Aefeso 6 – The Word of God in Contemporary Chichewa CCL

The Word of God in Contemporary Chichewa

Aefeso 6:1-24

Ana ndi Makolo Awo

1Inu ana, mverani makolo anu mwa Ambuye, pakuti zimenezi ndi zoyenera. 2“Lemekeza abambo ndi amayi ako.” Limeneli ndi lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo. 3Ngati ulemekeza abambo ako ndi amayi ako, “zinthu zidzakuyendera bwino ndipo udzasangalala ndi moyo wautali pa dziko lapansi.” 4Abambo musakwiyitse ana anu; mʼmalo mwake, muwalere mʼchiphunzitso ndi mʼchilangizo cha Ambuye.

Antchito ndi Mabwana Awo

5Inu antchito, mverani mabwana anu mwaulemu ndi mwamantha ndi moona mtima, monga momwe mungamvere Khristu. 6Musawamvere pamene akukuonani kuti akukomereni mtima, koma ngati akapolo a Khristu ochita chifuniro cha Mulungu kuchokera mu mtima mwanu. 7Tumikirani ndi mtima wonse, ngati kuti mukutumikira Ambuye, osati anthu. 8Inu mukudziwa kuti Ambuye adzamupatsa munthu aliyense mphotho chifukwa cha ntchito yake yabwino imene anagwira, kaya munthuyo ndi kapolo kapena mfulu.

9Ndipo inu mabwana, muziwachitiranso chimodzimodzi antchito anu. Musamawaopseze, popeza mukudziwa kuti Mbuye wawo ndi wanunso, nonse Mbuye wanu ali kumwamba, ndipo Iyeyo alibe tsankho.

Zida Zankhondo za Mulungu

10Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye ndi mwa mphamvu zake zazikulu. 11Valani zida zonse za Mulungu kuti muthe kuyima ndi kukana machenjerero a Satana. 12Pakuti sitikulimbana ndi thupi ndi magazi, koma tikulimbana ndi maufumu, maulamuliro, mphamvu za dziko la mdima, ndi mphamvu zoyipa kwambiri zauzimu zamlengalenga. 13Choncho valani zida zonse za Mulungu, kuti pamene tsiku loyipa kwambiri lifika, mudzathe kuyima chilili, ndipo mutatha kuchita zonse, mudzayimabe mwamphamvu. 14Tsono imani mwamphamvu, mutamangira choonadi ngati lamba mʼchiwuno mwanu, mutavala chilungamo ngati chitsulo chotchinjiriza pa chifuwa. 15Valani Uthenga Wabwino wamtendere ku mapazi anu ngati nsapato. 16Kuwonjezera pa zonsezi, nyamulani chishango cha chikhulupiriro, ndipo ndi chimenechi mudzatha kuzimitsa mivi yonse yoyaka moto ya oyipayo. 17Valani chipewa cha chipulumutso ndi kutenga lupanga la mzimu, limene ndi Mawu a Mulungu. 18Ndipo mupemphere mwa Mzimu nthawi zonse, mʼmitundu yonse ya mapemphero ndi zopempha. Ndipo pozindikira izi, khalani achangu kupempherera oyera mtima nthawi zonse.

19Mundipempherere inenso, kuti nthawi iliyonse pamene nditsekula pakamwa panga, andipatse mawu kuti ndiwulule zinsinsi za Uthenga Wabwino mopanda mantha. 20Ndine kazembe wa Uthenga Wabwinowu ngakhale ndili womangidwa mʼndende. Pempherani kuti ndilalikire mopanda mantha, monga ndiyenera.

Mawu Otsiriza

21Tukiko, mʼbale wanga wokondedwa ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye, adzakuwuzani zonse kuti inunso mudziwe mmene ndilili ndi zimene ndikuchita. 22Ine ndikumutumiza kwa inu, kuti mudziwe za moyo wathu, ndi kuti akulimbikitseni.

23Mtendere, chikondi pamodzi ndi chikhulupiriro kuchokera kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale ndi abale onse. 24Chisomo kwa onse amene amakonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosatha.