Kalata Yolembera Mpingo wa ku Efeso
1“Lembera mngelo wa mpingo wa ku Efeso kuti:
Awa ndi mawu ochokera kwa amene ali ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri zija mʼdzanja lake lamanja amene akuyenda pakati pa zoyikapo nyale zisanu ndi ziwiri zagolide. 2Ine ndimadziwa zochita zako, ntchito yako yowawa ndi kupirira kwako. Ine ndimadziwa kuti sungalekerere anthu oyipa amene amadzitcha atumwi pamene sichoncho, unawayesa, ndipo unawapeza kuti ndi abodza. 3Iwe wapirira ndipo wakumana ndi zovuta chifukwa cha dzina langa, ndipo sunatope.
4Komabe ndili ndi chotsutsana nawe: Wataya chikondi chako chapoyamba. 5Kumbukirani kuti munagwa kuchokera patali. Lapa ndikuchita zinthu zimene unkachita poyamba. Ngati sulapa ndidzabwera ndikukuchotsera choyikapo nyale chako pamalo pake. 6Komabe chokomera chako ndi chakuti umadana ndi zochita za Anikolai, zimene Inenso ndimadana nazo.
7Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo. Amene adzapambana, ndidzamupatsa ufulu wakudya zipatso za mtengo wopatsa moyo umene uli ku paradizo wa Mulungu.
Kalata Yolembera Mpingo wa ku Simurna
8“Lembera mngelo wa mpingo wa ku Simurna kuti:
Awa ndi mawu ochokera kwa amene ndi Woyamba ndi Wotsiriza, amene anafa nʼkukhalanso ndi moyo. 9Ine ndimadziwa masautso ako ndi umphawi wako, chonsecho ndiwe wolemera! Ndikudziwa zimene amakusinjirira anthu amene amati ndi Ayuda pamene sizili choncho, koma ndi a mpingo wa Satana. 10Musachite mantha ndi zimene muti musauke nazo posachedwapa. Ndithu, Satana adzayika ena a inu mʼndende pofuna kukuyesani, ndipo mudzazunzika kwa masiku khumi. Khalani okhulupirika ngakhale zitafika pa imfa, ndipo Ine ndidzakupatsani chipewa cha ulemerero wamoyo.
11Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo. Amene adzapambana sadzapwetekedwa ndi pangʼono pomwe ndi imfa yachiwiri.
Kalata Yolembera Mpingo wa ku Pergamo
12“Lembera mngelo wa mpingo wa ku Pergamo kuti:
Awa ndi mawu ochokera kwa amene ali ndi lupanga lakuthwa konsekonse. 13Iye akuti, ‘Ine ndimadziwa kumene mumakhala, kumene kuli mpando waufumu wa Satana. Komabe inu ndinu okhulupirika kwa Ine. Simunataye chikhulupiriro chanu pa Ine, ngakhale mʼmasiku a Antipa, mboni yanga yokhulupirika, amene anaphedwa mu mzinda wanu, kumene amakhala Satana.
14Komabe, ndili ndi zinthu zingapo zotsutsana nanu. Kumeneko muli ndi anthu ena amene amatsata ziphunzitso za Balaamu, uja amene anaphunzitsa Baraki kukopa Aisraeli kuti azidya nsembe zoperekedwa ku mafano ndi kumachita chigololo. 15Chimodzimodzinso inuyo muli ndi ena amene amatsatira ziphunzitso za Anikolai. 16Tsono tembenukani mtima. Mukapanda kutero, ndidzabwera kwanuko posachedwa ndipo ndidzachita nanu nkhondo ndi lupanga lotuluka mʼkamwa mwanga lija.
17Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo. Kwa amene adzapambane ndidzamupatsa chakudya chobisika cha mana. Ndidzamupatsanso mwala woyera wolembedwapo dzina latsopano, lodziwa iye yekha amene walandirayo.’ ”
Kalata Yolembera Mpingo wa ku Tiyatira
18“Lembera mngelo wampingo wa ku Tiyatira kuti:
Awa ndi mawu ochokera kwa Mwana wa Mulungu, amene maso ake ali ngati moto woyaka ndi mapazi ake ngati chitsulo chonyezimira. 19Iye akuti: Ndimadziwa ntchito zanu, chikondi chanu ndi chikhulupiriro chanu, kutumikira kwanu ndi kupirira kwanu. Ndikudziwa tsopano kuti ntchito zanu ndi zabwino kuposa zoyamba zija.
20Komabe ndili ndi chinthu chokudzudzula nacho. Umamulekerera mkazi uja Yezebeli amene amadzitcha yekha kuti ndi mneneri. Iye amaphunzitsa atumiki anga kuti azichita zadama ndi kumadya zansembe zoperekedwa ku mafano. 21Ndamupatsa nthawi kuti aleke zachigololo zake koma sakufuna. 22Tsono ndidzamugwetsa mʼmasautso ndipo amene amachita naye zadama zakezo ndidzawasautsa kwambiri akapanda kulapa ndi kuleka njira za mkaziyo. 23Ana ake ndidzawakantha ndi kuwapheratu. Kotero mipingo yonse idzadziwa kuti Ine ndine uja amene ndimafufuza mʼmitima mwa anthu ndi mʼmaganizo mwawo. Aliyense wa inu ndidzachita naye monga mwa ntchito zake.
24Tsopano ndikunena kwa enanu a ku Tiyatira, kwa inu amene simunatsate chiphunzitso cha mkaziyo ndipo simunaphunzire zimene iwo amati ndi ‘zinsinsi zonama’ za Satana. Kwa inu mawu anga ndi akuti sindikuwunjikirani malamulo ena. 25Inu mungogwiritsa zimene munaphunzira basi, mpaka Ine ndidzabwere.
26Amene adzapambana ndi kuchita chifuniro changa mpaka kumapeto, ndidzamupatsa ulamuliro pa mitundu yonse ya anthu. 27Adzayilamulira ndi ndodo yachitsulo ndipo nadzayiphwanyaphwanya ngati mbiya. Ulamuliro umenewu ndi omwe ndinalandira kwa Atate anga. 28Ine ndidzamupatsanso nthanda, nyenyezi yowala mʼmamawa ija. 29Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.