Chivumbulutso 9 – CCL & SNC

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Chivumbulutso 9:1-21

1Mngelo wachisanu anayimba lipenga lake, ndipo ndinaona nyenyezi ikugwa pa dziko lapansi kuchokera ku thambo. Nyenyeziyo inapatsidwa kiyi ya ku chidzenje chakuya. 2Nyenyeziyo itatsekula pa chidzenje chakuyacho panatuluka utsi ngati wochokera mʼngʼanjo yayikulu. Dzuwa ndi thambo zinada chifukwa cha utsi ochokera mʼdzenjemo. 3Ndipo mʼkati mwa utsimo munatuluka dzombe kukalowa mʼdziko lapansi ndipo linapatsidwa mphamvu zoluma ngati za zinkhanira pa dziko lapansi. 4Dzombelo linalamulidwa kuti lisawononge udzu wa pa dziko lapansi, kapena chomera chilichonse, kapena mtengo uliwonse, koma anthu okhawo amene analibe chizindikiro cha Mulungu pa mphumi zawo. 5Silinapatsidwe mphamvu yowapha koma yowazunza kwa miyezi isanu. Ndipo ululu umene anthuwo anawumva unali ngati wa chinkhanira chikaluma munthu. 6Masiku amenewo anthu adzafunafuna imfa koma sadzayipeza. Adzalakalaka kufa koma imfa izidzawathawa.

7Dzombe linkaoneka ngati akavalo okonzekera nkhondo. Pamitu pawo panali ngati zipewa zaufumu zagolide ndipo nkhope zawo ngati za anthu. 8Tsitsi lawo linali ngati la amayi, mano awo ngati a mikango. 9Dzombelo linavala za pachifuwa zachitsulo. Phokoso la mapiko awo linali ngati phokoso la magaleta ankhondo ambiri okokedwa ndi akavalo othamangira ku nkhondo. 10Linali ndi michira ngati zinkhanira ndi mbola. Mʼmichira yake munali mphamvu yozunza nayo anthu kwa miyezi isanu. 11Mfumu yawo inali mngelo wolamulira Chidzenje chakuya chija. Mʼchihebri dzina lake ndi Abadoni ndipo mʼChigriki ndi Apoliyoni (tanthauzo lake ndiye kuti, Wowononga).

12Tsoka loyamba lapita; matsoka ena awiri akubwerabe.

13Mngelo wachisanu ndi chimodzi anayimba lipenga lake, ndipo ndinamva liwu lochokera ku ngodya zinayi za guwa lansembe lagolide lija lokhala pamaso pa Mulungu. 14Liwulo linati kwa mngelo wachisanu ndi chimodzi amene anali ndi lipenga uja, “Masula angelo anayi amene anamangidwa pa mtsinje waukulu wa Yufurate.” 15Ndipo anamasulidwadi angelo anayi aja amene anasungidwa kukonzekera ora ili, tsiku ili, mwezi uwu ndi chaka ichi kuti aphe limodzi la magawo atatu a anthu. 16Ndinamva chiwerengero cha ankhondo a pa akavalo aja, kuti chinali 200 miliyoni.

17Akavalo ndi okwerapo amene ndinaona mʼmasomphenya anga ankaoneka motere: Zovala za pachifukwa pawo zinali zofiira ngati moto, zobiriwira ngati utsi, ndi zachikasu ngati miyala ya sulufule. Mitu ya akavalowo inali ngati ya mikango ndipo mʼkamwa mwawo munkatuluka moto, utsi ndi sulufule. 18Gawo limodzi la magawo atatu a anthu linaphedwa ndi miliri yamoto, utsi ndi sulufule zimene zinkachoka mʼkamwa mwawo. 19Mphamvu za akavalowo inali mʼkamwa mwawo ndi mʼmichira mwawo; pakuti michira yawo inali ngati njoka; ndi mitu imene inkalumira.

20Anthu ena onse amene sanaphedwe ndi miliri imeneyi sanalapebe kuti asiye ntchito zawo zoyipa. Iwo sanasiye kupembedza ziwanda ndi mafano agolide, asiliva, amkuwa, amwala ndi amtengo, mafano amene sangathe kuona, kumva kapena kuyankhula. 21Sanalapenso kuleka zakupha, zamatsenga awo, zachigololo zawo kapena umbava wawo.

Slovo na cestu

Zjevení Janovo 9:1-21

1Potom anděl pátý zatroubil, i viděl jsem, ano hvězda s nebe spadla na zem; a dán jest tomu andělu klíč od studnice propasti. 2Kterýžto otevřel studnici propasti. I vyšel dým z studnice jako dým z peci veliké, i zatmělo se slunce i povětří pro dým studnice. 3A z toho dýmu vyšly kobylky na zemi, jimžto dána jest moc taková, jakouž moc mají štírové zemští. 4Ale řečeno jim, aby neškodily trávě zemské, ani čemu zelenému, ani kterémukoli stromoví, než toliko lidem, kteříž nemají znamení Božího na čelích svých. 5Dáno jest pak jim, ne aby je zabíjely, ale trápily za pět měsíců, a aby trápení jejich bylo jako trápení od štíra, když by ušťknul člověka. 6A v těch dnech hledati budou lidé smrti, ale nenaleznou jí, a žádati budou zemříti, ale smrt uteče od nich. 7Způsob pak těch kobylek podobný byl koňům připraveným k boji, a na hlavách jejich byly jako koruny podobné zlatu, a tváři jejich jako tváři lidské. 8A měly vlasy jako vlasy ženské, a zuby jejich byly jako zubové lvů. 9Měly také pancíře jako pancíře železné, a zvuk křídel jejich jako zvuk vozů, když množství koní běží k boji. 10A měly ocasy podobné štírům, a žihadla v ocasích jejich byla, a moc jejich byla škoditi lidem za pět měsíců. 11A měly nad sebou krále, anděla propasti, jemuž jméno Židovsky Abaddon, a řecky Apollyon. 12Bída jedna pominula, a aj, přijdou ještě dvě bídy potom. 13Tedy šestý anděl zatroubil, i slyšel jsem hlas jeden ze čtyř rohů oltáře zlatého, kterýž jest před obličejem Božím, 14Řkoucí k šestému andělu, kterýž měl troubu: Rozvěž ty čtyři anděly, kteříž jsou u vězení při veliké řece Eufrates. 15I rozvázáni jsou ti čtyři andělé, kteříž byli připraveni k hodině, a ke dni, a k měsíci, a k roku, aby zmordovali třetí díl lidí. 16A byl počet vojska lidu jízdného dvěstěkrát tisíc tisíců; nebo slyšel jsem počet jejich. 17A též viděl jsem u vidění, koně a ti, kteříž seděli na nich, měli pancíře ohnivé a hyacintové a z síry. Hlavy pak těch koňů byly jako hlavy lvové, a z úst jejich vycházel oheň, a dým, a síra. 18A tímto trojím zmordována jest třetina lidu, totiž ohněm, a dýmem, a sirou, kteréž vycházely z úst jejich. 19Nebo moc jejich jest v ústech jejich a v ocasích jejich; ocasové zajisté jejich jsou podobni hadům, majíce hlavy, jimiž škodí. 20Jiní pak lidé, kteříž nejsou zmordováni těmi ranami, nečinili pokání z skutků rukou svých, aby se neklaněly ďáblům, a modlám zlatým, a stříbrným, a měděným, i kamenným, i dřevěným, kteréžto ani hleděti nemohou, ani slyšeti, ani choditi. 21Aniž činili pokání z vražd svých, ani z trávení svých, ani z smilstva svého, ani z krádeží svých.