Deuteronomo 30 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 30:1-20

Madalitso Akabwerera kwa Yehova

1Madalitso ndi matemberero awa onse amene ndawayika pamaso panu akadzafika pa inu, inu nʼkukumbukira kulikonse kumene Yehova Mulungu wanu wakubalalitsirani pakati pa mitundu ya anthu, 2ndipo inu pamodzi ndi ana anu nʼkudzatembenukira kwa Yehova Mulungu wanu ndi kumumvera ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse molingana ndi chilichonse chimene ndakulamulani lero lino, 3pamenepo Yehova Mulungu wanu adzakukhalitsani monga kale ndi kukuchitirani chifundo, ndipo adzakusonkhanitsani kukuchotsani ku mitundu ina ya anthu kumene anakubalalitsirani. 4Ngakhale atakupirikitsirani ku malekezero a dziko lapansi, adzakusonkhanitsani kuchokera kumeneko ndi kukubweretsaninso. 5Adzakubweretsani ku dziko limene linali la makolo anu, ndipo lidzakhala lanu. Iye adzakulemeretsani ndi kukuchulukitsani kupambana makolo anu. 6Yehova Mulungu wanu adzasintha mitima yanu pamodzi ndi mitima ya zidzukulu zanu, kotero kuti mudzamukonda ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, ndipo mudzakhala ndi moyo. 7Yehova Mulungu wanu adzayika matemberero awa onse pa adani anu amene amadana nanu ndi kukuzunzani. 8Inu mudzamveranso Yehova ndi kutsatira malamulo ake onse amene ndikukupatsani lero lino. 9Pamenepo Yehova Mulungu wanu adzakulemeretsani pa zochita zanu zonse ndipo adzakupatsani ana ambiri, zoweta zambiri, ndiponso mudzakhala ndi zokolola zambiri za mʼdziko lanu. Yehova adzakondwera nanunso ndi kukulemeretsani monga momwe anakondwera ndi makolo anu, 10ngati mudzamvera Yehova Mulungu wanu ndi kusunga malamulo ake ndi mawu ake amene alembedwa Mʼbuku ili la Malamulo ndi kutembenukira kwa Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.

Moyo kapena Imfa

11Tsopano zimene ndikukulamulirani leroli sizovuta kapena zapatali. 12Sizili kumwamba, kuti muzichita kufunsa kuti, “Kodi ndani amene akwere kumwamba kuti akazitenge ndi kudzatilalikira kuti timvere?” 13Komanso sizili pa tsidya la nyanja, kuti muzichita kufunsa kuti, “Kodi ndani amene adzawoloke nyanja kuti akatenge ndi kudzatilalikira kuti timvere?” 14Ayi, mawu ali pafupi ndi inu; ali mʼkamwa mwanu ndi mu mtima mwanu kuti muwamvere.

15Taonani, lero ine ndayika pamaso panu moyo ndi zokoma, imfa ndi chiwonongeko. 16Pakuti lero ndikukulamulani kuti mukonde Yehova Mulungu wanu, kuti muyende mʼnjira zake, ndi kusunga malamulo ake, malangizo ake. Mukatero mudzakhala ndi moyo ndi kuchulukana, ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mʼdziko limene mukulowa kukakhalamo.

17Koma ngati mtima wanu udzatembenuka, inu nʼkukhala osandimvera, ndipo ngati mudzatengeka ndi kupita kukagwadira milungu ina ndi kuyipembedza, 18lero ndikulengeza kwa inu kuti mudzawonongeka ndithu. Simudzakhala nthawi yayitali mʼdziko limene mukulowamo pamene mukuwoloka Yorodani kuti mulitenge.

19Lero kumwamba ndi dziko lapansi zikhale mboni zodzakutsutsani pakuti ndayika pamaso panu moyo ndi imfa, madalitso ndi matemberero. Tsopano sankhani moyo kuti inu ndi ana anu mukhale ndi moyo. 20Ndi kuti mukonde Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake, ndi kukhulupirika kwa Iye. Pakuti Yehova ndiye moyo wanu, ndipo mudzakhala zaka zambiri mʼdziko limene analumbira kulipereka kwa makolo anu, Abrahamu, Isake ndi Yakobo.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

申命記 30:1-20

歸向耶和華必蒙福

1「當我向你們陳明的這些祝福和咒詛都應驗在你們身上時,如果你們在你們的上帝耶和華驅逐你們去的各國中回想這些話, 2歸向你們的上帝耶和華,你們及子孫照我今天的吩咐全心全意地聽從祂的話, 3祂必改變你們被擄的境遇,憐憫你們,把你們從祂驅逐你們去的列國招聚回來。 4即使你們被驅逐到天涯,你們的上帝耶和華也會把你們帶回來, 5帶到你們祖先的土地上,使你們擁有那片土地,比你們祖先更加人丁興旺、繁榮昌盛。 6你們的上帝耶和華要潔淨你們和你們子孫的心,好讓你們全心全意地愛祂,並且存活。 7你們的上帝耶和華要把所有的咒詛加在你們的仇敵及憎惡你們、迫害你們的人身上。 8你們必再次聽從耶和華,遵行今天祂藉我吩咐你們的一切誡命。 9-10倘若你們聽從你們的上帝耶和華的話,遵守這律法書上的誡命和律例,全心全意地歸向祂,祂必使你們凡事蒙福、兒女眾多、牛羊成群、五穀豐登。因為祂必樂意再次賜福你們,像從前賜福你們祖先一樣。

生死抉擇

11「我今天頒佈給你們的誡命,對你們來說不難遵行,也非遙不可及。 12這誡命並非在天上,以致你們說,『誰替我們上天取下來,講給我們聽,讓我們遵行呢?』 13這誡命也不在海的彼岸,以致你們說,『誰替我們過海取來,講給我們聽,好讓我們遵行呢?』 14這誡命近在咫尺,就在你口裡,在你心中,好讓你們遵行。

15「看啊,今天我把生死禍福擺在你們面前。 16我今天吩咐你們要愛你們的上帝耶和華,遵行祂的旨意,遵守祂的誡命、律例和典章,以便你們可以存活,人口興旺,在你們將要佔領的土地上蒙祂賜福。 17但倘若你們心中偏離,不肯聽從,被引誘去祭拜、供奉別的神明, 18我今天警告你們,你們必定滅亡,在約旦河對岸——你們將要佔領的土地上無法長久。 19今天,我叫天地為你們作證,我已把生死禍福擺在你們面前。選擇生命吧,以便你們及子孫可以存活。 20要愛你們的上帝耶和華,聽從祂的話,倚靠祂,因為祂是你們的生命,祂必使你們長久住在祂起誓賜給你們祖先亞伯拉罕以撒雅各的土地上。」