Afilipi 1 – CCL & CRO

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Afilipi 1:1-30

1Paulo ndi Timoteyo, atumiki a Khristu Yesu.

Kulembera anthu onse oyera mtima a ku Filipi amene ali mwa Khristu Yesu, pamodzi ndi oyangʼanira ndi atumiki awo.

2Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale kwa inu.

Kuyamika ndi Pemphero

3Ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakumbukira inu. 4Mʼmapemphero anga onse opempherera inu, nthawi zonse ndimapemphera ndi chimwemwe 5chifukwa mwakhala mukundithandiza polalikira Uthenga Wabwino kuyambira tsiku loyamba mpaka tsopano. 6Sindikukayika konse kuti Iye amene anayamba ntchito yabwino mwa inu adzayipitiriza ndi kuyimaliza mpaka pa tsiku la kubweranso kwa Khristu Yesu.

7Kwa ine ndi bwino kuti ndiziganiza zotere za nonsenu, popeza ndimakukondani, ngakhale ndikhale mʼndende, kapena pamene ndikuteteza ndi kukhazikitsa Uthenga Wabwino, inu nonse mumagawana nane chisomo cha Mulungu. 8Mulungu angandichitire umboni kuti ndimakulakalakani ndi chikondi cha Khristu Yesu.

9Ndipo pemphero langa ndi lakuti chikondi chanu chipitirire kukulirakulira pa chidziwitso ndi kuzama mʼmaganizo, 10kuti mukhoza kuzindikira chabwino koposa zonse ndi chiti kuti muthe kukhala wopanda chodetsa ndi wopanda chilema kufikira tsiku la Khristu. 11Ndipo moyo wanu udzakhala odzazidwa ndi chipatso cha chilungamo chimene chimachokera mwa Yesu Khristu. Pakuti zimenezi zidzapereka ulemerero ndi matamando kwa Mulungu.

Maunyolo a Paulo Apititsa Mʼtsogolo Uthenga Wabwino

12Tsopano abale, ndikufuna mudziwe kuti chimene chandichitikira ine chathandiza kwambiri kupititsa patsogolo Uthenga Wabwino. 13Chotsatira chake nʼchakuti zadziwika bwino lomwe kwa onse amene ali ku nyumba yaufumu kuti ine ndili mʼmaunyolo chifukwa cha Khristu. 14Moti chifukwa cha maunyolo angawa, abale ambiri alimbikitsidwa kuyankhula Mawu a Mulungu molimbika ndi mopanda mantha.

15Nʼzoonadi kuti ena amalalikira Khristu chifukwa cha kaduka ndi mikangano, koma ena chifukwa cha zolinga zabwino. 16Olalikira ndi zolinga zabwinowa amachita izi mwachikondi, podziwa kuti ine ndili muno chifukwa cha kuteteza Uthenga Wabwino. 17Ena aja amalalikira Khristu modzikonda osati moona mtima namaganiza kuti kutero kubweretsa mavuto pamene ndili mʼmaunyolo. 18Nanga kodi zimenezo zili ndi ntchito? Chofunika ndi chakuti Khristu alalikidwe, kaya ndi mwachinyengo kapena moona. Ndipo ndikukondwera chifukwa cha chimenechi.

Ndithu, ndidzapitirira kukondwera, 19pakuti ndikudziwa kuti chifukwa cha mapemphero anu ndi thandizo lochokera kwa Mzimu wa Yesu Khristu, zimene zandionekera zidzathandiza kuti ndimasulidwe. 20Ndili ndi chiyembekezo chonse kuti sindidzachita manyazi ndi pangʼono pomwe, koma ndidzakhala ndi chilimbikitso chokwanira kuti monga mwa nthawi zonse, tsopano Khristu adzakwezedwa mʼthupi langa kaya ndi mʼmoyo kapena mu imfa. 21Pakuti kwa ine kukhala moyo ndi Khristu ndipo kufa ndi phindu. 22Ngati nditi ndipitirire kukhala ndi moyo mʼthupi ndiye kuti kwa ine ndi kugwira ntchito yopindulitsa. Kodi ndisankhe chiyani? Sindikudziwa. 23Ndathinidwa ndi zinthu ziwirizi: Ndikulakalaka kunyamuka kuti ndikakhale ndi Khristu, chimene ndi chinthu chabwino kwambiri. 24Komanso nʼkofunika kwambiri kuti ndikhalebe mʼthupi chifukwa cha inu. 25Ndili ndi chitsimikizo, ndikudziwa kuti ndidzakhala ndi moyo ndipo ndidzapitirira nanu kuti nonse mupite mʼtsogolo ndi kukhala ndi chimwemwe mu chikhulupiriro 26kuti pokhala nanunso, kudzitamandira kwanu mwa Khristu Yesu kudzasefukire chifukwa cha ine.

