Chivumbulutso 15 – CCL & NSP

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Chivumbulutso 15:1-8

Angelo Asanu ndi Awiri Okhala ndi Miliri Isanu ndi Iwiri

1Kumwamba ndinaona chizindikiro china chachikulu ndi chodabwitsa: angelo asanu ndi awiri ali ndi miliri isanu ndi iwiri yomaliza chifukwa Mulungu anakwiya kotheratu. 2Ndipo ndinaona chimene chinaoneka ngati nyanja yonyezimira yosakaniza ndi moto, ndipo pambali pa nyanjayo panayima amene anagonjetsa chirombo chija ndi fano lake, ndi nambala yotanthauza dzina lake. Anthuwo ananyamula azeze amene Mulungu anawapatsa. 3Iwo ankayimba nyimbo ya Mose, mtumiki wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwana Wankhosa. Nyimbo yake inkati,

“Zochita zanu ndi zazikulu ndi zodabwitsa,

Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse

Njira zanu ndi zachilungamo ndi zoona,

Mfumu ya mitundu yonse.

4Inu Ambuye, ndani angapande kukuopani,

ndi kulemekeza dzina lanu?

Pakuti Inu nokha ndiye woyera.

Anthu a mitundu yonse adzabwera

kudzapembedza pamaso panu,

pakuti ntchito zanu zolungama zaonekera poyera.”

5Zitatha izi, ndinaona kumwamba Nyumba ya Mulungu imene ndi Tenti ya Umboni, atatsekula. 6Mʼnyumbamo munatuluka angelo asanu ndi awiri ndi miliri isanu ndi iwiri. Angelowo anavala nsalu zoyera bwino zonyezimira ndi malamba agolide pa zifuwa zawo. 7Ndipo kenaka chimodzi cha zamoyo zinayi zija chinapereka kwa angelo asanu ndi awiri mbale zisanu ndi ziwiri zodzaza ndi ukali wa Mulungu amene ali ndi moyo mpaka muyaya. 8Ndipo Nyumba ya Mulungu inadzaza ndi utsi wochokera ku ulemerero wa Mulungu ndi ku mphamvu zake, ndipo panalibe yemwe akanalowa mʼNyumbayo mpaka miliri isanu ndi iwiri ya angelo asanu ndi awiri aja itatha.

New Serbian Translation

Откривење 15:1-8

Последњих седам пошасти

1Затим сам видео други велики и чудесни знак на небу: седам анђела са седам последњих зала, јер се са њима завршава Божији гнев. 2Видео сам и нешто налик мору од стакла, помешаном с огњем, и тамо оне који су победили Звер, њен кип и број њеног имена. Стајали су покрај мора од стакла са китарама које им је Бог дао. 3Певали су песму Мојсија, слуге Божијег, и Јагњетову песму:

„Велика су и чудесна твоја дела,

Господе Боже, Сведржитељу;

праведни су и истинити твоји путеви,

Царе народа.

4Ко се не би бојао тебе

и славио име твоје, Господе?

Јер ти си једини свет.

Зато ће сви народи доћи к теби

и поклонити се пред тобом,

јер се показаше твоја праведна дела!“

5После овога сам видео да се отворио храм на небу, то јест, Шатор сведочанства. 6Из храма изађоше седам анђела са седам зала, обучени у чист и светао лан, и опасани златним појасевима око прсију. 7А једно од четири жива бића даде седморици анђела седам златних здела испуњених гневом Бога који живи од сад и довека. 8Тада се храм испуни димом од Божије славе и од његове силе, тако да нико није могао ући у храм док се нису завршила седам зала седморице анђела.