Deuteronomo 18 – CCL & NASV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 18:1-22

Zopereka za kwa Ansembe ndi Alevi

1Ansembe Achilevi amene ndi fuko lonse la Alevi, asapatsidwe malo kapena cholowa pakati pa Aisraeli. Iwowa azidzadya zoperekedwa kwa Yehova ngati nsembe, popeza zimenezo ndiye cholowa chawo. 2Iwowa sadzakhala ndi cholowa pakati pa abale awo pakuti Yehova ndiye cholowa chawo monga anawalonjezera.

3Anthu amene abwera kudzapereka nsembe ya ngʼombe kapena nkhosa, azipereka kwa wansembe gawo lake motere: mwendo wakutsogolo, nyama yamʼmasaya ndi zamʼkati. 4Muziwapatsa zamasika zoyamba za tirigu wanu, vinyo watsopano ndi mafuta, ndi ubweya woyamba pometa nkhosa zanu, 5pakuti Yehova Mulungu wanu wawasankha iwowa ndi ana awo pakati pa mafuko anu onse kuti aziyimirira ndi kutumikira mʼdzina la Yehova nthawi zonse.

6Ngati Mlevi asuntha achoka ku mzinda wake ndi kupita kumalo kwina kumene Yehova wasankha mu Israeli momwemo ndi mtima wake wonse, 7kumeneko akhoza kukatumikirako mʼdzina la Yehova Mulungu wake monga Alevi anzake onse amene akutumikira pamaso pa Yehova. 8Iye ayenera kulandira zogawana zawo mofanana ndi anzakewo ngakhale kuti iye anagulitsa kale cholowa cha pa banja pawo.

Makhalidwe Oletsedwa

9Mukafika mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, musakaphunzire makhalidwe onyansa a anthu a mʼdzikolo. 10Pasapezeke pakati panu munthu wootcha pa moto mwana wake wamwamuna kapena wamkazi ngati nsembe. Asapezekenso pakati panu munthu wowombeza kapena wochita mawula, wolosera, wochita za ufiti, 11wolodza, kapena woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa ndi kumafunsira nzeru kwa anthu akufawo. 12Aliyense wochita zinthu zotere ndi wonyansa pamaso pa Yehova, ndipo chifukwa cha zonyansa zimenezi Yehova adzakupirikitsirani mitundu ya anthu imeneyi. 13Muzikhala angwiro pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

Aneneri

14Mitundu ya anthu imene mudzayipirikitseyo imamvera anyanga kapena owombeza mawula. Koma inu Yehova Mulungu wanu sanakuvomerezeni kutero. 15Yehova Mulungu wanu adzawutsa pakati pa abale anu mneneri ngati ine. Muyenera kumumvera ameneyo. 16Pakuti izi ndi zimene munapempha kwa Yehova Mulungu wanu ku Horebu pa tsiku la msonkhano lija pamene munati, “Ife tisamvenso mawu a Yehova Mulungu wathu kapena kuona moto woopsawu, kuopa kuti tingafe.”

17Yehova anati kwa ine, “Zimene akunenazi ndi zabwino. 18Ndidzawawutsira mneneri ngati iwe pakati pa abale awo ndipo ndidzayika mawu anga mʼkamwa mwake ndipo adzawawuza chilichonse chimene ndidzamulamula. 19Ine mwini ndidzaweruza aliyense amene sadzamvera mawu anga amene mneneriyo adzayankhula mʼdzina langa. 20Koma mneneri wonena zinthu mʼdzina langa ndisanamulamulire kutero, kapena mneneri wonenera mʼdzina la milungu ina, ayenera kuphedwa.”

21Mwina mukhoza kumadzifunsa kuti, “Kodi tingadziwe bwanji kuti uthengawu sanayankhule ndi Yehova?” 22Ngati zimene mneneriyo wanenera mʼdzina la Yehova sizinachitike kapena kukwaniritsidwa, ndiye kuti umenewo si uthenga umene Yehova wayankhula. Mneneri ameneyo amangoyankhula za mʼmutu mwake ndiye musadzidzimuke naye.

New Amharic Standard Version

ዘዳግም 18:1-22

የካህናትና የሌዋውያን የመባ ድርሻ

1ሌዋውያን ካህናት፣ የሌዊ ነገድም ሁሉ ከእስራኤል ጋር የመሬት ድርሻ ወይም ርስት አይኖራቸውም፤ ለእግዚአብሔር (ያህዌ) በእሳት ከሚቀርበው መባ ይብሉ፤ ድርሻቸው ነውና። 2በወንድሞቻቸው መካከል ርስት አይኖራቸውም፤ በሰጣቸው ተስፋ መሠረት እግዚአብሔር (ያህዌ) ርስታቸው ነው።

