2 Samueli 23 – The Word of God in Contemporary Chichewa CCL

The Word of God in Contemporary Chichewa

2 Samueli 23:1-39

Mawu Otsiriza a Davide

1Nawa mawu otsiriza a Davide:

“Mawu a Davide mwana wa Yese,

mawu a munthu amene wakwezedwa ndi Wammwambamwamba,

munthu wodzozedwa ndi Mulungu wa Yakobo,

woyimba nyimbo za Israeli:

2“Mzimu wa Yehova unayankhula kudzera mwa ine;

mawu ake anali pakamwa panga.

3Mulungu wa Israeli anayankhula,

Thanthwe la Israeli linati kwa ine:

‘Pamene munthu alamulira anthu mwachilungamo,

pamene alamulira moopa Mulungu,

4amakhala ngati kuwala kwa mmamawa,

mmawa wopanda mitambo,

monga kuwala pamene mvula yaleka kugwa

imene imameretsa udzu mʼnthaka.’

5“Kodi banja langa silolungama pamaso pa Mulungu?

Kodi Iye sanachite pangano losatha ndi ine,

lokonzedwa ndi lotetezedwa mbali zonse?

Kodi sadzakwaniritsa chipulumutso changa,

ndi kundipatsa chokhumba changa chilichonse?

6Koma anthu oyipa ndiwo ayenera kutayidwa kunja ngati minga,

imene sitengedwa ndi manja.

7Aliyense amene wayikhudza mingayo

amayidula pogwiritsa ntchito chigwandali kapena ndodo ya mkondo;

nayitentha pa moto.”

Ankhondo Otchuka a Davide

8Nawa mayina a ankhondo amphamvu a Davide:

Yosebu-Basebeti wa ku Takemoni mkulu wa atsogoleri a ankhondo atatu. Iye anapha ndi mkondo ankhondo 800 nthawi imodzi.

9Wotsatana naye anali Eliezara mwana wa Dodo Mwahohi. Monga mmodzi mwa ankhondo atatu amphamvu a Davide, iye anali ndi Davide pamene anazunza Afilisti amene anasonkhana ku Pasi-Damimu kuchita nkhondo. Kenaka ankhondo a Israeli anabwerera mʼmbuyo. 10Koma iye anayima osasuntha ndipo anakantha Afilisti mpaka mkono wake unatopa ndipo unakanirira ku lupanga lake. Yehova anapereka chigonjetso chachikulu pa tsiku limenelo. Asilikali anabwerera kwa Eliezara, kukatenga katundu wa anthu ophedwa.

11Wotsatana naye anali Sama mwana wa Age Mharari. Pamene Afilisti anasonkhana pamalo pamene panali munda wa mphodza, ankhondo a Israeli anathawa Afilistiwo. 12Koma Sama anayima pakati pa mundawo. Iye anawuteteza nakantha Afilistiwo ndipo Yehova anawapambanitsa koposa.

13Pa nthawi yokolola, atatu mwa atsogoleri makumi atatu anabwera kwa Davide ku phanga la Adulamu, pamene gulu la Afilisti linali litamanga misasa mʼchigwa cha Refaimu. 14Nthawi imeneyo Davide anali mu linga, ndipo boma la Afilisti linali ku Betelehemu. 15Davide analakalaka madzi ndipo anati, “Haa, pakanapezeka munthu wokanditungira madzi a mʼchitsime chomwe chili pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu!” 16Choncho anthu amphamvu atatuwa anadutsa mizere ya Afilisti, natunga madzi amene anali mʼchitsime chomwe chinali pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu nabwera nawo kwa Davide. Koma iye anakana kumwa. Mʼmalo mwake anathira pansi pamaso pa Yehova. 17Iye anati, “Inu Yehova, musalole kuti ine ndichite chinthu ichi! Kodi awa si magazi a anthu amene anayika miyoyo yawo pachiswe?” Ndipo Davide sanamwe madziwo.

Zimenezi ndi zimene anachita anthu amphamvu atatuwo.

18Abisai mʼbale wa Yowabu mwana wa Zeruya ndiye anali mtsogoleri wa anthu atatuwa. Iye anapha ndi mkondo ankhondo 300, choncho iyeyo anali wotchuka pakati pa anthu atatu aja. 19Kodi iyeyo sanali wolemekezeka koposa? Iye anakhala mtsogoleri wawo ngakhale kuti sanali mʼgulu la anthu atatu aja.

20Benaya mwana wa Yehoyada wa ku Kabizeeli anali munthu wolimba mtima amene anachita zinthu zamphamvu. Iye anakantha ankhondo awiri otchuka a ku Mowabu. Tsiku lina kukuzizira kwambiri, iye analowa mʼdzenje ndi kuphamo mkango. 21Ndipo iye anakanthanso Mwigupto wamkulu msinkhu. Ngakhale kuti Mwiguptoyo anali ndi mkondo mʼdzanja mwake, Benaya anapita kukamenyana naye ali ndi chibonga chokha mʼmanja. Iye analanda mkondo mʼdzanja la Mwiguptoyo ndi kumupha ndi mkondo wake womwe. 22Izi ndi zamphamvu zimene Benaya mwana wa Yehoyada anachita. Iyeyo analinso wotchuka ngati anthu atatu amphamvu aja. 23Iye ankalemekezedwa kuposa wina aliyense mwa anthu makumi atatu aja, koma sanali mʼgulu la anthu atatu aja. Ndipo Davide anamuyika kukhala woyangʼanira asilikali omuteteza.

24Mʼgulu la anthu makumi atatu aja munalinso awa:

Asaheli mʼbale wa Yowabu,

Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu,

25Sama Mharodi,

Elika Mherodi,

26Helezi Mpaliti,

Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa,

27Abiezeri wa ku Anatoti,

Sibekai Mhusati,

28Zalimoni Mwahohi,

Maharai Mnetofa,

29Heledi mwana wa Baana Mnetofa,

Itai mwana wa Ribai wa ku Gibeya ku Benjamini,

30Benaya Mpiratoni,

Hidayi wa ku zigwa za Gaasi.

31Abi-Aliboni Mwaribati,

Azimaveti Mbarihumi,

32Eliyahiba Msaaliboni,

ana a Yaseni,

Yonatani, 33mwana wa Sama Mharari,

Ahiamu mwana wa Sarari Mharari,

34Elifeleti mwana wa Ahasibai Mmaakati,

Eliamu mwana wa Ahitofele Mgiloni,

35Heziro wa ku Karimeli,

Paarai Mwaribi,

36Igala mwana wa Natani wa ku Zoba,

mwana wa Hagiri,

37Zeleki Mwamoni,

Naharai wa ku Beeroti, mnyamata wonyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya,

38Ira Mwitiri,

Garebu Mwitiri,

39ndi Uriya Mhiti.

Onse pamodzi analipo 37.