adzakana kukumvera, kuti zodabwitsa zanga zichuluke mʼdziko la Igupto.” 10Mose ndi Aaroni anachita zodabwitsa zonsezi pamaso pa Farao koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao, ndipo sanalole kuti Aisraeli atuluke mʼdziko lake.

La Bible du Semeur

Exode 11:1-10

La Pâque

L’annonce du dernier fléau

1L’Eternel dit à Moïse : Je vais encore faire venir un fléau pour frapper le pharaon et l’Egypte. Après cela, il vous laissera partir d’ici ; et même, il vous chassera définitivement de son pays. 2Va donc parler au peuple : que chacun demande à son voisin, et chacune à sa voisine, des objets d’or et d’argent.

3L’Eternel fit gagner au peuple la faveur des Egyptiens, Moïse lui-même était un personnage très respecté par les hauts fonctionnaires du pharaon et par la population.

4Moïse dit au pharaon : Voici ce que l’Eternel déclare : « Au milieu de la nuit, j’irai et je parcourrai l’Egypte 5et tout fils aîné11.5 Au Moyen-Orient l’avenir de la famille reposait sur le fils aîné. Un jugement frappant les premiers-nés touchait toute la communauté. dans ce pays mourra, depuis le fils aîné du pharaon qui est sur le trône jusqu’à celui de la servante qui fait tourner la meule, ainsi que tout premier-né du bétail. 6De grands cris s’élèveront dans tout le pays comme il n’y en a jamais eu et comme il n’y en aura plus de semblable. 7Mais chez les Israélites, on n’entendra pas même un chien aboyer contre un homme ou une bête. Vous saurez ainsi que l’Eternel fait une distinction entre l’Egypte et Israël. 8Alors tous tes hauts fonctionnaires qui t’entourent viendront me trouver et se jetteront à mes pieds en suppliant : “Va-t’en, toi et tout le peuple qui marche à ta suite.” Après cela, oui, je partirai. »

Moïse sortit alors de chez le pharaon dans une grande colère.

9L’Eternel lui avait dit : Le pharaon ne vous écoutera pas, afin que mes prodiges se multiplient en Egypte.

10Moïse et Aaron accomplirent donc tous ces prodiges en présence du pharaon. Mais l’Eternel rendit son cœur obstiné, de sorte qu’il ne laissa pas les Israélites quitter son pays.