Moyo Woyenerana ndi Uthenga Wabwino

27Chilichonse chimene chingachitike, chachikulu nʼchakuti mukhale moyo ofanana ndi Uthenga Wabwino wa Khristu. Tsono ngati ndingabwere kudzakuonani kapena kumangomva za inu ndili kutali, ndidzadziwa kuti mwayima mwamphamvu mwa Mzimu mmodzi, kulimbika pamodzi ngati munthu mmodzi chifukwa cha chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino 28osachita mantha ndi pangʼono pomwe ndi amene akutsutsana nanu. Ichi ndi chizindikiro kwa iwo kuti adzawonongedwa, koma inu mudzapulumutsidwa ndi Mulungu. 29Pakuti inu mwapatsidwa mwayi osati ongokhulupirira Khristu kokha, koma wakumva zowawa mʼmalo mwa Khristu. 30Inunso mukudutsa mʼzowawa zomwe zija munaona ndikudutsamo inenso ndipo pano mukumva kuti ndikukumana nazobe.

Knijga O Kristu

Filipljanima 1:1-30

Pavlovi pozdravi

1Ovo je pismo od Pavla i Timoteja, slugu Krista Isusa, svima svetima u Kristu Isusu koji su u Filipima te starješinama i đakonima.

2Neka vam je milost i mir od našega Boga Oca i Gospodina Isusa Krista.

Pavlova zahvalnost i molitva

3Kad god vas se sjetim, zahvaljujem Bogu. 4U svakoj svojoj molitvi radosno se molim za vas 5jer ste bili sudionicima navješćivanja Radosne vijesti o Kristu od prvoga dana pa sve do sada. 6Siguran sam da će Bog, koji je započeo dobro djelo među vama, to djelo i dovršiti do dana kad se Isus Krist vrati.

7I pravo je da tako osjećam prema vama. Nosim vas u srcu jer ste sa mnom dijelili Božju milost i kad sam bio u okovima, i u obrani i u utvrđivanju Radosne vijesti. 8Bog mi je svjedok da čeznem za svima vama ljubavlju Isusa Krista. 9Moja je molitva za vas da vaša ljubav još više uzraste, da rastete u znanju i razumijevanju, 10da znate odabrati najbolje. Tako ćete biti čisti od svake nečistoće i krivnje na Dan Kristova povratka, 11puni ploda pravednosti koja dolazi po Isusu Kristu.

Pavlova radost zbog propovijedanja Krista

12Želim, draga braćo, da znate da je sve što mi se ovdje dogodilo pomoglo širenju Radosne vijesti 13jer ovdje svi, pa čak i carska tjelesna straža, znaju da sam u okovima zbog Krista. 14A i većina braće osmjelila se zbog mojih okova još neustrašivije propovijedati Božju riječ.

15Neki, doduše, propovijedaju iz zavisti i nadmetanja, ali drugi zato iz dobre volje. 16Propovijedaju jer me vole i jer znaju da me je Gospodin doveo ovamo da branim Radosnu vijest. 17Oni drugi pak Krista navješćuju neiskreno, zaradi vlastite koristi. Misle da će mi time još više otežati okove. 18Ali što onda? Bile njihove pobude iskrene ili ne, Krist se navješćuje. Tomu se radujem. A i dalje ću se radovati 19jer znam da se molite za mene, da mi pomaže Duh Isusa Krista i da ću na koncu biti spašen.

Pavlov život za Krista

20Živim u žarkoj nadi da me ništa neće smesti, nego da ću uvijek, kao i sada, biti hrabar za Krista i da će se on u meni proslaviti, živio ja ili umro za njega. 21Jer za mene je život Krist, a smrt dobitak. 22Ipak, ako živim u tijelu, plodonosno ću djelovati. Što onda odabrati? Ne znam. 23Razdiru me dvije želje. Želim otići i biti s Kristom. To je mnogo bolje za mene. 24Ali zbog vas je potrebnije da ostanem živjeti u tijelu.

25Uvjeren sam u to. Ostat ću s vama da rastete i radujete se u vjeri. 26Tako ćete se, kad opet dođem k vama, imati još više razloga hvaliti onime što je Krist Isus učinio za mene.

Živjeti dostojno evanđelja

27Samo se ponašajte dostojno evanđelja tako da, došao li vas ja vidjeti ili samo slušao o vama, znam da ste postojani u jednome Duhu i da se jednodušno borite za evanđeosku vjeru 28te da se ni u čemu ne strašite protivnika. To će im biti Božji znak njihove propasti, a vašega spasenja. 29Jer dana vam je milost ne samo da vjerujete u Krista, nego i da trpite za njega 30u istoj borbi u kojoj ste me vidjeli i za koju sada čujete da ju vodim.