2 Yohane 1 – CCL & LCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Yohane 1:1-13

1Ndine mkulu wampingo, kulembera:

Mayi wosankhidwa ndi Mulungu ndi kwa ana ake amene ndimawakonda mʼchoonadi. Ndipo sindine ndekha amene ndimawakonda, komanso onse odziwa choonadi. 2Timakukondani chifukwa cha choonadi chimene chimakhala mwa ife ndipo chidzakhala mwa ife mpaka muyaya.

3Chisomo, chifundo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi kwa Yesu Khristu, Mwana wa Atate, zikhale ndi ife mʼchoonadi ndi mʼchikondi.

Choonadi ndi Chikondi

4Ndinakondwera kwambiri nditapeza ana anu ena akuyenda mʼchoonadi, monga Atate anatilamulira. 5Ndipo tsopano, amayi wokondedwa, sindikukulemberani lamulo latsopano koma lomwe lija takhala nalo kuyambira pachiyambi. Ine ndikukupemphani kuti tidzikondana wina ndi mnzake. 6Ndipo chikondi ndiye kuyenda momvera malamulo ake. Lamulo lake ndi lakuti mukhale moyo wachikondi monga munamva kuyambira pachiyambi.

7Ndikunena zimenezi chifukwa anthu ambiri onyenga, amene savomereza kuti Yesu Khristu anabwera monga munthu, akuyenda mʼdziko lapansi. Munthu aliyense otere ndi wonyenga ndiponso wokana Khristu. 8Chenjerani kuti mungataye chimene mwagwirira ntchito, koma chitani khama kuti mukalandire mphotho yanu yonse. 9Aliyense amene sasunga chiphunzitso cha Khristu, alibe Mulungu. Koma amene amasunga chiphunzitsochi, ameneyo alinso ndi Atate ndi Mwana. 10Ngati wina aliyense abwera kwa inu osaphunzitsa zimenezi, musamulandire mʼnyumba mwanu kapena kumupatsa moni. 11Aliyense wolandira munthu wotere ndiye kuti akuvomerezana nazo ntchito zake zoyipa.

12Ndili nazo zambiri zoti ndikulembereni, koma sindikufuna kuzilemba mʼkalata. Mʼmalo mwake, ndikuyembekeza kufika kwanuko kuti tidzakambirane nanu pamaso ndi pamaso, potero chimwemwe chathu chidzakhala chathunthu.

13Ana a mlongo wanu wosankhidwa ndi Mulungu akupereka moni.

Luganda Contemporary Bible

2 Yokaana 1:1-13

1Nze omukadde mpandiikira omukyala omulonde awamu n’abaana be, be njagalira ddala mu mazima, si nze mbaagala nzekka, wabula n’abo bonna abategeera amazima. 2Amazima ago gabeera mu ffe, era gajjanga kubeera mu ffe emirembe gyonna.

3Ekisa, n’okusaasira n’emirembe ebiva eri Katonda Kitaffe ne Yesu Kristo Omwana wa Kitaffe bijjanga kubeera naffe mu mazima ne mu kwagala.

4Nnasanyuka nnyo, bwe nnasanga abamu ku baana bo nga batambulira mu mazima nga bwe twalagirwa Kitaffe. 5Naye nnyabo kaakano nkusaba nga siri ng’akuwa ekiragiro ekiggya, naye nkujjukiza ekiragiro ekyo Katonda kye yatuwa okuva ku lubereberye nti, “Twagalanenga.” 6Era kuno kwe kwagalana nti tugonderenga ebiragiro bya Katonda. Kubanga okuva ku lubereberye twategeezebwa nga bwe tuteekwa okutambula.

7Mwekuume, abalimba bangi mu nsi abatakkiriza nti Yesu yayambala omubiri. Buli muntu ayogera bw’atyo mulimba era mulabe wa Kristo. 8Mwekuume, muleme okufiirwa kye twakolerera, wabula mukikuume kubanga mulifuna empeera yammwe yonna. 9Buli asukka ku ebyo Kristo by’ayigiriza n’atabinywereramu, talina Katonda; naye oyo anywerera mu kuyigiriza okwo alina Kitaffe n’Omwana. 10Omuntu yenna bw’ajja gye muli, n’atayigiriza bw’atyo, temumwanirizanga mu nnyumba yammwe, n’okulamusa temumulamusanga. 11Kubanga buli amusembeza aba yeenyigidde mu bikolwa ebyo ebibi.

12Mbadde na bingi eby’okubawandiikira, kyokka saagala byonna kubibawandiikira buwandiikizi, wabula nsuubira okubakyalira tulyoke twogeraganye nga tulabagana amaaso n’amaaso, essanyu lyaffe liryoke lituukirire.

13Abaana ba mwannyoko omulonde bakulamusizza.