Deuteronomo 13 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 13:1-18

Kupembedza Milungu Ina

1Ngati mneneri kapena wina aliyense amene amanena zamʼtsogolo mwa maloto atuluka pakati panu, nalengeza za chizindikiro chozizwitsa kapena chodabwitsa, 2chinthu nʼkuchitikadi, tsono iyeyo nʼkunena kuti, “Tiyeni titsatire milungu ina, tiyeni tiyipembedze,” (kunena milungu imene simunayidziwe), 3musamumvere mneneriyo kapena wolotayo. Yehova Mulungu wanu afuna akuyeseni kuti aone ngati mumamukonda ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. 4Muyenera kutsatira Yehova Mulungu wanu, ndipo ndi Iyeyo amene muyenera kumuopa. Muzisunga malamulo ake ndi kumamumvera, muzimutumikira ndipo kumukangamira Iyeyo. 5Mneneri kapena wolotayo ayenera kuphedwa, popeza analalikira zopandukira Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani ku Igupto ndi kukupulumutsani ku dziko la ukapolo. Wolalikirayo anafuna kukupatutsani pa njira imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani kuti muyitsatire. Muzichotsa choyipa pakati panu.

6Ngati mʼbale wanu weniweni kapena mwana wanu wamwamuna kapena wamkazi, kapena mkazi wanu wokondedwa, kapena mnzanu wapamtima akukakamizani mwachinsinsi, nʼkumati, “Tiyeni tipite tikapembedze milungu ina” (milungu imene inuyo kapena makolo anu sanayidziwe, 7milungu ya anthu okuzungulirani, kaya ndi apafupi kapena akutali, kuchokera kumapeto mpaka kumapeto kwina kwa dziko lapansi), 8musamugonjere kapena kumumvera. Musamumvere chisoni. Musamuleke kapena kumutchinjiriza. 9Mumuphe ndithu. Dzanja lanu likhale loyambirira kumupha, kenaka manja a anthu ena onse. 10Mumuponye miyala mpaka kumupha, chifukwa anafuna kukupatutsani pa njira ya Yehova Mulungu amene anakutulutsani ku Igupto, dziko la ukapolo. 11Tsono Aisraeli onse adzamva nachita mantha, ndipo palibe mmodzi pakati panu amene adzachitenso choyipa chotere.

12Ngati mumvetsedwa kuti ku umodzi mwa mizinda imene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti mukhalemo, 13kwapezeka anthu ena oyipa pakati panu ndipo asocheretsa anthu ambiri mʼmizinda yanu, pomanena kuti, “Tiyeni tikapembedze milungu ina” (milungu imene simunayidziwe), 14mukuyenera kufunsa, kulondola ndi kufufuza bwino nkhaniyo. Ndipo ngati zitatsimikizikadi kuti ndi zoona kuti chinthu chonyansa chotere chachitikadi pakati panu, 15muyenera kuwapha onse okhala mu mzinda umenewo. Muwonongeretu kwathunthu mzindawo, anthu ake ndi ziweto zake zomwe. 16Katundu yense wa anthu mu mzindawo mumuwunjike pamodzi pakatikati pa bwalo losonkhanako ndipo mutenthe mzindawo pamodzi ndi katundu wake yense monga nsembe yathunthu yopsereza ya kwa Yehova Mulungu wanu. Mzinda umenewo ukhale bwinja mpaka muyaya, usadzamangidwenso. 17Musapezeke ndi kanthu kalikonse koyenera kuwonongedwa kuti Yehova abweze mkwiyo wake wochititsa manthawu. Adzakuchitirani chifundo ndi kukumverani chisoni, ndipo adzakuchulukitsani monga analonjeza mwa lumbiro kwa makolo anu, 18chifukwa mumamvera Yehova Mulungu wanu, kusunga malamulo ake onse amene ndikukupatsani lero lino ndi kuchita zoyenera pamaso pake.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

申命記 13:1-18

不可拜假神

1「如果你們中間出現了先知或解夢的人,要顯神蹟奇事給你們看, 2勸你們隨從、供奉素不認識的神明,即使他們顯的神蹟奇事應驗了, 3你們也不可聽從他們。因為這是你們的上帝耶和華在試驗你們,要看看你們是否全心全意地愛祂。 4你們要跟從你們的上帝耶和華,敬畏祂,遵守祂的誡命,聽從祂的話,事奉祂,倚靠祂。 5必須處死那些先知或解夢的人,因為他們慫恿你們背叛你們的上帝耶和華、偏離祂吩咐你們當走的道路。你們的上帝耶和華曾帶你們離開埃及,救你們脫離奴役。你們必須清除你們當中的邪惡。

6「如果你們的兄弟、兒女、愛妻或摯友引誘你們去拜你們和你們祖先都不認識的神明, 7引誘你們去拜你們周圍各族的神明,或在附近或遠在天邊, 8你們不可遷就、聽從他們,不可憐惜他們,不可放過或包庇他們。 9必須處死他們。你們要首先下手,然後眾人一起打死他們。 10你們要用石頭打死他們,因為他們企圖使你們背棄你們的上帝耶和華,祂曾把你們從受奴役之地——埃及領出來。 11這樣,所有以色列人聽了就會害怕,必無人再敢做這種惡事。

12-13「在你們的上帝耶和華將要賜給你們居住的各城中,如果你們聽說某城裡有惡人引誘城中的居民偏離正路,唆使他們去供奉你們不認識的神明, 14你們要認真查明真相。如果傳聞屬實,你們當中確有此惡行, 15你們一定要殺光那城中的居民和牲畜。 16你們要把城中的財物堆在廣場中心,然後放火焚燒那城和城中的財物,作為燔祭獻給你們的上帝耶和華。城要永遠荒廢,不可重建。 17-18你們不可保留任何應當被毀滅的東西,這樣耶和華就不再向你們發怒,轉而施恩憐憫你們。

「只要你們遵守我今天吩咐你們的一切誡命,做耶和華視為正的事,祂必按照祂對你們祖先所起的誓,憐憫你們,使你們人丁興旺。