3ኰርማ ወይም በግ የሚሠዋው ሕዝብ ለካህኑ የሚሰጠው ድርሻ ወርቹን፣ መንገጭላውንና ሆድ ዕቃውን ነው። 4የእህልህን፣ የአዲሱን ወይንህንና የዘይትህን በኵራት እንዲሁም ከበጎችህ በመጀመሪያ የተሸለተውን ጠጕር ትሰጣለህ፤ 5በእግዚአብሔር (ያህዌ) ስም ቆሞ ለዘላለም ያገለግል ዘንድ አምላክህ እግዚአብሔር (ኤሎሂም ያህዌ) ከነገዶችህ ሁሉ እርሱንና ዘሮቹን መርጧል።

6አንድ ሌዋዊ ከሚኖርበት ከየትኛውም በእስራኤል ካሉት ከተሞችህ መካከል በፍጹም ፈቃድ እግዚአብሔር (ያህዌ) ወደሚመርጠው ስፍራ ቢመጣ፣ 7በእግዚአብሔር (ያህዌ) ፊት ቆመው እንደሚያገለግሉት ሌዋውያን ወንድሞቹ፣ እርሱም በአምላኩ በእግዚአብሔር (ኤሎሂም ያህዌ) ስም ያገልግል። 8ከቤተ ሰቡ ንብረት ሽያጭ ላይ ገንዘብ ቢቀበል እንኳ፣ ባልንጀሮቹ ከሚያገኙት ጥቅም እኩል ይካፈላል።

አስጸያፊ ድርጊቶች

9አምላክህ እግዚአብሔር (ኤሎሂም ያህዌ) ወደሚሰጥህ ምድር በምትገባበት ጊዜ፣ በዚያ የሚኖሩት አሕዛብ የሚፈጽሙትን አስጸያፊ መንገድ አትከተል። 10በመካከልህ ወንድ ወይም ሴት ልጁን በእሳት የሚሠዋ18፥10 ወይም ወንድ ወይም ሴት ልጁን የሚገድል ሟርተኛ ወይም መተተኛ፣ ሞራ ገላጭ፣ ጠንቋይ 11ወይም በድግምት የሚጠነቍል፣ መናፍስት ጠሪ ወይም ሙት አነጋጋሪ በመካከልህ ከቶ አይገኝ። 12እነዚህን የሚያደርግ ሁሉ በእግዚአብሔር (ያህዌ) ዘንድ አስጸያፊ ነውና። ከእነዚህ አስጸያፊ ልምዶች የተነሣም አምላክህ እግዚአብሔር (ኤሎሂም ያህዌ) እነዚያን አሕዛብ ከፊትህ ያባርራቸዋል። 13በአምላክህ በእግዚአብሔር (ኤሎሂም ያህዌ) ፊት ነውር አልባ ሁን።

ነቢይ ስለ መነሣቱ

14ምድራቸውን የምታስለቅቃቸው አሕዛብ፣ መተተኞችን ወይም ሟርተኞችን ያዳምጣሉ፤ አንተ ግን ይህን እንድታደርግ አምላክህ እግዚአብሔር (ኤሎሂም ያህዌ) አልፈቀደልህም። 15አምላክህ እግዚአብሔር (ኤሎሂም ያህዌ) ከገዛ ወንድሞችህ መካከል እንደ እኔ ያለ ነቢይ ያስነሣልሃል፤ እርሱን አድምጥ። 16በኮሬብ ጉባኤ በተደረገበት ዕለት፣ “እንዳልሞት የአምላክህ የእግዚአብሔርን (ኤሎሂም ያህዌ) ድምፅ አልስማ፤ እንዲህ ያለውንም አስፈሪ እሳት ደግሜ አልይ” ብለህ አምላክህን እግዚአብሔርን (ያህዌ ኤሎሂም) የጠየቅኸው ይህን ነውና።

17እግዚአብሔር (ያህዌ) እንዲህ አለኝ፤ “የተናገሩት መልካም ነው፤ 18ከወንድሞቻቸው መካከል እንደ አንተ ያለ ነቢይ አስነሣላቸዋለሁ፤ ቃሌን በአፉ አደርጋለሁ፤ የማዝዘውንም ሁሉ ይነግራቸዋል። 19ማንም ሰው ነቢዩ በስሜ የሚናገረውን ቃሌን ባይሰማ፣ እኔ ራሴ በተጠያቂነት እይዘዋለሁ። 20ነገር ግን እንዲናገር እኔ ያላዘዝሁትን ቃል በድፍረት በስሜ የሚናገርም ሆነ በሌሎች አማልክት ስም የሚናገር ነቢይ ይገደል።”

21አንተም በልብህ፣ “እግዚአብሔር (ያህዌ) ያልተናገረውን መልእክት እንዴት ማወቅ እንችላለን?” ብትል፣ 22ነቢዩ በእግዚአብሔር (ያህዌ) ስም የተናገረው ካልተፈጸመ ወይም እውነት ሆኖ ካልተገኘ፣ መልእክቱ እግዚአብሔር (ያህዌ) የተናገረው አይደለም። ያ ነቢይ በድፍረት ተናግሮታልና እርሱን አትፍራው።